Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chiyembekezo cha Chiukiriro N’chotsimikizirika!

Chiyembekezo cha Chiukiriro N’chotsimikizirika!

Chiyembekezo cha Chiukiriro N’chotsimikizirika!

“[Ndili] nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka.”​—MACHITIDWE 24:15.

1. N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chiyembekezo cha chiukiriro?

YEHOVA watipatsa zifukwa zomveka zokhalira ndi chiyembekezo cha chiukiriro. Mawu ake amatiuza kuti akufa adzauka, kuimiriranso kukhala ndi moyo. Ndiponso m’posakayikitsa kuti chifuno chake ponena za amene ali chigonere mu imfa chidzakwaniritsidwa. (Yesaya 55:11; Luka 18:27) Komanso, Mulungu wasonyeza kale mphamvu yake youkitsa akufa.

2. Kodi chiyembekezo cha chiukiriro chingatipindulitse motani?

2 Kukhala ndi chikhulupiriro m’makonzedwe a Mulungu oukitsa akufa kudzera mwa Mwana wake Yesu Kristu, kungatichirikize panthaŵi ya nsautso. Kutsimikizirika kwa chiyembekezo cha chiukiriro kungatithandizenso kukhalabe okhulupirika kwa Atate wathu wakumwamba ngakhale ngati zimenezo zingatifikitse ku imfa. Chiyembekezo chathu cha chiukiriro chiyenera kuti chidzalimbitsidwa pamene tikambirana nkhani zolembedwa m’Baibulo zokhudza anthu amene anaukitsidwa. Zozizwitsa zonsezi zinakwaniritsidwa mwa mphamvu yochokera kwa Ambuye Mfumu Yehova.

Analandira Akufa Awo mwa Chiukiriro

3. Kodi Eliya anapatsidwa mphamvu yochita chiyani pamene mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye ku Zarefati anamwalira?

3 M’nkhani yake yochititsa chidwi yolongosola za chikhulupiriro chomwe mboni za Yehova za m’nthaŵi yakale Chikristu chisanayambe zinasonyeza, mtumwi Paulo analemba kuti: “Akazi analandira akufa awo mwa kuuka kwa akufa.” (Ahebri 11:35; 12:1) Mmodzi wa akazi amenewo anali mkazi wamasiye waumphaŵi m’mudzi wa Zarefati ku Foinike. Chifukwa chakuti anachereza mneneri wa Mulungu Eliya, ufa wake ndi mafuta ake ophikira anawonjezeka mozizwitsa panthaŵi ya chilala pamene iyeyo ndi mwana wake wamwamuna akanafa ndi njala. Mwanayo atamwalira pambuyo pake, Eliya anam’goneka pakama, ndipo anapemphera, kum’fungatira mwanayo katatu, ndi kuchonderera kuti: “Yehova Mulungu wanga, ndikupemphani, ubwere moyo wake wa mwanayu m’chifuŵa mwake.” Mulungu anapangitsadi kuti moyo ubwerere m’thupi la mwanayo. (1 Mafumu 17:8-24) Talingalirani chimwemwe cha mkazi wamasiyeyo pamene chikhulupiriro chake chinafupidwa mwa chiukiriro choyambirira kulembedwa​—cha mwana wake wamwamuna weniweniyo wokondedwa!

4. Kodi ndi chozizwitsa chotani chimene Elisa anachita ku Sunemu?

4 Mkazi winanso amene analandira wakufa wake mwa chiukiriro ankakhala m’mudzi wa Sunemu. Iye anali mkazi wa mwamuna wachikulire, ndipo anasonyeza kukoma mtima kwa mneneri Elisa ndi mnyamata wake. Mkaziyo anafupidwa ndi mwana wamwamuna. Komabe, patapita zaka zambiri ndithu, iye anaitana mneneriyo, amene anapeza kuti mwana wake uja wamwalira m’nyumba ya mkaziyu. Elisa atapemphera ndi kuchitanso zinthu zina, “mnofu wa mwana unafunda.” Mwanayo “anayetsemula kasanu ndi kaŵiri, natsegula mwanayo maso ake.” Kuukitsidwa kumeneku mosakayikira kunapatsa amayiwo ndi mwana wawo chimwemwe chachikulu. (2 Mafumu 4:8-37; 8:1-6) Koma adzasangalala kwadzaoneni pamene iwo adzaukitsidwa kukhala amoyo padziko lapansi pa “kuuka koposa”​—kumene kudzawapatsa mpata wokhala ndi moyo popanda kuyembekezeranso kufa! N’chifukwatu chachikulu zedi chom’thokozera Mulungu wachikondi wachiukiriro, Yehova!​—Ahebri 11:35, 36.

5. Kodi Elisa anakhudzidwa motani ndi chozizwitsa china ngakhale atamwalira?

5 Ngakhale pambuyo poti Elisa wamwalira ndi kuikidwa m’manda, Mulungu anapangitsa mafupa ake kukhala amphamvu mwa mzimu woyera. Timaŵerenga kuti: “Pakuika maliro a munthu wina, [Aisrayeli ena] anaona gulu lankhondo [la Amoabu], naponya mtembo m’manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili.” (2 Mafumu 13:20, 21) Mwamunayo ayenera kuti anadabwa ndi kukondwera kwabasi! Talingalirani za chimwemwe chimene tidzakhala nacho pamene okondedwa athu adzaukitsidwa kukhalanso ndi moyo mogwirizana ndi chifuno chotsimikizirika cha Yehova Mulungu!

Mwana wa Mulungu Anaukitsa Akufa

6. Kodi Yesu anachita chozizwitsa chotani pafupi ndi mudzi wa Nayini, ndipo kodi chochitika chimenechi chingatikhudze motani?

6 Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, watipatsa zifukwa zomveka zokhulupirira kuti akufa angaukitsidwe, ndi kuyembekeza kukhala ndi moyo wosatha. Zimene zinachitika pafupi ndi mudzi wa Nayini zingatithandize kuzindikira kuti chozizwitsa ngati chimenecho n’chotheka mwa mphamvu ya Mulungu. Panthaŵi ina, Yesu anakumana ndi olira atanyamula mtembo wa mnyamata wina akutuluka m’mudzi kupita kumanda. Iye anali mwana yekhayo wa mkazi wina wamasiye. Yesu anauza mkaziyo kuti: “Usalire.” Kenako anakhudza chithatha nanena: “Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.” Pamenepo, mnyamatayo anakhala tsonga nayamba kuyankhula. (Luka 7:11-15) Chozizwitsa chimenechi chikulimbitsadi kutsimikiza mtima kwathu kuti chiyembekezo cha chiukiriro n’chotsimikizirika.

7. Kodi n’chiyani chinachitika chokhudza mwana wamkazi wa Yairo?

7 Lingaliraninso chochitika china chokhudza Yairo, mkulu wa sunagoge ku Kapernao. Iye anapempha Yesu kuti abwere kudzathandiza mwana wake wokondedwa wamkazi wazaka 12 zakubadwa, amene anali pafupi kufa. Posapita nthaŵi uthenga unafika wakuti mwanayo wamwalira. Polimbikitsa Yairo wogwidwa ndi chisoniyo kuti asonyeze chikhulupiriro, Yesu anatsagana naye kunyumba kwake, kumene khamu la anthu linali kulira maliro. Iwo anaseka Yesu atawauza kuti: “Mwana sanafa, koma ali m’tulo.” N’zoonadi kuti anali atamwalira, koma Yesu anali pafupi kusonyeza kuti anthu angaukitsidwe kukhalanso ndi moyo monga momwe angadzutsidwire atagona tulo tatikulu. Atagwira mtsikanayo padzanja, Yesu anati: “Buthu, tauka.” Nthaŵi yomweyo anadzuka, ndipo “atate wake ndi amake anadabwa” ndi kudabwa kwakukulu. (Marko 5:35-43; Luka 8:49-56) Mosakayikira, anthu m’mabanja ‘adzadabwa’ kwadzaoneni pamene okondedwa awo akufa adzaukitsidwira kumoyo m’dziko lapansi la paradaiso.

8. Kodi Yesu anachitanji kumanda a Lazaro?

8 Lazaro anali atamwalira kwa masiku anayi pamene Yesu anapita kumanda kwake ndipo mwala wa pakhomo pake unachotsedwa. Atapemphera poyera kuti oonerera onse adziŵe kuti akudalira mphamvu ya Mulungu, Yesu anafuula kuti: “Lazaro, tuluka.” Ndipo anatulukadi! Manja ake ndi miyendo yake zinali zokulungidwabe m’nsalu ya kumanda, ndipo nkhope yake inali yophimbidwa ndi nsalu. “M’masuleni iye, ndipo m’lekeni amuke,” anatero Yesu. Ataona chozizwitsa chimenechi, ambiri amene anabwera kudzatonthoza alongo a Lazaro, Mariya ndi Marita, anakhulupirira Yesu. (Yohane 11:1-45) Kodi nkhani imeneyi sikukupangitsani kukhala ndi chiyembekezo chachikulu chakuti okondedwa anu angadzauke kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu?

9. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikizira kuti Yesu angaukitse akufa tsopano lino?

9 Pamene Yohane Mbatizi anali m’ndende, Yesu anam’tumizira uthenga wolimbikitsawu: “Akhungu alandira kuona kwawo, . . . ndi akufa aukitsidwa.” (Mateyu 11:4-6) Popeza kuti Yesu pamene anali padziko lapansi anaukitsa akufa, iye atha kuchita zomwezo monga cholengedwa chauzimu champhamvu yopatsidwa ndi Mulungu. Yesu ndiye “kuuka ndi moyo,” ndipo n’kotonthozatu kwabasi kudziŵa kuti posachedwapa m’tsogolo “onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira”!​—Yohane 5:28, 29; 11:25.

Kuukitsidwa kwa Anthu Enanso Kulimbitsa Chiyembekezo Chathu

10. Kodi kuukitsa munthu kochitidwa ndi mtumwi koyamba kusimbidwa mungakulongosole motani?

10 Pamene Yesu anatumiza atumwi ake monga alaliki a Ufumu, iye anati: “Ukitsani akufa.” (Mateyu 10:5-8) Komano kuti achite zimenezi anayenera kudalira mphamvu ya Mulungu. M’mudzi wa Yopa m’chaka cha 36 C.E., Dorika (Tabita), mkazi woopa Mulungu, anamwalira. Ntchito zake zabwino zinaphatikizapo kupangira akazi amasiye aumphaŵi zovala, ndipo akaziwo analira kwambiri iye atamwalira. Ophunzira anam’konza kuti akamuike ndipo anatumiza uthenga woitana mtumwi Petro, mwina kuti adzawatonthoze. (Machitidwe 9:32-38) Atauza aliyense yemwe anali m’chipinda chapamwamba kuti atuluke, Petro anapemphera, nanena: “Tabita, uka.” Tabita anatsegula maso ake, kukhala tsonga, n’kugwira dzanja la Petro, ndipo Petro anam’dzutsa. Kuukitsa munthu kochitidwa ndi mtumwi koyamba kusimbidwa kumeneku kunapangitsa ambiri kukhala okhulupirira. (Machitidwe 9:39-42) Kukutipatsanso chifukwa chinanso choyembekezera chiukiriro.

11. Kodi chiukiriro chomalizira cholembedwa m’Baibulo ndicho chiti?

11 Chiukiriro chomalizira cholembedwa m’Baibulo chinachitikira ku Trowa. Paulo ataima kumeneko paulendo wake wachitatu waumishonale, anapitirizabe kuyankhula mpaka pakati pa usiku. Atatopa komanso mwina chifukwa cha kutentha kwa nyale zambiri ndi kuthinana kwa anthu m’chipinda momwe anasonkhanamo, mnyamata wina wotchedwa Utiko anagwidwa ndi tulo tatikulu ndipo anagwa kuchokera pazenera lachipinda chosanja chachiŵiri. “Anam’tola wakufa,” osati kungokomoka. Paulo anadziponya pa Utiko, ndipo anam’fungatira, nauza oonerera kuti: “Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo.” Paulo anatanthauza kuti moyo wa mnyamatayo wabwezeretsedwa. Awo amene analipo “[a]natonthozedwa kwakukulu.” (Machitidwe 20:7-12) Lerolino, atumiki a Mulungu amatothozedwa kwakukulu podziŵa kuti anzawo akale potumikira Mulungu adzaona kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo cha chiukiriro.

Chiukiriro Ndicho Chiyembekezo Chomwe Chakhalapo Kuyambira Kalekale

12. Kodi Paulo analongosola za chikhulupiriro chotani poyankhula ndi kazembe wa Roma Felike?

12 Pozengedwa mlandu pamaso pa kazembe wa Roma Felike, Paulo anachitira umboni kuti: “[Ndikhulupira] zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri; ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:14, 15) Kodi mbali za m’Mawu a Mulungu monga “chilamulo,” zimaloza motani ku kuukitsidwa kwa akufa?

13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu ankanenanso za chiukiriro pamene ananena ulosi woyambirira?

13 Mulungu iyemwini ananenapo za chiukiriro pamene ananena ulosi woyambirira mu Edeni. Poweruza “njoka yokalambayo,” Satana Mdyerekezi, Mulungu anati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:14, 15) Kulalira chitende cha mbewu ya mkaziyo kunatanthauza kupha Yesu Kristu. Kuti Mbewuyo kenako idzalalire mutu wa njoka pambuyo pake, Kristu anayenera kuukitsidwa kwa akufa.

14. Kodi zili motani kuti Yehova si “Mulungu wa akufa, koma wa amoyo”?

14 Yesu anati: “Za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pachitsamba chija, pamene iye am’tchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye.” (Luka 20:27, 37, 38; Eksodo 3:6) Abrahamu, Isake, ndi Yakobo anali akufa, koma chifuno cha Mulungu chowaukitsa chinali chotsimikizirika zedi kuti chidzakwaniritsidwa moti kwa iye anthuwo anali ngati amoyo.

15. N’chifukwa chiyani Abrahamu anali ndi chifukwa chokhulupirira chiukiriro?

15 Abrahamu anali ndi chifukwa chokhalira ndi chiyembekezo cha chiukiriro, popeza kuti pamene iyeyo ndi mkazi wake, Sara, anali okalamba kwambiri ndipo anali akufa ponena za mphamvu zawo zobala ana, Mulungu anabwezeretsa mphamvu zawozo mozizwitsa. Chimenechi chinali ngati chiukiriro. (Genesis 18:9-11; 21:1-3; Ahebri 11:11, 12) Mwana wawo wamwamuna, Isake, atafika zaka ngati 25 zakubadwa, Mulungu anauza Abrahamu kuti am’pereke nsembe. Koma pamene Abrahamu anali pafupi kupha Isake ndi mpeni, mngelo wa Yehova anam’letsa. Abrahamu ‘anayesera iye kuti Mulungu n’ngwokhoza kuukitsa [Isake], ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anam’landiranso.’​—Ahebri 11:17-19; Genesis 22:1-18.

16. Panopo Abrahamu ali chigonere mu imfa, kudikira chiyani?

16 Abrahamu anali ndi chiyembekezo cha chiukiriro mu ulamuliro wa Mesiya, Mbewu yolonjezedwayo. Poona zochitika asanadzakhale munthu padziko lapansi, Mwana wa Mulungu anaona chikhulupiriro cha Abrahamu. Chotero atakhala munthu padziko lapansi, Yesu Kristu anauza Ayuda kuti: “Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa.” (Yohane 8:56-58; Miyambo 8:30, 31) Panopo Abrahamu ali chigonere mu imfa, kudikira kuukitsidwira ku moyo padziko lapansi mu Ufumu Waumesiya wa Mulungu.​—Ahebri 11:8-10, 13.

Umboni wa M’Chilamulo ndi M’Masalmo

17. Kodi zinthu “zili monga mwa chilamulo” zinaloza motani ku kuukitsidwa kwa Yesu Kristu?

17 Chiyembekezo cha Paulo cha chiukiriro chinali chogwirizana ndi zinthu “zili monga mwa chilamulo.” Mulungu anauza Aisrayeli kuti: “Muzidza nawo mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe; ndipo [pa Nisani 16] iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu.” (Levitiko 23:9-14) Mwina Paulo ankaganiza za lamulo limeneli pamene analemba kuti: “Kristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choundukula [“choyamba,” NW] cha iwo akugona.” Monga “chipatso choyamba,” Yesu anaukitsidwa pa Nisani 16, 33 C.E. Pambuyo pake, pakukhalapo kwake, padzakhala kuukitsidwa kwa ‘zipatso zotsatira’​—otsatira ake odzozedwa ndi mzimu.​—1 Akorinto 15:20-23; 2 Akorinto 1:21; 1 Yohane 2:20, 27.

18. Kodi Petro anasonyeza motani kuti kuukitsidwa kwa Yesu kunaloseredwa m’Masalmo?

18 Masalmo nawonso amachirikiza chiukiriro. Patsiku la Pentekoste wa 33 C.E., mtumwi Petro anagwira mawu Salmo 16:8-11, nati: “Davide anena za [Kristu], Ndinaona Mbuye pamaso panga nthaŵi zonse; chifukwa ali padzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike; mwa ichi unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m’chiyembekezo. Pakuti simudzasiya moyo wanga ku Hade, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde.” Petro anawonjezera kuti: “[Davide] pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Kristu, kuti sanasiyidwa m’Hade, ndipo thupi lake silinaona chivundi. Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa.”​—Machitidwe 2:25-32.

19, 20. Ndi liti pamene Petro anagwira mawu Salmo 118:22, nanga zimenezi anazigwirizanitsa motani ndi imfa ya Yesu ndi kuukitsidwa kwake?

19 Masiku angapo pambuyo pake, Petro anali pamaso pa Sanihedirini ndipo anagwiranso mawu Masalmo. Atafunsidwa mmene anachiritsira wopemphapempha wolumala, mtumwiyo anati: “Zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israyeli, kuti m’dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, amene inu munam’pachika [pamtengo wozunzirapo, NW], amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo. Iye [Yesu] ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangondya. Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”​—Machitidwe 4:10-12.

20 Panopo Petro anagwira mawu Salmo 118:22, n’kuwagwirizanitsa ndi imfa ya Yesu ndi kuukitsidwa kwake. Posonkhezeredwa ndi atsogoleri awo achipembedzo, Ayuda anam’kana Yesu. (Yohane 19:14-18; Machitidwe 3:14, 15) Pamene ‘omanga nyumba anakana mwalawo,’ Kristu anaphedwa, koma ‘kukhala mutu wa pangondya kwa mwalawo’ kunasonyeza kuti adzaukitsidwa n’kukhala ndi ulemerero wauzimu kumwamba. Monga momwe wamasalmo ananeneratu, ‘chimenechi chinadza kuchokera kwa Yehova.’ (Salmo 118:23) Kupanga “mwalawo” kukhala Mutu wa pangondya kunaphatikizapo kum’kweza kukhala Mfumu Yosankhidwiratu.​—Aefeso 1:19, 20.

Olimbikitsidwa ndi Chiyembekezo cha Chiukiriro

21, 22. Kodi Yobu anali ndi chiyembekezo chotani, monga momwe zilili pa Yobu 14:13-15, ndipo zimenezi zingatonthoze motani ofedwa lerolino?

21 Ngakhale kuti ifeyo sitinaonepo munthu ataukitsidwa kwa akufa, taona nkhani zina za m’Malemba zotitsimikizira za chiukiriro. Chotero, tingakhale ndi chiyembekezo chomwe munthu wowongoka mtima Yobu anatchula. Pamene anali pamavuto, anachonderera kuti: “Ha! mukadandibisa kumanda, . . . mukadandiikira nthaŵi, ndi kundikumbukira. Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? . . . Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:13-15) Mulungu ‘adzakhumba ntchito ya manja ake,’ kukhala wofunitsitsa kuukitsa Yobu. Zimatipatsatu chiyembekezo cholimbikitsa zedi!

22 M’banja mwathu, munthu woopa Mulungu angadwale matenda a kayakaya, monga momwe anadwalira Yobu, ndipo mwinanso atha kugonja kwa mdani wathu imfa. Ofedwawo angalire pogwidwa ndi chisoni, monga momwe Yesu analirira pa imfa ya Lazaro. (Yohane 11:35) Komatu n’kotonthoza zedi kudziŵa kuti Mulungu adzaitana ndipo onse omwe ali m’chikumbukiro chake adzayankha! Zidzakhala ngati kuti abwerako paulendo​—osati odwala kapena opuwala, koma athanzi lawo labwino.

23. Kodi ena asonyeza motani chidaliro m’chiyembekezo cha chiukiriro?

23 Pamene Mkristu wokhulupirika wachikulire anamwalira, okhulupirira anzake anasonkhezereka kulemba kuti: “Pepani kwambiri pa imfa ya amayi anu. Posachedwa pompa tidzawalandiranso​—okongola ndi anyonga!” Makolo amene anatayikidwa mwana wawo wamwamuna anati: “Timalakalaka kwabasi kudzaonanso Jason atauka! Adzayang’ana malo onse ozungulira ndi kuona Paradaiso yemwe ankam’funitsitsa kwambiri. . . . Chimenecho n’chisonkhezeronso chachikulu kwa ife omwe tinkam’konda kuti nafenso tidzakhalepo.” Inde, ndipo ndife othokoza kwambiri kuti chiyembekezo cha chiukiriro n’chotsimikizirika!

Yankho Lanu N’lotani?

• Kodi kukhulupirira m’makonzedwe a Mulungu a kuukitsa akufa kungatipindulitse motani?

• N’zochitika zotani zolembedwa m’Malemba zomwe zimatipatsa chifukwa chokhalira ndi chiyembekezo m’chiukiriro?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti chiukiriro ndi chiyembekezo chomwe chakhalapo kuyambira kalekale?

• Kodi n’chiyembekezo chotani cholimbikitsa chokhudza akufa chomwe tingakhale nacho?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Ndi mphamvu ya Yehova, Eliya anabwezeretsa moyo wa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye

[Chithunzi patsamba 12]

Pamene Yesu anaukitsa mwana wamkazi wa Yairo, makolo ake anadabwa kwambiri

[Chithunzi patsamba 15]

Patsiku la Pentekoste 33 C.E., mtumwi Petro anapereka umboni molimba mtima kuti Yesu anaukitsidwa kwa akufa