Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tchinjiriza Mtima Wako”

“Tchinjiriza Mtima Wako”

“Tchinjiriza Mtima Wako”

YEHOVA anauza mneneri Samueli kuti: “Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) Ponenanso za mtima wophiphiritsa, wamasalmo Davide anaimba kuti: “Mwayesera mtima wanga [Yehova]; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu.”​—Salmo 17:3.

Inde, Yehova amayang’ana m’kati mwa mitima yathu ndi kuona tilidi otani. (Miyambo 17:3) Choncho, pachifukwa chabwino, Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inalangiza kuti: “Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Kodi tingautchinjirize motani mtima wathu wophiphiritsawo? Yankho pa funso limeneli timalipeza pa Miyambo chaputala chachinayi.

Mverani Mwambo wa Atate

Chaputala chachinayi cha Miyambo chimayamba ndi mawu akuti: “Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziŵe luntha; pakuti ndikuphunzitsani zabwino; musasiye chilangizo changa.”​Miyambo 4:1, 2.

Langizo kwa achinyamata n’lakuti atchere khutu ku uphungu wabwino wa makolo awo aumulungu, makamaka wa abambo awo. Bambo ali ndi udindo wa m’Malemba wopereka zofunika zakuthupi ndi zauzimu zabanja lake. (Deuteronomo 6:6, 7; 1 Timoteo 5:8) Popanda utsogoleri umenewo, kungakhale kovuta kwambiri kuti wachinyamata akule bwino ndi kukhwima! Choncho, kodi mwana sayenera kulandira mwaulemu mwambo wa atate wake?

Komabe, bwanji nanga za wachinyamata wopanda bambo wom’langiza? Mwachitsanzo, Jason wazaka khumi ndi chimodzi bambo wake anamwalira iye ali ndi zaka zinayi. * Wachikulire wachikristu atam’funsa za chimene chili vuto lake lalikulu kwambiri pamoyo wake, mwamsanga Jason anayankha kuti: “Vuto langa ndilo kusoŵa bambo. Nthaŵi zina zimandisautsa koopsa.” Komabe, langizo lotonthoza lilipo kaamba ka achinyamata omwe akusoŵa utsogoleri wa makolo. Jason ndi ana ena onga iye akhoza kufunsira ndi kulandira chilangizo cha atate kuchokera kwa akulu ndi achikulire ena mumpingo wachikristu.​—Yakobo 1:27.

Pokumbukira za kuphunzitsidwa kwake, Solomo akupitiriza kuti: “Ndinali mwana kwa atate wanga, wokondedwa ndi mayi, ndine ndekha, sanabala wina.” (Miyambo 4:3) Mwachionekere, mfumuyo inakumbukira kuti inaleredwa mwachikondi. Pokhala “mwana” amene anasamalira uphungu wa atate ndi mtima wonse, Solomo wachinyamatayo ayenera kuti anali paunansi woyandikana kwambiri ndi atate wake, Davide. Ndiponso, Solomo anali ‘iye yekha,’ kapena kuti wokondeka koposa. Motero, n’kofunika kwambiri kuti mwana akulire m’banja mmene mkhalidwe uli wachikondi, komanso mmene kulankhulana ndi makolo kumakhala komasuka!

Pezani Nzeru ndi Luntha

Pokumbukira uphungu wachikondi wa bambo wake, Solomo anati: “Nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mawu anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo. Tenga nzeru, tenga luntha; usaiŵale, usapatuke pa mawu a m’kamwa mwanga; usasiye nzeru, ndipo idzakusunga; uikonde, idzakutchinjiriza. Nzeru ipambana, tatenga nzeru; M’kutenga kwako konseko utenge luntha.”​Miyambo 4:4-7.

N’chifukwa chiyani “nzeru ipambana”? Nzeru imatanthauza kugwiritsa ntchito chidziŵitso ndi luntha m’njira yokhala ndi zotsatira zake zabwino. Chidziŵitso, ndicho kudziŵa kapena kuzoloŵera zoona zake mwa kuziona kapena kukumana nazo kapenanso mwa kuŵerenga ndi kuphunzira​—n’chofunika kwambiri popeza nzeru. Koma ngati sititha kuchigwiritsa bwino ntchito, chidziŵitso chathu chikakhala chopanda phindu lenileni. Sitiyenera kumangoŵerenga Baibulo nthaŵi zonse ndi zofalitsa zozikidwa pa Baibulo zoperekedwa ndi “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” koma tiyeneranso kuyesetsa kumagwiritsa ntchito zimene timaphunzira mmenemo.​—Mateyu 24:45.

Kupeza luntha n’kofunikanso kwambiri. Popanda luntha, kodi tingathe bwanji kuona mmene mfundo zimagwirizanirana ndi kutha kuona chithunzi chonse cha nkhaniyo? Ngati tisoŵa luntha, kodi tingathe bwanji kuzindikira zifukwa ndi mayankho pa zinthu? Inde, kuti tikathe kulumikiza mfundo zosiyanasiyana ndi kupeza mayankho, tifunikira luntha.​—Danieli 9:22, 23.

Solomo akupitiriza kusimba mawu a atate wake, akumati: “Uilemekeze [nzeru], ndipo idzakukweza; idzakutengera ulemu pamene uifungatira. Idzaika chisada cha chisomo pamtu pako; idzakupatsa kolona wokongola.” (Miyambo 4:8, 9) Nzeru yaumulungu imateteza amene aifungatira. Ndiponso, imam’tengera ulemu komanso imam’kongoletsa. Chifukwa chake, tiyenera kuchita chilichonse chotheka kuti tipeze nzeru.

“Gwira Mwambo”

Pomveketsa chilangizo cha atate wake, mfumu ya Israyeliyo inapitiriza ikumati: “Tamvera mwananga, nulandire mawu anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa m’njira ya nzeru, ndakuyendetsa m’mayendedwe olungama. Mapazi ako sadzawombana ulikuyenda; ukathamanga, sudzapunthwa. Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.”​Miyambo 4:10-13.

Monga mwana weniweni kwa bambo wake, Solomo ayenera kuti anazindikira phindu la uphungu wachikondi umene umaphunzitsa ndi kuwongolera. Popanda uphungu woyenerera, tingapite motani patsogolo ndi kufikira uchikulire wauzimu kapena tingayembekezere motani kukonza moyo wathu? Ngati sitiphunzirira pa zolakwa zathu kapena ngati tilephera kuwongola maganizo olakwika, kupita kwathu patsogolo mwauzimu kungakhale kosaphula kanthu. Chilangizo choyenerera chimadzetsa khalidwe laumulungu ndipo chimatithandiza ‘kuyenda m’mayendedwe olungama.’

Mtundu winanso wa chilangizo umatheketsanso ‘zaka za moyo wathu kuchuluka.’ Motani? Eya, Yesu Kristu anati: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m’chaching’onong’ono alinso wosalungama m’chachikulu.” (Luka 16:10) Kodi kudzilangiza tokha m’zinthu zazing’ono sikungatitheketse kuchita chimodzimodzi m’zinthu zazikulunso, zimene moyo wathu weniweniwo ungazidalire? Mwachitsanzo, kuphunzitsa diso kuti ‘lisamayang’ane mkazi mom’khumbitsa’ kudzatithandiza kusagonja ku chisembwere. (Mateyu 5:28) Mwachionekere, mfundo yachikhalidwe imeneyi imagwira ntchito kwa amuna ndi akazi omwe. Ngati tiphunzitsa maganizo athu ‘kugonjetsa ganizo lonse,’ sipadzakhala chiwopsezo chachikulu cha kuchita tchimo lalikulu m’mawu kapena m’zochita.​— 2 Akorinto 10:5.

Zoona, uphungu nthaŵi zambiri umakhala wovuta kuulandira ndipo ungaoneke ngati wotipanikiza pa ufulu wathu. (Ahebri 12:11) Komabe, mfumu yanzeruyo ikutitsimikizira kuti ngati tigwiritsa uphungu, mayendedwe athu adzakhala opita patsogolo. Monga momwe kukonzekera koyenerera kumatheketsera wampikisano wothamanga kuthamanga kwambiri popanda kugwa kapena kudzivulaza, kugwiritsa uphungu kumatitheketsa kuyendabe panjira ya kumoyo paliŵiro loyenerera popanda kupunthwa. Ndithudi, tiyenera kusankha bwino njira imene tikuitenga.

Peŵani “Njira ya Oipa”

Poona kufulumira kwa nthaŵi, Solomo akuchenjeza kuti: “Usaloŵe m’mayendedwe ochimwa, usayende m’njira ya oipa. Peŵapo, osapitamo; patukapo, nupitirire. Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tawo tiwachokera. Pakuti amadya chakudya cha uchimo, namwa vinyo wa chifwamba.”​Miyambo 4:14-17.

Anthu oipa, amene njira zawo Solomo akufuna kuti tizipeŵe, amakhalira moyo zochita zawo zonyansa. Kuchita choipa kuli ngati chakudya ndi chakumwa kwa iwo. Satha kugona popanda kuchita zachiwawa. Umunthu wawo weniweniwo ndi wopotoka! Kodi tingathedi kutchinjiriza mitima yathu ngati tiyanjana ndi anthu oterowo? Kupusa kwake nanga ‘kuyenda m’njira ya oipa’ mwa kuonerera chiwawa chosonyezedwa m’zosangalatsa zambiri za m’dziko lero! Kufuna kukhala wachifundo sikungayendere limodzi ndi kuonerera zochitika zoipa zakupha chikumbumtima za pawailesi yakanema.

Khalanibe M’kuunika

Pogwiritsabe ntchito chitsanzo cha njira, Solomo akunena kuti: “Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kumkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.” (Miyambo 4:18) Kuyamba kuphunzira Baibulo ndi kuyesetsa kugwiritsa ntchito m’moyo zimene limanena kungafanizidwe ndi kunyamuka ulendo mbandakucha. Pamene mdima wakumwamba ungoyamba kuchoka, sititha kuona chilichonse. Koma pamene kuŵala kuyamba kuonekera, pang’onopang’ono timayamba kuzindikira zinthu zotizinga. Pomalizira pake, dzuŵa limaŵala, ndipo timatha kuona chilichonse bwino lomwe. Inde, choonadi pang’onopang’ono chimayamba kuonekera bwino kwa ife pamene tilimbikira kuphunzira Malemba moleza mtima ndi mwakhama. Kudyetsa mtima wathu chakudya chauzimu n’kofunika kwambiri kuti tiutchinjirize ku malingaliro onyenga.

Tanthauzo kapena cholinga cha maulosi a Baibulo chikuvumbulukanso pang’onopang’ono. Maulosi akumka namvekera bwino kwa ife pamene mzimu woyera wa Yehova ukuwaunika ndi pamene akukwaniritsidwa ndi zochitika za dziko kapena mwa zimene anthu a Mulungu akukumana nazo. M’malo mwa kuti mwaphuma tiyambe kumaganizira patokha tanthauzo la kukwaniritsidwa kwake, tiyenera kuyembekeza ‘kuunika kwa mbandakucha kuti kuwalirewalirebe.’

Nanga bwanji za aja amene amakana utsogoleri wa Mulungu mwa kusafuna kuyenda m’kuunikako? “Njira ya oipa ikunga mdima; sadziŵa chimene chiwapunthwitsa,” anatero Solomo. (Miyambo 4:19) Anthu oipa ali ngati munthu amene apunthwa usiku koma osadziŵa chimene cham’punthwitsa. Ngakhale pamene anthu osapembedza angaoneke ngati zinthu zikuwayenera bwino chifukwa cha njira zawo zopanda chilungamo, kupambana kwawoko n’kwakanthaŵi chabe. Ponena za anthu oterowo, wamasalmo anaimba kuti: “Indedi muwaika poterera: [Inuyo Yehova] muwagwetsa kuti muwawononge.”​—Salmo 73:18.

Khalani Tcheru Nthaŵi Zonse

Mfumu ya Israyeliyo ikupitiriza kunena kuti: “Mwananga, tamvera mawu anga; tcherera makutu ku zonena zanga. Asachoke ku maso ako; uwasunge m’kati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lawo lonse. Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”​Miyambo 4:20-23.

Chitsanzo cha Solomo chimasonyeza phindu la kumvera uphungu wa kutchinjiriza mtima. Zoona, iye anakhaladi “mwana” womvera kwa bambo wake paunyamata wake ndipo anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova mpaka uchikulire wake. Komabe, Baibulo limasimba kuti: “Ndipo kunali, atakalamba Solomo, akazi ake [achilendo] anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.” (1 Mafumu 11:4) Popanda kukhala tcheru nthaŵi zonse, ngakhale mitima yabwino koposa inganyengedwe ndi kuchita choipa. (Yeremiya 17:9) Tiyenera kukonda zikumbutso za m’Mawu a Mulungu, tizisunge ‘m’kati mwa mitima yathu.’ Zimenezo zimaphatikizapo chilangizo chopezeka m’chaputala chachinayi cha Miyambo.

Pendani Mkhalidwe wa Mtima Wanu

Kodi timathadi kutchinjiriza mtima wathu wophiphiritsawo? Nanga mkhalidwe wa munthu wam’kati mwathu tingaudziŵe motani? Yesu Kristu anati: “M’kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.” (Mateyu 12:34) Iye anatinso: “Mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, zaumboni wonama, zamwano.” (Mateyu 15:19, 20) Inde, mawu ndi zochita zathu zimanena za mtima wathu.

Moyenerera, Solomo akutilangiza kuti: “Tasiya m’kamwa mokhota, uike patali milomo yopotoka. Maso ako ayang’ane m’tsogolo, zikope zako zipenye mowongoka. Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; njira zako zonse zikonzeke. Usapatuke ku dzanja lamanja kapena kulamanzere; suntha phazi lako kusiya zoipa.”​Miyambo 4:24-27.

Malinga ndi uphungu wa Solomo, tifunikira kupenda zolankhula ndi zochita zathu. Kuti titchinjirize mtima ndi kukondweretsa Mulungu, tiyenera kupeŵa malankhulidwe opotoka ndi machitidwe achinyengo. (Miyambo 3:32) Choncho, tiyenera kusinkhasinkha mwapemphero ndi kuona zimene mawu athu ndi zochita zathu zimavumbula ponena za ife. Tikatero, tipemphe chithandizo cha Yehova kotero kuti tikonze chofooka chilichonse chimene tingapeze.​—Salmo 139:23, 24.

Choposa zonse, ‘maso athu ayang’ane m’tsogolo.’ Tiwalunjikitse pa cholinga cha kutumikira Atate wathu wakumwamba ndi moyo wonse. (Akolose 3:23) Pamene mukulondola njira yolungama yoteroyo, Yehova akupatsenitu chipambano ‘m’njira zanu zonse,’ komanso akudalitseni kwambiri polabadira uphungu wouziridwa wa ‘kutchinjiriza mtima wanu.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Si dzina lake lenileni.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Kodi mumapeŵa zosangalatsa zosonyeza chiwawa?

[Chithunzi patsamba 21]

Pindulani ndi uphungu wa achikulire

[Chithunzi patsamba 23]

Chilango sichibweza m’mbuyo

[Chithunzi patsamba 24]

Limbikirani kuphunzira Baibulo