Mauthenga Abwino—Mkangano Wake Ukupitirirabe
Mauthenga Abwino—Mkangano Wake Ukupitirirabe
Kodi nkhani za kubadwa kwa Yesu Kristu za m’Mauthenga Abwino n’zoonadi?
Kodi anachitadi Ulaliki wa pa Phiri?
Kodi Yesu anaukitsidwadi?
Kodi ananenadi kuti: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo”?—Yohane 14:6.
AKATSWIRI pafupifupi 80 akambirana nkhani ngati zimenezi pa Msonkhano wa Yesu, umene wakhala ukuchitidwa kaŵiri pachaka kuyambira mu 1985. Gulu limeneli la akatswiri layankha mafunso ameneŵa m’njira yachilendo. Osonkhanawo aponya voti pa mawu alionse omwe Mauthenga Abwino amati ndi mawu a Yesu. Pepala la voti lofiira limasonyeza lingaliro lakuti mawuwo anatchulidwadi ndi Yesu. Pepala lofiirira pang’ono limatanthauza kuti mawuwo akungofanana ndi mawu amene mwina Yesu anatchulapo. Pepala lotuwa limasonyeza kuti malingalirowo angafananeko ndi a Yesu, koma sindiye anatchula mawu enieniwo. Pepala lakuda n’losonyeza kukaniratu, lonena kuti mawuwo anatengedwa kwa anthu ena nthaŵi ya Yesu itapita.
Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, osonkhana pa Msonkhano wa Yesu akana nkhani zonse zinayi zomwe zatchulidwa monga mafunso koyambirirako. Kwenikweni, 82 peresenti ya mawu amene Mauthenga Abwino amati ndi mawu a Yesu awaponyera voti lakuda. Malinga ndi akatswiriwo, 16 peresenti yokha ya zochitika zosimbidwa m’Mauthenga Abwino ndi m’zolembedwa zina ponena za Yesu n’zimene zikuoneka kukhala zoona.
Kutsutsa Mauthenga Abwino moteremu sikwachilendo. Kutsutsa Mauthenga Abwino kunaonekera mu 1774 pamene cholembedwa pamanja chamasamba 1,400 cholembedwa ndi Hermann Reimarus, pulofesa wa ku Hamburg, Germany, wa ziyankhulo za mayiko a Kum’maŵa, chinafalitsidwa iye atamwalira. M’cholembedwacho, Reimarus anasonyeza kukayikira kwakukulu ponena za mbiri yolembedwa m’Mauthenga Abwino. Zomwe anapeza zinazikidwa pa kufufuza chiyankhulo ndi nkhani za m’Mauthenga Abwino anayiwo zosimba za moyo wa Yesu zomwe zimaoneka ngati kuti zikutsutsana. Chiyambire nthaŵiyo, ofufuza nthaŵi zambiri asonyeza kukayikira zoti Mauthenga Abwino n’ngoona, kufooketsa chidaliro cha anthu ena m’zolembedwa zimenezi.
Akatswiri onseŵa ali ndi malingaliro amodzi ofanana: Amaona nkhani za m’Mauthenga Abwino ngati nthano zachipembedzo zolembedwa ndi anthu osiyanasiyana. Nthaŵi zonse mafunso amene akatswiri okayikiraŵa amafunsa ndi akuti: Kodi olemba Mauthenga Abwino anayiwo anawonjezapo malingaliro awo pa mfundo zenizenizo chifukwa cha zikhulupiriro zawo? Kodi ndale za m’nthaŵi ya Akristu oyambirirawo zinawapangitsa kusintha kapena kuwonjezeramo mfundo zina m’nkhani ya Yesu? Kodi ndi mbali ziti za Mauthenga Abwino zomwe zikusimba zochitika zenizeni ndipo osati nthano wamba?
Anthu omwe akulira pakati pa anthu okana kuti kuli Mulungu kapena ongosamala zochitika za dziko amakhulupirira kuti Baibulo, ndiponso Mauthenga Abwinowo, ndi buku longodzaza ndi nkhani zopeka ndi nthano wamba. Koma enanso amanyansidwa ndi mbiri ya Matchalitchi Achikristu ya kukhetsa magazi, kupondereza ena, kusagwirizana, ndi khalidwe losakhala laumulungu. Anthu ameneŵa saona chifukwa chilichonse chochitira chidwi ndi zolembedwa zomwe Matchalitchi Achikristu amati n’zopatulika. Amaona kuti zolembedwa zomwe zinapanga chipembedzo chachinyengo ziyenera kukhala nkhani zopeka.
Kodi inuyo mukuganizapo motani? Kodi muyenera kulola akatswiri ena amene amakayikira mbiri yolembedwa m’Mauthenga Abwino kukupangitsani kukhalanso ndi zikayiko zofananazo mumtima mwanu? Mukamva zonena zakuti olemba Mauthenga Abwino anangopeka nkhani zawo, kodi muyenera kulola zimenezi kugwedeza chidaliro chanu m’zolembedwa zawo? Kodi mbiri ya Matchalitchi Achikristu yosalemekeza Mulungu iyenera kukupangitsani kukayikira kudalirika kwa Mauthenga Abwino? Tikukupemphani kuti mufufuze mfundo zina.
[Chithunzi patsamba 4]
Kodi nkhani za m’Mauthenga Abwino n’zopeka kapena n’zochitika zenizeni?
[Mawu a Chithunzi]
Yesu akuyenda Panyanja/The Doré Bible Illustrations/Dover Publications
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Chithunzi chachikulu, masamba 3-5 ndi 8: Mwachilolezo cha Freer Gallery of Art, Smithsonian Institution, Washington, D.C.