Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Inu Nonse Muli Abale”

“Inu Nonse Muli Abale”

“Inu Nonse Muli Abale”

“Musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.”​—MATEYU 23:8.

1. Ndi nkhani iti imene tiyenera kuilingalira?

“KODI ndani woyenera ulemu waukulu? Mmishonale kapena wa pa Beteli?” Ndilo funso limene mkazi wina wachikristu ku dziko lina la Kum’maŵa anafunsa mmishonale wochokera ku Australia n’cholinga chofunadi kudziŵa. Iye anali kufuna kudziŵa amene ayenera kulemekezedwa kwambiri, mmishonale wochokera kudziko lina kapena mtumiki wa m’dziko lomwelo wotumikira pa nthambi ya Watch Tower Society. Funso lochokera pansi pa mtima limenelo, losonyeza chikhalidwe chosamala kwambiri ponena za malo a munthu pomuyerekeza ndi ena, linam’dzidzimutsa mmishonaleyo. Komabe, funso lakuti wamkulu ndani limakhalapo chifukwa chofunitsitsa kudziŵa kuti munthu aliyense ndi wamkulu chotani ndiponso ali ndi mphamvu zotani pomuyerekezera ndi ena.

2. Kodi olambira anzathu tiyenera kuwaona motani?

2 Malingaliro ameneŵa si alero iyayi. Ngakhale ophunzira a Yesu ankatsutsana nthaŵi ndi nthaŵi pamfundo yoti wamkulu ndani. (Mateyu 20:20-24; Marko 9:33-37; Luka 22:24-27) Iwo anakulira pakati pa anthu otsatira Chiyuda cha m’zaka za zana loyamba omwenso ankasamala kwambiri za malo a munthu. Podziŵa chikhalidwe chimenechi, Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.” (Mateyu 23:8) Dzina laulemu lachipembedzo monga lakuti “Rabi,” lomwe limatanthauza “Mphunzitsi,” “linali kupangitsa munthu yemwe wafika potchedwa dzinalo kukhala wonyada ndiponso wodziona kukhala wapamwamba mosiyana ndi ena, komanso linali kupangitsa awo amene sakutchedwa dzinalo kusirira ndiponso kudziona ngati onyozeka; chotero mzimu wake wonse ndi tanthauzo lake lonse la dzinalo n’zosemphana ndi ‘kudzichepetsa kwa Kristu,’” anatero Albert Barnes, katswiri wa Baibulo. Zoonadi, Akristu amapeŵa kutchula oyang’anira pakati pawo kuti “Mbale mkulu wakutiwakuti,” kugwiritsa ntchito mawuwo “mkulu” monga ulemu wachiphamaso. (Yobu 32:21, 22) M’malo mwake, akulu otsatiradi tanthauzo lenileni la uphungu wa Yesu amalemekeza anthu a mumpingo, monga momwe Yehova amalemekezera om’lambira okhulupirika ndiponso momwe Yesu Kristu amalemekezera om’tsatira ake okhulupirika.

Chitsanzo cha Yehova ndi cha Yesu

3. Kodi Yehova anasonyeza motani ulemu kwa zolengedwa zake zauzimu?

3 Kungoyambira pachiyambi, Yehova ankalemekeza zolengedwa zake mwa kuzigaŵira zochita pantchito zake ngakhale kuti iye ndi “Wam’mwambamwamba.” (Salmo 83:18) Polenga munthu woyambirira, Yehova anagwiritsa ntchito Mwana wake wobadwa yekha ngati “mmisiri” pantchitoyo. (Miyambo 8:27-30; Genesis 1:26) Yehova anapemphanso ngakhale angelo ake kumwamba kuti aperekepo malingaliro awo ponena za momwe angawonongere Mfumu Ahabu woipayo Yehova atagamula kuti awonongedwe.​—1 Mafumu 22:19-23.

4, 5. Kodi Yehova amachitira motani ulemu zolengedwa zake za umunthu?

4 Yehova ndiye Mfumu Yaikulukulu yomwe ikulamulira m’chilengedwe chonse. (Deuteronomo 3:24) Alibe chifukwa chochita kufunsira nzeru kwa anthu. Komabe, amadzichepetsa, tinene motero, kuti alingalire za anthu. Wamasalmo wina anaimba kuti: “Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali, nadzichepetsa apenye zam’mwamba ndi za padziko lapansi. Amene autsa wosauka kum’chotsa kufumbi.”​—Salmo 113:5-8.

5 Asanafafanize Sodomu ndi Gomora, Yehova anatchera khutu pamene Abrahamu anali kum’funsa mafunso ndipo anakhutiritsa nkhaŵa ya Abrahamu yofuna kuona chilungamo. (Genesis 18:23-33) Ngakhale kuti Yehova ankadziŵa chotsatira cha zimene Abrahamu anali kupempha, iye anamvetsera kwa Abrahamu modzichepetsa ndi kulandira malingaliro ake.

6. Kodi panali chotsatira chotani Yehova atasonyeza ulemu pamene Habakuku anafunsa funso?

6 Yehova anatcheranso khutu kwa Habakuku, amene anafunsa kuti: “Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva inu?” Kodi Yehova anaona funso limenelo ngati kutsutsa ulamuliro wake? Iyayi, iye anaona mafunso a Habakuku kukhala oyenera, kotero kuti anavumbula chifuno chake choutsa Akasidi kuti apereke chiweruzo chake. Anatsimikizira mneneriyo kuti ‘chiweruzo choloseredwachi chidzafika ndithu.’ (Habakuku 1:1, 2, 5, 6, 13, 14; 2:2, 3) Mwa kumvetseradi nkhaŵa za Habakuku ndi kum’yankha, Yehova anasonyeza ulemu kwa mneneriyu. Chotero, mneneri wogwidwa ndi nkhaŵayu anatsitsimulidwa nakhala wosangalala, ndi chikhulupiriro chonse mwa Mulungu wa chipulumutso chake. Izi tikuziona m’buku louziridwa la Habakuku lolimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova lerolino.​—Habakuku 3:18, 19.

7. N’chifukwa chiyani mbali ya Petro pa Pentekoste wa mu 33 C.E. inali yofunika kwambiri?

7 Chitsanzo chinanso chabwino zedi cha kusonyeza ena ulemu ndicho Yesu Kristu. Yesu anali atauza ophunzira ake kuti “yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzam’kana iye pamaso pa Atate wanga.” (Mateyu 10:32, 33) Koma usiku womwe anaperekedwa, ophunzira ake onse anam’thaŵa, ndipo mtumwi Petro anam’kana katatu. (Mateyu 26:34, 35, 69-75) Yesu anayang’ana m’kati mwenimweni osati kunja kokha ndipo anaona malingaliro a Petro a mumtima, kulapa kwake kochokera pansi pa mtima. (Luka 22:61, 62) Patangopita masiku 51 okha, Kristu analemekeza mtumwi wolapayo mwa kum’lola kuimira ophunzira 120 a Yesu patsiku la Pentekoste ndi kuti agwiritse ntchito oyamba mwa “mafungulo a Ufumu.” (Mateyu 16:19; Machitidwe 2:14-40) Petro anapatsidwa mpata wa ‘kutembenuka ndi kukhazikitsa abale ake.’​—Luka 22:31-33.

Kuchitira Ena Ulemu M’banja

8, 9. Pochitira ulemu mkazi wake, kodi mwamuna angatsanzire motani Yehova ndi Yesu?

8 Amuna okwatira ndiponso makolo amachita bwino kutsanzira Yehova ndi Yesu Kristu pochita ulamuliro wawo woperekedwa ndi Mulungu. Petro analangiza kuti: “Amuna inu, khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu.” (1 Petro 3:7) Yerekezani kuti mukunyamula mtsuko wosalimba wadongo, womwe mosakayikira utha kusweka mosavuta kusiyana ndi wosema. Kodi simungaunyamule mosamala kwambiri? Mwamuna angachite zimenezi mwa kutsanzira Yehova, kumvetsera malingaliro a mkazi wake pokambirana nkhani za m’banja. Kumbukirani kuti Yehova anam’pezera nthaŵi Abrahamu yoyankhula naye. Pokhala wopanda ungwiro, mwamuna angalephere kuona mbali zonse za nkhani inayake. Chotero kodi siingakhale nzeru kuti achitire ulemu mkazi wake mwa kumveranso malingaliro ake?

9 M’mayiko momwe ulamuliro wa mwamuna umalemekezedwa kwambiri, mwamuna ayenera kukumbukira kuti mkazi wake angavutike zedi kuti alongosole zakukhosi kwake zenizenidi. Tsanzirani momwe Yesu Kristu anachitira ndi ophunzira ake, omwe anali mbali ya gulu la mkwatibwi wake wam’tsogolo, pamene anali padziko lapansi. Iye anawakonda, pokumbukiranso zofooka zawo zakuthupi ndi zauzimu iwo asananene n’komwe zosoŵa zawo. (Marko 6:31; Yohane 16:12, 13; Aefeso 5:28-30) Kuwonjezera apo, khalani pansi ndi kuona zimene mkazi wanu akukuchitirani inuyo ndi banja lanu, ndipo m’thokozeni mwa kumuuza ndi mwa zochita zanu. Onse aŵiri Yehova ndi Yesu anayamikira, kutamanda, ndi kudalitsa anthu oyenerera zimenezo. (1 Mafumu 3:10-14; Yobu 42:12-15; Marko 12:41-44; Yohane 12:3-8) Mwamuna wake atakhala mmodzi wa Mboni za Yehova, mkazi wina wachikristu m’dziko la Kum’maŵa anati: “Amuna anga amati tikamayenda ankayenda mofulumira kundisiya kumbuyo, nditanyamula katundu yense. Koma tsopano ndiwo amanyamula zikwama ndipo amathokoza ntchito zanga zapanyumba!” Mawu othokoza ochokera pansi pa mtima amathandizadi mkazi wanu kumva kuti ndi wofunikadi.​—Miyambo 31:28.

10, 11. Kodi makolo angaphunzireponji pa chitsanzo chabwino cha Yehova cha mmene anachitira ndi mtundu wopanduka wa Israyeli?

10 Pokhala ndi ana awo, makamaka pamene akufunikira kudzudzulidwa, makolo ayenera kutsanzira chitsanzo cha Mulungu. “Yehova anachitira umboni [“anapitirizabe kuchenjeza,” NW] Israyeli ndi Yuda” kuti asiye njira zawo zoipa, koma “[a]naumitsa khosi lawo.” (2 Mafumu 17:13-15) Aisrayeli anayesanso ngakhale ‘kum’syasyalika ndi pakamwa pawo, nam’namiza ndi lilime lawo.’ Makolo ambiri angaone kuti ana awo nthaŵi zina amateronso. Aisrayeli “[a]nayesa Mulungu” ndi kum’pweteketsa mtima. Komabe, Yehova “pokhala n’ngwachifundo, anakhululukira choipa, osawawononga.”​—Salmo 78:36-41.

11 Yehova anachondereranso Aisrayeli kuti: “Tiyeni, tsono, tiweruzane, . . . ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala.” (Yesaya 1:18) Ngakhale kuti Yehova sanalakwe, iye anapempha mtundu wopandukawo kuti akambirane. Ndi malingalirotu abwino zedi oti makolo atsatire pokhala ndi ana awo! Ngati pakufunikira kutero, achitireni ulemu mwa kumvetsera zomwe anganene, ndipo kambiranani nawo chifukwa chimene ayenera kusinthira.

12. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupeŵa kuchitira ana athu ulemu koposa Yehova? (b) Kodi chofunika n’chiyani kuti tichitire ana athu ulemu powadzudzula?

12 Zoonadi, nthaŵi zina ana amafunikira uphungu wamphamvu. Makolo sangafune kukhala ngati Eli, amene ‘anachitira ana ake ulemu koposa Yehova.’ (1 Samueli 2:29) Ngakhale ndi tero, ana ayenera kuona cholinga chachikondi cha chilango. Ayenera kuzindikira kuti makolo awo amawakonda. Paulo analangiza atate kuti: “Musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Pamene atate akuchita ulamuliro wawo, mfundo yaikulu pano ndiyo kufunika kwakuti atatewo asonyeze ulemu kwa ana mwa kusawakwiyitsa chifukwa cha ukali wonyanyira. Inde, kuchitira ana ulemu kumafuna nthaŵi ndiponso kuyesayesa kwa makolo, koma mapeto ake amakhala abwino zedi.

13. Kodi Baibulo limati bwanji ponena za okalamba m’banja?

13 Kuchitira ena ulemu m’banja kumaphatikizapo zinanso zowonjezera pa kulemekeza mkazi wako ndi ana ako. “Ukakalamba, mvera ana ako,” umatero mwambi wina wa ku Japan. Mfundo ya mwambi umenewo ndi yakuti makolo achikulire ayenera kupeŵa kukokomeza ulamuliro wawo ndipo ayenera kumvetsera zimene ana awo aakulu akunena. Pamene kuli kwakuti Malemba amati makolo ayenera kuchitira ana awo ulemu mwa kumvetsera zomwe akunena, ana sayenera kukhala achipongwe kwa anthu achikulire m’banjamo. “Usapeputse amako atakalamba,” imatero Miyambo 23:22. Mfumu Solomo anatsatiradi mwambi umenewu ndipo anachitira amake ulemu atam’fikira kuti apereke pempho lawo. Solomo anaikitsa mpando winanso wachifumu kudzanja lake lamanja ndi kumvetsera zimene amayi ake okalambawo, Batiseba, anabwera nazo.​—1 Mafumu 2:19, 20.

14. Kodi anthu okalamba mumpingo tingawachitire motani ulemu?

14 M’banja lathu lalikulu lauzimu, tili ndi mwayi ‘wotsogolera’ pochita ulemu kwa anthu achikulire a mumpingo. (Aroma 12:10) Mwina iwo sangathe kuchita zambiri ngati kale, ndipo zimenezo zingawakhumudwitse. (Mlaliki 12:1-7) Mboni ina yachikulire yodzozedwa yomwe inagonekedwa m’chipatala inati pofotokoza kukhumudwa kwake: “Ndingofuna nditafa basi kuti ndiyambenso kugwira ntchito.” Kwa achikulire ngati ameneŵa, pamene tiwasonyeza kuti ndi ofunika ndi kutinso timawalemekeza zingawathandize kwambiri. Aisrayeli analamulidwa kuti: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.” (Levitiko 19:32) Sonyezani ulemu mwa kupangitsa okalamba kumva kuti timawakonda ndi kuwayamikira. ‘Kugwada’ kungaphatikizepo kukhala pansi ndi kuwamvetsera pamene akusimba za zinthu zimene anakwaniritsa zaka zam’mbuyomo. Kumeneko kudzakhala kulemekeza okalamba ndipo kudzalemeretsa moyo wathu.

‘Tsogolerani Pochitirana Ulemu’

15. Kodi n’chiyani chimene akulu angachite kuti achitire ulemu anthu a mumpingo?

15 Anthu a mumpingo amapita patsogolo pamene akulu awasonyeza chitsanzo chabwino. (1 Petro 5:2, 3) Ngakhale kuti amakhala ndi zochita zambiri, akulu osamala amayesetsa kufikira achinyamata, mitu ya mabanja, amayi osakwatiwa, amayi apabanja, ndi achikulire, kaya anthuwo ali pavuto kapena ayi. Akulu amamvetsera zonena za anthu a mumpingo ndipo amawayamikira pa zimene amatha kuchita. Mkulu wopenya bwino amene akuthokoza mbale kapena mlongo pa zimene akuchita akutsanzira Yehova, amene amathokoza zolengedwa zake za padziko lapansi.

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona akulu monga oyenera ulemu monga ena onse a mumpingo?

16 Mwa kutsanzira Yehova, akulu amapereka chitsanzo chabwino potsatira uphungu wa Paulo wakuti: “M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Zimenezi zingakhale zovuta kwambiri kwa akulu amene akukhala m’mayiko momwe anthu amasamala kwambiri za malo a munthu pomuyerekeza ndi ena. Mwachitsanzo, m’dziko lina Kum’maŵa, pali mawu aŵiri onse otanthauza “mbale,” lina lolemekeza ndiponso lina lawamba. Mpaka posachedwapa, anthu mumpingo ankagwiritsa ntchito liwu lolemekeza pofuna kutchula akulu ndi achikulire, koma lawamba pofuna kutchula ena onse. Komabe, iwo analimbikitsidwa kugwiritsa ntchito lawambalo nthaŵi zonse chifukwa chakuti, monga momwe Yesu anauzira otsatira ake, “inu nonse muli abale.” (Mateyu 23:8) Ngakhale kuti m’mayiko ena kusiyana sikungakhale koonekera chotere, tonsefe tiyenera kukhala tcheru ndi chizoloŵezi chaumunthu chofuna kusiyanitsa anthu.​—Yakobo 2:4.

17. (a) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kukhala ofikirika? (b) Kodi akulu angatsanzire motani Yehova pochita ndi anthu a mumpingo?

17 N’zoona kuti Paulo anatilimbikitsa kuona akulu ena kukhala oyenera “ulemu woŵirikiza,” koma ndi abalebe. (1 Timoteo 5:17) Ngati timatha ‘kulimbika mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo’ wa Mfumu Yachilengedwe Chonse, kodi sitiyeneranso kumasuka pofikira akulu, amene amafunikira kutsanzira Yehova? (Ahebri 4:16; Aefeso 5:1) Oyang’anira angayeze kufikirika kwawo mwa kufufuza kuti ndi anthu angati amene amawafikira kudzafunsira uphungu kapena kudzapereka malingaliro. Tengeraponi phunziro pa mmene Yehova amaphatikizirapo ena pantchito zake. Amalemekeza ena mwa kuwagaŵira zochita. Ngakhale kuti malingaliro ena operekedwa ndi Mboni ina angaoneke kukhala osathandiza kwenikweni, akulu ayenera kuyamikirabe nkhaŵa yosonyezedwa ndi Mboniyo. Kumbukirani mmene Yehova anaonera mafunso ofufuza a Abrahamu ndi kulira kwa Habakuku chifukwa cha nkhaŵa.

18. Kodi akulu angatsanzire motani Yehova powongolera anthu ofunikira thandizo?

18 Akristu anzathu ena amafunikiradi kuwongolera. (Agalatiya 6:1) Koma Yehova amawaonabe kukhala a mtengo wapamwamba, oyenerabe ulemu. “Ngati munthu amene akundipatsa uphungu andisonyeza ulemu, ndimakhala womasuka kum’fikira,” inatero Mboni ina. Anthu ambiri amamvera uphungu ngati asonyezedwa ulemu. Zingatenge nthaŵi yaitali, koma kumvetsera kwa anthu amene alakwa kumawapangitsa kuti alandire uphungu wofunikira uliwonse mosavuta. Kumbukirani mmene Yehova anayankhulira ndi Aisrayeli mobwerezabwereza chifukwa chowamvera chifundo. (2 Mbiri 36:15; Tito 3:2) Uphungu woperekedwa mowamvetsetsa anthuwo ndiponso mowamvera chifundo udzaloŵadi mumtima wa anthu ofunikira chithandizowo.​—Miyambo 17:17; Afilipi 2:2, 3; 1 Petro 3:8.

19. Kodi anthu a zikhulupiriro zosiyana ndi zachikristu tiyenera kuwaona motani?

19 Kuchitira ena ulemu kumaphatikizapo kuchitira ulemu aja amene angadzakhale abale athu auzimu m’tsogolo. Anthu amenewo angazengereze kulandira uthenga wathu panopo, koma tiyenera kukhalabe oleza mtima ndi kuzindikirabe kuti ndi anthu oyenera ulemu. Yehova “safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Kodi sitiyenera kukhala ndi malingaliro a Yehova? Ponena za anthu onse, tingatsegule njira yochitira umboni ngati nthaŵi zonse tiyesa kukhala monga anansi. Komanso paja timapeŵabe mtundu wa mayanjano umene ungatiloŵetse m’ngozi zauzimu. (1 Akorinto 15:33) Koma timasonyeza ‘chikondi,’ posanyalanyaza anthu amene ali ndi zikhulupiriro zosiyana ndi zathu.​—Machitidwe 27:3.

20. Kodi chitsanzo cha Yehova ndi cha Yesu Kristu chiyenera kutisonkhezera kuchitanji?

20 Inde, Yehova ndi Yesu Kristu amaona aliyense wa ife kukhala woyenera ulemu. Tiyenitu tikumbukire nthaŵi zonse mmene iwo amachitira zinthu ndipo ife mofananamo titsogolere pochitirana ulemu. Ndipo nthaŵi zonse tizikumbukira mawu a Ambuye wathu Yesu Kristu akuti: “Inu nonse muli abale.”​—Mateyu 23:8.

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi olambira anzanu muyenera kuwaona motani?

• Kodi chitsanzo cha Yehova ndi cha Yesu chikukusonkhezerani motani kulemekeza ena?

• Kodi amuna okwatira ndi makolo angalemekeze ena motani?

• Kuona Akristu anzawo monga abale awo kumasonkhezera akulu kuchita zinthu m’njira yotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Chitirani mkazi wanu ulemu ndi mawu othokoza

[Chithunzi patsamba 18]

Lemekezani ana anu mwa kuwamvetsera

[Chithunzi patsamba 18]

Sonyezani anthu a mumpingo ulemu