Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinathandizidwa Kuthetsa Manyazi

Ndinathandizidwa Kuthetsa Manyazi

Mbiri ya Moyo Wanga

Ndinathandizidwa Kuthetsa Manyazi

YOSIMBIDWA NDI RUTH L. ULRICH

Ndinalephera kupirira ndipo ndinalira ndili chiimire pakhomo la nyumba ya wansembe. Anali atangolalata kumene kutchula nkhani zambirimbiri zonamizira Charles T. Russell, amene anali kutumikira monga pulezidenti woyamba wa Watch Tower Bible and Tract Society. Choyamba, ndifotokoze kaye mmene ineyo, monga mtsikana wamng’ono, ndinali kuchezera anthu motero.

NDINABADWIRA m’banja lokonda kupembedza pafamu inayake ku Nebraska, U.S.A., m’chaka cha 1910. Pabanja pathu tinkaŵerengera pamodzi Baibulo tsiku lililonse m’maŵa ndi madzulo tikatha kudya. Atate ndiwo ankayang’anira Sande sukulu ya tchalitchi cha Methodist m’tauni yaing’ono ya Winside, makilomita ngati asanu ndi limodzi kuchokera pafamu yathu. Tinali ndi ngolo yokokedwa ndi akavalo yomwe inali ndi mazenera ophimba ndi makatani, moti kaya kunja kuche motani, tinkapitabe kutchalitchi Lamlungu m’maŵa.

Ndili ndi zaka ngati zisanu ndi zitatu, mlongo wanga yemwe anali wakhanda anadwala matenda a kufa ziwalo, ndipo amayi anapita naye kuchipatala cha matenda osatherapo msanga m’chigawo cha Iowa kuti akapeze nawo mankhwala. Ngakhale kuti amayi anayesetsa kum’samalira, mlongo wangayo anamwalira kuchipatala komweko. Koma adakali ku Iowa komweko, amayi anakumana ndi Wophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo. Nthaŵi zambiri ankacheza, ndipo amayi anapitanso ndi mkaziyo ngakhale ku ina mwa misonkhano ya Ophunzira Baibulo.

Amayi atabwerako, anabwera ndi mavoliyumu angapo a buku la Studies in the Scriptures, amene anali kufalitsidwa ndi Watch Tower Society. Posapita nthaŵi anakhala otsimikizira kuti Ophunzira Baibulo anali kuphunzitsa choonadi ndi kuti chiphunzitso cha kusafa kwa moyo wa munthu ndinso chakuti anthu oipa amazunzidwa kwamuyaya sizinali zoona.​—Genesis 2:7; Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4.

Koma atate anakhumudwa kwabasi, ndipo anali kuwaletsa amayi akafuna kupita kumisonkhano ya Ophunzira Baibulo. Iwo anapitirizabe kunditenga ineyo ndi mlongo wanga wamkulu, Clarence, popita kutchalitchi kwawo. Koma atate akakhala kuti atalikira, amayi ankaphunzira nafe Baibulo. Chotero, anafe tinali oti n’kuyerekeza bwino lomwe ziphunzitso za Ophunzira Baibulo ndi za tchalitchi chathu.

Ineyo ndi Clarence sitinali kujomba ku Sande sukulu ya kutchalitchi kwathu, ndipo Clarence ankafunsa mphunzitsi wathu wamkazi mafunso amene mphunzitsiyo analephera kuwayankha. Tikapita kunyumba, tinali kuwasimbira amayi, ndipo zimenezi zinapangitsa kuti tizikambirana nkhani zimenezi kwa nthaŵi yaitali. Pomalizira pake, ndinasiya kupita kutchalitchi ndipo ndinayamba kupita kumisonkhano ya Ophunzira Baibulo pamodzi ndi amayi, ndipo sipanapite nthaŵi yaitali Clarence nayenso anatsatira.

Kulimbana ndi Manyazi

Mu September 1922, amayi ndi ineyo tinapita ku msonkhano wosaiŵalika wa Ophunzira Baibulo ku Cedar Point, Ohio. Ndimakumbukirabe bwino lomwe chinsalu chachikulu chija akuchifunyulula pamene Joseph F. Rutherford, amene anali pulezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo, analimbikitsa opezeka pamsonkhanowo oposa 18,000, ndi mawu omwe analembedwa pachinsalucho akuti: “Lengezani Mfumu ndi Ufumu.” Ndinakhudzidwa kwambiri mumtima ndipo ndinaona kufunika kwa kuuza ena mwamsanga za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.​—Mateyu 6:9, 10; 24:14.

Pamisonkhano yomwe inachitika kuyambira mu 1922 mpaka 1928, panali zosankha zingapo zomwe zinavomerezedwa, ndipo uthengawo unalembedwanso m’mathirakiti amene Ophunzira Baibulo anagaŵira kwa anthu padziko lonse lapansi, makope mamiliyoni ambirimbiri. Ndinali woonda ndi wamtali​—ankanditcha kuti greyhound (mtundu winawake wa agalu oonda ndi aatali)​—ndipo ndinali kuyenda mokangalika kunyumba ndi nyumba kugaŵira mauthenga osindikizidwa ameneŵa. Ndinasangalaladi kuchita ntchito imeneyi. Komabe, kuyankhula ndi munthu pakhomo, ineyo kuuza ena za Ufumu wa Mulungu, inali nkhani ina.

Simungakhulupirire, koma ndinali wamanyazi moti mantha anali kundigwira amayi akaitana magulu a achibale athu chaka ndi chaka. Ndinkabisala m’chipinda changa. Nthaŵi inayake, amayi ankafuna kujambula chithunzi cha banja lonse, ndipo anandiuza kuti ndituluke. Pofuna kukhala kwandekha, ndinakuwa kwadzaoneni pamene amayi anandiduduluzira panja.

Komano tsiku linadzafika pamene molimba mtima ndinalongedza mabuku ena ofotokoza Baibulo m’chikwama. Mumtima ndinali kungoti, “Sindingathe,” koma kenako ndinangoti, “Nditha.” Basi ndinapita kukalalikira. Pambuyo pake ndinasangalala kwambiri kuti ndinalimba mtima kuti ndipite. Ndinali wosangalala kwambiri kuti ndaichita ntchitoyo, osati poichita penipenipo. Nthaŵi yake inali ngati imeneyi pamene ndinakumana ndi m’tsogoleri wachipembedzo amene ndam’tchula kale uja ndipo ndinachoka ndikulira. M’kupita kwa nthaŵi, mothandizidwa ndi Yehova ndinayamba kukwanitsa kuyankhula ndi anthu pamakomo awo, ndipo chimwemwe changa chinawonjezeka. Kenako, mu 1925, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi.

Kuyamba Utumiki Wanthaŵi Zonse

Pamene ndinali ndi zaka 18, ndinagula galimoto ndi ndalama zomwe azakhali anga anandisiyira ndipo ndinayamba upainiya, dzina la utumiki wa nthaŵi zonse. Patapita zaka ziŵiri, mu 1930, ineyo ndi mnzanga wochita naye upainiya tinalandira gawo lolalikiramo. Panthaŵi imeneyo Clarence nayenso anali atayamba upainiya. Posapita nthaŵi anaitanidwa kutii akatumikire pa Beteli, likulu ladziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York.

Cha panthaŵi imeneyo makolo athu anapatukana, chotero ineyo ndi amayi tinapangitsa ngolo yokokedwa ndi galimoto yoti tidzikhalamo monga nyumba ndipo tinayamba kuchitira upainiya pamodzi. Inali nthaŵi pamene nyengo ya mavuto aakulu a zachuma inayamba m’dziko la United States. Kupitirizabe ndi upainiya kunali kovuta, koma tinali otsimikiza mtima kuti sitisiya. Tinali kusinthanitsa mabuku olongosola Baibulo ndi nkhuku, mazira, ndi zakudimba, pamodzinso ndi zinthu monga mabatire akale ndi zitsulo zotayidwa. Mabatire ndi zitsulo zimenezi tinali kuzigulitsa kuti tipeze ndalama zogulira mafuta a galimoto ndi zofunika zina. Ndinaphunziranso kupaka galimoto girizi ndi kusintha oilo kuti tisawononge ndalama zambiri. Mogwirizanadi ndi lonjezo lake, tinaona Yehova akutitsegulira njira yolakira zopinga.​—Mateyu 6:33.

Kupita ku Ntchito Yaumishonale

Mu 1946, ndinaitanidwa kukaloŵa kalasi lachisanu ndi chiŵiri la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, yomwe inali pafupi ndi South Lansing, New York. Pofika nthaŵiyo, ineyo ndi amayi tinali titachitira upainiya pamodzi kwa zaka 15, koma sanafune kundiletsa kupeza nawo mpata wokaphunzitsidwa ntchito yaumishonale. Chotero anandilimbikitsa kulandira mwayi wopita ku Sukulu ya Gileadi. Nditamaliza maphunzirowo, Martha Hess wa ku Peoria, Illinois, ndi ineyo tinali kukagwira ntchito limodzi. Aŵirife, limodzi ndi enanso aŵiri, tinatumizidwa ku Cleveland, Ohio, kwa chaka chimodzi podikira kuti atitumize kudziko lina.

Mu 1947 tinatumizidwa. Ineyo ndi Martha tinatumizidwa ku Hawaii. Popeza kuti kusamukira ku zilumba zimenezi kunali kosavuta, amayi anasamuka kudzakhala nafe pafupi mu mzinda wa Honolulu. Thanzi lawo linali kufooka, chotero kuwonjezera pa kusamalira ntchito yanga yaumishonale, ndinali kuthandizanso amayi. Ndinakwanitsa kuwasamalira mpaka imfa yawo ku Hawaii komweko mu 1956, ali ndi zaka 77. Pamene timafika, kunali Mboni ngati 130 ku Hawaii, koma pofika nthaŵi imene amayi amamwalira, kunali Mboni zoposa 1,000, ndipo amishonale sanalinso ofunikira.

Kenako, ineyo ndi Martha tinalandira kalata yochokera ku Watch Tower Society yotiuza kuti tikagwirire ntchito yathu ku Japan. Nkhaŵa yathu yaikulu inali yakuti kaya ngati tidzatha kuphunzira chinenero cha Chijapani pamsinkhu wathu. Apo ndili ndi zaka 48 zakubadwa, ndipo Martha anali wamng’onopo ndi zaka zinayi. Koma nkhaniyo tinaisiya m’manja mwa Yehova ndipo tinavomereza kusamuka.

Mu 1958, msonkhano wa mayiko womwe unachitikira m’mabwalo a maseŵera a Yankee Stadium ndi Polo Grounds mu mzinda wa New York utangotha, tinauyamba ulendo wa ku Tokyo pasitima yapamadzi. Namondwe anatikuntha kuti tiziyandikira doko la Yokohama, kumene tinalandiridwa ndi Don ndi Mabel Haslett, Lloyd ndi Melba Barry, ndi amishonale ena. Nthaŵi imeneyo n’kuti m’Japan muli Mboni 1,124 zokha.

Nthaŵi yomweyo tinayamba kuphunzira chinenero cha Chijapani ndi kuchita utumiki wa ku khomo ndi khomo. Pogwiritsa ntchito zilembo zachingelezi, tinalemba maulaliki athu a m’Chijapani, amene tinkachita kuŵerenga. Potiyankha eninyumba ankanena kuti, “Yoroshii desu” kapena, “Kekko desu,” zimene tinauzidwa kuti zimatanthauza kuti “Ayi zili bwino” kapena, “N’zabwino.” Koma nthaŵi zina sitinali kudziŵa kaya mwininyumbayo anali ndi chidwi kapena ayi, popeza kuti mawu omwewonso amanenedwa munthu akafuna kukana. Tanthauzo lake linadalira pa kamvekedwe ka mawu kapena pa mmene munthuyo anali kusonyezera nkhope yake. Zinatitengera nthaŵi kuti tiphunzire zimenezi.

Zokumana Nazo Zimene Zinasangalatsa Mtima Wanga

Tikuphunzirabe chinenero, tsiku lina ndinapita ku mdadada wa zipinda zogona za kampani ya Mitsubishi kumene ndinakumana ndi mkazi wina wa zaka 20. Iye anapita patsogolo ndi chidziŵitso cha Baibulo ndipo anabatizidwa mu 1966. Patatha chaka chimodzi anayamba upainiya ndipo posapita nthaŵi anaikidwa kukhala mpainiya wapadera. Wakhala akutumikira motero mpaka lero. Zandisonkhezera mtima nthaŵi zonse kuona mmene wagwiritsira ntchito nthaŵi yake ndi nyonga zake mu utumiki wanthaŵi zonse kuyambira unyamata wake.

Kuima kumbali ya choonadi cha Baibulo ndi vuto lomwe limakhala lalikulu kwambiri kwa amene akukhala pakati pa anthu osakhala achikristu. Komabe, anthu zikwi zambiri alipirira vutoli, kuphatikizapo angapo a amene ndaphunzira nawo Baibulo. Iwo ataya akachisi awo achibuda ndi mashelefu achishinto a ndalama zambiri omwe mwamwambo amapezeka m’nyumba zambiri m’Japani. Popeza kuti achibale amaona kuchita zimenezi ngati kusalemekeza makolo akufa, kuti munthu amene akuphunzira Baibulo achite zimenezi amafunikira kulimba mtima. Kulimba mtima kwawo kumeneko kumatikumbutsa kulimba mtima kwa Akristu oyambirira amene anawononga zinthu zawo zogwirizana ndi kulambira konama.​—Machitidwe 19:18-20.

Ndikukumbukira wophunzira Baibulo wina, mkazi wapabanja, amene ankafuna kusamuka mu mzinda wa Tokyo pamodzi ndi banja lake. Ankafuna kukaloŵa m’nyumba yatsopano momwe munalibe zinthu zogwirizana ndi kulambira kwachikunja. Chotero anauza mwamuna wake zimene angakonde kuchita, ndipo iye anavomereza. Anandisimbira nkhaniyo mosangalala komano anakumbukira kuti walongedzanso mtsuko winawake waukulu wodula wopangidwa ndi mwala wa nsangalabwi umene anaugula pomva kuti umatetezera mtendere wa m’nyumba. Popeza kuti anali kuukayikira kuti mwina unali mbali ya kulambira konama, anauswa ndi hamala n’kuutaya.

Kuona mkazi ameneyu ndi enanso akutaya zinthu zamtengo wapatali zogwirizana ndi kulambira konama kenako n’kuyamba moyo watsopano wolambira Yehova kwakhala kosangalatsa kwabasi ndiponso kokhutiritsa zedi. Nthaŵi zonse ndimathokoza Yehova kuti ndasangalala ndi utumiki waumishonale kwa zaka zoposa 40 m’Japan.

“Zozizwitsa” Zamakono

Ndikakumbukira zaka zoposa 70 zomwe ndathera mu utumiki wanthaŵi zonse, ndimadabwa kuona zomwe kwa ine zimaoneka ngati zozizwitsa zamakono. Pamene ndinali wachinyamata wamanyazi kwambiri, sindinaganizepo kuti ndingakhale moyo wanga wonse ndikuyankhula anthu za Ufumu umene ochuluka safuna n’komwe kumva ukuutchula. Komabe, sizokhazo zomwe ndatha kuchita koma ndaonanso anthu mazanamazana, mwinanso zikwi zambiri, akuchitanso chimodzimodzi. Ndipo achita zimenezo mogwira mtima kwambiri moti Mboni zosaposa kwenikweni chikwi chimodzi zimene zinali m’Japan pamene ndinafika mu 1958 zawonjezeka kukhala zoposa 222,000 lerolino!

Pamene ineyo ndi Martha tinangofika kumene m’Japan, tinafikira pa ofesi ya nthambi m’Tokyo. Mu 1963 nyumba yatsopano ya nthambi yosanjikizana kasanu ndi kamodzi inamangidwa pamalopo, ndipo ndi mmene takhala mpaka lero. M’November 1963 tinali pakati pa anthu 163 amene anapezeka pa nkhani ya kupatulira yoperekedwa ndi woyang’anira nthambi wathu, Lloyd Barry. Pamenepo tinali titafika Mboni 3,000 m’Japan.

Chakhala chinthu chosangalatsa kwambiri kuona ntchito yolalikira Ufumu ikukula modabwitsa, kufika pa anthu oposa 14,000 mu 1972 pamene nthambi yatsopano yaikulupo inamalizidwa mu mzinda wa Numazu. Koma pofika 1982, m’Japan munali olengeza Ufumu oposa 68,000, ndipo nthambi yaikulu kwambiri inamangidwa mu mzinda wa Ebina, makilomita ngati 80 kuchokera ku Tokyo.

Panthaŵiyi, nyumba ya nthambi yakaleyo pakatikati pa Tokyo inakonzedwanso. M’kupita kwa nthaŵi, inakhala nyumba ya amishonale oposa 20 amene atumikira m’Japan kwa zaka zoposa 40 kapena 50 kapena kuposapo, kuphatikizapo ineyo ndi mnzanga wakalekaleyo, Martha Hess. Dokotala wina ndi mkazi wake, amenenso ndi nesi, amakhalanso m’nyumba yathuyi. Amatiyang’anira, kutisamalira mwachikondi pa zovuta za thanzi lathu. Posachedwapa, panawonjezedwanso nesi wina, ndipo alongo achikristu amabwera kudzathandiza nesi tsiku lililonse. Anthu aŵiri a m’banja la Beteli ku Ebina amabwera mosinthanasinthana kudzathandiza kuphika ndi kuyeretsa nyumba yathu. Ndithudi, Yehova watikomera mtima.​—Salmo 34:8, 10.

Chinthu chosangalatsa kwambiri m’moyo wanga waumishonale chinachitika m’November wapita, zaka 36 pambuyo pa kupatulidwa kwa nyumba imene ambiri mwa amishonale akalekalefe tikukhalamo tsopano. Pa November 13, 1999, ndinali pakati pa anthu 4,486, kuphatikizapo mazana a Mboni zakalekale zochokera m’mayiko 37, amene anapezeka pa kupatulidwa kwa nthambi ya Watch Tower Bible and Tract Society ya m’Japan ku Ebina yomwe inakulitsidwa. Panopa, muli anthu ngati 650 m’banja lapanthambi limenelo.

Pazaka pafupifupi 80 kuchokera pamene ndinayamba kupita kunyumba ndi nyumba mwamanyazi kufalitsa uthenga wa m’Baibulo, Yehova wakhala chilimbikitso changa. Wandithandiza kuthetsa manyazi. Ndili ndi chikhulupiriro cholimba chakuti Yehova angagwiritse ntchito aliyense amene amasonyeza kuti amam’dalira, ngakhale anthu amanyazi kwambiri ngati ineyo. Ndipotu ndakhala moyo wokhutiritsa kwambiritu zedi poyankhula ndi anthu achilendo ponena za Mulungu wathu, Yehova!

[Chithunzi patsamba 21]

Pamodzi ndi amayi ndi Clarence, amene anali kudzatichezera kuchokera ku Beteli

[Chithunzi patsamba 23]

A m’kalasi mwathu akuphunzira pakapinga ku Sukulu ya Gileadi pafupi ndi South Lansing, New York

[Chithunzi patsamba 23]

Kulamanzere: Ineyo, Martha Hess, ndi amayi, ku Hawaii

[Chithunzi patsamba 24]

Kulamanja: Amene timakhala nawo m’nyumba yathu ya amishonale ku Tokyo

[Chithunzi patsamba 24]

M’munsi: Pamodzi ndi mnzanga wakalekaleyo, Martha Hess

[Chithunzi patsamba 25]

Nthambi yathu yokulitsidwa ku Ebina inapatulidwa m’November wapitayu