Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kubukitsa Uthenga Wabwino M’minda ya Mpunga ku Taiwan

Kubukitsa Uthenga Wabwino M’minda ya Mpunga ku Taiwan

Ndife a Iwo Omwe Ali Ndi Chikhulupiriro

Kubukitsa Uthenga Wabwino M’minda ya Mpunga ku Taiwan

DZIKO la Taiwan kaŵirikaŵiri limalandira mvula yambiri ndipo zimenezi zimalitheketsa kulima ndi kukolola mpunga wambiri kaŵiri chaka ndi chaka. Komabe, nthaŵi zina mvula siibwera panthaŵi yake ndipo mbewu zimafa. Pamene zoterezi zachitika kodi alimi amagwa mphwayi? Ayi. Amadziŵa kuti m’pofunika kupirira. Amafesa njere zina n’kukadzalanso m’munda muja. Ndiye, mvula ikagwa bwino alimiwo amakolola kwambiri. Kudzala ndi kututa kwauzimu nthaŵi zina n’kofanana kwambiri ndi zimenezi.

Kupirira Potuta Mwauzimu

Kwa zaka zambiri, Mboni za Yehova ku Taiwan zagwira ntchito molimba kudzala ndi kututa mbewu za choonadi cha m’Malemba kumalo amene ankaoneka ngati osabala. Chitsanzo chimodzi ndi dera la Miao-li. M’deralo kulalikira n’kwa apo ndi apo ndipo ndi anthu ochepa chabe amene akhudzidwa nako. Choncho mu 1973 banja lina la apainiya apadera linatumizidwa kumeneko kukagwira ntchito monga alaliki anthaŵi zonse olengeza Ufumu. Poyambirira, ena anasonyeza chidwi ndi uthenga wabwino umenewu. Komabe, posapita nthaŵi chidwi chimenechi chinazimiririka. Kenako apainiya apadera ameneŵa anatumizidwa kudera lina.

Mu 1991 apainiya ena aŵiri anatumizidwanso kumeneku. Koma zinthu zinasonyezanso kuti mkhalidwe wa kumeneko sunali woyenera pa kukula kwauzimu. Patapita zaka zochepa, apainiya apadera ameneŵa anatumizidwa kumadera amene ankayembekezeka kukhala obala zipatso. Motero, kwakanthaŵi derali linali losalimidwa.

Kupambana Chifukwa Choyesanso

Mu September 1998 anaganiza zoyesetsa kuti apeze madera omwe akanakhala obala zipatso kugawo lalikulu lomwe linali lisanagaŵiridwepo ku Taiwan. Kodi zimenezi zikanatheka bwanji? Potumiza apainiya apadera akanthaŵi okwana 40 kukagwira ntchito kugawo lokhala ndi anthu ambiri lomwe linali losagaŵiridwa.

Mizinda iŵiri yoyandikana ku Miao-li inali m’gulu la madera osankhidwa kuti akagwireko ntchitoyo. Alongo anayi osakwatiwa anakagwirako ntchito kwa miyezi inayi kuti akaone mmene deralo lilili. Atangofika, analemba lipoti losonyeza kupita patsogolo kwa chiŵerengero cha anthu okondwerera amene amawapeza. Panthaŵi imene anamaliza miyezi yawo itatu yochita upainiya ku deralo, ankachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba ambiri. Komanso anakhazikitsa kagulu ka phunziro la buku mothandizidwa ndi mkulu wochokera ku mpingo wapafupi.

Atatu mwa alongo ameneŵa ananena motsimikiza kuti apitiriza kusamalira “mbewu zanthete” zimene zimakula bwino kwambiri. Choncho, alongo aŵiri anasankhidwa kukhala apainiya apadera okhazikika, ndipo wachitatu anapitiriza kutumikira ngati mpainiya wokhazikika. Mkulu wochokera ku mpingo wapafupi anasamukira kuderalo kuti akawathandize. Anthu opitirira 60 anamvetsera nkhani yapoyera yoyamba kukambidwa m’deralo. Tsopano mpingo woyandikana nawowo ukuthandiza kagulu katsopano kameneka kuchita misonkhano lamlungu lililonse mokhazikika, kuwonjezera pa maphunziro angapo a buku. Posachedwa mpingo watsopano ungadzakhazikitsidwe m’deralo.

Kupirira Kunabweretsa Madalitso ku Mbali Zina za Taiwan

Madera ena anachita mofananamo. Dera la I-lan, limene lili m’chigawo cha kumpoto chakumadzulo kwa chilumbacho, Phunziro la Buku la Mpingo latsopano linakhazikitsidwa m’dera limene apainiya apadera akanthaŵi aja anagwirako ntchito.

Pamene ankalalikira ku nyumba ndi nyumba madzulo, mpainiya wapadera wakanthaŵi anakumana ndi mnyamata amene anamusonyeza ndandanda yamisonkhano yampingo. Mwamsanga mnyamatayo anafunsa kuti: “Kodi ndingadzabwere ku msonkhano wamaŵa usiku? Ngati n’kotheka, ndidzavale chiyani?” Mpainiyayo anangozindikira kuti akuchititsa maphunziro a Baibulo asanu ndi atatu apanyumba mlungu uliwonse. Angapo mwa ophunzira Baibulo ameneŵa posachedwapa anali kukonzekera kuti akhale ofalitsa a uthenga wabwino, ndi cholinga choti abatizidwe.

Munthu wina wamkazi m’tauni yomweyi anakhala akupita ku tchalitchi kwa zaka zambiri koma sanathe kupeza munthu woti am’phunzitse Baibulo. Atamva zakuti kuli phunziro la Baibulo, anagwiritsa ntchito mwayiwu. Analimbikitsidwa kukonzekera phunziro lake pasadakhale. Mpainiya wapadera wakanthaŵiyo atapita kukachititsa phunzirolo, anapeza mayiyo atakonzekera kale pogula kope limene analembamo mafunso a m’buku limene anali kuphunzira. Komanso anali atalemberatu mayankho a funso lililonse. Analinso atalemba m’kope lake malemba onse opezeka m’phunziro lake. Panthaŵi imene mlongoyo amafika kudzachititsa phunziro loyamba, mayiyu anali atakonzekera kale mitu itatu yoyambirira!

Zochitika zofanana zinaoneka m’tauni ya Dongshih m’chigawo chapakati ku Taiwan. Apainiya apadera akanthaŵi anagaŵira mabulosha opitirira 2,000 pa miyezi itatu imene anagwira ntchito kumeneko. Pofika mwezi wachitatu, ankachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 16. Tauniyo inawonongedwa kwambiri ndi chivomezi chimene chinachitika m’chigawo chapakati cha dziko la Taiwan pa September 21, 1999, koma okondwerera ena akupitirizabe kupita patsogolo mwauzimu, ngakhale kuti amafunikira kuyenda kwa ola lathunthu kuti akachite misonkhano ku Nyumba ya Ufumu yapafupi. Inde, kupirira n’kofunika kuti tikolole mbewu zabwino, kaya zikhale mbewu zenizeni kapena zauzimu.

[Mapu patsamba 8]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

CHINA

Nyanja ya Taiwan

TAIWAN

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.