Yehova Ali Wamkulu Kuposa Mitima Yathu
Yehova Ali Wamkulu Kuposa Mitima Yathu
“YEHOVA akondwera nawo akumuopa Iye,” analemba motero wamasalmo. Zoonadi, Mlengi amasangalala kuona aliyense wa atumiki ake aumunthu akuchirikiza mwakhama mikhalidwe yake yolungama. Mulungu amadalitsa okhulupirika onse, kuwalimbikitsa, ndiponso kuwatonthoza nthaŵi zamavuto. Amadziŵa kuti omulambira ake ndi opanda ungwiro, ndiyetu amawaganizira pa zimene amayembekeza kwa iwo.—Salmo 147:11.
Sikungakhale kovuta kwa ife kukhulupirira kuti Yehova amakonda atumiki ake. Komabe, ena amaoneka kukhala odera nkhaŵa kwambiri ndi zolakwa zawo moti amakhulupirira kuti Yehova sangawakonde. Anganenetse kuti: “Ndine wochimwa kwambiri
moti Yehova sangandikonde.” N’zoona kuti tonsefe timakhala ndi maganizo otivutitsa nthaŵi ndi nthaŵi. Koma ena amakhala akulimbana nthaŵi zonse ndi maganizo odziona kukhala osafunika.Kudzimva Kukhala Osafunika
M’nthaŵi za Baibulo ena mwa anthu okhulupirika anavutika chifukwa cha kudzimva kukhala osafunika. Yobu ananyansidwa ndi moyo moti anaganiza kuti Mulungu anali atam’taya. Hana, amene anadzakhala mayi wa Samueli, nthaŵi inanso anapsinjika maganizo chifukwa chosoŵa mwana ndipo analira kwambiri. Davide nayenso anati “ndawerama kwakukulu,” ndiponso Epafrodito anapsinjika maganizo chifukwa chakuti mbiri yakudwala kwake inavutitsa abale ake.—Salmo 38:6; 1 Samueli 1:7, 10; Yobu 29:2, 4, 5; Afilipi 2:25, 26.
Bwanji nanga kwa Akristu lerolino? Mwina matenda, ukalamba, kapena mikhalidwe yaumwini ingalepheretse ena kuchita mmene akufunira mu utumiki wopatulika. Zimenezi zingawapangitse kuganiza kuti akulephera kukondweretsa Yehova pamodzi ndi okhulupirira anzawo. Mwinanso ena angakhale akudziimba mlandu mosalekeza chifukwa cha zolakwa zakale, n’kumakayikira ngati Yehova anawakhululukiradi. N’kuthekanso kuti ena amene akuchokera ku mabanja omwe kale anali ndi mavuto angakhulupirire kuti safunikira kukondedwa. Kodi izi n’zotheka motani?
Ena anakulira m’mabanja osakhala ndi mzimu wachikondi, mabanja okonda kunyozana, ndi okhalitsana mwa mantha. Otero sangadziŵe mmene amakhalira tate amene amawakonda, amene amawayamikira ndi kuwalimbikitsa, amene amanyalanyaza zolakwa zazing’ono ndipo amakhala okonzeka kukhululukira ngakhale zolakwa zazikulu, ndiponso amene khalidwe lake limapangitsa banja lonse kumva kukhala lotetezeka. Ndiye popeza sanakhalepo ndi tate wowakonda padzikoli, kungakhale kowavuta kukhulupirira zakuti kuli Tate wachikondi wakumwamba.
Mwachitsanzo, Fritz analemba kuti: “Pa ubwana ndi unyamata wanga ndinakhudzidwa kwambiri ndi mkhalidwe wopanda chikondi wa atate wanga. * Sanandiyamikireko, ndipo sindinamve kuti ndimawakonda. Kunena zoona, nthaŵi zambiri ndinkawaopa.” Ndiye chotsatira chake, Fritz, amene tsopano ali ndi zaka za m’ma 50, amadzimvabe kukhala wopereŵera penapake. Ndipo Margarette akufotokoza kuti: “Makolo anga anali osachezeka ndiponso opanda chikondi. Pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo, kunali kovuta kuyerekeza mmene tate wachikondi alili.”
Pazifukwa zosiyanasiyana, kuganiza kotere kungatanthauze kuti sititumikira Mulungu chifukwa cha kumukonda, koma kwenikweni chifukwa cha maganizo odziimba mlandu ndi mantha. Zabwino zonse zomwe timachita zimaoneka zosakwanira. Chikhumbo chofuna kusangalatsa Yehova ndi okhulupirira anzathu chingatipangitse kumva ngati sitikupanga zinthu mmene tifunikira kuchitira. Chotsatira chake, tingalephere kukwaniritsa zolinga zathu, n’kudziimba mlandu, komanso kudzimva kukhala opereŵera.
Zikatero ndiye titani? Mwinamwake tingachite bwino kudzikumbutsa za ukulu wa chifundo cha Yehova. Munthu amene anamvetsa chikondi cha Mulungu anali mtumwi Yohane.
“Mulungu Ali Wamkulu Woposa Mitima Yathu”
Kumapeto kwa zaka za zana loyamba C.E., Yohane analembera okhulupirira anzake kuti: “Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m’choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake, m’mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.” N’chifukwa chiyani Yohane analemba mawu ameneŵa?—1 Yohane 3:19, 20.
Mwachionekere Yohane anadziŵa kuti n’kotheka kwa mtumiki wa Yehova kudzimva kukhala wolakwa mu mtima. Mwinanso Yohane anakhalako ndi maganizo otero. Ali mnyamata wa mtima wapachala, Yohane panthaŵi ina anadzudzulidwapo ndi Yesu Kristu chifukwa chochita mwa udyo ndi ena. Ndipotu Yesu anawatcha Yohane ndi mbale wake Yakobo kuti “Boanerge ndiko kuti, Ana a bingu.”—Marko 3:17; Luka 9:49-56.
Patapita zaka 60, Yohane anafatsa n’kukhala wachikatikati, wachikondi, komanso Mkristu wachifundo. Pa nthaŵi imene iye, monga mtumwi womalizira, analemba kalata yake yoyamba youziridwa, anadziŵa kuti Yehova sasamala cholakwa chaching’ono china chilichonse chimene atumiki ake achita. M’malo mwake, amakhala Tate wabwino, wachikondi, wopatsa, wachifundo, amene ali ndi chikondi chenicheni pa onse amene amam’konda ndi kum’lambira m’choonadi. Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.
Yehova Amasangalala ndi Zimene Timam’chitira
Mulungu amadziŵa zofooka zathu zobadwa nazo ndi zophophonya zathu, ndipo amakumbukira zimenezi. “Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi,” analemba motero Davide. Yehova amadziŵa mmene gwero lathu limatikhudzira. Kwenikweni, amatidziŵa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziŵira.—Salmo 103:14.
Amadziŵa kuti ambiri timafuna kuchita zabwino, koma timalephera chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu. Mkhalidwe wathu ungafanizidwe ndi wa mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichita.” Tonsefe timalimbana ndi vuto lofananalo. Ndipo nthaŵi zina zingatipangitse kukhala ndi mtima wodziimba mlandu.—Aroma 7:19.
Nthaŵi zonse kumbukirani kuti: Chofunika choposa mmene timadzionera ife eni, ndi mmene Yehova amationera. Nthaŵi zonse akationa tikuyesa kum’sangalatsa, amasangalala osati mokhutira pang’ono chabe koma ndi chimwemwe. (Miyambo 27:11) Ngakhale kuti zimene tingakwanitse zingaoneke kukhala zochepa kwa ife, kufunitsitsa kwathu ndi zolinga zathu zabwino zimam’kondweretsa. Amaona mopitirira zimene timakwanitsa, amazindikira zimene tikufuna kuchita; amadziŵa zofuna ndi zokhumba zathu. Yehova amatha kudziŵa za mumtima mwathu.—Yeremiya 12:3; 17:10.
Mwachitsanzo, Mboni za Yehova zambiri mwachibadwa ndi zamantha ndi zofatsa, anthu amene sakonda kukopa chidwi cha anthu ambiri. Kwa anthu otere, kulalikira uthenga wabwino nyumba ndi nyumba kungakhale kovuta. Komatu, chifukwa chosonkhezeredwa ndi chikhumbo chofuna kutumikira Mulungu ndi kuthandiza anansi awo, ngakhale amanyaziwo amaphunzira kufikira anansi awo ndi kukambirana nkhani za m’Baibulo. Angamve kuti akukwaniritsa zochepa, ndipo izi zingawalande chimwemwe chawo. Mtima wawo ungawauze kuti utumiki wawo ndiwopanda phindu. Koma Yehova amasangalala ndi zoyesayesa zamphamvu zimene otere amapanga mu utumiki wawo. Kuwonjezera apo, sangatsimikize kuti ndi liti kapena n’kuti kumene mbewu za choonadi zidzamera, zidzakula ndi kubala zipatso.—Mlaliki 11:6; Marko 12:41-44; 2 Akorinto 8:12.
Mboni zina zimavutika ndi matenda osatha kapena ukalamba. Kwa amenewo, kupezeka pamisonkhano pa Nyumba za Ufumu mokhazikika kungakhale kovuta chifukwa cha kupweteka kwa m’thupi ndi nkhaŵa zina. Kumvetsera nkhani zonena za ntchito yolalikira kungawakumbutse zimene ankachita ndi zimene afunikira kuchita, ngakhale kuti zoofoka za m’thupi zikuwalepheretsa. Oterowo angakhale akudziimba mlandu chifukwa sakutha kutsatira uphungu ngati mmene akufunira. Komatu Yehova amayamikira kukhulupirika ndi kupirira kwawo. Malinga ngati akhalabe okhulupirika, Yehova saiŵala mbiri ya kukhulupirika kwawo.—Salmo 18:25; 37:28.
“Tidzakhazikitsa Mtima Wathu Pansi”
Panthaŵi imene Yohane anafika pa ukalamba, ayenera kuti anamvetsa kwambiri kukoma mtima kwa Mulungu. Kumbukirani kuti analemba kuti: “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu.” Kuwonjezera apo, Yohane anatilimbikitsa kuti “tidzakhazikitsa mitima pansi.” Kodi Yohane anatanthauzanji ponena mawu ameneŵa?
Malinga ndi kunena kwa Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words, mneni wachigiriki wotembunizidwa kuti “khazikitsa” amatanthauza “kukopa, kum’gonjetsa kapena kum’pambana, kum’pangitsa kukumvetsetsa.” Kunena kwina, kuti tikhazikitse mtima wathu, tifunikira kuugonjetsa, kuukopa, kuupangitsa kumvetsetsa ndi kukhulupirira kuti Yehova amatikonda. Koma motani?
Fritz wotchulidwa poyambayo m’nkhani ino, watumikira monga mkulu mumpingo wa Mboni za Yehova kwa zaka zopitirira 25 ndipo wapeza kuti phunziro laumwini lam’limbikitsa mtima za chikondi cha Yehova. “Ndimaŵerenga Baibulo ndi zofalitsa zathu kaŵirikaŵiri komanso mosamalitsa. Izi zimandithandiza kusaika malingaliro anga pa zinthu zakale koma kukhala ndi chithunzi
chabwino cha m’tsogolo. Nthaŵi zina, ndimakumbukiradi zakale ndipo ndimamva ngati kuti Mulungu sangandikonde. Koma mokulira, ndimapeza kuti phunziro lokhazikika limalimbikitsa mtima wanga, limawonjezera chikhulupiriro ndiponso limandithandiza kukhala wosangalala ndi wokhazikika.”Inde, kuŵerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha sikungasinthe mkhalidwe wathu weniweni. Komatu lingasinthe mmene timaonera mkhalidwe wathu. Kutenga maganizo m’Mawu a Mulungu n’kuwaika mu mtima wathu kungatithandize kumvetsa za kukoma mtima kwake. Kuwonjezera apo, phunziro limatithandiza kukula m’kumvetsa kukoma mtima kwa Mulungu. Ndiyetu pang’onopang’ono tingafike povomereza kuti Yehova sangalephere kutikonda chifukwa cha mkhalidwe wathu wa paubwana ndiponso chifukwa cha zofooka zathu za m’thupi. Amadziŵa kuti mtolo wa zothetsa nzeru zambiri zomwe timanyamula kaya zikhale zamaganizo kapena zathupi, sizikhala zoziyambitsa ife eni nthaŵi zambiri ndipo mwachikondi amaziganizira.
Nanga bwanji Margarette wotchulidwa poyambirira uja? Pamene anadziŵa Yehova, kuphunzira Baibulo kunamuthandiza kwambiri. Mofanana ndi Fritz, anafunikira kusintha kaonedwe kake ka tate. Pemphero linam’thandiza Margarette kumvetsa zimene anali kuŵerenga pa phunziro lake. Margarette anati: “Poyambirira ndimam’tenga Yehova kukhala bwenzi lapamtima, chifukwa ndimadziŵa kwambiri za mabwenzi kusiyana ndi tate wachikondi. Pang’onopang’ono, ndinaphunzira kum’sezetsa Yehova nkhaŵa zanga, zikayikiro, madandaulo ndi mavuto. Mobwerezabwereza ndinayamba kulankhula naye m’pemphero, nthaŵi yofananayo ndinayamba kusonkhanitsa pamodzi zinthu zatsopano zimene ndimaphunzira za iye, ngati mmene misiri waluso amasonkhanitsira mitundu yosiyanasiyana ya utoto n’kupanga chithunzi chokongola. Patapita nthaŵi, malingaliro anga pa Yehova anakula pamlingo wakuti tsopano sindipeza vuto kumuona ngati Tate wachikondi.”
Kumasulidwa ku Nkhaŵa Zonse
Malinga ngati dziko loipali likhalapobe, palibe angayembekezere kumasuka ku nkhaŵa zake. Kwa Akristu ena, izi zimatanthauza kuti maganizo odandaula kapena odzikayikira angamabuke mobwerezabwereza n’kupangitsa kusweka mtima. Koma tikhale otsimikiza mtima kuti Yehova amadziŵa zolinga zathu ndi ntchito yaikulu imene timachita mu utumiki wake. Sadzaiwala chikondi chimene timaonetsa chifukwa cha dzina lake.—Ahebri 6:10.
M’dziko lapansi latsopano likubwerali pansi pa Ufumu wa Umesiya, anthu onse okhulupirika angayembekezere kumasulidwa ku mtolo wamavuto a dongosolo la Satanali. Kudzakhala kumasuka kosangalatsa zedi! Ndiyetu tidzakhala ndi umboni wokwanira kuona mmene kukoma mtima kwa Yehova kulili. Kufikira nthaŵi imeneyo, tiyeni tonse titsimikizire kuti Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.”—1 Yohane 3:20.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Mayina asinthidwa.
[Mawu Otsindika patsamba 30]
Yehova sali wankhanza koma wachikondi, wokoma mtima ndi Tate wachifundo
[Chithunzi patsamba 31]
Kuphunzira Mawu a Mulungu kumatithandiza kuganiza mofanana naye