Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Abusa Achikristu, ‘Tsegulani Mtima Wanu’!

Abusa Achikristu, ‘Tsegulani Mtima Wanu’!

Abusa Achikristu, Tsegulani Mtima Wanu’!

“YEHOVA ndiye mbusa wanga; sindidzasoŵa.” Mwa mawu amenewo, Davide anasonyeza chidaliro chake chachikulu mwa Mulungu wake. Mwauzimu, Yehova anam’tsogolera ku “busa lamsipu” ndi ku “madzi odikha,” kum’tsogolera “m’mabande a chilungamo.” Pozingidwa ndi otsutsa, Davide anachirikizidwa ndi kulimbikitsidwa, zomwe zinam’pangitsa kunena kwa Yehova kuti: “Sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine.” Pokhala ndi Mbusa Wamkulu wotero, Davide anatsimikiza mtima kuti “[a]dzakhala m’nyumba ya Yehova masiku onse.”​—Salmo 23:1-6.

Mwana wobadwa yekha wa Mulungu nayenso anaona chisamaliro chachikondi cha Yehova, ndipo iyenso anasonyeza chisamaliro chofananacho mwangwiro mwa kachitidwe kake ka zinthu ndi ophunzira ake pamene anali padziko lapansi. Chotero Malemba amamutcha “Mbusa Wabwino,” ndi “Mbusa wamkulu.”​—Yohane 10:11; Ahebri 13:20; 1 Petro 5:2-4.

Yehova ndi Yesu akupitirizabe kuŵeta anthu owakonda. Mbali ina ya kuŵeta kwawo imachitidwa mwa dongosolo lachikondi la kukhala ndi abusa aang’ono a mumpingo. Paulo anali kuyankhula ndi abusa aang’ono ameneŵa pamene anati: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang’anira, kuti muŵete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye yekha.”​—Machitidwe 20:28.

Kuŵeta nkhosa motsatira njira imene Yehova ndi Kristu Yesu anaika si ntchito yaing’ono, koma n’kofunika kwambiri tsopano kusiyana ndi kale lonse. Lingalirani za Mboni zoposa miliyoni imodzi zomwe zabatizidwa m’zaka zitatu zapitazi! Atsopano ngati amenewo alibe chidziŵitso chauzimu chimene chimadza mwa ntchito ya zaka zambiri. Lingaliraninso za Mboni zomwe zidakali ana kapena zosakwanitsa zaka 20 zakubadwa. Iwo amafunikira chisamaliro osati cha makolo okha komanso cha abusa aang’ono a mumpingo.

Ndithudi, Mkristu aliyense atha kukumana ndi chisonkhezero chochokera kwina, kuphatikizapo chisonkhezero cha mabwenzi. Onse ayenera kulimbikira kukana mphamvu yofuna kutikokera ku njira yadziko yongofuna kukhutiritsa zikhumbo za iwe mwini. M’mayiko ena, ofalitsa Ufumu angafooledwe posaona zipatso za uthenga wawo. Ofalitsa ambiri ali ndi mavuto aakulu okhudza thanzi. Mavuto a ndalama atha kumalanda ena chifuno chawo chofunafuna Ufumu choyamba. Kunena zoona, tonsefe​—kuphatikizapo awo amene akhalitsa m’choonadi​—tifunikira ndipo ndife oyenera kulandira thandizo la abusa achikondi.

Chisonkhezero Chabwino

Akristu a m’zaka za zana loyamba analangizidwa kuti: ‘Tsegulani mtima wanu’! (2 Akorinto 6:11-13, NW) Akulu achikristu angachite bwino kutsatira uphungu umenewu pochita ntchito yawo yoŵeta. Kodi angazichite motani zimenezo? Ndiponso bwanji za atumiki otumikira, ochuluka amene adzakhalanso abusa?

Kuti akulu achikristu akhale dalitso kwa nkhosa, sayenera kungosokhezeredwa ndi malingaliro akuti popeza imeneyo ndi ntchito yawo. Akulangizidwa kuti: ‘Ŵetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu [“mofunitsitsa,” NW], kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu.’ (1 Petro 5:2) Chotero kuŵeta kothandizadi kumaphatikizapo kufunitsitsa ndiponso changu chotumikira ena. (Yohane 21:15-17) Kumatanthauza kuona zosoŵa za nkhosa ndi kuchitapo kanthu mofulumira. Kumatanthauza kusonyeza mikhalidwe yabwino yachikristu yodziŵika monga zipatso za mzimu wa Mulungu pokhala ndi ena.​—Agalatiya 5:22, 23.

Nthaŵi zina, kuŵeta kumaphatikizapo kuchezera abale m’nyumba zawo. * Koma abusa amene ‘atsegula mtima wawo’ amadzipereka. Ndiko kuti, amachita zambiri kuwonjezera pa maulendo aubusa a nthaŵi zina. Amapezerapo mwayi pa mpata uliwonse kuti aŵete ena mumpingo.

Kuphunzitsa Ena Kukhala Abusa

Mbale aliyense, mosasamala kanthu za msinkhu wake, amene “akhumba udindo wa woyang’anira, aifuna ntchito yabwino.” (1 Timoteo 3:1) Atumiki otumikira ambiri asonyeza kuti n’ngofunitsitsa atalandiranso maudindo ena. Chotero, mwachimwemwe akulu amathandiza abale ofunitsitsa ameneŵa kuti apite patsogolo pokalamira udindo wa woyang’anira. Zimenezi zimatanthauza kuwaphunzitsa kukhala abusa aluso.

Chifukwa chomamatira ku miyezo yapamwamba ya Mulungu, mpingo wachikristu wa Yehova sunafooledwe ndi abusa onyenga ngati olongosoledwa pa Ezekieli 34:2-6. Ameneŵa anali onyansa m’maso mwa Yehova ndiponso pachifukwa chabwino. M’malo modyetsa nkhosa, iwo anadzidyetsa okha. Analephera kulimbikitsa odwala, kuchiritsa odwala, kumangirira othyoka, kapena kubweza omwazikana kapena osokera. Pochita zinthu monga mimbulu ndipo osati abusa, iwo anali kuopseza nkhosa. Nkhosa zonyalanyazidwazo zinamwazikana, n’kumangodziyendera uku ndi uko popanda wozisamalira.​—Yeremiya 23:1, 2; Nahumu 3:18; Mateyu 9:36.

Mosiyana ndi abusa osakhulupirika amenewo, abusa achikristu amatsatira chitsanzo cha Yehova. Amathandiza potsogolera nkhosa mwauzimu ku “busa lamsipu” ndi ku “madzi odikha.” Amayesetsa kuwatsogolera “m’mabande a chilungamo” mwa kuwathandiza kumvetsa Mawu a Yehova ndi kuwatsatira aliyense payekha. Angachite zimenezi bwino lomwe chifukwa chakuti ali “okhoza kuphunzitsa.”​—1 Timoteo 3:2.

Nthaŵi zambiri akulu amaphunzitsira papulatifomu pamisonkhano ya mpingo. Komabe, akulu amaphunzitsanso munthu aliyense payekha mwachindunji. Zoonadi, ena n’ngaluso pophunzitsa munthu payekha mwachindunji, pamene ena n’ngaluso kwambiri pokamba nkhani. Koma ngati wina alibe luso kwambiri pa mbali imodzi ya kuphunzitsa sizitanthauza kuti siwoyenera kukhala mphunzitsi. Akulu amaphunzitsa, pogwiritsa ntchito njira zonse zomwe angathe kugwiritsa ntchito, kuphatikizapo kuŵeta. Kuŵeta kwina kumachitidwa mochita kukonzekera, mwachitsanzo, maulendo aubusa olinganizidwa bwino. Koma kuŵeta kochuluka kungachitidwenso mwamwayi, zimenenso zimathandiza kwambiri.

Abusa ndi Aphunzitsi Nthaŵi Zonse

Dokotala amafunikira luso ndi chidziŵitso kuti agwire ntchito yake. Koma odwala amayamikira pamene awasonyeza kukoma mtima, chifundo, nkhaŵa, ndi chisamaliro chenicheni. Mikhalidwe imeneyi iyenera kukhala yophatikana ndi umunthu wake. Mikhalidwe yofananayo iyeneranso kukhala yophatikana ndi umunthu wa mphunzitsi ndi mbusa wabwino, iyenera kukhala mbali ya moyo wake wa tsiku ndi tsiku. Mphunzitsi weniweni amakhala wokonzeka kulangiza anthu amene ayandikana naye nthaŵi ina iliyonse yoyenera. “Mawu a pa nthaŵi yake kodi sali abwino?” imatero Miyambo 15:23. “Nthaŵi yake” ingakhale pamene akuyankhula papulatifomu, pamene akulalikira kunyumba ndi nyumba, kapena pamene akucheza ndi wina m’Nyumba ya Ufumu kapena patelefoni. Momwemonso, mbusa wabwino amayesetsa kusonyeza mikhalidwe yabwino, yosamala ena panthaŵi zonse, osati chabe popanga maulendo aubusa. Pokhala ‘atatsegula mtima wake,’ adzagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti aŵete nkhosa, kuzisamalira moyenera panthaŵi yake. N’zimene zimam’pangitsa kukhala wokondedwa pamaso pa nkhosa.​—Marko 10:43.

Wolfgang, amene tsopano ndi mkulu, akukumbukira nthaŵi pamene banja lake linachezeredwa ndi mtumiki wotumikira ndi mkazi wake. Iye akuti: “Ana athu anasangalala kwambiri poona mmene anasamalidwira ndiponso chisangalalo chimene tinali nacho. Mpaka pano amasimbabe.” Inde, mtumiki wotumikira ameneyu anasonyeza kuti amasamala; anali ‘kutsegula mtima wake.’

Mpata winanso ‘wotsegulira mtima wanu’ ndiwo mwa kuchezera odwala, kuwalembera kalata yaifupi yowalimbikitsa, kapena kuwaimbira telefoni​—china chilichonse kuti muwasonyeze kuti mumasamala za iwo! Athandizeni ngati n’kofunikira. Ngati ali ndi mawu, mvetserani. Kambani za zochitika zateokalase zabwino ndiponso zosangalatsa za mumpingo wanu ndi kwina. Athandizeni kulingalira kwambiri za tsogolo laulemerero losungidwira anthu okonda Yehova.​—2 Akorinto 4:16-18.

Kuwonjezera pa Maulendo Aubusa

Pokumbukira cholinga cha kuŵeta, n’zoonekeratu kuti kupanga maulendo olinganizidwa aubusa m’nyumba za abale, ngakhale kuti n’kofunika, ndi mbali imodzi chabe ya zonse zoloŵetsedwapo. Mbusa wachikondi ‘amatsegula mtima wake’ mwa kukhala wofikirika m’mikhalidwe yonse ndiponso panthaŵi ina iliyonse. Unansi wabwino umene amakulitsa ndi abale ake umawatsimikizira kuti m’nthaŵi ya zovuta, sayenera kuopa choipa, podziŵa kuti mbale wawo wachikondi, mbusa wachikristu, amasamala za iwo.​—Salmo 23:4.

Inde, abusa achikristu nonsenu ‘tsegulani mtima wanu.’ Sonyezani chikondi chenicheni kwa abale anu​—alimbikitseni, atsitsimuleni, amangirireni mwauzimu m’njira iliyonse yomwe mungathe. Athandizeni kukhala okhazikika m’chikhulupiriro. (Akolose 1:23) Podalitsidwa ndi abusa achikristu amene ‘amatsegula mtima wawo,’ nkhosa sizidzasoŵa kanthu. Zidzatsimikiza mtima, monga momwe anachitira Davide, kukhala m’nyumba ya Yehova masiku onse. (Salmo 23:1, 6) Mbusa wachikondi angafunenso chiyani?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Njira zopangira maulendo aubusa mungazipeze mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993, masamba 20-3, ndi ya March 15, 1996, masamba 24-7.

[Bokosi patsamba 30]

Abusa Achikristu

• Amatumikira mwakhama komanso mofunitsitsa

• Amadyetsa ndi kusamalira nkhosa

• Amathandiza ena kuti akalamire kukhala abusa

• Amachezera odwala ndi kuwasamalira

• Amakhala okonzeka kuthandiza abale awo nthaŵi zonse

[Zithunzi patsamba 31]

Kaya ali muutumiki wakumunda, pamisonkhano yampingo, kapena pa macheza, akulu ndi abusa nthaŵi zonse