Kodi Malangizo Abwino Mungawapeze Kuti?
Kodi Malangizo Abwino Mungawapeze Kuti?
“Kulangiza mwaukatswiri” tsopano kwasanduka malonda opezetsa chuma chadzaoneni pachaka. Anthu akufunadi thandizo. Katswiri wina wa matenda a maganizo, Heinz Lehmann anati: [“M’chitaganya chamakono] maphunziro n’ngopereŵera ndipo mikhalidwe ya anthu yafika poipa zedi. Makhalidwe achipembedzo salinso monga momwe analili kale. Mabanja n’ngotekeseka . . . , ndipo chifukwa cha chimenecho anthu akuvutika kwambiri.” Wolemba mabuku wotchedwa Eric Maisel anati: “Awo amene nthaŵi inayake anatembenukira kwa alauli amatsenga, mkulu wa tchalitchi kapena dokotala wabanja kuti awathandize pa mavuto awo amaganizo, auzimu ndi akuthupi tsopano akufufuza mayankho m’mabuku opereka malangizo a momwe munthu angatukukire kapena kupita patsogolo.”
BUNGWE la American Psychological Association (Bungwe Loona za Mavuto a M’maganizo la ku America) linakhazikitsa gulu lapadera lofufuza mchitidwe womwe ukufalikirawu. Gulu lapaderali linati pamene kuli kwakuti pali “kuthekera konse kwakuti n’kuthandiza anthu kuzindikira umunthu wawo ndi wa ena . . . , mawu otsatsira malonda ndi mitu yotsatizana ndi mapulogalamu ameneŵa azikokomeza moŵirikiza ndipo azikometsera mopambanitsa.” Wolemba Toronto Star anati: “Chenjerani ndi aphungu ochuluka a zipembedzo zachinyengo zamizimu. . . . Chenjerani makamaka ndi mabuku, matepi kapena maphunziro othandiza munthu kudzithandiza yekha amene amalonjeza zochuluka monkitsa, pakanthaŵi kochepa zedi, popanda kuti muyesetse kwambiri kapena kudziletsa kwenikweni.” Zoona, alipo ena ambirimbiri amene akufunitsitsadi kuthandiza osoŵa chithandizo. Komabe, chomvetsa chisoni n’chakuti pali anthu opanda khalidwe ochuluka omwe akupezerapo mwayi pa kusukidwa ndi kuvutika kwa anthu, koma osapereka chithandizo chenicheni kapena njira zothetsera mavutowo.
Poona zochitika zimenezi, kodi ndi gwero lalikulu liti la chithandizo lomwe tingalikhulupirire? N’kuti kumene tingakapeze uphungu wothandiza womwe nthaŵi zonse ungagwiritsidwe ntchito?
Gwero la Chitsogozo Chosalephera
Mlaliki wa ku America wa m’zaka za m’ma 1800 Henry Ward Beecher anati: “Baibulo lili ngati mapu a Mulungu otsogolera woyendetsa chombo, kuti chombo chanu chisasweke, ndi kuti akusonyezeni kumene kuli gombe, ndiponso mmene mungafikire pagombepo popanda kuwomba matanthwe kapena ziunda.” Munthu winanso anati ponena za Baibulo: “Palibe amene angakule kuposa Malemba; bukulo limakula ndi kuzama m’kupita kwa zaka.” N’chifukwa chiyani mufunika kulingalira mosamalitsa za gwero limeneli?
Podzivomereza lokha Baibulo limati: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteo 3:16, 17) Mawu onse a m’Baibulo n’ngochokera ku Chitsime cha moyo chenichenicho, Yehova Mulungu. (Salmo 36:9) Chifukwa cha chimenecho, iye akudziŵa bwino lomwe mapangidwe athu, monga momwe Salmo 103:14 likutikumbutsira kuti: “Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” Chotero tingakhale ndi chidaliro chonse kuti Baibulo lidzatithandiza.
Ndithudi, Baibulo lili ndi mfundo zambirimbiri za makhalidwe abwino ndi malangizo oyenera kutsatira zomwe mungapindule nazo pozigwiritsa ntchito mu mkhalidwe wina uliwonse umene mungakhale. Kupyolera m’Baibulomo Mulungu akutiuza ife kuti: “Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo.” (Yesaya 30:21) Kodi Baibulo lingakwaniritsedi zosoŵa za anthu lerolino? Tiyeni tione.
Baibulo Limakwaniritsa Zosoŵa Zathu . . .
Popirira Nkhaŵa. Baibulo likutiuza kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Kodi pemphero lasonyeza kukhala lothandiza popirira nkhaŵa za maganizo zokhudza mavuto a zachuma, kugwiriridwa ndi kunyozedwa, kapena imfa ya wokondedwa? Talingalirani zochitika zotsatirazi.
Jackie, atamva za kugwiriridwa kwa mwana wake wamkazi, anavomereza kuti: “Kudziimba mlandu chifukwa cholephera kuteteza mwana wako n’kosaneneka. Ndinayesetsa kulimbana ndi malingaliro opweteka, kunyansidwa, ndi mkwiyo. Malingaliro ameneŵa anayamba kuipsa moyo wanga. Ndinafunitsitsa kwambiri kuti Yehova atetezere mtima wanga.” Ataŵerenga Afilipi 4:6, 7 ndi kubwerezanso kuŵerenga, mayiyu analimbika kugwiritsa ntchito uphungu wakewo. “Ndimapemphera tsiku lililonse, mobwerezabwereza ndimapempha kuti ndisalole kudziwononga ndekha ndi malingaliro oipa, ndipo Yehova wandithandiza kukulitsa mtima wodekha ndi wachimwemwe. Ndilidi pamtendere tsopano,” akusimba motero Jackie.
Nanunso mungakhale mu mkhalidwe womwe panokha simungathe kuchitapo kanthu kapena kuthetsa vutolo ndipo zoterozo zimadzetsa nkhaŵa ya maganizo. Mwa kutsatira malangizo a Baibulo akuti mupemphere, mungakhoze kupirira mosavuta. Wamasalmo akutilimbikitsa ndi mawu aŵa: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.”—Salmo 37:5.
Chilimbikitso. Wamasalmo ananena mawu oyamikira aŵa akuti: “Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu. Phazi langa liponda pachidikha; m’masonkhano ndidzalemekeza Yehova.” (Salmo 26:8, 12) Baibulo likutilimbikitsa kusonkhana pamodzi nthaŵi zonse kuti tilambire Yehova. Kodi kusonkhanako kungakwaniritse bwanji zosoŵa zanu? Kodi ena apezanji?
Becky akusimba kuti: “Makolo anga satumikira Yehova, chotero amandiika pampanipani nthaŵi zonse pamene ndiyesa kuchita china chilichonse chokhudzana ndi kutumikira Mulungu. Ndimachita kuyesetsa mwakhama kuti ine ndikapezeke ku misonkhano.” Becky akuona kuti walandira madalitso ambiri chifukwa chakuti wayesetsa mwakhama kuti azipezeka pamisokhano yachikristu nthaŵi zonse. “Misonkhano imalimbikitsa chikhulupiriro changa, kotero kuti ndimakhoza kupirira zipsinjo zatsiku ndi tsiku monga wophunzira, mwana wapanyumba, komanso mtumiki wa Yehova. Anthu ku Nyumba ya Ufumu n’ngosiyana kotheratu ndi ophunzira ku sukulu! Amasamala ndipo n’ngothandiza, ndipo zokambirana zathu zimakhala zolimbikitsa nthaŵi zonse. Alidi mabwenzi enieni.”
Inde, mwa kutsatira chitsogozo cha Baibulo cha kusonkhana pamodzi nthaŵi zonse, Yehova angakwaniritse zosoŵa zathu za chilimbikitso. Pano m’pomwe timaona kukwaniritsidwa kwenikweni kwa mawu a wamasalmo akuti: “Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.”—Salmo 46:1.
Pa Ntchito Yokhutiritsa ndi Yofunika kwambiri. “Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye,” likulimbikitsa motero Baibulo. (1 Akorinto 15:58) Kodi “ntchito ya Ambuye” n’njokhutiritsadi? Kodi utumiki wachikristu umakwaniritsa china chilichonse chofunika kwambiri?
Amelia akusimba momwe amamvera kuti: “Ndinaphunzira Baibulo ndi banja lina lomwe linali pafupi kutha. Ndinathandizanso mayi wina amene mwana wake wamkazi anaphedwa mwachiwawa. Mayiyu anavutika maganizo kwambiri ndi kusamvetsa momwe imfa ya mwana wakeyo inachitikira. M’zochitika zonse ziŵirizi, kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo kunadzetsa mtendere ndi chiyembekezo m’miyoyo yawo. Ndili ndi chimwemwe chochuluka ndipo ndine wokhutira chifukwa chakuti ndinachita mbali yanga pa kuwathandiza.” Scott anati: “Ngati mwakhala ndi chokumana nacho chabwino muutumiki wakumunda, kuyambitsa phunziro la Baibulo latsopano, kapena kusangalala ndi zotsatira zinazake zabwino za kuchitira umboni wa mwamwayi, mudzasimba lokoma kwa zaka zambiri m’tsogolomu. Malingaliro ndi chisangalalo zimodzimodzizo m’makhala nazonso pamene mukumbukira chimodzi ndi chimodzi! Muutumiki m’momwe chimwemwe chochuluka ndi chosatha chimachokera.”
Mwachionekere, kugwiritsa ntchito zitsogozo za m’Baibulo zakuti tikhale atumiki achangu kunakwaniritsa zosoŵa za anthu ameneŵa za ntchito yokhutiritsa ndi yofunika kwambiri. Nanunso mukupemphedwa kutenga nawo mbali pa ntchito imeneyi yophunzitsa ena za njira za Mulungu ndi mfundo zachikhalidwe, panthaŵi imodzimodziyo mukumapindula inu eni.—Yesaya 48:17; Mateyu 28:19, 20.
Kupindula ndi Mawu a Mulungu
Mosakayikira, Baibulo ndi gwero lokhulupirika la chitsogozo chopindulitsa m’dziko lamakonoli. Kuti tipindule nalo, tiyenera kuchita khama mosaleka. Tiyenera kuliŵerenga nthaŵi zonse, kuliphunzira, ndi kusinkhasinkha pa zomwe taŵerengazo. Paulo analangiza kuti: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.” (1 Timoteo 4:15; Deuteronomo 11:18-21) Mulungu akutsimikizira kuti ngati mudzayesetsa kugwiritsa ntchito uphungu wake wopezeka m’Baibulo, mudzapambana. Iye akulonjeza kuti: “Khulupirira Yehova . . . Um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”—Miyambo 3:5, 6.
[Zithunzi patsamba 31]
Kutsatira uphungu wa m’Baibulo kumakhutiritsa moyo ndi kuupanga kukwaniritsa zofuna zake