Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu a M’tsiku Lathu

Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu a M’tsiku Lathu

Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu a M’tsiku Lathu

“Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthaŵi ya chimaliziro.”​—DANIELI 8:17.

1. Kodi Yehova akufuna kuti mtundu wonse wa anthu udziŵe chiyani ponena za tsiku lathu?

YEHOVA sabisa chidziŵitso cha zimene zidzachitika m’tsogolo. M’malo mwake, iye ali Wovumbula zinsinsi. Ndithudi, iye akufuna kuti tonsefe tidziŵe kuti tikukhala m’kati mwenimweni mwa “nthaŵi ya chimaliziro.” Imeneyotu ndi nkhani yofunika kwambiri kwa anthu mabiliyoni asanu ndi limodzi omwe akukhala padziko lapansi tsopano lino!

2. N’chifukwa chiyani anthu akudera nkhaŵa za tsogolo la mtundu wa anthu?

2 Kodi n’zodabwitsa kuti dzikoli layandikira mapeto ake? Munthu angayende pamwezi, koma m’mayiko ambiri sangayende mopanda mantha m’misewu ya padziko lino lapansi. Munthu angadzaze nyumba yake ndi katundu wamakono, koma sangachepetse vuto lomwe likuwonjezerekali la kusweka kwa mabanja. Munthu angayambitse nyengo ya makompyuta, koma sangaphunzitse anthu kukhala pamodzi mwamtendere. Kulephera konseku kukuchirikiza umboni wochuluka wa m’Malemba wakuti tikukhala m’nthaŵi ya chimaliziro.

3. Ndi liti pamene mawu akuti “nthaŵi ya chimaliziro” anatchulidwa kwa nthaŵi yoyamba padziko lapansi?

3 Mawu ochititsa chidwi amenewo, akuti “nthaŵi ya chimaliziro,” anatchulidwa kwa nthaŵi yoyamba pano padziko lapansi ndi mngelo Gabrieli zaka pafupifupi 2,600 zapitazo. Mneneri wa Mulungu, mantha atam’gwira, anamva Gabrieli akumuuza kuti: “Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthaŵi ya chimaliziro.”​—Danieli 8:17.

Ino Ndiyo “Nthaŵi ya Chimaliziro”!

4 Kodi Baibulo limatchula za nthaŵi ya chimaliziro m’njira zina ziti?

4 Mawu akuti ‘nthaŵi ya chimaliziro’ ndiponso akuti “nthaŵi yoikika [“ya chimaliziro,” NW]” amapezeka kasanu ndi kamodzi m’buku la Danieli. (Danieli 8:17, 19; 11:35, 40; 12:4, 9) Akusimba za “masiku otsiriza” amene mtumwi Paulo ananeneratu. (2 Timoteo 3:1-5) Yesu Kristu anatchula nyengo yomweyi kuti ndiyo nyengo ya “kukhalapo” kwake monga Mfumu yoikidwa pampando kumwamba.​—Mateyu 24:37-39, NW.

5, 6. Kodi ndani omwe akhala ‘akuthamanga chauko ndi chauko’ m’nthaŵi ya chimaliziro, ndipo ndi zotsatira zotani?

5 Danieli 12:4 amati: “Koma iwe Danieli, tsekera mawu aŵa, nukhomere chizindikiro buku, mpaka nthaŵi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziŵitso chidzachuluka.” Zambiri zimene Danieli analemba zinakhalabe chinsinsi moti anthu sanazizindikire kwa zaka mazana ambiri. Komano bwanji lerolino?

6 M’nthaŵi ino ya chimaliziro, Akristu ambiri okhulupirika akhala ‘akuthamanga chauko ndi chauko’ m’masamba a Mawu a Mulungu, Baibulo. Zotsatira zake? Chifukwa chakuti Yehova wadalitsa kuyesayesa kwawo, chidziŵitso choona chawachulukira. Mwachitsanzo, Mboni zodzozedwa za Yehova zadalitsidwa ndi luntha, kuwatheketsa kuzindikira kuti Yesu Kristu anakhala Mfumu yakumwamba m’chaka cha 1914. Mogwirizana ndi mawu a mtumwi olembedwa pa 2 Petro 1:19-21, odzozedwa ameneŵa limodzi ndi mabwenzi awo okhulupirika, ‘akulabadira mawu aulosi’ ndipo n’ngotsimikizira kotheratu kuti inoyi ndiyo nthaŵi ya chimaliziro.

7. Ndi nkhani zina ziti zomwe zimapanga buku la Danieli kukhala lapadera?

7 Buku la Danieli, n’lapadera m’njira zingapo. M’masamba ake, mfumu ikufuna kupha amuna ake anzeru chifukwa alephera kuvumbula ndi kumasulira loto lake lothetsa nzeru, koma mneneri wa Mulungu wakhoza kumuuza ndi kum’tanthauzira. Anyamata atatu amene akana kulambira fano lalitali aponyedwa m’ng’anjo ya moto yotentha koopsa, komabe atulukamo osawauka ngakhale tsitsi limodzi. Phwando lina lili m’kati, anthu ambirimbiri akuona dzanja likulemba mawu ozizwitsa pakhoma la nyumba ya mfumu. Anthu ena oipa achita chiwembu chakuti mwamuna wina wokalamba aponyedwe m’dzenje la mikango, koma mwamunayo akutulukamo wosakandika ngakhale pang’ono. Pakuoneka zilombo zinayi m’masomphenya, ndipo tanthauzo lake laulosi likufika mpaka mu nthaŵi ya chimaliziro.

8, 9. Kodi buku la Danieli lingatipindulitse motani, makamaka tsopano lino, m’nthaŵi ya chimaliziro?

8 Mwachionekere, buku la Danieli lili ndi mitundu iŵiri ya nkhani zosiyana kwambiri. Woyamba ndi wosimba zochitika, wachiŵiri ndi ulosi. Mitundu yonse iŵiri ingalimbitse chikhulupiriro chathu. Nkhani zosimba zochitikazo zikutisonyeza kuti Yehova Mulungu amadalitsa amene amakhalabe okhulupirika kwa iye. Ndipo magawo amaulosiwo amalimbitsa chikhulupiriro mwa kusonyeza kuti Yehova amadziŵiratu mmene zinthu zidzachitikira zaka mazana ambiri ngakhale zaka zikwi zambiri m’tsogolo.

9 Maulosi osiyanasiyana amene Danieli analemba akunena za Ufumu wa Mulungu. Tikamaona maulosi ameneŵa akukwaniritsidwa, chikhulupiriro chathu chimalimba, komanso timakhutira kuti tikukhaladi m’nthaŵi ya chimaliziro. Koma anthu ena amam’tsutsa Danieli akumanena kuti maulosi amene ali m’buku la dzina lakewo kwenikweni analembedwa zinthuzo zimene zinaoneka ngati zikuwakwaniritsa zitachitika kale. Ngati zimenezo zili zoona, pangabuke mafunso ovuta okhudza zimene buku la Danieli linaneneratu za nthaŵi ya chimaliziro. Anthu okayikira nawonso amatsutsa ngakhale nkhani zochitikadi zosimbidwa m’bukumo. Choncho, tiyeni tifufuze.

Kuzengedwa Mlandu!

10. Kodi buku la Danieli likuzengedwa mlandu m’lingaliro lotani?

10 Tayerekezani kuti muli m’bwalo lamilandu, mukumvetsera wina akuzengedwa mlandu. Ndiyeno loya waboma akuumirira kuti munthuyo ali ndi mlandu wochita chinyengo. Ndithudi, buku la Danieli limadzisonyeza lokha kukhala buku lodalirika lolembedwa ndi mneneri wachihebri amene anakhalako pakati pa zaka za m’ma 600 ndi m’ma 500 B.C.E. Komabe, otsutsawo akunenetsa kuti bukulo n’lonyenga. Choncho tiyeni tione choyamba ngati nkhani zosimbidwa m’bukulo zikugwirizana ndi zochitika m’mbiri.

11, 12. Kodi chinachitika n’chiyani pa chinenezo chakuti Belisazara anali munthu wongopeka?

11 Tinene kuti tikukamba nkhani imene ingatchedwe mlandu wa mfumu yosoŵeka. Danieli chaputala 5 chikusonyeza kuti Belisazara anali kulamulira monga mfumu ku Babulo pamene mzindawo unagwetsedwa mu 539 B.C.E. Otsutsa anakana mfundo imeneyo chifukwa chakuti dzina la Belisazara silinali kupezeka m’buku lina lililonse kupatulapo m’Baibulo. M’malo mwake, olemba mbiri akale ananena kuti Nabonidasi ndiye anali mfumu yomaliza ya Babulo.

12 Komabe, m’chaka cha 1854, anakumba zolembapo zadongo zing’onozing’ono m’mabwinja a mzinda wakale wa Uri ku Babulo, mu Iraq wamakono. Pa zolemba zozokota zimenezo palinso pemphero limene Mfumu Nabonidasi anatchulamo za “Bel-sar-ussur, mwana wanga wamkulu.” Ngakhale anthu otsutsawo sakanachitira mwina koma kuvomereza kuti: Ameneyu anali Belisazara wa m’buku la Danieli. Choncho mfumu yosoŵeka imeneyo siinasoŵe n’komwe, kungoti sinadziŵikebe m’mabuku enawo. Umenewu ndi umodzi chabe wa maumboni ambirimbiri osonyeza kuti zimene Danieli analemba n’zenizenidi. Umboniwu ukusonyeza poyera kuti buku la Danieli lilidi mbali ya Mawu a Mulungu omwe tiyeneradi kuwalabadira mosamalitsa tsopano lino, m’nthaŵi ino ya chimaliziro.

13, 14. Kodi Nebukadinezara anali yani, ndipo ndi mulungu wonyenga uti amene iye kwenikweni ankamulambira kotheratu?

13 Mbali yaikulu m’buku la Danieli ndiyo maulosi onena za kubwera ndi kupita kwa maulamuliro a dziko lonse ndi zochita zina za olamulira ake. Mmodzi wa olamulirawo angatchedwe wankhondo yemwe anamanga ufumu. Monga kalonga woloŵa ufumu wa Babulo, iyeyu ndi gulu lake lankhondo anagonjetsa kotheratu magulu ankhondo a Farao Neko wa ku Igupto, ku Karikemisi. Koma uthenga umene kalonga wa Babulo wogonjetsayo analandira unam’kakamiza kusiya zotsala zonse m’manja mwa akazembe ake ankhondo. Atamva za imfa ya Nabopolasara atate wake, mnyamatayo wotchedwa Nebukadinezara anakhala pa mpando wachifumu mu 624 B.C.E. M’zaka 43 za ulamuliro wake, anamanga ufumu umene unalanda madera amene pa nthaŵi inayake anali m’manja mwa Asuri, ndipo iyeyu anafutukula malire a ufumu wake ndi kufika ku Suriya ndi ku Palestina mpaka kumalire a Igupto.

14 Nebukadinezara anali kulambira kwambiri Maduki, mulungu wamkulu wa ku Babulo. Mfumuyo imakhulupirira kuti Maduki ndiye amene anali kum’thandiza kuti apambane m’nkhondo zake zonse. M’Babulomo, Nebukadinezara anamanga ndi kukongoletsa akachisi a Maduki ndi a milungu inanso yambiri yachibabulo. Mwina fano lagolidi limene mfumu ya Babulo inaimika m’chigwa cha Dura linali la Maduki yemweyo. (Danieli 3:1, 2) Ndipo zikuoneka kuti Nebukadinezara anali kudalira matsenga kwambiri pokonzekera zankhondo.

15, 16. Kodi Nebukadinezara anachitira Babulo chiyani, ndipo n’chiyani chinachitika pamene iye anadzitama chifukwa cha ukulu wake?

15 Mwa kutsiriza kumanga makoma aakulu aŵiriaŵiri a Babulo amene atate wake anali atayamba kumanga, Nebukadinezara anaupanga mzinda waukuluwo kuoneka ngati wosagonjetseka. Pofuna kusangalatsa mfumukazi yake ya ku Mediya, imene inkalakalaka kwambiri mapiri ndi nkhalango zakwawo, Nebukadinezara akuti anamanga minda yolenjekeka ya maluŵa, yomwe ndi chimodzi mwa zinthu zisanu ndi ziŵiri zodabwitsa kwambiri za m’nthaŵi yakaleyo. Anapanga Babulo kukhala mzinda waukulu kwambiri wokhala ndi malinga masiku amenewo. Ndipotu iye anali kunyadira kwambiri malo amenewo komwe chipembedzo chonyenga chinali chitakhazikika!

16 Tsiku lina Nebukadinezara anadzitama kuti: “Suyu Babulo wamkulu ndinam’manga?” Komabe, malinga ndi kunena kwa Danieli 4:30-36, “akali m’kamwa mwa mfumu mawu aŵa,” anachita misala. Kwa zaka zisanu ndi ziŵiri zomwe sanalinso wokhoza kulamulira, anadya udzu, monga momwedi Danieli anali ataneneratu. Kenako ufumu wakewo unabwezeretsedwa. Kodi mukudziŵa kuti ulosi umenewu ukutanthauzanji? Kodi mungafotokoze mmene kukwaniritsidwa kwake kwakukulu kukutifikitsira m’nthaŵi ya chimaliziro?

Kusonkhanitsa Nkhosi za Ulosi

17. Kodi maloto a ulosi omwe Mulungu analotetsa Nebukadinezara m’chaka chachiŵiri cha ufumu wake monga wolamulira dziko lonse mungawalongosole motani?

17 Tsono tiyeni tisonkhanitse zina mwa nkhosi za ulosi wa m’buku la Danieli. M’chaka chachiŵiri cha kulamulira kwa Nebukadinezara monga wolamulira wa dziko lonse wa muulosi wa m’Baibulo (606/605 B.C.E.), Mulungu anam’lotetsa loto loopsa. Malinga ndi Danieli chaputala 2, lotolo linali la fano lalikulu lokhala ndi mutu wagolidi, chifuŵa chake ndi manja ake zasiliva, mimba yake ndi chuuno chake zamkuwa, miyendo yake yachitsulo, ndipo mapazi ake osakanikirana mwina chitsulo mwina dongo. Kodi ziŵalo zosiyanasiyanazo za fanolo zinali kuimira chiyani?

18. Kodi mutu wa golide, chifuŵa ndi manja zasiliva, komanso mimba ndi chuuno zamkuwa, za fano la m’lotolo zinali kuimira chiyani?

18 Mneneri wa Mulungu anauza Nebukadinezara kuti: “Inu mfumu, . . . inu ndinu mutuwo wagolidi.” (Danieli 2:37, 38) Nebukadinezara ndiye anali woyamba pa mndandanda wa mafumu omwe analamulira mu Ufumu wa Babulo. Ufumuwo unagwetsedwa ndi Amedi ndi Aperisi, oimiridwa ndi chifuŵa ndi manja zasiliva za fanolo. Kenaka kunadza Ufumu wa Girisi, woimiridwa ndi mimba ndi chuuno zamkuwa. Kodi ulamuliro wamphamvu padziko lonse umenewo unayamba bwanji?

19, 20. Kodi Alesandro Wamkulu anali yani, ndipo kodi anachitanji popanga Girisi kukhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse?

19 M’zaka za zana lachinayi B.C.E., wachinyamata wina anachita mbali yofunika kwambiri pakukwaniritsidwa kwa ulosi wa Danieli. Anabadwa mu 356 B.C.E., ndipo dziko linam’tcha Alesandro Wamkulu. Atate wake, Filipo, ataphedwa mu 336 B.C.E., Alesandro wazaka 20 zakubadwa analoŵa ufumu wa Makedoniya.

20 Kuchiyambiyambi kwa mwezi wa May mu 334 B.C.E., Alesandro anayamba ndawala yogonjetsa adani. Anali ndi gulu lankhondo laling’ono koma lamphamvu la asilikali oyenda pansi okwana 30,000 ndi ena okwera akavalo okwana 5,000. Pamtsinje wa Grunicus kumpoto chakumadzulo kwa Asia Minor (amene panopo ndi Turkey), Alesandro anapambana nkhondo yake yoyamba kumenyana ndi Aperisi m’chaka cha 334 B.C.E. Pomafika chaka cha 326 B.C.E., msilikali wosagonjetseka ameneyu anagonjetsa Aperisi ndipo anapitirizabe mpaka kum’maŵa cha ku Mtsinje wa Indus, womwe uli m’dziko la Pakistan wamakono. Koma Alesandro anagonja pankhondo yake yotsirizira ku Babulo. Pa June 13, 323 B.C.E., atangokhala moyo zaka 32 ndi miyezi 8 zokha, iye anagonjetsedwa ndi mdani woopsa kwambiri, imfa. (1 Akorinto 15:55) Komabe, pogonjetsa mayiko enawo, dziko la Girisi linakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse, monga mmene ulosi wa Danieli unaneneratu.

21. Kuwonjezera pa Ufumu wa Roma, kodi ndi ulamuliro wina uti wamphamvu padziko lonse umene ukuimiridwa ndi miyendo yachitsulo ya fano la m’loto?

21 Kodi miyendo yachitsulo ya fano lalikululo ikuimira chiyani? Eya, inaimira Roma wonga chitsulo amene anaphwanya ndi kuwononga Ufumu wa Girisi. Posonyeza kusalemekeza Ufumu wa Mulungu womwe Yesu Kristu anali kulalikira, Aroma anamupha pamtengo wozunzirapo mu 33 C.E. Pofuna kuthetseratu Chikristu choona, Roma anazunza ophunzira a Yesu. Komabe, miyendo yachitsulo ya fano la m’loto la Nebukadinezara sinaimire Ufumu wa Roma wokha, komanso mphukira yake yandale​—Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa America ndi Britain.

22. Kodi fano la m’loto likutithandiza motani kuona kuti tili m’kati mwenimweni mwa nthaŵi ya chimaliziro?

22 Kupenda mosamalitsa kukusonyeza kuti tilidi m’kati mwenimweni mwa nthaŵi yachimaliziro, popeza kuti tsopano tafika ku mapazi achitsulo ndi dongo a fanolo. Maboma ena amakono ali ngati chitsulo kapena kuti n’ngopondereza, pamene ena ali ngati dongo. Ngakhale kuti dongo ndi losalimba, komwenso “ana a anthu wamba” anapangidwako, maulamuliro onga chitsulo akakamizika kwambiri kupatsa anthu wamba ufulu wolankhula m’maboma owalamulira. (Danieli 2:43; Yobu 10:9) Komatu palibe kugwirizana kwenikweni pakati pa ulamuliro wopondereza ndi anthu wamba monga mmene chitsulo sichingagwirizanire ndi dongo. Koma Ufumu wa Mulungu posachedwapa uthetsa dziko landale logamphukagamphukali.​—Danieli 2:44.

23. Kodi maloto ndi masomphenya za Danieli m’chaka choyamba cha ulamuliro wa Belisazara mungazifotokoze motani?

23 Chaputala 7 cha ulosi wochititsa chidwi wa Danieli chikutifikitsanso mu nthaŵi ya chimaliziro. Chaputala chimenechi chikunena zimene zinachitika m’chaka choyamba cha Mfumu Belisazara ya Babulo. Panthaŵi imeneyo ali m’zaka zake za m’ma 70, Danieli “anaona loto, naona masomphenya a m’mtima mwake pakama pake.” Masomphenya amenewo anamuopsa zedi! “Taonani,” iye anafuula motero. Mphepo zinayi za mumlengalenga zinabuka panyanja yaikulu. Ndipo zinatuluka m’nyanja zilombo zazikulu zinayi zosiyanasiyana.” (Danieli 7:1-8,15) Zilombo zochititsadi nthumanzi! Choyamba ndicho mkango wokhala ndi mapiko, ndipo chachiŵiri chili ngati chimbalangondo. Kenaka pakubwera nyalugwe wokhala ndi mapiko anayi ndi mitu inayi! Chilombo chachinayi champhamvu zedi chili ndi mano achitsulo ndi nyanga khumi. Pakati pa nyanga zake khumi pakumera nyanga yaing’ono yokhala ndi “maso ngati maso a munthu” ndi “pakamwa palikunena zazikulu.” N’zilombotu zoopsa kwabasi!

24. Malinga n’kunena kwa Danieli 7:9-14, kodi Danieli anaonanji kumwamba, ndipo kodi masomphenya ameneŵa akunena za chiyani?

24 Kenako masomphenya a Danieli akum’sonyeza kumwamba. (Danieli 7:9-14) “Nkhalamba yakale lomwe,” Yehova Mulungu, akuoneka atakhala mwaulemerero pa mpando wachifumu monga Woweruza. ‘Zikwizikwi akum’tumikira, ndi unyinji wosaŵerengeka ukuima pamaso pake.’ Poweruza zilombozo mozikhaulitsa, Mulungu akuzilanda ulamuliro ndipo akuwononga chilombo chachinayicho. Ndiyeno ulamuliro wosatha pa “anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu ndi a manenedwe onse” akuupereka kwa “wina ngati mwana wa munthu.” Zimenezi zinali kusonya ku ‘nthaŵi ya chimaliziro’ ndi kulongedwa ufumu kwa Mwana wa munthu, Yesu Kristu, m’chaka cha 1914.

25, 26. Ndi mafunso ati omwe angabuke pamene tiŵerenga buku la Danieli, ndipo n’chofalitsa chiti chomwe chingatithandize kuwayankha?

25 Aliyense amene adzaŵerenga buku la Danieli mwachionekere adzakhala ndi mafunso ambirimbiri. Mwachitsanzo, Kodi zilombo zinayi za mu Danieli chaputala 7 zikuimira chiyani? Kodi ulosi wonena za masabata “makumi asanu ndi aŵiri,” wotchulidwa pa Danieli 9:24-27 ungafotokozedwe motani? Bwanji nanga za Danieli chaputala 11 ndi ulosi wa mkangano wa “mfumu ya kumpoto” ndi wa “mfumu ya kumwera”? Kodi tingayembekezere chiyani mwa mafumu ameneŵa mu nthaŵi ya chimaliziro?

26 Yehova wapereka chidziŵitso m’nkhani ngati zimenezi kwa atumiki ake odzozedwa padziko lapansi, “opatulika a Wam’mwambamwamba,” monga momwe akuwatchulira pa Danieli 7:18. Ndiponso, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapanga dongosolo lakuti tonsefe tipeze chidziŵitso chowonjezereka cha malembo ouziridwa a mneneri Danieli. (Mateyu 24:45) Chimenechitu tilinachodi tsopano kupyolera m’kutulutsidwa kwa buku latsopano la mutu wakuti Pay Attention to Daniel’s Prophecy! Buku lazithunzithunzi zokongola limeneli la masamba 320 likukhudza mbali iliyonse ya m’buku la Danieli. Likusimba ulosi uliwonse wolimbitsa chikhulupiriro ndiponso nkhani iliyonse imene mneneri wokondedwayo Danieli analemba.

Tanthauzo Lenileni Kaamba ka Tsiku Lathu

27, 28. (a) Kodi zoona zake n’ziti za kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’buku la Danieli? (b) Kodi ifeyo tikukhala m’nyengo iti, ndipo kodi tiyenera kuchita chiyani?

27 Talingalirani mfundo yofunika iyi: Maulosi onse a m’buku la Danieli akwaniritsidwa kale, kusiyapo mfundo zoŵerengeka chabe. Mwachitsanzo, tsopano tikuona kuti zinthu padzikoli zili monga momwe zikusonyezedwera ndi miyendo ya fano la m’maloto a m’Danieli chaputala 2. Chitsa cha mtengo wa m’Danieli chaputala 4 chinachotsedwa mikombero yake pamene Mfumu ya Umesiya, Yesu Kristu, inakhala pampando wachifumu kumwamba mu 1914. Inde, malinga ndi ulosi wa m’Danieli chaputala 7, Nkhalamba Yakale Lomwe kenako inapatsa Mwana wa munthu ulamuliro.​—Danieli 7:13, 14; Mateyu 16:27–17:9.

28 Masiku 2,300 a m’Danieli chaputala 8 ndi masiku 1,290 ndiponso masiku 1,335 a m’chaputala 12, onsewo anapita​—kale kwambiri mbuyomo. Tikafufuza Danieli chaputala 11, tipeza kuti kulimbana pakati pa “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwera” kwatsala pang’ono kutha. Zonsezi zikusonyeza umboni wa m’Malemba wakuti tikukhaladi mu nthaŵi ya chimaliziro. Polingalira malo athu apadera m’nthaŵi imene tafika ino, kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani? Mosakayikira, tiyenera kulabadira mawu aulosi a Yehova Mulungu.

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi Mulungu akufuna kuti mtundu wonse wa anthu udziŵe chiyani ponena za tsiku lathu?

• Kodi buku la Danieli lingalimbitse motani chikhulupiriro chathu?

• Kodi fano la m’loto la Nebukadinezara linali ndi zigawo zooneka motani, ndipo kodi zimenezi zikuimira chiyani?

• N’chiyani chomwe chili chofunika kudziŵa ponena za kukwaniritsidwa kwa maulosi opezeka m’buku la Danieli?

[Mafunso]