Kodi Mukupindula ndi Zitsanzo Zabwino?
Kodi Mukupindula ndi Zitsanzo Zabwino?
“MUNAYAMBA kukhala inu chitsanzo kwa onse akukhulupirira m’Makedoniya ndi m’Akaya.” Mtumwi Paulo ndiye analemba mawu ameneŵa kwa Akristu okhulupirika a ku Tesalonika. Iwo anaperekadi chitsanzo chabwino zedi kwa okhulupirira anzawo. Ngakhale zili motero, Atesalonika nawonso anali kutsatira chitsanzo chimene Paulo ndi anzake anapereka. Paulo anati: “Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu; monga mudziŵa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu. Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu.”—1 Atesalonika 1:5-7.
Inde, Paulo sanali kungolalikira mwa kuphunzitsa kokha ayi. Moyo wake weniweniwo unalinso ulaliki, unali chitsanzo cha chikhulupiriro, chipiriro, ndi kudzimana. Pachifukwa chimenechi, Paulo ndi anzake anadzakhala chisonkhezero champhamvu m’moyo wa Atesalonika, kuwasonkhezera kulandira choonadi “m’chisautso chambiri.” Komano, si kuti Paulo ndi antchito anzake ndiwo okha amene anali ndi chisonkhezero chabwino pa okhulupirira amenewo. Chitsanzo cha enanso amene anapirira chisautso chinawalimbikitsanso. Paulo analembera Atesalonika kuti: “Inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m’Yudeya mwa Kristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva koŵaŵa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda.”—1 Atesalonika 2:14.
Yesu Kristu—Chitsanzo Chabwino Koposa
Ngakhale kuti Paulo iyemwini anali atapereka chitsanzo chotsanzirika, sanalephere kuloza kwa Yesu Kristu monga chitsanzo choyambirira chimene Akristu ayenera kutsatira. (1 Atesalonika 1:6) Kristu anali ndipo ndiyebe Chitsanzo chathu chabwino koposa. Mtumwi Petro analemba kuti: “Kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zoŵaŵa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.”—1 Petro 2:21.
Komabe, Yesu anamaliza moyo wake monga munthu padziko lapansi zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Tsopano “akukhala m’kuunika kosakhozeka kufikako” monga cholengedwa chauzimu chosakhoza kufa. Pamene alipo, “munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona.” (1 Timoteo 6:16) Nangano tingam’tsanzire motani? Njira imodzi ndiyo kuphunzira nkhani zinayi za m’Baibulo zosimba moyo wa Yesu. Mauthenga Abwino amatiunikira ponena za umunthu wake, njira yake ya moyo, ndi “mtima” wake. (Afilipi 2:5-8) Chidziŵitso chowonjezeka chingapezeke mwa kuphunzira buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, lomwe limalongosola mwatsatanetsatane zochitika m’moyo wa Yesu motsatira nthaŵi imene zinachitika. *
Chitsanzo cha Yesu cha kudzimana chinam’khudzadi mtima mtumwi Paulo. Iye anauza Akristu a ku Korinto kuti: “Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu.” (2 Akorinto 12:15) Mtimatu wa Kristu weniweni! Pamene tilingalira za chitsanzo changwiro cha Kristu, ifenso tiyenera kukhudzidwa mtima kuti tifune kum’tsanzira m’njira yathu ya moyo.
Mwachitsanzo, Yesu anatiphunzitsa kuti tiyenera kudalira lonjezo la Mulungu lakuti adzatipatsa zosoŵa zathu zakuthupi. Koma sanalekezere pomwepo. Anasonyeza chikhulupiriro ndi chidaliro Mateyu 6:25; 8:20) Kodi nkhaŵa ya zinthu zakuthupi ndi imene ikulamulira maganizo ndi zochita zanu? Kapena kodi moyo wanu ukusonyeza umboni wakuti mukufunafuna Ufumu choyamba? Nanga bwanji za maganizo anu ponena za utumiki wa Yehova? Kodi akufanana ndi a Chitsanzo chathu, Yesu? Baibulo limasonyeza kuti Yesu sanali kungolimbikitsa changu koma nthaŵi zambiri anasonyeza changu choyaka moto. (Yohane 2:14-17) Komanso, Yesu anapereka chitsanzo chabwino zedi pankhani ya chikondi! Eyatu, mpaka anapereka moyo wake m’malo mwa ophunzira ake! (Yohane 15:13) Kodi mukutsanzira Yesu mwa kusonyeza chikondi kwa abale anu achikristu? Kapena kodi mumalola zophophonya za ena kukuletsani kuwasonyeza chikondi?
chachikulu zedi mwa Yehova tsiku ndi tsiku. Anati: “Ankhandwe ali nazo nkhwimba zawo, ndi mbalame za m’mlengalenga zisa zawo, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wake.” (Pamene tikuyesayesa kutsatira chitsanzo cha Kristu, nthaŵi zambiri tidzapereŵera. Koma ndithudi Yehova amasangalala ndi zoyesayesa zathu kuti ‘tivale Ambuye Yesu Kristu.’—Aroma 13:14.
“Zitsanzo za Gulu”
Kodi lerolino muli anthu ena mumpingo amene angakhale zitsanzo kwa ife? Eya, alimodi! N’kofunika kwambiri kuti abale oikidwa m’maudindo azipereka chitsanzo. Paulo anauza Tito, yemwe ankatumikira mipingo ya ku Krete ndi kuika oyang’anira, kuti mkulu aliyense woikidwa ayenera kukhala “wopanda chirema [“wosanenezedwa mlandu,” NW].” (Tito 1:5, 6) Mtumwi Petro mofananamo analangiza “akulu” kuti akhale “zitsanzo za gululo.” (1 Petro 5:1-3) Bwanjinso za amene akutumikira monga atumiki otumikira? Iwonso ayenera kukhala “akutumikira bwino.”—1 Timoteo 3:13.
Ndithudi, ndi kukokomeza zinthu kuyembekeza kuti mkulu kapena mtumiki wotumikira aliyense akhale wamaluso apadera m’mbali zonse za utumiki wachikristu. Paulo anauza Akristu a ku Roma kuti: “[Tili] ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chopatsidwa kwa ife.” (Aroma 12:6) Abale osiyanasiyana ali ndi maluso m’mbali zosiyanasiyana. Si bwino kuyembekeza kuti zonse zomwe akulu adzachita ndi kunena zidzakhala zangwiro. “Timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri,” limaterotu Baibulo pa Yakobo 3:2. “Munthu akapanda kukhumudwa pa mawu, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.” Koma mosasamala kanthu za zophophonya zawo, akulu athabe “[kukhala zitsanzo] kwa iwo okhulupirira, m’mawu, m’mayendedwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima” monga analili Timoteo. (1 Timoteo 4:12) Akulu akakhala otero, awo a m’gulu adzatsatira mosavuta uphungu wa pa Ahebri 13:7 wakuti: “Kumbukilani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mawu a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.”
Zitsanzo Zinanso Zamakono
Pazaka makumi angapo zapitazi, anthu enanso ambirimbiri asonyeza kukhala zitsanzo zabwino. Bwanji za zikwizikwi za amishonale odzimana amene “adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena ana, kapena minda” kuti akakwaniritse ntchito yachikristu m’mayiko ena? (Mateyu 19:29) Lingaliraninso za oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo, amuna ndi akazi amene akutumikira monga antchito odzifunira pamaofesi a Watch Tower Society, ndi apainiya amene akutumikira m’mipingo. Kodi zitsanzo zimenezi zingasonkhezere ena? Mlaliki wina wachikristu ku Asia akukumbukira mmishonale wa m’kalasi lachisanu ndi chitatu la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Ananena kuti mbale wokhulupirikayu anali “wokonzeka kupirira udzudzu wadzaoneni ndi kutentha konyamula mtima. . . . Koma chochititsanso chidwi kwambiri chinali luso lake lolalikira m’zinenero za Chitchaina ndi Chimalaya ngakhale kuti iyeyo kwawo kunali ku Mangalande.” Chotsatira cha chitsanzo chabwino chimenechi? Mbaleyo anati: “Kudekha kwake ndi chidaliro chake zinandisonkhezera kuti ndidzakhale mmishonale ndikadzakula.” M’posadabwitsa kuti mbaleyu anadzakhaladi mmishonale.
Buku la Watch Tower Publications Index lili ndi mpambo wa nkhani zosimba mbiri ya moyo wa anthu ambirimbiri zimene zatuluka m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Nkhani zimenezi zimasimba za anthu amene anasiya ntchito ndi zolinga zawo zakudziko, amene anagonjetsa zofooka zawo, kusanduliziratu maumunthu awo, amene anasunga kaonedwe koyenera poyang’anizana ndi mavuto aakulu, ndipo anasonyeza khama, anapirira, anakhulupirika, anasonyeza kudzichepetsa, ndi mzimu wodzimana. Ponena za nkhani zimenezi, woŵerenga wina analemba kuti: “Zimandipanga kukhala Mkristu wodzichepetsa ndi woyamikira kwambiri pamene ndiŵerenga zimene ena akumana nazo, ndipo zandipangitsa kusaganiza kwambiri zandekha kapena kungosamala za mwinine.”
Kuwonjezera pamenepa, musaiŵale zitsanzo zabwino za mumpingo mwanu: mitu yamabanja amene amayesetsa kusamalira mabanja awo pazosoŵa zawo zakuthupi ndi zauzimu zomwe; alongo—kuphatikizapo amayi osakwatiwa—amene amalimbana ndi mavuto a kulera ana pamene akukhalabe otanganidwa mu utumiki; achikulire ndi olumala amene akupitirizabe kukhala okhulupirika mosasamala kanthu za kuwonjezeka kwa zofooka zawo za m’thupi ndi matenda. Kodi zitsanzo ngati zimenezo sizikukhudzani?
Zoonadi, dziko lapansi n’lodzaza ndi zitsanzo zoipa. (2 Timoteo 3:13) Komabe, talingalirani mawu olimbikitsa a Paulo kwa Akristu a ku Yudeya. Atasimba kaye za khalidwe lopereka chitsanzo chabwino la amuna ndi akazi ambiri achikhulupiriro akale, mtumwi Paulo anawalimbikitsa kuti: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, . . . [tiyeni] tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu.” (Ahebri 12:1, 2) Akristu lerolinonso ndi ozingidwa ndi ‘mtambo waukulu’ wa zitsanzo zabwino—zakale ndi zamakono zomwe. Kodi mukupinduladi nazo? Mutha kutero ngati ndinu wotsimikiza mtima kukhala ‘wosatsanza chimene chili choipa komatu chimene chili chokoma.’—3 Yohane 11.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mawu Otsindika patsamba 20]
Ndi kukokomeza zinthu kuyembekeza kuti mkulu kapena mtumiki wotumikira aliyense akhale wamaluso apadera m’mbali zonse za utumiki wachikristu
[Zithunzi patsamba 21]
Akulu ayenera kukhala “zitsanzo za gulu”