Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wonyamula Kuunika ku Mayiko Ambiri

Wonyamula Kuunika ku Mayiko Ambiri

Mbiri ya Moyo Wake

Wonyamula Kuunika ku Mayiko Ambiri

NKHANI YA GEORGE YOUNG YOSIMBIDWA NDI RUTH YOUNG NICHOLSON

“N’chifukwa chiyani pali bata lonseli pamagome athu? . . . Kodi ndife anthu amtundu wanji ngati sitilankhula pamene tatsimikizira zinthu kukhala zoona ngati zimene ndalembazi? Tiyeni tisawabisire anthu, komatu tilalikire choonadi mosalakwitsa kapena mosabisa.”

MAWU ameneŵa anali m’kalata ya masamba 33 imene abambo anga analemba yopempha kuti dzina lawo lichotsedwe mu kaundula wa tchalitchi. Chinali chaka cha 1913. Kuyambira m’chaka chimenecho kupita m’tsogolo, anayamba zochita zina m’moyo zimene zinawatsogolera kutumikira ngati wonyamula kuunika ku mayiko ambiri. (Afilipi 2:15) Kuyambira nthaŵi imene ndinali kamtsikana kakang’ono, ndinasonkhanitsa nkhani zosimba zimene abambo anakumana nazo. Achibale ndi magwero onse osunga mbiri ndiponso mabwenzi anandithandiza kusonkhanitsa nkhani za moyo wawo. M’njira zambiri, moyo wa abambo umandikumbutsa za mtumwi Paulo. Mofanana ndi “mtumwi wa anthu amitundu” ameneyo, abambo nthaŵi zonse anali okonzekera kuyenda, kukalalikira uthenga wa Yehova kwa anthu ku mayiko onse ndi zisumbu. (Aroma 11:13; Salmo 107:1-3) Ndiloleni ndikuuzeni za abambo anga a George Young.

Zaka Zoyambirira

Abambo anga anali mwana wamng’ono wa a John ndi a Margaret Young, atchalitchi cha Presbyterian cha ku Scotland. Anabadwa pa September 8, 1886, banja lawo litasamuka ku Edinburgh ku Scotland kupita ku British Columbia kumadzulo kwa Canada. Akulu awo atatu​—Alexander, John ndi Malcolm anabadwira ku Scoltand zaka zoŵerengeka asanasamuke. Marion, mlongo wawo wamng’ono wa anyamatawa, amene anamsemera dzina lachikondi loti Nellie, anali wocheperapo ndi zaka ziŵiri kwa abambo.

Anawo anakulira pa famu ku Saanich, pafupi ndi mzinda wa Victoria, ku British Columbia kumene anakhala mosangalala. Panthaŵi imodzimodziyo, anaphunzira kukhala ndi udindo. Moti makolo awo akabwera kuchokera ku ulendo wa ku Victoria, ankapeza ntchito zapakhomo atagwira kale ndipo panyumba pamaoneka posamalika.

M’kupita kwa nthaŵi, abambo anga a George ndi abale awo atatuwo, Alexander, John ndi Malcolm, anayamba ntchito ya migodi ndi yogulitsa matabwa. Anyamataŵa anadziŵika kwambiri ndi kufufuza malo obzala mitengo yamatabwa komanso kugula ndi kugulitsa matabwa. Abambo anga ankayendetsa zachuma.

Pambuyo pake, maganizo a abambo okonda zinthu zauzimu anawapangitsa kusankha kukhala mtumiki wa Presbyterian. Komabe, nthaŵi yomweyo ulaliki umene unkatuluka m’nyuzipepala wa Charles Taze Russell, pulezidenti woyamba wa Zion’s Watch Tower Tract Society unakhudza kwambiri moyo wawo. Zimene abambo anaphunzira zinawasonkhezera kulemba ndi kutumiza kalata yopempha kuchotsedwa yotchulidwa poyambirirayo.

Mwachikondi komanso momveka bwino abambo anagwiritsa ntchito Baibulo kutsutsa chiphunzitso cha tchalitchicho chakuti mzimu wa munthu sukufa komanso kuti Mulungu adzatentha mizimu ya anthu m’moto wa helo kosatha. Komanso anavumbula chiphunzitso cha Utatu, kutsimikizira kuti sichinali chozikidwa pa maziko a Chikristu ndi kuti sichichirikizidwa ndi Malemba. Kuyambira nthaŵi imeneyo kupita m’tsogolo anayamba utumiki wachikristu motsanzira Yesu Kristu, modzichepetsa akumagwiritsa ntchito luso ndi mphamvu zawo kulemekeza Yehova.

M’chaka cha 1917, atauzidwa ndi Watch Tower Society, abambo anga anayamba kutumikira ngati mlaliki woyendayenda, ngati mmene oyang’anira oyendayenda a Mboni za Yehova amadziŵikira pa nthaŵiyo. Ankakamba nkhani ndi kuonetsa “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe” kuzungulira m’mizinda ndi m’matauni a ku Canada. Mabwalo amadzaza ndi anthu chifukwa cha kubwera kwa abambo. Ndandanda ya ulendo wa ulaliki wawo imasonyezedwa mu Nsanja ya Olonda mpaka chaka cha 1921.

Nyuzipepala ya ku Winnipeg inalengeza kuti, Mlaliki Young analankhula kwa anthu 2,500 komanso inati, anthu ambiri sanathe kuloŵa m’holo chifukwa munadzaza kwambiri. Ku Ottawa, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Ku Helo ndi Kubwererako.” Kumeneko mwamuna wina wokalamba anasimba kuti: “Utatha msonkhanowo, George Young anaitana atsogoleri achipembedzo ambiri kupulatifomu kuti akakambirane naye nkhaniyo, koma palibe amene anapita. Nthaŵiyo ndinadziŵa kuti ndapeza choonadi.”

Abambo anayesetsa kuchita zinthu zauzimu zambiri monga mmene akanathera pa maulendo awo a ulaliki. Akatha, amathamangira kukakwera sitima kupita ku msonkhano wina. Akamayenda pagalimoto, nthaŵi zonse amanyamuka mbanda kucha ulendo wa ku msonkhano wina asanadye kadzutsa. Kuwonjezera pa kukhala wokangalika, abambo ankasonyeza khalidwe loganizira ena ndiponso ankadziŵika chifukwa cha ntchito zawo zachikristu ndi kupatsa.

Pakati pa misonkhano yoyambirira imene abambo anapezekapo, umene umakumbukika mwapadera ndi umene unachitikira ku Edmonton, ku Alberta mu 1918. Banja lawo lonse linali komweko kukaonera ubatizo wa Nellie. Inalinso nthaŵi yomaliza imene anyamataŵa anakhalira pamodzi. Zaka ziŵiri pambuyo pake, Malcolm anamwalira ndi chibayo. Mofanana ndi abale ake atatu komanso abambo ake, Malcolm anali ndi chiyembekezo cha moyo wakumwamba, ndipo anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu mpaka imfa yake.​—Afilipi 3:14.

Ulendo wa Kumayiko Ena

Abambo atamaliza ulendo wa ulaliki wa ku Canada mu September 1921, anauzidwa ndi Joseph F. Rutherford, amene panthaŵiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society, kuti apitirire ku zisumbu za m’nyanja ya Caribbean. Kulikonse kumene abambo anasonyeza “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe” anthu ankasangalala nalo kwambiri. Ali ku Trinidad, analemba kuti: “Kunali anthu ambiri ndipo ena anachita kubwezedwa. Usiku wotsatira nyumbayo inadzazanso ndi anthu.”

Kenako, m’chaka cha 1923, abambo anatumizidwa ku Brazil. Kumeneko analankhula kwa anthu ambiri, nthaŵi zina akumagwiritsa ntchito omasulira aganyu. Nsanja ya Olonda yachingelezi ya December 15, 1923, inalengeza kuti: “Kuyambira pa June 1, mpaka pa September 30, Mbale Young wachititsa misonkhano yapoyera 21, onse ofikapo anali 3,600; misonkhano yapampingo 48, ofikapo 1,100; wagaŵira kwaulere mabuku okwana 5,000 achipwitikizi.” Ambiri anakhala ndi chidwi pamene abambo anakamba nkhani yakuti: “Mamiliyoni Okhala ndi Moyo Lero Sadzafa Konse.”

Pamene anapatulira nthambi yatsopano ku Brazil pa March 8, 1997, bulosha lopatulira linalengeza kuti: “1923: George Young anafika ku Brazil. Anakhazikitsa ofesi yanthambi pakati pa mzinda wa Rio de Janeiro.” Ngakhale kuti mabuku ophunzitsa Baibulo analipo m’Chisipanya, panafunikirabe kuti ena azipezeka m’Chipwitikizi, chinenero chofala ku Brazil. Ndiye pa October 1, 1923, Nsanja ya Olonda inayamba kusindikizidwa m’Chipwitikizi.

Abambo anakumana ndi anthu osaiŵalika ku Brazil. Mmodzi wa iwo anali Mpwitikizi wolemera wodziŵika ndi dzina loti Jacintho Pimentel Cabral, amene anapereka nyumba yake kuti azichitiramo misonkhano. Posapita nthaŵi Jacintho analandira choonadi cha m’Baibulo kenako anakhala wa banja la Beteli. Winanso anali Manuel da Silva Jordão, mlimi wachinyamata wachipwitikizi. Anamvetsera nkhani yapoyera yokambidwa ndi abambo imene inam’sonkhezera kubwerera ku Portugal kukatumikira ngati koputala, dzina lapanthaŵiyo la atumiki anthaŵi zonse a Mboni za Yehova.

Abambo anayenda kwambiri pasitima zapamtunda kuzungulira Brazil, ndipo anatha kupeza okondwerera. Pa umodzi wa maulendo awo, anakumana ndi Bony ndi Catarina Green, ndipo anakhala nawo kwa milungu iŵiri akuwafotokozera Malemba. Okwanira ngati asanu ndi aŵiri apabanjapo anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi.

Winanso amene anakumana naye anali Sarah Bellona Ferguson mu 1923. Mu 1867 ali mtsikana wamng’ono, iye pamodzi ndi mlongo wake Erasmus Fulton Smith pamodzi ndi banja lawo, anasamukira ku Brazil kuchoka ku United States of America. Chiyambire mu 1899 wakhala akulandira mokhazikika magazini a Nsanja ya Olonda papositi. Ulendo wa abambo unali mwayi umene Sarah, ana ake anayi ndi wachibale wina dzina lake Sallie, amene abambo ankamutcha kuti azakhali, anayembekezera kwa nthaŵi yaitali kuti abatizidwe. Panali pa March 11, 1924.

Pasanapite nthaŵi yaitali, abambo anakalalikira ku mayiko ena akumwera kwa America. Pa November 8, 1924, ali ku Peru analemba kuti: “Ndangomaliza kumene kugaŵira mathirakiti 17,000 ku Lima ndi ku Callao.” Kenako ananyamuka ulendo wa ku Bolivia kukagaŵira mathirakiti kumeneko. Pofotokoza za ulendo umenewo, analemba kuti: “Atate wathu akudalitsa zoyesayesa zathu. Mmwenye wina anandithandiza. Kwawo ndi kumene kunagwera mtsinje wa Amazon. Watenga mathirakiti 1,000 ndi mabuku ena.”

Kupyolera mu zoyesayesa za abambo choonadi cha Baibulo chinafala m’mayiko ambiri apakati ndi kumwera kwa America. Nsanja ya Olonda ya December 1, 1924, inalengeza kuti: “George Young tsopano wakhala ali kumwera kwa America kwa zaka ziŵiri. . . . Wakhala mwayi kwa mbale wokondedwa ameneyu kufikitsa uthenga wabwino wa choonadi ku Punta Arenas, ku Straits of Magellan.” Abambo anatsogoleranso ntchito yolalikira ku mayiko ngati Costa Rica, Panama ndi Venezuela. Ngakhale pamene amadwala malungo ndipo thanzi lawo silinali bwino, anapitirizabe kulalikira.

Kenako ku Ulaya

Mu March 1925, abambo ananyamuka ulendo wa ku Ulaya, kumene anayembekezera kugaŵira mathirakiti a Baibulo 300,000 ku Spain ndi ku Portugal komanso kukakonzekera kuti Mbale Rutherford akakambe nkhani. Komabe atafika ku Spain, abambo anafotokoza nkhaŵa yawo ndi kulimbikitsa kuti Mbale Rutherford asakakambe nkhani poona mzimu wachidani wa achipembedzo kumeneko.

Poyankha, Mbale Rutherford anagwira mawu a pa Yesaya 51:16 akuti: “Ndaika mawu anga m’kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, inu ndinu anthu anga.” Pakumva mawu amenewo, abambo anatsimikizira kuti: “Zoona, ndi cholinga cha Ambuye kuti ndilinganizebe msonkhanowo ndi kusiya zotsatira zake m’manja mwa ambuye.”

Pa May 10, 1925, Mbale Rutherford anakamba nkhani yake mothandizidwa ndi wotembenuza pa bwalo lamaseŵero la Novedades ku Barcelona. Osonkhana pamenepo anapitirira 2,000, kuphatikizapo mkulu waboma ndi msilikali wom’teteza. Njira yofananayo inachitika ku Madrid, komwe kunasonkhana anthu 1,200. Chidwi chimene chinadzutsidwa chifukwa cha nkhani zimenezi chinapangitsa kuti ofesi ya nthambi ikhazikitsidwe mu Spain, “yotsogoleredwa ndi George Young,” malinga n’kunena kwa Yearbook ya Mboni za Yehova ya 1978.

Pa May 13, 1925, Mbale Rutherford anakamba nkhani ku Lisbon ku Portugal. Ulendo wake kumeneko unalinso wopambana kwambiri, ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo anayesa kusokoneza pochititsa mapokoso ndi kuphwanya mipando. Motsatira nkhani zokambidwa ndi Mbale Rutherford ku Spain ndi ku Portugal, abambo anapitirizabe kuonetsa “Sewero la Pakanema,” ndiponso analinganiza kuti mabuku ophunzitsa Baibulo asindikizidwe ndi kufalitsidwa ku madera amenewo. Mu 1927 analengeza kuti uthenga wabwino “walengezedwa kuzungulira mizinda ndi matauni onse mu Spain.”

Kulalikira ku Soviet Union

Ulendo wotsatira wa ntchito ya abambo ya umishonale unali ku Soviet Union kumene anafikako pa August 28, 1928. Mbali ya kalata imene analemba pa October 10, 1928 imati:

“Chibwerereni kuno ku Russia, ndingapemphere moona mtima kuti: ‘Ufumu wanu udze’ ndi mtima wanga wonse. Ndikuphunzira chinenero koma ndi mwapang’onopang’ono. Wotanthauzira wanga ndi mwamuna wapadera, Myuda, koma amakhulupirira Kristu ndiponso amakonda Baibulo. Ndakumana ndi zina zosangalatsa koma sindikudziŵa kuti andilola kukhala mpaka liti. Mlungu wapitawu ndinalandira chidziŵitso kuti ndichoke m’maola 24 okha koma titakambirana anandilola kuti ndikhalebe kwa kanthaŵi.”

Tinayendera Ophunzira Baibulo ku Kharkov, umene tsopano ndi mzinda waukulu mu Ukraine. Misozi yachisangalalo inadzala m’maso mwa ophunzirawo chifukwa cha kucheza kwathu kwabwino. Usiku uliwonse tinali kuchita kamsonkhano kachigawo mpaka pakati pa usiku. Pofotokoza za kukumana kumeneku ndi abalewo, bambo analemba kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti abalewo alandidwa mabuku awo ochepa omwe anali nawo ndipo akuluakulu a boma alibenso chisoni komabe abalewo ndi osangalala.”

Utumiki wa abambo ku Soviet Union unafotokozedwa bwino mu bulosha limene linaperekedwa kwa omwe anapezeka pa kupatulira kwa nthambi yatsopano ku St. Petersburg ku Russia pa June 21, 1997. Buloshalo linafotokoza kuti abambo anatumizidwa ku Moscow, komanso linati, analandira chilolezo “kusindikiza makope 15,000 a timabuku takuti: Freedom for the Peoples ndi Where Are the Dead? kuti tigaŵiridwe ku Russia.”

Atabwererako ku Russia, abambo anatumizidwa kukakhala mlaliki woyendayenda ku United States. Ali kumwera kwa Dakota anakacheza kunyumba kwa Nellena ndi Verda Pool, alongo aŵiri akuthupi apachibale amene pambuyo pa zaka zina anakhala amishonale ku Peru. Anayamikira abambo chifukwa cha kuchita khama kwawo ndipo anati: “Abale m’masiku akale analidi ndi mzimu waupaniya ndipo ankapita ku utumuki wakunja ndi zochepa za dziko ili koma odzala ndi mtima wachikondi cha Yehova. N’zimene zinawasonkhezera kukwaniritsa zimene anachita.”

Ukwati Ndiyeno Ulendo Wachiŵiri

Kwa zaka zonsezi abambo ankalemberana makalata ndi Clara Hubbert wa ku chilumba cha Manitoulin ku Ontario. Onse analipo pa msonkhano wachigawo wa ku Columbus ku Ohio pa July 26, 1931, pamene Ophunzira Baibulo analandira dzina latsopano lakuti Mboni za Yehova. (Yesaya 43:10-12) Mlungu umodzi pambuyo pake anakwatirana. Posapita nthaŵi, abambo anachokanso, ulendo wachiŵiri wa umishonale kuzungulira zisumbu za m’nyanja ya Caribbean. Kumeneko anathandiza kupangitsa misonkhano komanso kuphunzitsa ena ntchito ya utumiki wa kunyumba ndi nyumba.

Amayi analandira zithunzi, makadi ndi makalata kuchokera ku Suriname, St. Kitts ndi malo ena osiyanasiyana. Makalatawo anasimba za kupita patsogolo kwa ntchito yolalikira ndipo nthaŵi zina ankafotokoza za mbalame, nyama ndi mbewu zopezeka ku mbali ya dziko imene anali. Mu June 1932, abambo anamaliza ntchito yawo pazilumba za Caribbean ndipo monga mwachizoloŵezi anakwera m’gawo la sitima yapamadzi la mtengo wotsika pobwerera ku Canada. Kenako anachitira limodzi ndi amayi ntchito yolalikira yanthaŵi zonse m’chilimwe chonse cha 1932 ndi 1933 ku Ottawa pamodzi ndi gulu lina lalikulu la atumiki anthaŵi zonse.

Moyo wa Banja Waufupi

Mlongo wanga David anabadwa mu 1934. Ali mwana amaimirira pabokosi limene amayi ankaikamo chisoti chawo n’kumayerekeza kukamba “nkhani.” Kwa moyo wake wonse, wasonyeza changu cha pa Yehova mofanana ndi abambo ake. Anthu atatu ameneŵa ankayenda pa galimoto atamangirira zokuzira mawu padenga la galimoto pamene amakayendera mipingo kuyambira kum’maŵa kwa gombe la Canada mpaka ku gombe la kumadzulo. Ndinabadwa mu 1938 pamene abambo ankatumikira ku British Columbia. David amakumbukira abambo akundiika pabedi ndipo iwo, amayi ndi David atagwada mozungulira bedilo, pamenepo abambo amapereka pemphero loyamikira chifukwa cha ine.

M’dzinja la 1939, tinakakhala ku Vancouver pamene abambo amachezetsa mipingo ya deralo. Pakati pa makalata onse amene tinasungira pa zaka zonsezi, imodzi ndi ya pa January 14, 1939, imene bambo analemba ali ku Vernom ku British Columbia. Kalatayi analembera amayi anga a Clara, David ndi Ruth akumati: “Ndingofuna kukupsopsonani pang’ono ndi kukukumbatirani.” Munalinso uthenga wa aliyense wa ife. Anatiuza kuti zotuta zinali zochuluka koma antchito anali ochepa.​—Mateyu 9:37, 38.

Mlungu wotsatira atangobwerera kuchoka ku ntchito yawo ku Vancouver, abambo anakomoka pa msonkhano. Atawapima zinasonyeza kuti anali ndi kansa yotupa mu ubongo. Pa May 1, 1939, anamaliza moyo wawo wapadziko lapansi. Ndinali ndi miyezi isanu ndi inayi ndipo David anali ndi zaka pafupifupi zisanu. Amayi athu okondedwa amene analinso ndi chiyembekezo chakumwamba, anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu mpaka imfa yawo pa June 19, 1963.

Mmene abambo anauonera mwayi wawo wotengera uthenga wabwino ku mayiko ambiri, kukusonyezedwa bwino m’kalata imodzi mwa makalata awo amene analembera amayi. Mbali ina ya kalatayi inati: “Chisomo cha Yehova chinandilola kuti ndipite ku mayiko ameneŵa ngati wonyamula kuunika kwa uthenga wa Ufumu. Dzina lake loyera lilemekezeke. Kudzera mu zophophonya ndi zolephera ndi zofooka, ulemerero wake uwale.”

Tsopano ana a George ndi Clara Young, zidzukulu, ndi zidzukulutudzi zikutumikira Mulungu wathu wachikondi Yehova. Ndinauzidwa kuti abambo nthaŵi zambiri ankagwira lemba la Ahebri 6:10 limene limati: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” Nafenso sitinaiwale ntchito ya abambo.

[Chithunzi patsamba 23]

Abambo anga kudzanja lamanja ndi abale awo atatu

[Zithunzi patsamba 25]

Abambo (aimirira) ndi Mbale Woodworth, Rutherford ndi Macmillan

M’munsi: Abambo (kumbuyo kumanzere) pagulu ndi Mbale Russell

[Zithunzi patsamba 26]

Abambo ndi amayi

M’munsi: Tsiku lawo la ukwati

[Chithunzi patsamba 27]

Ndili ndi David ndi amayi zaka zingapo bambo atamwalira