Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupulumutsidwa pa Chilumba cha Robinson Crusoe

Kupulumutsidwa pa Chilumba cha Robinson Crusoe

Kupulumutsidwa pa Chilumba cha Robinson Crusoe

ROBINSON CRUSOE ndi chimodzi mwa zilumba zitatu m’nyanja ya Pacific zimene zimapanga dera la zilumba lotchedwa Juan Fernández. Zilumbazi zili pa mtunda wa makilomita pafupifupi 640 kuchokera ku gombe la dziko la Chile. * Kukula kwake kwa chilumba cha Robinson Crusoe ndi makilomita 93 ndipo anachitcha dzina limeneli kuchokera ku buku la m’zaka za m’ma 1700 lotchedwa Robinson Crusoe, lolembedwa ndi mlembi wachingelezi Daniel Defoe. Bukulo kwenikweni linazikidwa pa zokumana nazo za mwamuna wa ku Scotland, Alexander Selkirk, amene anakhala yekha pa chilumbachi kwa zaka zinayi.

Mbali ina ya chikwangwani chopezeka pachilumbachi imati: “Pamalo ano, tsiku ndi tsiku, kwa zaka zopitirira zinayi, m’malinyero wachisikotishi Alexander Selkirk ankangoyang’anira nkhaŵa ili bi kuti mwina angaone bwato lodzam’pulumutsa likubwera patali kudzam’chotsa ku maloŵa amene amakhalako yekha.” Pomalizira pake, Selkirk anapulumutsidwa ndi kum’tengera ku dziko lakwawo, kudziko limene silinam’khutiritsenso atakhala ku paradaiso wake wamng’onoyo. Akuti anafika ponena kuti: “Chilumba changa chokondedwa! Bwenzi ndisanakusiye!”

Patapita nthaŵi, chilumbachi chinkagwiritsidwa ntchito ngati malo achilango, kokhala anthu amene amachita “machimo a chikhulupiriro” otsutsana ndi Tchalitchi cha Katolika. Chilumba chimene Selkirk anachidziŵa kukhala paradaiso chidasinthiratu! Komatu, okhala pachilumbachi tsopano amasangalala ndi bata lomwe n’losadziŵika mbali zambiri za dziko lapansili. Moyo wosatekeseka, umene uli chikhalidwe pazilumba zambiri, umatheketsa munthu kuyambitsa zokambirana ndi wina aliyense.

Chilumba cha Robinson Crusoe chili ndi chiŵerengero chodziŵika kuboma cha anthu okwana pafupifupi 500, koma nthaŵi zambiri pafupifupi anthu 400 okha amapezeka pachilumbachi pachaka. Chifukwa chimodzi n’chakuti amayi ena ndi ana awo amakakhala kudziko la Chile nthaŵi ya sukulu, ndipo amabwera ku chilumbacho ndi mabanja awo m’miyezi ya tchuthi yokha.

Ngakhale kuti chilumba cha Robinson Crusoe ndi malo okongola ngati paki, anthu ena okhala pachilumbachi amasoŵa kanthu kena kauzimu ndipo akufunafuna mayankho. Ena afika poganiza kuti akufunikira kupulumutsidwa mwauzimu.

Kupulumutsa Mwauzimu

Ntchito yopulumutsa mwauzimu imeneyo inayamba m’chaka cha 1979. Mayi wina amene ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ku Santiago m’dziko la Chile, anasamukira ku chilumbachi nayamba kuphunzitsa ena zimene anali ataphunzira. Patapita nthaŵi, mwamuna wina amene amayendera za ntchito yake koma ndi mkulu mumpingo anafika pachilumbachi, ndipo anadabwa kupeza kagulu ka ophunzira Baibulo kakupita patsogolo mwauzimu ndi chithandizo cha mayiyo. Panthaŵi imene mkulu ameneyu anapitanso pachilumbachi patapita miyezi itatu, mphunzitsi wa Baibulo wokhala kutali ameneyu komanso ophunzira ake aŵiri anali okonzekera kubatizidwa, ndiyetu mkuluyo anatsogolera ubatizo wawo. Kenako, mmodzi mwa Akristu obatizidwa kumenewo anakwatiwa, ndipo pamodzi ndi mwamuna wake anapitiriza kufunafuna ena amene amafuna kupulumutsidwa mwauzimu. Mwamuna wake anatsogolera pomanga Nyumba ya Ufumu yaing’ono bwino imene ikugwiritsidwabe ntchito pachilumbacho. Posapita nthaŵi, chifukwa cha mavuto azachuma, anachoka ku Robinson Crusoe kupita ku mpingo wina m’chigawo chapakati cha dziko la Chile, kumene akutumikirabe Yehova mokangalika.

Pang’ono ndi pang’ono, kagulu ka pachilumbachi kanapitirira kukula pamene ena anali kupulumutsidwabe ku chipembedzo chonyenga. Komabe, popeza kuti ana a sukulu amayenera kuchoka kupita kudziko la Chile kuti akapitirize maphunziro a sekondale, gululo linachepa kungokhala alongo aŵiri obatizidwa ndi mtsikana wam’ng’ono. Gululo limakula nthaŵi ya tchuthi pamene amayi ena amabwerera ku chilumbacho. Zimenezi zimapatsanso mphamvu Akristu atatu amene amakhala kwa okhawo chaka chonse chathunthu. Ndiyetu Mboni za Yehova zimadziŵika pachilumba cha Robinson Crusoe chifukwa cha ntchito yaikulu ya alongo ameneŵa. N’zoona kuti ena okhala pa chilumbachi atsutsa ntchito yawo ngakhalenso kusonkhezera ena kuti akane uthenga wa Ufumu. Ngakhale zili choncho, mbewu za choonadi cha Baibulo zobzalidwa m’mitima yabwino zikupitirira kukula.

Kulimbikitsa Amene Apulumutsidwa

Kamodzi pachaka woyang’anira woyendayenda amakacheza pachilumbachi. Kodi zimakhala motani kukachezera Mboni zoŵerengeka zokhala ku chilumba chakutalicho? Woyang’anira dera wina akufotokoza ulendo wake woyamba wa ku Robinson Crusoe kuti:

“Ulendo umenewo unali wosangalatsa kwabasi. Unayamba 7:00 a.m. pamene tinanyamuka ku Valparaiso ulendo wa kubwalo la ndege la Cerrillos ku Santiago. Tinakwera ndege yaing’ono yokwera anthu asanu ndi aŵiri. Titayenda kwa maola aŵiri ndi mphindi 45, tinaona chakutali nsonga ya phiri m’kati mwa mitambo. Pamene timayandikira, chilumbacho chinayamba kuonekera​—thanthwe lochititsa chidwi pakati pa nyanja. Chimaoneka ngati sitima yosokera ikuyandama panyanja.

“Titatera, tinakwera bwato ulendo wakumudzi. Apa ndi apo, timaona miyala panyanja yopanga tizilumba timene pamapumulira akatumbu a ubweya a ku Juan Fernández. Akatumbu a ubweya ameneŵa ndi otetezedwa chifukwa alipo ochepa kwambiri. Mwadzidzidzi, china chake chinauluka pafupi ndi bwato n’kuloŵanso m’nyanja. Inali nsomba youluka imene zilimba zake zolukana zimafanana ndi mapiko. Imaoneka kuti imasangalala kujowera kunja kwa madzi kuti igwire tizilombo touluka. Inde, nthaŵi zina pogwira tizilomboto imagwidwa; kujowa kwake kumakopa chidwi cha adani amene amakhala okonzeka kuigwira pamene ikubwerera m’madzi.

“Pomalizira pake tinafika kumudzi wa San Juan Bautista (Yohane Mbatizi Woyera). Anthu oŵerengeka anali padokolo, mwina kudikira alendo kapena kungofuna kudziŵa amene azifika nthaŵi imeneyi. Tinachita chidwi ndi kaonekedwe kake kokongola​—phiri lalikulu ndi losongoka lotchedwa El Yunque (Chipala) lokutidwa ndi msipu wobiriŵira ndipo kumwamba thambo lili tetete ndi mitambo yoyera apo ndi apo.

“Kenako tinaona alongo athu achikristu ndi ana awo akutiyembekezera padoko. Inali nthaŵi yatchuti, ndiye anali ambiri kusiyana ndi mmene zimakhalira masiku onse. Titalonjerana mwachisangalalo, anatitengera ku chipinda chaching’ono koma chokongola chimene chinakhala nyumba yathu kwa mlungu umodzi.

“Unalidi mlungu wapadera, ndipo tinazindikira kuti udzatha mofulumira. Nthaŵi yathu inafunika kuigwiritsa ntchito bwino. Tsiku lomwelo, titangomaliza chakudya chamasana, tinakayendera wophunzira Baibulo amene amayembekezeka kukhala mlongo wathu wachikristu ndiponso kuloŵa m’paradaiso wauzimu wa Mulungu. Anali ndi chimwemwe chodzaza tsaya koma analinso ndi mantha. Ubatizo wake umene amauyembekezera kwa nthaŵi yaitali unali utafika. Tinakambirana naye zinthu zina zofunika kuti ayeneretsedwe kukhala wofalitsa wosabatizidwa wa uthenga wabwino. Tsiku lotsatira, anachita nawo ntchito yolalikira kwa nthaŵi yoyamba. Tsiku lachitatu, tinakambirana naye zofunika kuti abatizidwe. Mlunguwo usanathe, anabatizidwa.

“Misonkhano imene inachitika m’kati mwa mlunguwo inachirikizidwa bwino, ndi chiŵerengero chapamwamba chokwana 14. Tsiku lililonse panali dongosolo lopita muutumiki wakumunda, maulendo obwereza, maphunziro a Baibulo ndi maulendo aubusa. Chinalitu chilimbikitso kwa alongo athu amene amachita ntchitoyi okha chaka chonse!”

Pachilumbachi n’kovuta kuti amuna alandire choonadi, mwina chifukwa chakuti ntchito yawo yakuthupi sipereka mpata wokwanira. Ntchito yawo kwenikweni ndi yogwira nkhanu za mtundu wina, imene imafuna kudzipereka kwambiri. Malingaliro olakwika amene ambiri ali nawo amachititsa ambiri kusakhala ndi chidwi. Ngakhale zili choncho, tikuyembekeza kuti ambiri okhala pachilumbachi, amuna ndi akazi, adzalandira choonadi m’tsogolo.

Kufikira tsopano, anthu khumi apulumutsidwa pachilumbachi mwa kuzindikira choonadi komanso zolinga za Yehova Mulungu. Ena anasamuka pachilumbachi pazifukwa zosiyanasiyana. Koma ngakhale asamuke kapena akhale, kupulumutsidwa kwawo kwauzimu kwakhala kwatanthauzo kwambiri kusiyana ndi kupulumutsidwa kwa Alexander Selkirk. Tsopano ali m’paradaiso wauzimu kulikonse kumene angakhale. Alongo amene akukhalabe pachilumbachi pamodzi ndi ana awo akusangalala ndi malo okongolawo, koma kopambana zonse, ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo pamene dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso weniweni.

Ntchito Yopulumutsayo Ikupitiriza

Malinga ndi malo akeŵa, kagulu kochepa kameneka ka Mboni za Yehova kokhala ku Robinson Crusoe kamakhala kutali ndi abale ndi alongo ena onse auzimu. Komatu saona kuti ali okhaokha, ngati mwamuna wa ku Scotland uja, Selkirk. Mwa kulandira mabuku ateokalase, matepi avidiyo a misonkhano yadera ndi yachigawo mokhazikika kuchokera ku nthambi ya Watch Tower Society ya ku Chile katatu pachaka, komanso kuchezetsa kwa pachaka kwa woyang’anira dera, amakhalabe ogwirizana ndi gulu la Yehova. Chotero, akupitirizabe mokangalika monga anthu a ‘m’gulu lonse la abale m’dziko.’​—1 Petro 5:9, NW.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Chilumbachi chimadziŵika kuti Más a Tierra.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 9]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

CHILE

Santiago

CHILUMBA CHA ROBINSON CRUSOE

San Juan Bautista

El Yunque

NYANJA YA PACIFIC

CHILUMBA CHA SANTA CLARA

[Chithunzi]

Poyamba kuona chilumbachi, munthu amaona thanthwe lochititsa chidwi pakati pa nyanja

[Mawu a Chithunzi]

Mapu a Chile: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Phiri lalikulu komanso losongoka lotchedwa El Yunque (Chipala)

[Chithunzi patsamba 9]

Mudzi wa San Juan Bautista (Yohane Mbatizi Woyera)

[Chithunzi patsamba 9]

Tizilumba tating’ono timakhala malo opumulira akatumbu aubweya ndi akatumbu ena

[Zithunzi patsamba 10]

Tinakwera ndege yaing’ono kuchokera ku Santiago, m’dziko la Chile

[Chithunzi patsamba 10]

Gombe lamapiri la Chilumba cha Robinson Crusoe

[Chithunzi patsamba 10]

Nyumba ya Ufumu yaing’ono bwino pachilumbachi