Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chiyembekezo cha Chiukiriro N’champhamvu

Chiyembekezo cha Chiukiriro N’champhamvu

Chiyembekezo cha Chiukiriro N’champhamvu

“Ndinatayikitsa zinthu zonse . . . kuti ndim’zindikire [Yesu Kristu], ndi mphamvu ya kuuka kwake.”​—AFILIPI 3:8-10.

1, 2. (a) Zaka za m’mbuyomu, kodi mtsogoleri wina wachipembedzo anachilongosola motani chiukiriro? (b) Kodi chiukiriro chidzachitika motani?

KUCHIYAMBI kwa ma 1890, manyuzipepala anasimba za ulaliki wachilendo woperekedwa ndi mtsogoleri wina wachipembedzo ku Brooklyn, mumzinda wa New York, ku U.S.A. Iye ananena kuti chiukiriro chidzakhala kusonkhanitsanso mafupa onse ndi mnofu wonse zomwe zinkapanga thupi la munthu, ndi kuzipatsanso moyo, kaya thupilo linanyeka m’moto kapena linanyenyeka pangozi, kaya linadyedwa ndi chilombo kapena linasanduka manyowa. Mlalikiyo ananena kuti patsiku lina la maola 24, mpweyawu udzada bi ndi manja, miyendo, mafupa, minofu, ndi khungu la miyandamiyanda ya anthu akufa. Ziŵalo zimenezi zidzakhala zikufufuza ziŵalo zinanso za thupi limodzimodzi. Kenako miyoyo idzatsika kuchokera kumwamba ndi kuhelo kudzaloŵa m’matupi oukitsidwa ameneŵa.

2 Kuukitsidwa mwa kugwirizanitsanso ziŵalo zathupi lakale n’kosamveka, komanso anthu alibe moyo womwe siufa. (Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4) Yehova, Mulungu wachiukiriro, safunikira kulumikizanso ziŵalo zomwe zinkapanga thupi la munthu munthuyo asanafe. Atha kupanga matupi enanso atsopano a anthu oukitsidwawo. Yehova wapatsa Mwana wake, Yesu Kristu, mphamvu youkitsa akufa omwe angadzathe kukhala ndi moyo wosatha. (Yohane 5:26) Chotero Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” (Yohane 11:25, 26) Lonjezo losangalatsa zedi! Limatilimbitsa kuti tipirire ziyeso ngakhalenso kuyang’anizana ndi imfa monga Mboni zokhulupirika za Yehova.

3. N’chifukwa chiyani Paulo anatchula mfundo zochirikiza chiukiriro?

3 Nkhani ya chiukiriro siigwirizana ndi chiphunzitso chakuti anthu ali ndi moyo womwe siufa​—malingaliro a wafilosofi wachigiriki Plato. Choncho, kodi panaoneka zotani pa Areopagi ku Atene pamene mtumwi Paulo anachitira umboni kwa Agiriki ophunzira, nanena nkhani yokhudza Yesu, kuti Mulungu anamuukitsa? Nkhaniyo imati: “Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete.” (Machitidwe 17:29-34) Ambiri amene anaona Yesu Kristu ataukitsidwa anali adakalipo ndipo, ngakhale kuti anali kunyozedwa, anachitira umboni wakuti iye anaukitsidwa kwa akufa. Koma aphunzitsi onyenga mumpingo wa Korinto anatsutsa za chiukiriro. Chotero Paulo anapereka mfundo zamphamvu mu chaputala 15 cha 1 Akorinto pochirikiza chiphunzitso chachikristu chimenechi. Kuziphunzira bwino mfundozo kukusonyeza mosakayikitsa m’pang’ono ponse kuti chiyembekezo cha chiukiriro n’chotsimikizirika ndiponso n’champhamvu.

Umboni Wotsimikizirika wa Kuukitsidwa kwa Yesu

4. Kodi Paulo anapereka umboni wotani woona ndi maso ponena za kuukitsidwa kwa Yesu?

4 Taonani mmene Paulo anayambira mfundo zake. (1 Akorinto 15:1-11) Pokhapokha ngati Akorinto anakhala okhulupirira popanda chifuno, anayenera kugwiritsitsa uthenga wabwino wa chipulumutso. Kristu anafera machimo athu, anaikidwa m’manda, ndipo anaukitsidwa. Kwenikweni, ataukitsidwa, Yesu anaonekera kwa Kefa (Petro), “pamenepo kwa khumi ndi aŵiriwo.” (Yohane 20:19-23) Anaonedwa ndi anthu ngati 500, mwinamwake pamene analamula kuti: ‘Mukani, mukaphunzitse anthu.’ (Mateyu 28:19, 20) Yakobo anamuona, monga momwe anachitira atumwi onse okhulupirika. (Machitidwe 1:6-11) Pafupi ndi Damasiko, Yesu anaonekera kwa Saulo “monga mtayo”​—ngati kuti anali ataukitsidwira kale ku moyo wauzimu. (Machitidwe 9:1-9) Akorinto anakhala okhulupirira chifukwa chakuti Paulo analalikira kwa iwo, ndipo analandira uthenga wabwino.

5. Kodi Paulo anaiona motani nkhaniyo monga momwe yalembedwera pa 1 Akorinto 15:12-19?

5 Taonani mmene Paulo anaionera nkhaniyo. (1 Akorinto 15:12-19) Popeza kuti anthu omwe anaonadi kuti Yesu waukitsidwa akulalikira kuti Kristu anaukitsidwa, ena anganene bwanji kuti kulibe chiukiriro? Ngati Yesu sanaukitsidwe kwa akufa, kulalikira kwathu ndi chikhulupiriro chathu n’zachabe, ndipo ndife anthu amabodza amene tikunamizira Mulungu ponena kuti anaukitsa Kristu. Ngati akufa sadzaukitsidwa, ‘tili chikhalire m’machimo athu,’ ndipo anthu amene anafa mwa Kristu anangotayika. Komanso, “ngati tiyembekezera Kristu m’moyo uno wokha, tili ife aumphaŵi oposa a anthu onse.”

6. (a) Kodi Paulo anati chiyani pochirikiza nkhani ya kuukitsidwa kwa Yesu? (b) Kodi “mdani wotsiriza” ndani, ndipo adzathetsedwa motani?

6 Paulo akuchirikiza nkhani ya kuukitsidwa kwa Yesu. (1 Akorinto 15:20-28) Popeza kuti Kristu ndiye “chipatso choundukula” cha amene akugona mu imfa, enanso adzaukitsidwa. Monga momwe imfa inayambira chifukwa cha kusamvera kwa munthuyo Adamu, chiukirironso chidzakhalapo kudzera mwa munthu winanso​—Yesu. Anthu ake anali kudzaukitsidwa panthaŵi ya kukhalapo kwake. Kristu ‘akutha chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe’ zotsutsana ndi ufumu wa Mulungu ndipo akulamulira monga Mfumu kufikira Yehova ataika adani ake onse pansi pa mapazi ake. Ngakhale “mdani wotsiriza”​—imfa yomwe tinailandira kuchokera kwa Adamu​—adzathetsedwa kudzera mwa nsembe ya Yesu. Kenako Yesu adzabwezera Ufumu kwa Mulungu ndi Atate wake, kudziika pansi pa “Iye amene anam’gonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.”

Kubatizidwa Chifukwa cha Akufa?

7. Kodi ndani amene “abatizidwa kuti akhale akufa,” ndipo kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa iwo?

7 Otsutsa za kuukitsidwa akufunsidwa kuti: “Adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa [“kuti akhale akufa?” NW]?” (1 Akorinto 15:29) Paulo sanali kunena kuti amoyo ayenera kubatizidwa m’malo mwa akufa, popeza kuti ophunzira a Yesu ayenera kuti iwowo aphunzire, kukhulupirira, ndiyeno kubatizidwa. (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 2:41) Akristu odzozedwa ‘amabatizidwa kuti akhale akufa’ mwa kuloŵa m’njira ya moyo yomwe imawatsogolera ku imfa ndi kuukitsidwa. Ubatizo woterewu umayamba pamene mzimu wa Mulungu uwapangitsa kukhala ndi chiyembekezo chopita kumwamba ndipo umatha pamene aukitsidwa kwa akufa kukhala ndi moyo wosakhoza kufa kumwamba.​—Aroma 6:3-5; 8:16, 17; 1 Akorinto 6:14.

8. Kodi Akristu angakhale otsimikizira za chiyani ngakhale Satana ndi atumiki ake atati awaphe?

8 Monga momwe mawu a Paulo akusonyezera, chiyembekezo cha chiukiriro chimatheketsa Akristu kuyang’anizana ndi ngozi ola lililonse ndi kuyang’anizana ndi imfa tsiku ndi tsiku chifukwa chochita ntchito yolalikira Ufumu. (1 Akorinto 15:30, 31) Akudziŵa kuti Yehova angawaukitse atalola Satana ndi atumiki ake kuwapha. Mulungu yekha ndiye angawononge moyo wawo m’Gehena, kutanthauza chiwonongeko chosatha.​—Luka 12:5.

Kufunika Kokhala Tcheru

9. Ngati tikufuna kuti chiyembekezo cha chiukiriro chikhale cholimbikitsa m’moyo wathu, kodi tiyenera kupeŵa chiyani?

9 Chiyembekezo cha chiukiriro chinam’limbikitsa Paulo. Pamene anali ku Efeso, adani ake ayenera kuti anam’ponya m’bwalo kuti amenyane ndi zilombo. (1 Akorinto 15:32) Ngati zimenezo zinachitika, iye analanditsidwa, monga momwenso Danieli analanditsidwira ku mikango. (Danieli 6:16-22; Ahebri 11:32, 33) Popeza kuti anali kuyembekezera chiukiriro, Paulo sanali kulingalira monga anthu a mpatuko a m’dziko la Yuda m’tsiku la Yesaya. Iwo ankanena kuti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa maŵa tidzafa.” (Yesaya 22:13) Ngati tikufuna kuti chiyembekezo cha chiukiriro chikhale cholimbikitsa m’moyo wathu monga momwe chinalili kwa Paulo, tiyenera kupeŵa anthu amene ali ndi mzimu woipa umenewo. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Zoonadi, mfundo yachikhalidwe imeneyi imagwira ntchito pa mbali zosiyanasiyana za moyo.

10. Kodi n’chiyani chidzatikumbutsa za chiyembekezo cha chiukiriro nthaŵi zonse?

10 Kwa okayika za chiukiriro, Paulo anati: “Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziŵitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.” (1 Akorinto 15:34) Mu “nthaŵi [ino] ya chimaliziro,” tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Kristu. (Danieli 12:4; Yohane 17:3) Zimenezi zidzatikumbutsa za chiyembekezo cha chiukiriro nthaŵi zonse.

Kuukitsidwa ndi Thupi Lotani?

11. Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani polongosola kuukitsidwa kwa Akristu odzozedwa?

11 Kenako Paulo anayankha mafunso ena ndi ena. (1 Akorinto 15:35-41) Mwinamwake pofuna kusonyeza kuti nkhani ya chiukiriro ndi yokayikitsa, wofufuza angafunse kuti: “Akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani?” Monga momwe Paulo anasonyezera, mbewu yodzalidwa m’nthaka imafa ikamasinthika kukhala mmera. Momwemonso, munthu wobadwa mwa mzimu ayenera kufa. Monga momwe chomera chimatulukira m’mbewu chili ndi thupi latsopano, momwemonso thupi la Mkristu wodzozedwa woukitsidwa limakhala losiyana ndi thupi laumunthu. Ngakhale kuti moyo wake umakhala wofanana ndi womwe anali nawo asanamwalire, amaukitsidwa monga cholengedwa chatsopano chokhala ndi thupi lauzimu loti lingakhale kumwamba. Motero, awo amene adzaukitsidwira padziko lapansi adzaukitsidwa ndi matupi aumunthu.

12. Kodi mawu akuti “matupi am’mwamba” ndi “matupi apadziko” amatanthauzanji?

12 Monga mmene ananenera Paulo, nyama ya munthu ndi yosiyana ndi nyama ya zinyama. Zinyamanso zimasiyanasiyana nyama yake. (Genesis 1:20-25) “Matupi am’mwamba” a zolengedwa zauzimu amasiyana ulemerero wake ndi “matupi apadziko” okhala ndi nyama. Dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi zimasiyananso ulemerero wake. Koma oukitsidwa odzozedwa ali ndi ulemerero waukulu kopambana.

13. Malinga ndi kunena kwa 1 Akorinto 15:42-44, kodi n’chiyani chimafesedwa ndipo n’chiyaninso chimaukitsidwa?

13 Atatchula kusiyana kumeneko, Paulo anawonjezera kuti: “Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa.” (1 Akorinto 15:42-44) Iye anati: “Lifesedwa m’chivundi, liukitsidwa m’chisavundi.” Panopo Paulo ayenera kuti ankanena za odzozedwa monga gulu limodzi. Litafesedwa m’chivundi pa imfa, limaukitsidwa m’chisavundi, lopanda uchimo. Ngakhale kuti thupilo linyozedwa ndi dziko, liukitsidwira ku moyo wakumwamba ndi kuonekera pamodzi ndi Kristu mu ulemerero. (Machitidwe 5:41; Akolose 3:4) Pa imfa lifesedwa “thupi lachibadwidwe” ndipo liukitsidwa “thupi lauzimu.” Popeza kuti zimenezi n’zotheka kwa Akristu obadwa m’mzimu, tingakhale otsimikizira kuti enanso angaukitsidwe kukhala ndi moyo padziko lapansi.

14. Kodi Paulo anawasiyanitsa motani Kristu ndi Adamu?

14 Kenako Paulo anasiyanitsa Kristu ndi Adamu. (1 Akorinto 15:45-49) Adamu, munthu woyambirira, “[a]nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7) “Adamu wotsirizayo”​—Yesu​—“anakhala mzimu wakulenga moyo.” Anapereka moyo wake monga nsembe ya dipo, choyamba m’malo mwa otsatira ake odzozedwa. (Marko 10:45) Monga anthu, iwo ali ‘m’chifanizo cha wanthakayo,’ koma akaukitsidwa adzakhala monga Adamu wotsiriza. Komansotu paja nsembe ya Yesu idzapindulitsa anthu onse omvera, kuphatikizapo amene adzaukitsidwira padziko lapansi.​—1 Yohane 2:1, 2.

15. N’chifukwa chiyani Akristu odzozedwa saukitsidwa ndi thupi lanyama, ndipo akuukitsidwa motani panthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu?

15 Akristu odzozedwa akamwalira, saukitsidwa ndi thupi lanyama. (1 Akorinto 15:50-53) Thupi lotha kuvunda lanyama ndi mwazi silingathe kuloŵa chisavundi ndi Ufumu wa kumwamba. Odzozedwa ena sadzagona mu imfa kwa nthaŵi yaitali. Akamaliza njira yawo yapadziko lapansi mokhulupirika m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Yesu, iwo ‘adzasandulika, m’kamphindi, m’kutwanima kwa diso.’ Adzaukitsidwa nthaŵi yomweyo kukhala ndi moyo wauzimu wosavunda komanso waulemerero. M’kupita kwa nthaŵi, “mkwatibwi” wakumwamba wa Kristu adzakwanira 144,000.​—Chivumbulutso 14:1; 19:7-9; 21:9; 1 Atesalonika 4:15-17.

Kugonjetsa Imfa!

16. Malinga ndi Paulo ndi aneneri ena oyambirirapo, kodi n’chiyani chidzachitikira imfa yomwe tinailandira kuchokera kwa Adamu wochimwayo?

16 Paulo analengeza mosangalala kwambiri kuti imfa idzamezedwa kunthaŵi zonse. (1 Akorinto 15:54-57) Pamene chovunda ndi chotha kufa chidzavala chosavunda ndi chosafa, mawu awa adzakwaniritsidwa: “Imfayo yamezedwa m’chigonjetso.” “Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti?” (Yesaya 25:8; Hoseya 13:14) Mbola ya imfa ndiyo uchimo, ndipo mphamvu ya uchimo inali Chilamulo, chimene chinalamula kuphedwa kwa olakwa. Koma chifukwa cha nsembe ya Yesu ndi kuukitsidwa kwake, imfa yomwe tinalandira kuchokera kwa Adamu wochimwayo siidzagonjetsanso aliyense.​—Aroma 5:12; 6:23.

17. Kodi mawu a pa 1 Akorinto 15:58 akugwira ntchito motani lerolino?

17 “Chifukwa chake, abale anga okondedwa,” anatero Paulo, “khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Mawu amenewo akugwira ntchito kwa otsalira odzozedwa amakono ndi kwa “nkhosa zina” za Yesu ngakhale atamwalira m’masiku ano. (Yohane 10:16) Kugwiritsa kwawo ntchito monga olengeza Ufumu sikuli chabe, popeza kuti patsogolo pawo pali chiukiriro. Monga atumiki a Yehova, tiyenitu tikhale otanganitsidwa m’ntchito ya Ambuye pamene tikudikira tsiku pamene mwachimwemwe tidzafuula kuti: “Imfawe, chigonjetso chako chili kuti?”

Chiyembekezo cha Chiukiriro Chikwaniritsidwa!

18. Kodi chiyembekezo cha chiukiriro chinali champhamvu motani mwa Paulo?

18 Mawu a Paulo olembedwa mu 1 Akorinto chaputala 15 akusonyezeratu kuti chiyembekezo cha chiukiriro chinali champhamvu m’moyo wake. Anali wotsimikizira kotheratu kuti Yesu anaukitsidwa kwa akufa ndi kuti enanso adzamasulidwa kuchoka m’manda a munthu. Kodi inuyo muli ndi chikhulupiriro champhamvu ngati chimenecho? Paulo anaona mapindu adyera kukhala “zapadzala” ndipo ‘anataya zinthu zonse’ kuti ‘azindikire Kristu, ndi mphamvu ya kuuka kwake.’ Mtumwiyo anali wokonzeka kufa imfa yofanana ndi ya Kristu pokhala ndi chiyembekezo cholandira “kuuka [koyambirira, NW] kwa akufa.” “Kuuka kwa akufa koyamba” kumeneku kumachitika kwa otsatira odzozedwa a Yesu okwanira 144,000. Inde, amaukitsidwira ku moyo wauzimu wakumwamba, pamene “otsala a akufa” adzaukitsidwira padziko lapansi.​—Afilipi 3:8-11; Chivumbulutso 7:4; 20:5, 6.

19, 20. (a) Kodi ndi anthu ati otchulidwa m’Baibulo omwe adzaukitsidwa padziko lapansi? (b) Kodi mukuyembekezera chiukiriro cha ndani?

19 Chiyembekezo cha chiukiriro chakhala chochitika chaulemerero kwa odzozedwa amene akhala okhulupirika mpaka imfa. (Aroma 8:18; 1 Atesalonika 4:15-18; Chivumbulutso 2:10) Opulumuka “chisautso chachikulu” adzaona chiyembekezo cha chiukiriro chikukwaniritsidwa padziko lapansi pamene ‘nyanja idzapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade idzapereka akufawo anali mmenemo.’ (Chivumbulutso 7:9, 13, 14; 20:13) Pakati pa anthu amene adzaukitsidwa kukhala ndi moyo padziko lapansi padzakhalanso Yobu, amene anatayikidwa ana aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana aakazi atatu. Talingalirani chisangalalo chake powalandiranso​—ndiponso iwo adzasangalala kwadzaoneni poona kuti ali ndi abale awo enanso asanu ndi aŵiri ndi alongonso ena atatu okongola!​—Yobu 1:1, 2, 18, 19; 42:12-15.

20 Lidzakhalatu dalitso losangalatsa pamene Abrahamu ndi Sara, Isake ndi Rabeka​—inde ndi enanso ambirimbiri, kuphatikizapo “aneneri onse”​—adzaukitsidwa kukhala padziko lapansi! (Luka 13:28) Mmodzi wa aneneri amenewo anali Danieli, amene analonjezedwa kuti adzaukitsidwa mu ulamuliro wa Mesiya. Danieli wakhala ali m’manda kwa zaka ngati 2,500, koma mwa mphamvu ya chiukiriro, posachedwapa ‘adzaima m’gawo lake’ monga mmodzi wa “mafumu [“akalonga,” NW] m’dziko lonse lapansi.” (Danieli 12:13; Salmo 45:16) Zidzakhalatu zosangalatsa zedi kulandiranso osati chabe anthu okhulupirika akale komanso atate anu, amayi anu, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapena enanso okondedwa omwe mdaniyo imfa anakulandani!

21. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuzengereza kuchitira ena zabwino?

21 Mabwenzi athu ndi okondedwa athu ena angakhale atatumikira Mulungu kwa zaka zambiri ndipo mwina angakhale achikulire. Uchikulirewo ungawalepheretse kulimbana ndi zovuta za m’moyo. Ndi chikonditu chachikulu kuwathandiza monga momwe tingathere panopo! Ndiyeno sitidzachita chisoni m’tsogolo kuti tinalephera kuwathandiza m’njira zina ngati imfa ingawapeze. (Mlaliki 9:11; 12:1-7; 1 Timoteo 5:3, 8) Tingakhale otsimikizira kuti Yehova sadzaiŵala zinthu zabwino zimene tichitira ena, kaya akhale a msinkhu wotani kapena akhale m’mikhalidwe yotani. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.”​—Agalatiya 6:10; Ahebri 6:10.

22. Kufikira chiyembekezo cha chiukiriro chitakwaniritsidwa, kodi tiyenera kukhala otsimikizira kuchitanji?

22 Yehova ndi “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Mawu ake amatitonthoza ndipo amatithandiza potonthoza ena ndi chiyembekezo champhamvu cha chiukiriro. Kufikira pamene tidzaona kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chimenecho mwa kuukitsidwa kwa akufa kukhala padziko lapansi, tiyeni tikhale monga Paulo, amene anali ndi chikhulupiriro m’chiukiriro. Makamaka, tiyeni titsanzire Yesu, amene chiyembekezo chake m’mphamvu ya Mulungu yomuukitsa chinakwaniritsidwa. Posachedwapa, awo amene ali m’manda achikumbukiro adzamva mawu a Kristu ndipo adzatulukira. Zimenezi zititonthoze ndi kutipatsa chimwemwe. Koma kwenikweni, tiyeni tikhale othokoza kwa Yehova, amene wapangitsa kuti imfa igonjetsedwe kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Kristu!

Yankho Lanu N’lotani?

• Kodi Paulo anapereka umboni woona ndi maso wotani ponena za kuukitsidwa kwa Yesu?

• Kodi “mdani wotsiriza” ndiye ndani, ndipo kodi adzathetsedwa motani?

• Kwa Akristu odzozedwa, kodi n’chiyani chimafesedwa ndipo n’chiyani chimaukitsidwa?

• Ndi anthu otchulidwa m’Baibulo ati amene mukufuna kudzaonana nawo akadzaukitsidwa padziko lapansi?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Mtumwi Paulo anapereka mfundo zamphamvu zochirikiza chiukiriro

[Zithunzi patsamba 20]

Kuukitsidwa kwa Yobu, banja lake, ndi enanso ambiri kudzadzetsa chisangalalo chosaneneka!