Kodi Mungapeze Mtendere wa Mumtima?
Kodi Mungapeze Mtendere wa Mumtima?
Kalero mu 1854, wolemba mabuku wa ku America, Henry Thoreau analemba kuti: “Unyinji wa anthu ukukhala movutika m’maganizo.”
Maumboni akusonyeza kuti, m’tsiku lake anthu ambiri analibe mtendere wa mumtima. Komatu, zimenezo ndi zaka pafupifupi 150 zapitazo. Kodi zinthu zasintha lerolino? Kapena kodi mawu a Thoreau akugwirabe ntchito? Nanga bwanji ponena za inuyo panokha? Kodi ndinu wokhutitsidwa ndi mtendere? Kapena kodi ndinu wosatetezeka, wosatsimikiza ponena za m’tsogolo, ‘wovutika m’maganizo,’ kuti tinene m’mawu ena zimene Thoreau ananena?
N’ZOMVETSA chisoni kuti m’dzikoli muli zinthu zambiri zimene zimasoŵetsa anthu mtendere wa mumtima. Tiyeni tingotchulako zochepa chabe. M’mayiko ambiri ulova ndi kupeza ndalama zochepa zimadzetsa umphaŵi pamodzi ndi mavuto a zachuma. M’mayiko ena anthu ambiri amathera nyonga zawo zochuluka kufunafuna chuma cha mtengo wapatali ndiponso katundu wakuthupi. Komabe, kaŵirikaŵiri kukhala mwa mpikisano chifukwa cha zinthu zimenezi kumadzetsa nkhaŵa, osati mtendere. Matenda, nkhondo, upandu, kusoŵeka chilungamo, ndi kuponderezana zimasoŵetsanso anthu mtendere.
Iwo Ankafuna Mtendere wa Mumtima
Anthu ambiri safuna kupirira mmene zinthu zilili pa dzikoli. Antônio * anali mtsogoleri wa gulu la anthu a pantchito pa fakitale ina yaikulu mumzinda wa São Paulo, m’dziko la Brazil. Poyembekeza kuti adzatukula moyo wake, iye anachita nawo zionetsero zotsutsa ndi zosonyeza kukwiya, koma zimenezi sizinam’dzetsere mtendere wa mumtima.
Ena amayembekezera kuti ukwati udzawadzetsera mtendere m’moyo wawo, koma angathe kukhumudwa. Marcos anali wamalonda wopambana kwambiri. Analoŵa m’ndale ndi kukhala woyang’anira mzinda wina wamafakitale ambiri. Komabe, moyo wake wam’banja sunali wopambana m’pang’ono pomwe. Ana ake atachoka panyumbapo, iye anapatukana ndi mkazi wake chifukwa cha kusiyana maganizo kwakukulu.
Gerson, mwana wongoyendayenda m’misewu ya mumzinda wa Salvador, m’dziko la Brazil, ankafuna zinthu zosangalatsa. Anayenda m’mizinda yosiyanasiyana, pamodzi ndi madalaivala a magalimoto akuluakulu. Posapita nthaŵi yaitali analoŵerera m’kugwiritsa ntchito mankhwala
osokoneza bongo, n’kumabera anthu kuti alipirire khalidwe lake loipalo. Anagwidwapo ndi apolisi kwa maulendo angapo. Komabe, ngakhale kuti anali ndi makhalidwe aukali ndi achiwawa, Gerson ankalakalaka mtendere wa mumtima. Kodi akanatha kuupeza?Amayi ake a Vania anamwalira iye akadali wamng’ono, ndipo Vania ndiye anakhala wosamalira panyumba, kuphatikizapo kusamalira mlongo wake wamng’ono yemwe amadwala. Vania ankapita kutchalitchi komabe ankadzimva kuti wasiyidwa ndi Mulungu. Iye analibiretu mtendere wa mumtima.
Ndiyeno panali Marcelo. Zimene Marcelo ankafuna zinali kumangosangalala basi. Ankakonda kuchita mapwando ndi achinyamata ena—kuvina, kumwa, ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Nthaŵi ina anachita ndewu ndi kupweteka mnyamata wina. Pambuyo pake, anagwidwa ndi chisoni chifukwa cha zimene anachitazo ndipo anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize. Nayenso ankafuna mtendere wa mumtima.
Zochitika zimenezi zikusonyeza ina mwa mikhalidwe yomwe ingasokoneze mtendere wa mumtima. Kodi panali njira ina yomwe mtsogoleri wa gulu la anthu a pantchito, mwamuna wandale, mwana wongoyendayenda m’misewu, mtsikana wopanikizika ndi ntchito, ndiponso mnyamata wokonda mapwando akanapezera mtendere wa mumtima womwe amaulakalaka? Kodi zimene zinawachitikira zikutiphunzitsa kanthu kalikonse? Yankho la mafunso onse aŵiriŵa ndi lakuti inde, monga momwe tionere m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Maina ena asinthidwa.
[Chithunzi patsamba 3]
Kodi mumalakalaka mtendere wa mumtima?