Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Lalikani Uthenga Wabwino Mwachangu

Lalikani Uthenga Wabwino Mwachangu

Lalikani Uthenga Wabwino Mwachangu

“Khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye.”​—AROMA 12:11.

1, 2. Ndi malingaliro otani omwe Akristu amayesetsa kukhala nawobe monga alaliki a uthenga wabwino?

MNYAMATA ali n’chimwemwe chodzala tsaya chifukwa chakuti wapeza ntchito yatsopano. Patsiku lake loyamba kupita kuntchitoko, akuyembekezera mwachidwi malangizo omwe womlemba ntchito adzam’patsa. Akufunitsitsa kuona momwe adzagwirira ntchito yake yoyambirira yeniyeni ndipo akugwiradi ndi mtima wonse. Akufunitsitsa kuchita bwino koposa monga momwe angathere.

2 Mofananamo, ifeyo monga Akristu tingadzione monga antchito ongoyamba kumene. Popeza kuti chiyembekezo chathu n’chodzakhala ndi moyo kosatha, tingatero kuti tangoyamba kumene kutumikira Yehova. Ndithudi Mlengi wathu akulingalira zotipatsa ntchito yochuluka yomwe idzatitanganitsa kunthaŵi zomka muyaya. Koma ntchito yoyambirira imene tinalandira ndiyo yakulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wake. (1 Atesalonika 2:4) Kodi ntchito imeneyi yochokera kwa Mulungu timaiona motani? Mofanana ndi mnyamatayo, n’kofunikatu kuigwira ndi mphamvu zathu zonse, mwachangu, mwachimwemwe​—inde, mofunitsitsa!

3. Kodi chofunika n’chiyani kuti tipambane monga mtumiki wa uthenga wabwino?

3 Ndithudi, kukhalabe ndi malingaliro abwino amenewo kungakhale kovuta. Kuwonjezera pa utumiki wathuwu, tilinso ndi maudindo ena ambirimbiri, ena mwa ameneŵa angatilemetse mwakuthupi ndi mwamalingaliro. Mokulira, timakwanitsa kusamalira zinthu zimenezi kwinaku tikutumikira mokwanira. Komabe vutolo lingakhale losatha. (Marko 8:34) Yesu anagogomeza kuti padzafunikira kuyesetsa mwakhama kuti tipambane monga Akristu.​—Luka 13:24.

4. Kodi nkhaŵa za tsiku ndi tsiku zingakhudze motani kaonedwe kathu kauzimu?

4 Popeza kuti tili n’zochita zambiri, nthaŵi zina n’chapafupi kulefulidwa kapena kulemetsedwa. “Zosamalira za moyo uno” zingatsamwitse changu chathu ndi kuyamikira kwathu ntchito za teokalase. (Luka 21:34, 35; Marko 4:18, 19) Chifukwa cha chibadwa chathu chopanda ungwirochi, tingataye ‘chikondi chathu choyamba.’ (Chivumbulutso 2:1-4) Mbali zina za utumiki wathu kwa Yehova zingangokhala chizoloŵezi wamba. Kodi Baibulo limapereka motani chilimbikitso chofunika kuti changu chathu muutumiki chipitirize kukhalebe chamoyo?

Monga “Moto Wotentha” M’mitima Yathu

5, 6. Kodi mtumwi Paulo anauona motani mwayi wake wa kulalikira?

5 Utumiki umene Yehova watipatsa n’ngwamtengo wapatali zedi, wosayenera kuonedwa ngati ntchito wamba. Mtumwi Paulo analingalira ntchito yolalikira uthenga wabwinoyo kukhala mwayi waukulu koposa, ndipo anadziona monga wosayenera kupatsidwa utumiki umenewu. Iye anati: “Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Kristu; ndi kuŵalitsira onse adziŵe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa Mulungu wolenga zonse.”​—Aefeso 3:8, 9.

6 Kaonedwe koyenera ka Paulo ka utumiki wake ndiko chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. M’kalata yake yopita kwa Aroma, iye anafotokoza kuti: “Momwe ndingakhoze ine, ndilikufuna kulalikira uthenga wabwino.” Analibe manyazi ndi uthenga wabwino. (Aroma 1:15, 16) Anali ndi malingaliro abwino ndipo anali wofunitsitsa kuchita utumiki wake.

7. M’kalata yomwe analembera Aroma, kodi Paulo anachenjeza za chiyani?

7 Mtumwi Paulo anaona kufunika kwa kukhalabe wachangu, chotero analangiza Akristu a ku Roma kuti: “Musakhale aulesi m’machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye.” (Aroma 12:11) Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “aulesi” limatanthauza “ozizira nkhongono, amphwayi.” Ngakhale kuti sitikuchita ulesi muutumiki wathu, tonsefe tiyenera kukhala tcheru pa kubuka kulikonse kwa zizindikiro za kugwa ulesi mwauzimu kotero kuti tisinthe kaonedwe kathu moyenerera ngati taonadi zizindikirozo mwa ife.​—Miyambo 22:3.

8. (a) N’chiyani chomwe chinali ngati “moto wotentha” mumtima wa Yeremiya, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi tikuphunziranji pa zomwe zinam’chitikira Yeremiya?

8 Mzimu wa Mulungu ungathenso kutithandiza pamene tafooketsedwa. Mwachitsanzo, pa nthaŵi inayake mneneri Yeremiya anali atafooka, ndipo analingalira zosiya ntchito yake yonenera. Iye ananenanso za Yehova kuti: “Sindidzam’tchula Iye, sindidzanenanso m’dzina lake.” Kodi umenewu unali umboni wakuti Yeremiya anali atafooka kotheratu mwauzimu? Ayi. Kwenikweni, uzimu wamphamvu wa Yeremiya, kukonda kwake Yehova, ndi changu chake pa choonadi zinam’patsa nyonga yopitirizabe kunenera. Iye anati: “M’mtima mwanga muli [mawu a Yehova] ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.” (Yeremiya 20:9) Si chachilendo kuti nthaŵi ndi nthaŵi atumiki okhulupirika a Mulungu akumane ndi zofooketsa. Koma pamene apempha thandizo kwa Yehova, iye adzapenda mitima yawo ndipo adzawapatsa mzimu woyera mwaufulu ngati nawonso, mofanana ndi Yeremiya, ali ndi mawu ake m’mitima yawo.​—Luka 11:9-13; Machitidwe 15:8.

“Musazime Mzimuyo”

9. N’chiyani chomwe chingajejemetse mzimu woyera kutigwirira ntchito?

9 Mtumwi Paulo analangiza Atesalonika kuti: “Musazime Mzimuyo.” (1 Atesalonika 5:19) Inde, zochita ndi malingaliro osemphana ndi mfundo zachikhalidwe chaumulungu zingajejemetse mzimu woyera kutigwirira ntchito. (Aefeso 4:30) Akristu lerolino ali ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino. Timalemekeza kwambiri mwayi umenewu. Sizitidabwitsa kuti osam’dziŵa Mulungu amanyoza kwambiri ntchito yathu yolalikirayi. Koma ngati Mkristu mwadala anyalanyaza utumiki wake, zotsatira zake zingakhale kuzima kwa moto wa mzimu wosonkhezera wa Mulungu.

10. (a) Kodi malingaliro a munthu mnzathu angatikhudze motani? (b) Ndi kaonedwe kapamwamba kotani ka utumiki wathu komwe kafotokozedwa pa 2 Akorinto 2:17?

10 Anthu ena kunja kwa mpingo wachikristu angaone ntchito yathu yolalikirayi monga kungogaŵa chabe mabuku. Ena angatione molakwa akumati timapita kunyumba ndi nyumba kuti tikangolandirako zopereka zaufulu basi. Ngati tingalole malingaliro olakwa ngati ameneŵa kukhudza mitima yathu, angabweze m’mbuyo kuchita kwathu bwino muutumiki. M’malo mwa kulola maganizo otereŵa kutikhudza, tiyeni nthaŵi zonse tiziona utumiki wathuwu monga momwe Yehova ndi Yesu amauonera. Mtumwi Paulo anatchula kaonedwe kapamwambako pamene amalengeza kuti: “Sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nawo mawu a Mulungu; koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.”​—2 Akorinto 2:17.

11. N’chiyani chinatheketsa Akristu oyambirira kukhalabe achangu ngakhale m’kati mwa chizunzo, ndipo chitsanzo chawocho chiyenera kutikhudza motani?

11 Posapita nthaŵi pambuyo pa imfa ya Yesu, ophunzira ake m’Yerusalemu anayang’anizana ndi nyengo ya chizunzo. Anaopsezedwa ndi kulamulidwa kuleka kulalikira. Ngakhale kuti zinali choncho, Baibulo limati “anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.” (Machitidwe 4:17, 21, 31) Mawu a Paulo kwa Timoteo zaka zingapo pambuyo pake akusonyeza malingaliro abwino kwambiri omwe Akristu ayenera kuwasunga. Pauloyo anati: “Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso. Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu.”​—2 Timoteo 1:7, 8.

Kodi Tili ndi Mangaŵa Otani kwa Mnansi Wathu?

12. Kodi chifukwa chachikulu chomwe timalalikirira uthenga wabwino n’chotani?

12 Kuti kaonedwe ka utumiki wathuwu kakhale koyenera, m’pofunika kuti tikhale ndi cholinga chabwino. N’chifukwa chiyani timalalikira? Chifukwa chachikulu n’choonekeratu m’mawu a wamasalmo akuti: “Okondedwa anu adzakulemekezani [Yehova]. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu; kudziŵitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake.” (Salmo 145:10-12) Inde, timalalikira kuti titamande Yehova poyera ndi kuyeretsa dzina lake kumtundu wonse wa anthu. Ngakhale kuti oŵerengeka chabe n’ngomwe amatimvetsera, kulengeza kwathu mokhulupirika uthenga wachipulumutso kumadzetsa chitamando kwa Yehova.

13. N’chiyani chomwe chimatisonkhezera kuuza ena za chiyembekezo chachipulumutso?

13 Komanso timalalikira chifukwa chakuti timakonda anthu ndi kuti tipeŵe liwongo la mwazi. (Ezekieli 33:8; Marko 6:34) Zimenezi n’zogwirizana zedi ndi mawu a Paulo pamene ankanena za anthu omwe anali kunja kwa mpingo wachikristu kuti: “Ine ndili wamangawa wa Ahelene ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa.” (Aroma 1:14) Paulo anadzimva kukhala wamangaŵa a kulengeza uthenga wabwino kwa anthu, popeza cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Lerolino, timakondanso mnansi wathu ndipo tili nayenso mangaŵa. Chikondi cha Yehova pa mtundu wa anthu chinam’sonkhezera kutumiza Mwana wake padziko lapansi kudzawafera. (Yohane 3:16) Imeneyotu inali nsembe yaikulu. Timatsanzira chikondi cha Yehova pamene timagwiritsa ntchito nthaŵi ndi khama lathu tikumauza ena uthenga wabwino wa chipulumutso kupyolera m’nsembe ya Yesu.

14. Kodi Baibulo limalongosola motani dziko la kunja kwa mpingo wachikristu?

14 Mboni za Yehova zimaona anthu anzawo monga omwe angakhoze kukhala abale awo achikristu. Tiyenera kulalikira molimba mtima, komano kulimba mtima kwathuko sikutanthauza kuti tizikangana ndi anthu. Zoonadi, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu amphamvu zedi ponena za dziko lonse lapansi. Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti “dziko,” pofuna kusonyeza kuipa kwa zinthu zina pamene anatchula za “nzeru ya dziko lino lapansi” ndi “zilakolako za dziko lapansi.” (1 Akorinto 3:19; Tito 2:12) Paulo anakumbutsanso Akristu a kwa Aefeso kuti pamene anali kuyenda “monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino,” anali “akufa” mwauzimu. (Aefeso 2:1-3) Mawu ameneŵa ndi enanso ofanana nawo n’ngogwirizana ndi mawu a mtumwi Yohane akuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”​—1 Yohane 5:19.

15. Ponena za anthu kunja kwa mpingo wachikristu, kodi sitichitanji, ndipo n’chifukwa chiyani sititero?

15 Komano, kumbukirani kuti mawu ngati ameneŵa amanena dziko lonse lotalikirana ndi Mulunguli, osati munthu payekha. Akristu sayesa n’komwe kuweruziratu momwe munthu aliyense adzailandirira ntchito yolalikirayi. Alibe maziko aliwonse om’nenera munthu aliyense kukhala mbuzi. Sikuli kwa ife kunena zotsatira zomwe zidzakhalapo pamene Yesu adzadza kudzalekanitsa “nkhosa” ndi “mbuzi.” (Mateyu 25:31-46) Yesu ndiye woweruza wosankhidwa; si ndife ayi. Komanso zochitika zasonyeza kuti ena omwe kale analoŵerera kotheratu m’mikhalidwe yoipitsitsa alandira uthenga wa m’Baibulo, asintha, ndipo tsopano ndi Akristu audongo. Choncho, ngakhale kuti sitingafune kuyanjana ndi anthu ena ake, sitizengereza kuwauza za chiyembekezo cha Ufumu ngati mwayi wochita zimenezi utapezeka. Malemba amanena za anthu ena omwe, ngakhale kuti n’ngosakhulupirira, “anaikidwiratu ku [‘n’ngofuna,’ NW] moyo wosatha.” Iwoŵa pambuyo pake amadzakhala okhulupirira. (Machitidwe 13:48) Choncho sitingadziŵe kuti wofunitsitsa ndi uti pokhapokha titachitira umboni​—mwinamwake kuposa kamodzi. Podziŵa zimenezi, timachitira onse omwe pakali pano sanalandire uthenga wa chipulumutso “mofatsa” ndi “mwaulemu wakuya,” tikumayembekezera kuti ena mwa ameneŵa adzalandira uthenga wamoyo m’tsogolomu.​—2 Timoteo 2:25; 1 Petro 3:15, NW.

16. Kodi n’chifukwa chimodzi chotani chomwe tiyenera kukulitsira “luso la kuphunzitsa”?

16 Kuphunzira maluso monga aphunzitsi kudzawonjezera changu chathu cha kulalikira uthenga wabwino. Mwachitsanzo: Maseŵero osangalatsa kwabasi angakhale osakondweretsa kwa munthu amene sadziŵa kuseŵera kwake. Koma katswiri wa maseŵero amenewo amasangalala nawo kwambiri. Mofananamo, Akristu amene amaphunzira “luso la kuphunzitsa” amawonjezera chimwemwe chawo muutumiki. (2 Timoteo 4:2; Tito 1:9, NW) Paulo analangiza Timoteo kuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (2 Timoteo 2:15) Kodi maluso athu a kuphunzitsa tingawakulitse motani?

17. Kodi ‘tingakulitse motani chilakolako’ cha chidziŵitso cha Baibulo, ndipo kodi chidziŵitsocho chidzapindulitsa motani utumiki wathu?

17 Njira imodzi ndiyo kuwonjezera chidziŵitso chathu cholondolacho. Mtumwi Petro akutilimbikitsa kuti: “Monga makanda obadwa chatsopano, kulitsani chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu, kuti kupyolera mwa iwo mukafikire chipulumutso.” (1 Petro 2:2, NW) Khanda lathanzi limakhala ndi chilakolako chachibadwa cha mkaka. Komatu Mkristu angafunikire ‘kukulitsa chilakolako’ cha chidziŵitso cha Baibulo. Zimenezi zingachitike mwa kukulitsa zizoloŵezi zabwino za kuphunzira ndi kuŵerenga. (Miyambo 2:1-6) Khama ndi kudziletsa n’zofunika kuti tikhaledi aphunzitsi aluso a Mawu a Mulungu, komatu khama lotereli limadzetsa mphoto. Chimwemwe chomwe chimadza pophunzira Mawu a Mulungu chidzatipatsa changu cha mzimu wa Mulungu, kufunitsitsa kugaŵana ndi ena zinthu zomwe timaphunzira.

18. Kodi misonkhano yachikristu ingatikonzekeretse motani kulunjika nawo bwino mawu a choonadi?

18 Misonkhano yachikristu nayonso imachita mbali yofunika kwambiri pa kugwiritsa kwathu ntchito Mawu a Mulungu mwaluso. Pamene malemba a m’Baibulo aŵerengedwa m’kati mwa nkhani zapoyera ndi pazokambirana zina zilizonse za m’Malemba, tingachite bwino kuŵerenga nawo limodzi m’Baibulo lathu. N’kwabwino kumvetsera mwatcheru mbali zonse za misonkhano, kuphatikizapo zomwe kwenikweni zimakhudza ntchito yathu yolalikira. Tisachepetse phindu la zitsanzo, mwinamwake kuyamba kuganizira zinthu zina. Kachiŵirinso, kudekha ndi kumvetsera mwatcheru n’zofunika. (1 Timoteo 4:16) Misonkhano yachikristu imalimbitsa chikhulupiriro chathu, imatithandiza kuphunzira kukhala ndi chilakolako cha Mawu a Mulungu, ndi kutiphunzitsa kukhala achangu polengeza uthenga wabwino.

Tingadalire Chichirikizo cha Yehova

19. N’chifukwa chiyani kutenga nawo mbali muutumiki nthaŵi zonse kuli kofunika?

19 Akristu omwe ndi “achangu mumzimu” omwenso ali akhama polengeza uthenga wabwino amayesetsa kuchita utumikiwu nthaŵi zonse. (Aefeso 5:15, 16) N’zoona kuti mikhalidwe imasiyana, ndipo si onse amene angathere nthaŵi yofanana m’ntchito imeneyi yopulumutsa moyo. (Agalatiya 6:4, 5) Komabe, chofunika kwambiri kuposa kuchuluka kwa nthaŵi yomwe tingathere muntchito yathu yolalikirayi ndicho kuchuluka kwa nthaŵi zimene timalankhula ndi anthu za chiyembekezo chathu. (2 Timoteo 4:1, 2) Pamene tilalikira kwambiri m’pamenenso timazindikira bwino zedi kufunika kwa ntchito imeneyi. (Aroma 10:14,15) Chifundo chathu ndi kulingalira anansi athu zidzawonjezeka pamene nthaŵi zonse tidzakhala tikukumana ndi anthu odzichepetsa omwe akuusa moyo ndi kulira ndiponso omwe alibe chiyembekezo.​—Ezekieli 9:4; Aroma 8:22.

20, 21. (a) Kodi m’tsogolo mwathumu mudakali ntchito yotani? (b) Kodi Yehova akuchirikiza motani kuyesayesa kwathu?

20 Yehova watipatsa uthenga wabwino. Imeneyitu ndi ntchito yoyamba yomwe timalandira kuchokera kwa iye monga “antchito anzake.” (1 Akorinto 3:6-9) Tikuchita changu kukwaniritsa udindo wopatsidwa ndi Mulunguwu ndi mtima wonse, monga momwe tingathere. (Marko 12:30; Aroma 12:1) Anthu ofuna kumvetsera alipobe ambiri m’dzikoli omwe ali ndi njala ya choonadi. Ntchito yoti tichite n’njambiri, koma tiyenera kudalira chichirikizo cha Yehova pamene tikukwaniritsa utumiki wathu kotheratu.​—2 Timoteo 4:5.

21 Yehova amatipatsa mzimu wake ndi kutikonzekeretsa ndi “lupanga la Mzimu,” Mawu a Mulungu. Ndi thandizo lake tingatsegule pakamwa pathu ‘molimbika kuti tizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino.’ (Aefeso 6:17-20) Zomwe mtumwi Paulo analembera Akristu a ku Tesalonika, zinenedwetu kwa ife. Iye anati: “Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu.” (1 Atesalonika 1:5) Inde, tiyenitu tilengeze uthenga wabwino mwachangu!

Kubwereramo Mwachidule

• Chifukwa cha nkhaŵa m’moyo, kodi chingachitike n’chiyani ku changu chathu muutumiki?

• Kodi kufunitsitsa kwathu kulengeza uthenga wabwino kuyenera kukhala ngati “moto wotentha” m’mitima yathu m’njira iti?

• Ndi malingaliro oipa ati okhudza utumiki wathu omwe tiyenera kuwapeŵa?

• Kodi anthu omwe sali okhulupirira anzathu tiyenera kuwaona motani nthaŵi zonse?

• Kodi Yehova amatithandiza motani kukhalabe achangu pa ntchito yathu yolalikira?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 9]

Akristu amatsanzira changu cha Yeremiya ndi Paulo

[Zithunzi patsamba 10]

Kukangalika kwathu muutumiki kumasonkhezeredwa ndi chikondi cha Mulungu ndi cha mnansi