Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Moyo Wanu Ungakhale ndi Tanthauzo Lalikulu?

Kodi Moyo Wanu Ungakhale ndi Tanthauzo Lalikulu?

Kodi Moyo Wanu Ungakhale ndi Tanthauzo Lalikulu?

NTHAŴI zambiri, mphamvu zosonyezedwa pa nkhope ya ndalama si ndizo mtengo wake weniweni. Ndalama yapepala yamphamvu kwambiri yomwe inagwiritsidwapo ntchito mu United States inali $10,000. Komabe, pepala lomwe anapangira ndalamayo n’lotsika mtengo kwambiri.

Kodi munayamba mwalingalirapo kaya ngati mapepala otsika mtengowo angapereke tanthauzo lenileni ku moyo wanu? Anthu ambiri amalingalira kuti angaterodi. Anthu mamiliyoni ambiri amagwira ntchito usana ndi usiku n’cholinga chofuna kupeza ndalama zochuluka monga momwe angathere. Nthaŵi zina kufunafuna kwawo ndalama kumatanthauza kunyalanyaza thanzi lawo, mabwenzi awo, ngakhalenso mabanja awo. Kodi amapindulanji? Kodi ndalama kapena zinthu zomwe timagula ndi ndalamazo, zingadzetse chikhutiro chenicheni ndiponso chosatha?

Malinga n’kunena kwa ofufuza ena, pamene tilimbikira kufunafuna chikhutiro m’chuma, m’pamenenso zimakhala zokayikitsa kwambiri kuti tingachipeze. Mtolankhani Alfie Kohn anatsimikizira kuti “sitingagule chikhutiro. . . . Anthu omwe amaika patsogolo kulemera m’moyo amavutika ndi nkhaŵa yosaneneka ndi kupsinjika maganizo ndipo nthaŵi zambiri sakhala pamtendere.”​—International Herald Tribune.

Ngakhale kuti ochita kafukufuku azindikira kuti moyo watanthauzo umafuna chinachake osati ndalama, anthu ambiri sakuganiza choncho. Zimenezi n’zosadabwitsa, popeza kuti anthu a m’mayiko a Kum’maŵa amalandira mauthenga otsatsa malonda ambiri pafupifupi 3,000 tsiku lililonse. Kaya kumeneku kukhale kutsatsa malonda a galimoto kapena masuwiti, mfundo yaikulu pamenepa imakhala yakuti: ‘Gulani chinthu ichi, ndipo mudzasangalala kwambiri.’

Kodi zotsatira za kulimbikitsabe moyo wofunafuna chuma n’zotani? Eya, nthaŵi zambiri zofunika zauzimu zimanyalanyazidwa! Malinga ndi lipoti la m’magazini ya Newsweek, bishopu wamkulu ku Cologne, Germany, analengeza posachedwapa kuti “m’chitaganya chathu chino, anthu alekeratu kukamba za Mulungu.”

Mwinamwake inuyo mwathera pafupifupi mphamvu zanu zonse pofuna kupeza zofunika m’moyo wanu. Mwina mukulingalira kuti simungachite kena kalikonse chifukwa chakuti muli ndi nthaŵi yochepa. Komabe, nthaŵi zina, mungaganize kuti muyenera kuti m’moyo muli zochita zambiri kuposa kungothamanga liŵiro lotopetsa mosaleka kufikira pamene thanzi lanu kapena zaka zanu zikukakamizani kuima.

Kodi kulabadira kwambiri zinthu zauzimu kungakukhutiritseni mowonjezereka? Kodi chomwe chingapereke tanthauzo lalikulu ku moyo wanu n’chiyani?