Kodi Mtendere wa Mumtima Mungaupeze Kuti?
Kodi Mtendere wa Mumtima Mungaupeze Kuti?
Pali zinthu zambiri zosiyana pakati pa nthaŵi yathu ino ndi nthaŵi ya Thoreau, yemwe watchulidwa m’nkhani yapitayo. Kusiyana kwakukulu ndi kwakuti, lerolino pali malangizo ambiri a mmene munthu angapezere mtendere wa mumtima. Akatswiri a zamaganizo ndi olemba mabuku odziphunzitsira munthu payekha, ngakhalenso olemba manyuzipepala amapereka malingaliro awo. Malangizo awowo angakhale othandiza kwa kanthaŵi chabe; koma kupeza njira zothetseratu mavuto ameneŵo, n’kofunika malangizo akuya kwambiri. Ndi omwe anthu amene atchulidwa m’nkhani yapitayo anapeza.
ANTÔNIO, Marcos, Gerson, Vania, ndi Marcelo anakulira m’mikhalidwe yosiyanasiyana ndipo anali ndi mavuto osiyanasiyananso. Komabe, iwo anali ndi zinthu pafupifupi zitatu zofanana. Choyamba, panali nthaŵi ina pamene anali “opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m’dziko lapansi.” (Aefeso 2:12) Chachiŵiri, iwo ankalakalaka mtendere wa mumtima. Ndipo chachitatu ndi chakuti, onsewo anapeza mtendere wa mumtima umene amafunawo atavomera phunziro la Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pamene anapita patsogolo ndi phunzirolo, iwo anazindikira kuti Mulungu amachita nawo chidwi. Inde, monga momwedi Paulo anauzira Aatene a m’tsiku lake, Mulungu “sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Kukhulupirira zimenezi ndi mtima wonse ndiko chinthu chachikulu chopezera mtendere wa mumtima.
N’chifukwa Chiyani Pali Mtendere Wochepa Chonchi?
Baibulo limapereka zifukwa ziŵiri zikuluzikulu zomwe zikuchititsa kuti padziko lapansi pano pakhale mtendere wochepa, kaya ndi mtendere wa mumtima kapena mtendere wa pakati pa anthu. Chifukwa choyamba chafotokozedwa pa Yeremiya 10:23 kuti: “Njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Munthu alibe nzeru komanso samatha kuoneratu patali kuti adzilamulire yekha popanda thandizo, ndipo ndi thandizo lochokera kwa Mulungu lokha lomwe ndi lopindulitsadi. Anthu amene safuna kutsogozedwa ndi Mulungu sadzapeza mtendere wokhalitsa m’pang’ono pomwe. Chifukwa chachiŵiri chimene chikuchititsa kuti mtendere ukhale wochepa chimapezeka m’mawu a mtumwi Yohane akuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Popanda kutsogozedwa ndi Mulungu, zoyesayesa za munthu zopezera mtendere zizilepheretsedwa nthaŵi zonse chifukwa cha ntchito za wosaonekayo koma weniweni, ndiponso wamphamvu kwambiri—“woipayo,” Satana.
Pazifukwa ziŵiri zimenezi—zakuti anthu safuna kutsogozedwa ndi Mulungu ndi kuti Satana ndi wotanganidwa kwambiri padziko lapansi pano—mtundu wonse wa anthu uli pamavuto kwambiri. Mtumwi Paulo anafotokoza bwino lomwe zimenezi kuti: “Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano.” (Aroma 8:22) Ndani angatsutse zimenezi? M’mayiko olemera pamodzi ndi osauka omwe, mavuto a m’banja, upandu, kusoŵeka chilungamo, kusemphana malingaliro, kusadalirika kwa nkhani zachuma, kudana kwa mitundu ndi kwa mafuko, kuponderezedwa, matenda, ndi zina zambiri, zimasoŵetsa anthu mtendere wawo wa mumtima.
Komwe Kungapezeke Mtendere wa Mumtima
Antônio, Marcos, Gerson, Vania, ndi Marcelo ataphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo, anaphunzira zinthu zomwe zinasintha miyoyo yawo. Mwa zina, iwo anaphunzira kuti mkhalidwe wa dzikoli udzasintha tsiku lina. Chimenechi si chiyembekezo chosamvetsetseka bwino chongoti zinthu zonse zidzakhala bwino pamapeto, ayi. Ndi chiyembekezo choona, chikhulupiriro chokhala ndi maziko olimba chakuti Mulungu ali ndi chifuno pa mtundu wa anthu ndiponso kuti ngakhale panopo tingapindule ndi chifuno chimenecho ngati tichita cholinga chake. Iwo anagwiritsa ntchito zimene anaphunzira m’Baibulo, pa miyoyo yawo ndipo zinthu zinawayendera bwino. Anapeza chimwemwe ndiponso mtendere wochuluka kusiyana ndi mmene ankalingalilira.
Antônio sachita nawonso zionetsero za kukwiya ndiponso ndewu pantchito. Akudziŵa kuti kusintha komwe kungabwere mwanjira imeneyo n’kochepa ndiponso kwa kanthaŵi chabe. Mtsogoleri wakale wa gulu la anthu a pantchito ameneyu anaphunzira za Ufumu wa Mulungu. Ndiwo Ufumu umene anthu ambiri amapempherera akamanena pamtima Pemphero la Ambuye (kapena, la Atate Wathu) ndi kunena kwa Mulungu kuti: “Ufumu wanu udze.” (Mateyu 6:10a) Antônio anaphunzira kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni la kumwamba limene lidzadzetsere anthu mtendere weniweni.
Marcos anaphunzira kugwiritsa ntchito uphungu wanzeru wa m’Baibulo pankhani ya ukwati. Chotsatira chake n’chakuti, munthu yemwe kale anali wandale ameneyu tsopano mwachimwemwe wagwirizananso ndi mkazi wake. Nayenso akuyembekezera nthaŵi, posachedwapa, pamene Ufumu wa Mulungu udzasinthe dongosolo ladziko ladyera, laumbombo lino ndi kubweretsa dongosolo labwino. Amamvetsa bwino kwambiri tanthauzo la chiganizo cha m’Pemphero la Ambuye chomwe timaŵerenga kuti: “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10b) Chifuno cha Mulungu chikadzachitidwa padziko lapansi, anthu adzakhala ndi moyo umene sanakhalepo nawo n’kale lonse.
Bwanji ponena za Gerson? Si munthunso wongoyendayenda mwachisawawa ndi wakuba. Moyo wa mwana yemwe kale anali wongoyendayenda m’misewu ameneyu uli ndi tanthauzo tsopano chifukwa chakuti akugwiritsa ntchito mphamvu zake
kuthandiza ena kupeza mtendere wa mumtima. Monga momwe zochitika zimenezi zikusonyezera, kuphunzira Baibulo ndi kugwiritsa ntchito zinthu zomwe limanena kungasinthe moyo wa munthu ndi kukhala wabwino.Mtendere wa Mumtima M’dziko Lodzala ndi Mavuto
Tsinde la kukwaniritsidwa kwa chifuno cha Mulungu m’mbiri yonse ndilo Yesu Kristu, ndipo pamene anthu aphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, amaphunzira zambiri ponena za iye. Pausiku womwe anabadwa, angelo anaimbira Yehova zitamando kuti: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.” (Luka 2:14) Yesu atakula, ankafunitsitsa kutukula miyoyo ya anthu. Ankamvetsa malingaliro awo ndipo ankasonyeza chifundo chachikulu kwa ovutika ndi odwala. Ndipo, mogwirizana ndi mawu a angelo aja, iye anadzetsa mtendere wa mumtima kwa ofatsa. Pamapeto pa utumiki wake, iye anauza ophunzira ake kuti: “Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.”—Yohane 14:27.
Yesu sanali munthu wongothandiza anthu chabe koma analinso ndi zinthu zina zambiri. Anadziyerekezera ndi mbusa, ndipo otsatira ake ofatsa anawafanizira ndi nkhosa pamene anati: “Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka. Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.” (Yohane 10:10, 11) Inde, mosiyana ndi atsogoleri ambiri lerolino amene poyamba penipeni amasamalira zawo zokha, Yesu anataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.
Kodi tingapindule motani ndi zimene Yesu anachita? Anthu ochuluka amadziŵa bwino kwambiri mawu akuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu kumafuna, choyamba pa zinthu zonse, kum’dziŵa iye ndi Atate wake, Yehova. Kudziŵa Mulungu ndi Yesu Kristu kungatsogolere ku unansi wolimba ndi Yehova Mulungu umene udzatithandiza kupeza mtendere wa mumtima.
Yesu anati: “Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine. Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzawonongeka ku nthaŵi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m’dzanja langa.” (Yohane 10:27, 28) Ndi mawu abwino ndi otonthoza kwambiritu ameneŵa! Inde, Yesu anayankhula mawu ameneŵa zaka pafupifupi 2000 zapitazo, komatu lerolino n’ngamphamvu kwambiri mofanana ndi panthaŵiyo. Osaiwala kuti Yesu Kristu ndi wamoyo ndipo akugwira ntchito, akulamulira tsopano monga Mfumu yokhazikitsidwa ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Mofanana kwambiri ndi momwe analiri pamene anayenda padziko lapansi zaka zambiri zapitazo, iye akuderabe nkhaŵa anthu ofatsa amene akulakalaka mtendere wa mumtima. Komanso, iye akadali Mbusa wa nkhosa zake. Ngati titamutsata, iye adzatithandiza kupeza mtendere wa mumtima, umene umaphatikizapo chiyembekezo chotsimikizirika cha kudzaona m’tsogolo mwa bata, zimene zidzatanthauza kuti mudzakhala mopanda chiwawa, nkhondo, ndi upandu.
Mapindu enieni amadza mwa kudziŵa ndi kukhulupirira kuti Yehova adzatithandiza kudzera mwa Yesu. Kodi mukukumbukira za Vania, yemwe anasiyiridwa ntchito zikuluzikulu pamene anali mtsikana ndiponso ankaganiza kuti Mulungu anamuiwala? Tsopano Vania akudziŵa kuti Mulungu sanamusiye. Iye akuti: “Ndinaphunzira kuti Mulungu ndi munthu weniweni wokhala ndi mikhalidwe yabwino. Chikondi chake chinam’sonkhezera kutumiza mwana wake ku dziko lapansi kuti adzatipatse moyo. N’kofunika kwambiri kudziŵa zimenezi.”
Marcelo akuchitira umboni kuti unansi wake ndi Mulungu ndi weniweni. Mnyamata amene kale ankakonda kupita ku mapwando ameneyu akuthirira ndemanga kuti: “Kaŵirikaŵiri achinyamata sadziŵa choti achite, ndipo pomaliza pake amagwa m’mavuto. Ena amayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, monga momwe ndinkachitira ine. Ndili ndi chiyembekezo chakuti enanso
ambiri adzadalitsidwa, monga ndadalitsidwira ine, mwa kuphunzira choonadi ponena za Mulungu ndi Mwana wake.”Mwa kuphunzira Baibulo mosamalitsa, Vania ndi Marcelo anayamba kukhulupirira Mulungu kwambiri ndiponso anayamba kum’dalira chifukwa cha kufunitsitsa kwake kuwathandiza kuthana ndi mavuto awo. Ngati titachita zimene iwo anachita, kuphunzira Baibulo ndi kugwiritsa ntchito zomwe limanena, tidzapeza mtendere wochuluka wa mumtima, ngati womwe iwo anapeza. Ndiyeno kulimbikitsa kwa mtumwi Paulo kudzakhala kothandiza kwambiri kwa ife: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.
Kupeza Mtendere Weniweni Lerolino
Yesu Kristu akutsogolera anthu anjala ya choonadi kuyenda m’njira yomwe imatsogolera ku moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso. Pamene akuwatsogolera ku kulambira Mulungu koona, iwo amapeza mtendere wofanana ndi uja wofotokozedwa m’Baibulo kuti: “Ndipo anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.” (Yesaya 32:18) Ndipo mtendere umenewo ndi chifaniziro chabe cha mtendere womwe adzakhale nawo m’tsogolo muno. Timaŵerenga kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:11, 29.
Chotero, kodi tingakhale ndi mtendere wa mumtima lerolino? Inde. Kuwonjezera pamenepo, tingakhale otsimikiza kuti posachedwapa, Mulungu adzadalitsa anthu omvera ndi mtendere wochuluka kusiyana ndi kale lonse. Nangano, bwanji osam’pempha mwa pemphero kuti akupatseni mtendere wake? Ngati muli ndi mavuto omwe akukusoŵetsani mtendere, pempherani monga momwe Davide anapempherera kuti: “Masautso a mtima wanga akula: Munditulutse m’zondipsinja. Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga; ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.” (Salmo 25:17, 18) Khalani otsimikiza kuti Mulungu amamva mapemphero oterowo. Iye amatambasula dzanja lake ndi kugaŵira mtendere anthu onse amene akuufunitsitsa. Mwachikondi, timatsimikiziridwa kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m’choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwawo, nadzawapulumutsa.”—Salmo 145:18, 19.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Munthu alibe nzeru komanso samatha kuoneratu patali kuti adzilamulire yekha popanda thandizo, ndipo ndi thandizo lochokera kwa Mulungu lokha lomwe ndi lopindulitsadi
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Kudziŵa Mulungu ndi Yesu Kristu kungatsogolere ku unansi wolimba ndi Yehova Mulungu umene udzatithandiza kupeza mtendere wa mumtima
[Chithunzi patsamba 7]
Kutsatira uphungu wa m’Baibulo kumadzetsa mtendere m’moyo wabanja