Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalasi la Gileadi la 108 Lilimbikitsidwa Kuchita Utumiki Wopatulika

Kalasi la Gileadi la 108 Lilimbikitsidwa Kuchita Utumiki Wopatulika

Kalasi la Gileadi la 108 Lilimbikitsidwa Kuchita Utumiki Wopatulika

M’BAIBULO, kulambira Mulungu nthaŵi zambiri amakutcha “utumiki wopatulika.” Mawuŵa amachokera m’mawu achigiriki omwe amatanthauza kutumikira Mulungu. (Aroma 9:4) Anthu okwana 5,562 omwe anamvetsera pulogalamu ya kumaliza maphunziro m’kalasi la 108 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, anamva okamba nkhani akupereka malangizo othandiza amene adzathandizadi omaliza maphunzirowo kuchita utumiki wopatulika wovomerezeka kwa Yehova Mulungu. *

Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anali tcheyamani. Pulogalamuyi inayamba ndi nyimbo nambala 52 yakuti, “Dzina la Atate Wathu.” Vesi lachiŵiri la nyimbo imeneyo limati: “Tifunanso kuyeretsa dzina lanu loyera.” Zimenezi zinasonyeza kuti ophunzira a kalasi lomaliza maphunzirowo (omwe anachokera m’mayiko 10) n’ngofunitsitsadi kuchokera mumtima kukagwiritsa ntchito zomwe aphunzira komwe adzatumizidwa monga amishonale, m’mayiko osiyanasiyana okwana 17.

M’mawu ake oyamba, Mbale Jaracz anasumika maganizo pa miyezi isanu yomwe ophunziraŵa anali kuphunzira Baibulo mozama komwe kunawakonzekeretsa kutumikira m’mayiko ena. Maphunziro ameneŵa anawathandiza ‘kuyesa zonse,’ kapena kuti, kupenda mosamalitsa m’kuunika kwa Mawu a Mulungu zomwe anali ataphunzira kale, ndi ‘kusunga chokomacho.’ (1 Atesalonika 5:21) Anawalimbikitsa kumamatira mokhulupirika kwa Yehova, Mawu ake, ndi ntchito yomwe anali kuphunzirayo. N’chiyani chomwe chidzawathandiza pochita zonsezi?

Malangizo Othandiza Pochita Utumiki Wopatulika

Lon Schilling, wa m’Komiti Yoyang’anira Beteli, anakamba nkhani yakuti “Kodi Mudzapambana Mayeso a Kuchita Zinthu Mosapambanitsa?” Anagogomeza phindu la kuchita zinthu mosapambanitsa, kumene kumasonyeza nzeru yaumulungu. (Yakobo 3:17) Kuchita zinthu mosapambanitsa kumaphatikizamo kulolera, kusakondera, kusachita monkitsa, kulingalira ena, ndi kudziletsa. “Anthu osapambanitsa pochita zinthu amakhala osamala pochita zinthu ndi ena. Safuna kuchita zinthu monkitsa,” anatero Mbale Schilling. Kodi chomwe chingam’thandize mmishonale kuchita mosapambanitsa n’chiyani? Kudzichepetsa, kugwiritsa ntchito mwayi wa kumvetsera ndi kuphunzira kuchokera kwa ena, ndi kufunitsitsa kulingalira maganizo a ena posanyalanyaza mfundo zachikhalidwe zaumulungu.​—1 Akorinto 9:19-23.

“Musaiwale Kudya!” unali mutu wochititsa chidwi wankhani yotsatira pa pulogalamu imeneyi. Nkhani imeneyi anaikamba ndi Samuel Herd, winanso wa m’Bungwe Lolamulira. Anagogomeza ubwino wa kudya mokwanira chakudya chauzimu kuti tikhalebe anyonga pochita utumiki wopatulikawu. “Changu chanu chauzimu,” anatero Mbale Herd, “chidzawonjezeka posachedwapa pamene mukuyamba ntchito yanu yolalikira ndi kuphunzitsa. Choncho, mudzafunikira kuwonjezera kadyedwe kanu ka chakudya chauzimu kuti mulinganize ndi kuchulutsa nyonga zanu.” Kudya mokwanira nthaŵi zonse chakudya chauzimu kungathandize mmishonale kupeŵa kufooka mwauzimu ndi kulakalaka kumudzi. Kumathandiza kukhutiritsa munthu ndi kum’chititsa kufunitsitsa kumamatira ku ntchito yake ya utumiki wopatulika.​—Afilipi 4:13.

Mlangizi wina wa Gileadi, Lawrence Bowen, analimbikitsa ophunzira omaliza maphunzirowo “Kubwerera Kuchiyambi.” Kodi anatanthauzanji? Anapempha omvetsera ake onse kutembenukira ku Miyambo 1:7, lomwe limati: “Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziŵa.” Wokamba nkhaniyu anafotokoza kuti: “Chidziŵitso chilichonse chosalabadira mfundo yofunika kwambiri ya kukhalapo kwa Yehova ndithudi sitingati n’chidziŵitso chenicheni kapenanso sichingapereke nzeru yeniyeni.” Mbale Bowen anayerekezera mfundo za m’Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi zidutswa za chithunzi. Pamene zidutswazo zilumikizidwa, chithunzicho chimayamba kuoneka. Pamene zidutswa zowonjezeka ziikidwa, chithunzicho chimakula kotero kuti chimaoneka bwino zedi ndipo munthu angachizindikire kwambiri. Zimenezi zingathandize aliyense kuchita utumiki wopatulika kwa Mulungu.

Wallace Liverance, wosunga kaundula wa Sukulu ya Gileadi, anakamba nkhani yotsiriza. Mutu wankhani yake unali wakuti “Perekani Chiyamiko Monga Nsembe Yanu kwa Mulungu.” Anasumika kwambiri pa nkhani ya Yesu ya kuchiritsa akhate khumi. (Luka 17:11-19) Mmodzi yekha ndiye amene anabwerera kukatamanda Mulungu ndi kukathokoza Yesu. “Mosakayika, ena onsewo anali okondwa kuti anayeretsedwa. Anakhutira ndi kuyeretsedwako, ndipotu zikuoneka kuti zomwe iwo ankafuna n’zakuti wansembe akadziŵe kuti iwo n’ngoyera,” anatero Mbale Liverance pothirira ndemanga. Kuyeretsedwa mwauzimu kupyolera mwa kuphunzira choonadi, limodzi ndi chiyamiko, ziyenera kusonkhezera aliyense kuthokoza Mulungu chifukwa cha ubwino wake. Ophunzira a kalasi la 108 la Gileadi analimbikitsidwa kusinkhasinkha pa ntchito zonse za Mulungu ndi ubwino wake n’cholinga chopanga utumiki wawo ndi kudzipereka kwawo chisonyezero cha kuyamikira Mulungu.​—Salmo 50:14, 23; 116:12, 17.

Zokumana Nazo ndi Mafunso a Mmene Angachitire

Mark Noumair, mlangizi wina wa Gileadi, anachititsa chigawo chotsatira cha pulogalamuyo. Chinali chokhudza zomwe a m’kalasilo anakumana nazo muutumiki wakumunda m’nthaŵi yonse yomwe anali kuchita maphunziro awo. Pa avareji, ophunziraŵa anathera zaka pafupifupi 12 muutumiki wa nthaŵi zonse asanabwere ku Gileadi. Adakali kusukulu komweko, anayambitsa maphunziro a Baibulo ochuluka ndi anthu amafuko osiyanasiyana, kusonyeza kuti ophunziraŵa akudziŵa mmene ‘angakhalire zonse kwa anthu onse.’​—1 Akorinto 9:22.

Pambuyo pa zokumana nazo za ophunzira, Charles Molohan ndi William Samuelson anafunsa ena a m’banja la Beteli ndi oyang’anira oyendayenda omwe nthaŵi inayake anakaphunzira pa Gileadi. Mmodzi mwa abale omwe anafunsidwawo, Robert Pevy, ankatumikira ku Philippines atatsiriza maphunziro m’kalasi la 51 la Gileadi. Anakumbutsa kalasilo kuti: “Nthaŵi zonse pakakhala vuto, aliyense amapereka maganizo ake a mmene vutolo lingathetsedwere. Ndiyeno nthaŵi zonse pamakhala winawake wanzeru kwambiri kuposa inuyo, amene adzapereka malingaliro abwino. Koma ngati muyang’ana m’Baibulo ndi kuyesa kufufuza malingaliro a Mulungu pa zinthu zinazake, palibe amene adzapereka malingaliro abwino kuposa amenewo. Nthaŵi zonse limenelo ndilo lidzakhala yankho lolondola.”

Potsiriza pulogalamu yauzimu yabwinoyo, John Barr, wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yamutu wakuti “Chitani Utumiki Wopatulika Wovomerezeka kwa Yehova.” Iye anasonyeza momwe utumiki wopatulika ungasonyezedwere muutumiki wakumunda pothandiza anthu owongoka mtima kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Atatchula mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 4:10, Mbale Barr anati: “Ngati tikufuna kulambira Yehova yekha, tiyenera kukana mitundu yonse yamachenjera ya kupembedza mafano, monga kusirira, kufunitsitsa chuma, ndi kudzikuza. Timakondwatu kwabasi tikaganizira za ntchito yabwino kwambiri imene amishonale athu aigwira kwa zaka zambiri chiyambire kuchiyambi kwa zaka za m’ma 1940! Ndipo tili ndi chikhulupiriro chonse kuti inuyo omaliza maphunziro a kalasi la Gileadi la 108 mutsatira chitsanzo chawo chabwinocho. Mudzachita utumiki wopatulika kwa Yehova, yemwe ndi yekhayo woyenera kuulandira.”

Chimenecho chinali chimake chabwino kwambiri cha pulogalamu yolimbikitsa imeneyi. Ndiyeno nthaŵi inakwana yolandira moni wochokera kwa anthu a mafuno abwino padziko lonse lapansi, komanso nthaŵi yopereka ma dipuloma, ndi yoŵerenga kalata yolembedwa ndi ophunziraŵa, kusonyeza kuyamikira kwawo maphunziro omwe alandira. Kalasi lomaliza maphunziroli linapemphedwa kukasonyeza kulimbikira kumalo awo antchito ndi potumikira Yehova. Onse amene analipo, kuphatikizapo alendo ochokera m’mayiko 25, anagwirizana potsiriza pulogalamu imeneyi ndi nyimbo ndi pemphero.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Pulogalamu imeneyi inachitika pa March 11, 2000, ku Likulu la Maphunziro a Watchtower ku Patterson, New York.

[Bokosi patsamba 23]

ZIŴERENGERO ZA KALASI

Chiŵerengero cha mayiko komwe achokera: 10

Chiŵerengero cha mayiko komwe atumizidwa: 17

Chiŵerengero cha ophunzira: 46

Avareji ya zaka zawo: 34

Avareji ya zaka m’choonadi: 16

Avareji ya zaka muutumiki wanthaŵi zonse: 12

[Chithunzi patsamba 24]

Kalasi la 108 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda uli m’munsiwu, mizera ikuŵerengedwa kuchokera kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kupita kulamanja m’mzera uliwonse.

(1) Amadori, E.; Cook, O.; Byrne, M.; Lee, A. (2) Newsome, D.; Pederzolli, A.; Bigras, H.; Kato, T.; Gatewood, D. (3) Eade, D.; Eade, J.; Wells, S.; Jamison, J.; Gonzales, M.; Gonzales, J. (4) Kato, T.; Lohn, D.; Niklaus, Y.; Preiss, S.; Foster, P.; Ibarra, J. (5) Amadori, M.; Manning, M.; James, M.; Boström, A.; Gatewood, B.; Newsome, D. (6) Foster, B.; Jamison, R.; Hifinger, A.; Koffel, C.; Koffel, T.; Byrne, G. (7) Hifinger, K.; Manning, C.; Cook, J.; Boström, J.; Lohn, E.; Pederzolli, A. (8) James, A.; Wells, L.; Preiss, D.; Niklaus, E.; Lee, M.; Ibarra, P.; Bigras, Y.