Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani ndi Chikhulupiriro M’mawu Aulosi a Mulungu!

Khalani ndi Chikhulupiriro M’mawu Aulosi a Mulungu!

Khalani ndi Chikhulupiriro M’mawu Aulosi a Mulungu!

“Tili nawo mawu a chinenero [“aulosi,” NW] okhazikika koposa.”​—2 PETRO 1:19.

1, 2. Kodi ulosi woyambirira kulembedwa unali uti, ndipo limodzi mwa mafunso omwe unabutsa ndi lotani?

YEHOVA ndiye amene anali Gwero la ulosi woyambirira kulembedwa. Adamu ndi Hava atachimwa, Mulungu anauza njoka kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:1-7, 14, 15) Panadutsa zaka mazana ambiri tanthauzo la mawu aulosi amenewo lisanadziŵike kwenikweni.

2 Ulosi woyambirirawo unapereka chiyembekezo chenicheni ku mtundu wa anthu auchimo. Pambuyo pake Malemba anatcha Satana Mdyerekezi kukhala “njoka yokalambayo.” (Chivumbulutso 12:9) Komano kodi Mbewu ya Mulungu yolonjezedwayo anali yani?

Kufunafuna Mbewu

3. Kodi Abele anasonyeza motani chikhulupiriro pa ulosi woyambirirawo?

3 Mosiyana ndi atate wake, Abele woopa Mulunguyo anasonyeza kukhulupirira ulosi woyambirirawo. Mwachionekere Abele anazindikira kuti mwazi unayenera kukhetsedwa kuti uphimbe machimo. Chotero chikhulupiriro chinam’sonkhezera kupereka nsembe ya nyama yomwe Mulungu anaivomereza. (Genesis 4:2-4) Komabe woimira Mbewu yolonjezedwayo sanali kum’dziŵabe.

4. N’lonjezo lotani lomwe Mulungu anapatsa Abrahamu, ndipo kodi linasonyeza chiyani ponena za Mbewu yolonjezedwayo?

4 Zaka ngati 2,000 kuchokera m’tsiku la Abele, Yehova anapatsa kholo lakalelo Abrahamu lonjezo laulosi lakuti: “Kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, . . . m’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:17, 18) Mawu amenewo anagwirizanitsa Abrahamu ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi woyambirira uja. Mawuŵa anasonyeza kuti Mbewu imene inali kudzawononga kotheratu ntchito za Satana inali kudzaonekera mu mzera wobadwira wa Abrahamu. (1 Yohane 3:8) “Poyang’anira lonjezo la Mulungu [Abrahamu] sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira” chimodzimodzinso mboni zina za Yehova zomwe zinaliko Chikristu chisanayambe zimene ‘sizinalandira lonjezanolo.’ (Aroma 4:20, 21; Ahebri 11:39) M’malo mwake, anakhulupirirabe Mawu aulosi a Mulungu.

5. Kodi lonjezo la Mulungu la Mbewu linakwaniritsidwa mwa yani, ndipo n’chifukwa chiyani mukuyankha motero?

5 Mtumwi Paulo anasonyeza Mbewu yolonjezedwa ya Mulungu pamene analemba kuti: “Malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Sanena, ‘Ndipo kwa zimbewu,’ ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbewu yako, ndiye Kristu.” (Agalatiya 3:16) Mbewu yomwe mitundu inali kudzadalitsidwa nayo sinaphatikize mbadwa zonse za Abrahamu. Mbadwa za mwana wake Ismayeli ndi za ana ake omwe Ketura anam’balira sizinagwiritsidwe ntchito kudalitsa mtundu wa anthu. Mbewu ya madalitso inabwera kudzera mwa mwana wake Isake ndi mdzukulu wake wamwamuna Yakobo. (Genesis 21:12; 25:23, 31-34; 27:18-29, 37; 28:14) Yakobo anasonyeza kuti “anthu” adzamvera Silo wa fuko la Yuda, koma pambuyo pake zinaonekeratu kuti Mbewuyo idzachokera m’mbadwo wa Davide wokha. (Genesis 49:10; 2 Samueli 7:12-16) Ayuda a m’zaka za zana loyamba anayembekezera munthu mmodzi kudza monga Mesiya, kapena Kristu. (Yohane 7:41, 42) Ndipo ulosi wa Mulungu wa Mbewu unakwaniritsidwa mwa Mwana wake, Yesu Kristu.

Mesiya Aonekera!

6. (a) Kodi ulosi wa masabata 70 tiyenera kuumva motani? (b) Ndi liti ndipo ndi motani mmene Yesu ‘anatsirizira machimo’?

6 Mneneri Danieli analemba ulosi wofunika kwambiri wa Umesiya. M’chaka choyamba cha Dariyo m’Medi, iye anazindikira kuti kukhala kwa Yerusalemu zaka 70 ali wabwinja kunali kuyandikira mapeto ake. (Yeremiya 29:10; Danieli 9:1-4) Danieli ali m’kati mopemphera, mngelo Gabrieli anadza ndi kum’vumbulira kuti ‘masabata makumi asanu ndi aŵiri alamulidwira kutsiriza machimo.’ Mesiyayo anali kudzalikhidwa m’kati mwa sabata la 70. “Masabata makumi asanu ndi aŵiri azaka” anayamba m’chaka cha 455 B.C.E. pamene Mfumu ya Perisiya Aritasasta I ‘anatumiza munthu kukamanganso Yerusalemu.’ (Danieli 9:20-27; Nehemiya 2:1-8) Mesiya anali kudza pambuyo pa milungu 7 kuphatikiza milungu 62. Zaka zimenezi zokwana 483 zinayamba m’chaka cha 455 B.C.E kukafika mu 29 C.E., pomwe Yesu anabatizidwa ndipo Mulungu anam’dzoza kukhala Mesiya, kapena kuti Kristu. (Luka 3:21, 22) Yesu ‘anatsiriza machimo’ mwa kupereka moyo wake dipo m’chaka cha 33 C.E. (Marko 10:45) N’chifukwatu chabwino kwabasi chokhalira ndi chikhulupiriro m’mawu aulosi a Mulungu! *

7. Mwa kugwiritsa ntchito Malemba, sonyezani mmene Yesu anakwaniritsira ulosi wa Umesiya.

7 Kukhulupirira Mawu aulosi a Mulungu kumatitheketsa kum’dziŵa bwino Mesiya. Mwa maulosi ambirimbiri a Umesiya olembedwa m’Malemba Achihebri, ambiri a iwo anagwiritsidwa ntchito mwachindunji ndi olemba Malemba Achigiriki Achikristu ponena za Yesu. Mwachitsanzo: Yesu anabadwa kwa namwali mu Betelehemu. (Yesaya 7:14; Mika 5:2; Mateyu 1:18-23; Luka 2:4-11) Anaitanidwa atuluke m’Aigupto, ndipo makanda anaphedwa iyeyu atangobadwa. (Yeremiya 31:15; Hoseya 11:1; Mateyu 2:13-18) Yesu ananyamula zowawa zathu. (Yesaya 53:4; Mateyu 8:16, 17) Monga kunanenedweratu, iye analoŵa m’Yerusalemu atakwera pa bulu. (Zekariya 9:9; Yohane 12:12-15) Mawu a wamasalmo anakwaniritsidwa pambuyo pa kupachikidwa kwa Yesu pamene asilikali anagaŵana zovala zake mwa iwo okha ndi kuchitira maere pa malaya ake. (Salmo 22:18; Yohane 19:23, 24) Kusathyoledwa kwa mafupa a Yesu ndi kupyozedwa kwake zinakwaniritsanso ulosi. (Salmo 34:20; Zekariya 12:10; Yohane 19:33-37) Izitu n’zochepa chabe mwa zitsanzo zambiri za maulosi a Umesiya omwe olemba Baibulo ouziridwa ndi Mulungu analemba ponena za Yesu. *

Tamandani Mfumu ya Umesiya!

8. Kodi Nkhalamba Yakale lomwe ndani, ndipo kodi ulosi wolembedwa pa Danieli 7:9-14 unakwaniritsidwa motani?

8 M’chaka choyamba cha Mfumu ya Babulo, Belisazara, Yehova anapatsa mneneri wake Danieli loto ndi masomphenya ochititsa chidwi zedi. Mneneriyu choyamba anaona zilombo zikuluzikulu zinayi. Mngelo wa Mulungu anazitcha “mafumu anayi,” chotero anasonyeza kuti izo zikuimira maufumu otsatizana amphamvu kwambiri padziko lapansi. (Danieli 7:1-8, 17) Kenako Danieli anaona Yehova, “Nkhalamba yakale lomwe” atakhala mwaulemerero pampando wachifumu. Poŵeruza zilombozo mozikhaulitsa, iye anazilanda ulamuliro ndipo anawononga chilombo chachinayicho. Ulamuliro wosatha pa “anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu ndi a manenedwe onse” anaupereka kwa “wina ngati mwana wa munthu.” (Danieli 7:9-14) Umenewu ndi ulosi wosangalatsa zedi wonena za kulongedwa ufumu kwa “Mwana wa munthu,” Yesu Kristu, kumwamba m’chaka cha 1914!​—Mateyu 16:13.

9, 10. (a) Ziŵalo zosiyanasiyana za fano la m’loto zinali kuimira chiyani? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa Danieli 2:44 mungakulongosole motani?

9 Danieli anadziŵa kuti Mulungu ‘akuchotsa mafumu, nalonga mafumu.’ (Danieli 2:21) Ndi chikhulupiriro mwa Yehova, “Wakuvumbulutsa zinsinsi” mneneriyu anamasulira tanthauzo la maloto a fano lalikulu a Mfumu Nebukadinezara ya Babulo. Ziŵalo zake zosiyanasiyana zinaimira kuyamba ndi kugwa kwa maulamuliro amphamvu padziko lapansi monga Babulo, Amedi ndi Aperisi, Girisi, ndi Roma. Mulungu anagwiritsanso ntchito Danieli kulongosola zochitika m’dziko m’nthaŵi yathu ino komanso m’tsogolo.​—Danieli 2:24-30.

10 “Masiku a mafumu aja” umatero ulosiwo, “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) “Nthaŵi zawo za anthu akunja” zitatha m’chaka cha 1914, Mulungu anakhazikitsa Ufumu kumwamba muulamuliro wa Kristu. (Luka 21:24; Chivumbulutso 12:1-5) M’mphamvu ya Mulungu “mwala” Ufumu wa Umesiya unasemedwa mu “phiri” la ulamuliro wa Mulungu wa chilengedwe chonse. Pa Armagedo mwala umenewu udzatswanya fanolo ndi kulipera ngati ufa. Ufumu wa Umesiya womwe udzakhala monga boma longa phiri lokuta “dziko lonse lapansi,” udzakhala kosatha.​—Danieli 2:35, 45; Chivumbulutso 16:14, 16. *

11. Kusandulika kwa Yesu kunali chitsanzo cha chiyani, ndipo kodi masomphenya amenewo anam’khudza motani Petro?

11 Ali ndi malingaliro a ulamuliro wa Ufumuwo m’maganizo mwake, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Alipo ena a iwo aima pano sadzalaŵa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wake.” (Mateyu 16:28) Atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane, napita nawo paphiri lalitali komwe iye anasandulika pamaso pawo. Mtambo wowala utaphimba atumwiwo, Mulungu ananena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” (Mateyu 17:1-9; Marko 9:1-9) Chitsanzotu cha ulemelero wa Ufumu wa Kristu wochititsa chidwi! Ndiye chifukwa chake Petro ananena za masomphenya ochititsa chidwiwo kuti: “Ndipo tili nawo mawu a chinenero okhazikika koposa.”​—2 Petro 1:16-19. *

12. N’chifukwa chiyani ino kwenikweni ilidi nthaŵi yakuti tisonyeze chikhulupiriro chathu m’mawu aulosi a Mulungu?

12 Mwachionekere “mawu aulosi” akuphatikizapo osati kokha Malemba Achihebri aulosi onena za Mesiya komanso mawu a Yesu akuti akadza “ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:30) Kusandulikako kunatsimikizira mawu aulosi onena za kudza kwa ulemerero kwa Kristu mumphamvu ya Ufumu. Posachedwapa, vumbulutso lake mu ulemerero lidzatanthauza chiwonongeko kwa opanda chikhulupiriro ndiponso madalitso kwa amene akusonyeza chikhulupiriro. (2 Atesalonika 1:6-10) Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa m’Baibulo kukusonyeza kuti ano ndiwo “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5, 16, 17; Mateyu 24:3-14) Monga Wakupha Wamkulu wa Yehova, Mikaeli, yemwe ndi Yesu Kristu, wakonzeka kudzetsa mapeto a dongosolo loipali la zinthu m’kati mwa “chisautso chachikulu.” (Mateyu 24:21; Danieli 12:1) Chotero ino ndiyodi nthaŵi yosonyeza kuti tili nacho chikhulupiriro m’mawu aulosi a Mulungu.

Khalanibe ndi Chikhulupiriro M’Mawu Aulosi a Mulungu

13. Kodi n’chiyani chomwe chingatithandize kum’kondabe Mulungu ndi kusunga chikhulupiriro chathu pa mawu ake chili cha moyo?

13 Ndithudi tinali achimwemwe kumva kwanthaŵi yoyamba za kukwaniritsidwa kwa Mawu aulosi a Mulungu. Koma kuchokera pa nthaŵi imeneyo kodi chikhulupiriro chathu chafooka ndipo kodi chikondi chathu chazirala? Tisakhaletu ngati Akristu a ku Efeso omwe ‘anataya chikondi chawo choyamba.’ (Chivumbulutso 2:1-4) Kaya tatumikira Yehova kwa utali wotani, nafenso tingataye chikondi chathu pokhapokha ‘titathanga tafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa ife.’ (Mateyu 6:19-21, 31-33) Kuphunzira Baibulo mwakhama, kutenga mbali mokhazikika pamisonkhano yachikristu, ndi kulalikira za Ufumu mwachangu zidzatithandiza kukhalabe ndi chikondi pa Yehova, pa Mwana wake, ndi pa Malemba. (Salmo 119:105; Marko 13:10; Ahebri 10:24, 25) Ndiyeno zimenezi zidzatithandiza kusunga chikhulupiriro chathu pa Mawu a Mulungu chili chamoyo.​—Salmo 106:12.

14. Kodi Akristu odzozedwa akufupidwa motani kaamba ka chikhulupiriro chawo m’mawu aulosi a Yehova?

14 Mongatu momwe Mawu aulosi a Mulungu anakwaniritsidwira m’mbuyomu, chotero ifenso tingakhale ndi chikhulupiriro pa zomwe ananeneratu kuti zidzachitika m’tsogolo. Mwachitsanzo, kukhalapo kwa Kristu mu ulemerero wa Ufumu tsopano n’chochitika chenicheni, ndipo Akristu odzozedwa omwe anakhalabe okhulupirika kufikira imfa aona kukwaniritsidwa kwa malonjezo aulosi akuti: “Kwa iye amene alakika ndidzam’patsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m’paradaiso wa Mulungu.” (Chivumbulutso 2:7, 10; 1 Atesalonika 4:14-17) Yesu wapatsa olakika ameneŵa mwayi wa “kudya za ku mtengo wa moyo” mu “paradaiso wa Mulungu” wakumwamba. Pa chiukiriro chawo ndiponso kupyolera mwa Yesu Kristu, iwo amavala matupi osafa ndi osavunda opatsidwa ndi Yehova, “Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha.” (1 Timoteo 1:17; 1 Akorinto 15:50-54; 2 Timoteo 1:10) Ilitu mphotho yaikulu zedi imeneyo kaamba ka chikondi chawo chosafa cha pa Mulungu ndi chikhulupiriro chosagwedera m’mawu ake aulosi!

15. Kodi maziko a “dziko lapansi latsopano” anayalidwa mwa yani, nanga anzawo ndani?

15 Posapita nthaŵi pambuyo pakuti odzozedwa okhulupirika omwalirawo aukitsidwira ku “paradaiso wa Mulungu” kumwamba, otsalira a Israyeli wauzimu padziko lapansi anatuluka kuchoka mu “Babulo Wamkulu,” ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 14:8; Agalatiya 6:16) Mwa iwo munayalidwa maziko a “dziko latsopano.” (Chivumbulutso 21:1) Choncho “dziko” linabadwa, ndipo linamangidwa kukhala paradaiso wauzimu yemwe ali padziko lonse lapansi lerolino. (Yesaya 66:8) Makamu aakulu a mabwenzi onga nkhosawo a Israyeli wauzimu akusonkhaniramo tsopano lino, mu “masiku otsiriza.”​—Yesaya 2:2-4; Zekariya 8:23; Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9.

Tsogolo la Mtundu wa Anthu Linenedweratu M’Mawu Aulosi a Mulungu

16. Kodi ziyembekezo za ochirikiza okhulupirika a odzozedwa n’zotani?

16 Kodi n’ziyembekezo zotani zomwe othandizana ndi odzozedwa okhulupirika ali nazo? Nawonso ali ndi chikhulupiriro m’mawu aulosi a Mulungu, ndipo chiyembekezo chawo ndicho cha kudzaloŵa m’paradaiso wa padziko lapansi. (Luka 23: 39-43) Mmenemo iwo adzamwa madzi ochirikiza moyo ochokera mu “mtsinje wa madzi a moyo” ndipo adzachiritsidwa ndi “masamba a mtengo” wodzalidwa m’mphepete mwake. (Chivumbulutso 22:1, 2) Ngati inu muli ndi chiyembekezo chabwino choterocho, pitirizanibe kusonyeza chikondi chakuya kwa Yehova ndi chikhulupiriro m’mawu ake aulosi. Khalani mmodzi wa awo amene amapeza chimwemwe chosefukira cha moyo wosatha m’dziko lapansi la Paradaiso.

17. Kodi moyo m’Paradaiso wa padziko lapansi udzaphatikiza madalitso otani?

17 Anthu opanda ungwiro akulephera kulongosola mokwanira momwe moyo udzakhalira m’paradaiso wa padziko lapansi akudzayo, koma mawu aulosi a Mulungu akutipatsa chidziŵitso cha madalitso omwe mtundu wokhulupirika wa anthu ukuyembekezera. Pamene Ufumu wa Mulungu udzalamulira popanda kutsutsidwa ndipo chifuno chake chitachitidwa padziko lapansi monga kumwamba, sikudzakhalanso anthu olusa ayi, ngakhale nyama zolusa sizidzakhalako ‘sizidzaipitsa kapena kusakaza.’ (Yesaya 11:9; Mateyu 6:9, 10) Ofatsa adzalandira dziko lapansi, “nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:11) Sikudzakhalanso aliyense wovutika ndi njala, chifukwa chakuti “m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” (Salmo 72:16) Misozi ya chisoni siidzakhetsedwanso. Sikudzakhalanso matenda, ndipo ngakhale imfa siidzakhalako. (Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4) Tangolingalirani! Kudzakhala kulibe madokotala, mankhwala, zipatala kapena malo osungira anthu odwala matenda a m’maganizo, sikudzakhalanso maliro. N’chiyembekezo chabwino bwanji!

18. (a) Kodi Danieli anam’tsimikizira za chiyani? (b) N’chiyani chomwe chidzakhala “gawo” la Danieli?

18 Ngakhale manda a mtundu wa anthu adzakhala pululu pamene imfa idzaloŵedwa m’malo ndi chiukiriro. Munthu wangwiroyo Yobu anali ndi chiyembekezo chofananacho. (Yobu 14:14, 15) Zinalinso chimodzimodzi ndi mneneri Danieli, potitu mngelo wa Yehova anam’patsa chilimbikitso chotonthoza chakuti: “Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.” (Danieli 12:13) Danieli anatumikira Mulungu mokhulupirika kufikira mapeto a moyo wake. Tsopano iye akupumula mu imfa, koma ‘adzaima’ pa “kuuka kwa olungama” mu Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi. (Luka 14:14) Kodi Danieli “gawo” lake lidzakhala chiyani? Chabwino, m’kukwaniritsidwa kwake kwa Paradaiso, ulosi wa Ezekieli ukusonyeza kuti anthu onse a Yehova adzakhala nawo malo, ngakhalenso dziko logaŵidwa mwachilungamo ndi mwadongosolo. (Ezekieli 47:13–48:35) Choncho Danieli adzakhala ndi malo m’Paradaiso, koma choloŵa chakecho m’menemo chidzaphatikiza zambiri osati dziko lokhalo. Chidzaphatikiza malo ake m’chifuno cha Yehova.

19. Kodi chofunika n’chiyani kuti tidzakhale ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi?

19 Bwanji nanga inuyo ndi gawo lanu? Ngati muli ndi chikhulupiriro m’Mawu a Mulungu, Baibulo, mwachidziŵikire mukufuna moyo m’dziko lapansi la Paradaiso. Mwinamwake mungamalingalire muli m’dziko limenelo, mukusangalala ndi madalitso ake ambirimbiri, mukusamalira dziko lapansi, komanso mukulandira anthu oukitsidwa. Kwenikweni, Paradaiso ndiko kwawo kwa mtundu wa anthu. Mulungu analenga anthu aŵiri oyambawo kuti akhale m’malo oterowo. (Genesis 2:7-9) Ndipo akufuna anthu omvera kuti adzakhale kosatha m’Paradaiso. Kodi mudzachita zinthu mogwirizana ndi Malemba kotero kuti mukhale mmodzi wa mabiliyoni ambiri omwe posachedwapa adzakhale m’dziko lapansi la Paradaiso? Mungadzakhalemo ngati muli ndi chikondi choona pa Atate wathu wakumwamba, Yehova, ndi chikhulupiriro chopirira m’mawu aulosi a Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani mutu 11 m’buku lakuti Pay Attention to Daniel’s Prophecy! ndi mutu wakuti “Seventy Weeks” mu Insight on the Scriptures, ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

^ ndime 7 Onani buku la “All Scriptures Is Inspired of God and Beneficial,” masamba 343-4, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

^ ndime 10 Onani mutu 4 ndi 9 wa buku lakuti Pay Attention to Daniel’s Prophecy!

^ ndime 11 Onani nkhani ya mutu wakuti “Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu,” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2000.

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi ulosi woyambirira unali woti chiyani, ndipo ndani yemwe anali Mbewu yolonjezedwa?

• Ndi maulosi ena ati a Umesiya omwe anakwaniritsidwa mwa Yesu?

• Kodi Danieli 2:44, 45 adzakwaniritsidwa motani?

• Mawu aulosi a Mulungu amanena za tsogolo lotani kwa mtundu wa anthu womvera?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi muli n’chiyembekezo chodzakhala m’Paradaiso padziko lapansi?