Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumakhulupirira Zomwe Simungathe Kuziona?

Kodi Mumakhulupirira Zomwe Simungathe Kuziona?

Kodi Mumakhulupirira Zomwe Simungathe Kuziona?

WINA akati, ‘Ndimangokhulupirira zokhazo zomwe ndingazione,’ sakhala akutanthauzadi zomwe akunenazo. Kwenikweni, tonsefe timakhulupirira zinthu zomwe sitingathe kuziona.

Mwachitsanzo, kusukulu mungakhale kuti munachitapo kafukufuku wokhala ndi cholinga choti mutsimikize kuti mphamvu ya maginito ilipodi. Zingachitike motere: Ikani tizidutswa tazitsulo pa pepala. Kenako ikani pepalalo pamwamba pa maginito. Mukayendetsa pepalalo, ngati matsenga, tizidutswa tazitsulo timasonkhana pamodzi chakumapeto kwa mbali zonse ziŵiri za maginito aja. Zimenezi zimapanga timizere toonetsa mphamvu ya maginitowo. Ngati munachita zimenezi, kodi munaona mphamvu yeniyeniyo ya maginito? Ayi, koma kuona mmene imakhudzira tizidutswa tazitsulo. Zimenezi zingakutsimikizireni kuti mphamvu ya maginito ilipodi.

Timavomereza zinthu zina zomwe sitingathe kuziona popanda kufunsa. Pamene tiona chithunzi chokongola chojambulidwa kapena kusirira chiboliboli, sitikayikira kuti panali mmisiri kapena wopanga chibolibolicho. Chotero pamene tilingalira za mathithi kapena kuona dzuŵa likuloŵa, kodi sitiyenera kusonkhezeredwa kulingalira kuti ziyenera kukhala ntchito za Mmisiri kapena Mpangi Wamkulu?

Chifukwa Chimene Ena Sakhulupirira

Chodabwitsa n’chakuti, anthu ena aleka kukhulupirira Mulungu chifukwa cha zimene anaphunzitsidwa kumatchalitchi. Izi n’zimene zinachitikira mwamuna wina ku Norway amene anauzidwa kuti Mulungu amatentha anthu oipa m’moto wa helo. Mwamunayu sanathe kumvetsa kuti ndi Mulungu wamtundu wanji amene angatenthe anthu mwanjirayi, ndiyetu anakhala wosakhulupirira kuti kuli Mulungu.

Koma pambuyo pake, mwamunayu anavomera kufufuza m’Baibulo, mothandizidwa ndi Mboni ya Yehova. Anadabwa kuphunzira kuti Baibulo siliphunzitsa kuti oipa amazunzika kumoto wa helo. Baibulo limayerekeza imfa ndi tulo. M’manda, sitimva kupweteka; sitilingalira kena kalikonse. (Mlaliki 9:5, 10) Mwamunayu anaphunziranso kuti anthu amene Mulungu adzawaweruza kukhala oipiratu osati n’kusintha adzakhala m’manda kosatha. (Mateyu 12:31, 32) Ena onse akufa adzaukitsidwa panthaŵi yoikika ya Mulungu, ndi chiyembekezo cholandira moyo wosatha m’Paradaiso. (Yohane 5:28, 29; 17:3) Kufotokozera kumeneku kunali komveka. Kunagwirizana ndi kunena kwa Baibulo kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Mwamuna woona mtima ameneyu anapitiriza phunziro lake la Mawu a Mulungu, ndipo m’kupita kwa nthaŵi, anakonda Mulungu wa Baibulo.

Ena amakana kuti kulibe Mlengi wachikondi chifukwa cha kuchuluka kwa mavuto komanso kusowa kwa chilungamo. Amagwirizana ndi mwamuna wa ku Sweden amene analoza kumwamba ndi kufunsa kuti: “Kodi zingatheke bwanji kuti kumwambaku kukhale Mulungu Wamphamvuyonse ndi wokoma mtima pamene pali katangale wochuluka ndi kuipa kotereku pansi pano?” Ndiye chifukwa chakuti palibe amene akadayankha funso limeneli, iyenso anakhala wosakhulupirira kuti kuli Mulungu. Pambuyo pake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Anaphunzira kuti Mawu a Mulungu amapereka yankho logwira mtima pafunso lakale kwambirilo lakuti, Chifukwa chiyani Mulungu amalola kuipa? *

Mwamuna woona mtima ameneyu anaphunzira kuti kuipa kumene kulipo sikutsimikizira kuti Mulungu kulibe. Tifotokoze motere: Munthu angapange mpeni kuti ugwiritsidwe ntchito pocheka nyama. Kasitomala angagule mpeniwo kuti akagwiritse ntchito osati yokachekera nyama koma kukaphera munthu. Ndiye chifukwa chokha chakuti mpeniwo wagwiritsidwa ntchito molakwika sizitanthauza kuti kulibe amene anaupanga mpeniwo. Mofananamo, chifukwa chokha chakuti dziko lapansili silikugwiritsidwa ntchito mogwirizana ndi cholinga chake sizikutanthauza kuti lilibe Mlengi wake.

Baibulo limaphunzitsa kuti ntchito za Mulungu ndi zangwiro. Iye ali “wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Mulungu amapereka mphatso zabwino kwa anthu, koma mphatso zina zagwiritsidwa ntchito molakwa, kuchititsa kuvutika kosasimbika. (Yakobo 1:17) Komabe, Mulungu adzathetsa kuvutika konse. Ndiyetu, “ofatsa adzalandira dziko lapansi, . . . nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:11, 29.

Mwamuna wa ku Sweden wotchulidwa poyamba uja anakhudzika mtima pamene anaona kuvutika kwa anthu anzake. Kunena zoona, kukhudzika mtima kwake kumasonyeza kuti Mulungu alipo. Koma motani?

Kwa anthu ambiri, pamene asiya kukhulupirira kuti kuli Mulungu amayamba kukhulupirira chisinthiko. Okhulupirira chisinthiko amaphunzitsa zakuti “zamoyo zamphamvu n’zokhazo zimapulumuka”​—kuti anthu ndi nyama zimapikisana mwa mitundu yawo kuti zikhale ndi moyo. Zamphamvu zimakhala ndi moyo; ndipo zofooka zimafa. Aka ndiko kakonzedwe kachilengedwe, amatero. Koma ngati “n’zachilengedwe” kuti zofooka zizifa kuti zipereke malo kwa zamphamvu, tingapereke zifukwa zotani pofotokoza mfundo yakuti, mofanana ndi mwamuna wa ku Sweden uja, anthu ena amphamvu amakhudzika mtima akaona anthu ena akuvutika?

Kufika pa Kum’dziŵa Mulungu

Sitingathe kuona Mulungu chifukwa sali ndi thupi laumunthu. Komabe, Mulungu amafuna kuti tim’dziŵe. Njira ina imene tingam’dziŵire ndi mwa kuyang’ana ntchito zake zodabwitsa​—“zithunzi zojambula” ndi “ziboliboli” za m’chilengedwe. Pa Aroma 1:20, Baibulo limafotokoza kuti: “Chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka [za Mulungu] ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.” Inde, ngati momwe kuyang’ana chithunzi chojambula kapena chiboliboli kungakuthandizireni kudziŵa umunthu wa mmisiri, kusinkhasinkha pa ntchito zodabwitsa za Mulungu kungakuthandizeni kuudziŵa bwino umunthu wake.

Zoona, sitingayankhe mafunso onse osautsa m’moyo mwa kungoyang’ana zimene Mulungu analenga. Koma tingapeze mayankho a mafunso otere mwa kufufuza m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Kuŵerenga Baibulo ndi maganizo abwino n’kumene kunathandiza amuna aŵiri otchulidwa koyambirira aja kufika potsimikiza kuti Mulungu alikodi, ndi kuti amasamaladi zimene zimatichitikira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kuti mudziŵe zifukwa zambiri zimene Mulungu walolera kuipa, chonde onani buku lakuti, Is There a Creator Who Cares About You?, mutu 10, losindikizidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu a Chithunzi patsamba 28]

J. Hester and P. Scowen (AZ State Univ.), NASA