Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Moyo Wanu Ungakhalire ndi Tanthauzo Lalikulu

Mmene Moyo Wanu Ungakhalire ndi Tanthauzo Lalikulu

Mmene Moyo Wanu Ungakhalire ndi Tanthauzo Lalikulu

MWAMBI wina wakale umati: “Usadzitopetse kuti ulemere. Leka nzeru yakoyako. Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.” (Miyambo 23:4, 5) M’mawu ena, si kwanzeru kudzitopetsa n’kufuna kulemera, pakuti chuma chingauluke ngati kuti chamera mapiko a mphungu.

Monga momwe Baibulo likusonyezera, chuma chingathe mwamsanga. Chingazimiririke usiku umodzi wokha chifukwa cha tsoka lachilengedwe, kuchepa mphamvu mwadzidzidzi kwa chuma, kapena zochitika zina zosadziŵika. Komanso, ngakhale ochita bwino m’zachuma nthaŵi zambiri amagwiritsidwa mwala. Lingalirani za John, amene ntchito yake inali yokhudza kusangalatsa andale, otchuka m’zamaseŵero, ndi mafumu.

John anati: “Ndinadzipereka kotheratu ku ntchito yanga. Ndinapeza chuma chochuluka, ndinali kukhala mu mahotela apamwamba, ndipo nthaŵi zina ndinali kuyenda pandege ya hayala yamtundu wa jeti popita kuntchito. Poyamba zinkandisangalatsa kwabasi, koma pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kunyansidwa. Anthu omwe ndimayesa kuwasangalatsawo anali opanda pake. Moyo wanga unalibe tanthauzo lenileni.”

Monga momwe John anaonera, moyo wopanda chitsogozo chauzimu n’ngwosakhutiritsa. Pa Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu Kristu anasonyeza momwe munthu angapezere chimwemwe chosatha. Iye anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu, popeza kuti ufumu wakumwamba uli wawo.” (Mateyu 5:3, NW) Choncho n’zoonekeratu kuti n’chanzeru kuika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo. Komabe, zinthu zinanso zingathandize kupereka tanthauzo lalikulu la moyo.

Banja Lanu ndi Mabwenzi Anu N’ngofunikira

Kodi mukanasangalala ndi moyo kukanakhala kuti simunali wokhoza kulankhulana ndi banja lanu ndipo munalibe mabwenzi apamtima? Mwachidziŵikire ayi. Mlengi wathu anatipanga ndi chifuno cha kukonda ndi kukondedwa. Chimenecho n’chifukwa chimodzi chomwe Yesu anagogomezera kufunika kwa ‘kukonda mnzathu momwe tidzikondera ife eni.’ (Mateyu 22:39) Banja ndi mphatso ya Mulungu yomwe imapereka malo abwino osonyezera chikondi chopanda dyera.​—Aefeso 3:14, 15.

Kodi banja lathu lingapatse motani moyo wathu tanthauzo lalikulu? Eya, banja logwirizana tingathe kuliyerekezera ndi munda wokongola umene uli ngati malo otsitsimula kupsinjika maganizo kwa moyo wa tsiku ndi tsiku. Mofananamo, m’banja tingapeze ubwenzi wotsitsimula ndi chikondi chomwe chingathetse kunyong’onyeka. Komabe, banja silingadzetse chisungiko choterechi mwachisaŵaŵa. Koma pamene tilimbitsa mgwirizano m’banja, timayandikana kwambiri wina ndi mnzake, ndipo moyo umakhutiritsa. Mwachitsanzo, nthaŵi ndi chisamaliro zomwe timapereka posonyeza chikondi ndi ulemu kwa mnzathu wamuukwati zimaikizidwa tsiku ndi tsiku ndipo pambuyo pake zingadzetse phindu lalikulu.​—Aefeso 5:33.

Ngati tili ndi ana, tiyenera tiyesetse kuti anawo akulire m’malo abwino. Kucheza nawo, kulankhula nawo momasuka, ndi kuwapatsa malangizo auzimu zingafune nthaŵi yochulukirapo. Koma nthaŵi imeneyo ndi kuyesayesa kwathuko zingatikhutiritse kwambiri. Makolo ochita zinthu bwino amaona ana monga madalitso, monga choloŵa chochokera kwa Mulungu chimene chiyenera kusamalidwa bwino.​—Salmo 127:3.

Mabwenzi abwino nawonso amathandizira kuti moyo ukhale wokhutiritsa ndi watanthauzo. (Miyambo 27:9) Tingapange ubwenzi ndi anthu ambiri mwa kukhala a mtima umodzi. (1 Petro 3:8) Mabwenzi enieni amatidzutsa tikagwa. (Mlaliki 4:9, 10) Ndipo “bwenzi lenileni . . . limakhala mbale panthaŵi ya tsoka.”​—Miyambo 17:17, NW.

Ubwenzi weniweni n’ngokhutiritsatu zedi! Kuloŵa kwa dzuwa kumachititsa chidwi kwambiri, chakudya chimakoma zedi, ndipo nyimbo zimakhala zosangalatsa kwambiri ngati muli ndi mabwenzi anu. Inde, banja labwino ndi mabwenzi okhulupirika ndi mbali ziŵiri zokha zofunika za moyo watanthauzo. N’zinthu zina ziti zomwe Mulungu wapereka zimene zingapatse miyoyo yathu tanthauzo lalikulu?

Kukhutiritsa Chosoŵa Chathu Chauzimu

Monga momwe taonera kale, Yesu Kristu anagwirizanitsa chimwemwe ndi kuzindikira zosoŵa zathu zauzimu. Tinalengedwa ndi kuyenerera kwa kukhala auzimu ndi olungama. Chifukwa cha chimenecho, Baibulo limatchula za “munthu wauzimu” ndi “munthu wobisika wamtima.”​—1 Akorinto 2:15; 1 Petro 3:3, 4.

Malinga n’kunena kwa An Expository Dictionary of New Testament Words, lolembedwa ndi W.E. Vine, mtima wophiphiritsawo ukuimira “malingaliro ndi makhalidwe onse a munthu, kulingalira kwa munthuyo payekha, ndiponso maganizo ake.” Pofotokoza, Vine anawonjezera kuti: “M’mawu ena, mtima ukugwiritsidwa ntchito mophiphiritsira gwero lobisika la moyo wa munthu wam’kati.” Buku lomweli linanenanso kuti “mtima, monga momwe wakhalira m’kati mwenimwenimo, uli ndi ‘munthu wobisika,’ . . . munthu weniweni.”

Kodi tingakhutiritse motani zofuna za “munthu wauzimu,” yemwe ndi “munthu wobisika,” kapena kuti, “munthu wobisika wamtima”? Pochita zimenezi timachita mbali yofunika kwambiri ndipo timakhutiritsa chofuna chathu chauzimu pamene tazindikira mfundo yotchulidwa ndi wamasalmo wouziridwayo yemwe anaimba kuti: “Dziŵani kuti Yehova ndiye Mulungu. Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake. Ndife anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake.” (Salmo 100:3) Moyenerera, kuzindikira zimenezi kumatitsogolera kuvomereza kuti tikutsogozedwa ndi Mulungu. Ngati tikufuna kukhala m’gulu la “anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake,” tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi mawu ake, Baibulo.

Kodi kukhala ake a Mulungu n’koipa? Ayi, pakuti kuzindikira kuti zochita zathu zimam’khudza Mulungu kumapereka tanthauzo ku miyoyo yathu. Kumatilimbikitsa kukhala anthu abwino, chimene chilidi cholinga choyenera. “Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake,” limatero Salmo 112:1. Mantha aulemu kwa Mulungu ndi kumvera malamulo ake kuchokera mumtima kungapatse miyoyo yathu tanthauzo lalikulu.

N’chifukwa chiyani kumvera Mulungu kumatikhutiritsa? Chifukwa chakuti tili ndi chikumbumtima, mphatso yomwe Mulungu wapereka ku mtundu wonse wa anthu. Chikumbumtima chimapenda mikhalidwe ndipo chimavomereza kapena kutsutsa zomwe tachita kapena zomwe tikulingalira kuchita. Tonsefe tatsutsidwapo m’maganizo nthaŵi inayake chikumbumtima chathu chitavutitsidwa kwambiri. (Aroma 2:15) Komatu chikumbumtima chathucho chingathenso kutifupa. Pamene tichitira Mulungu ndi anthu anzathu mopanda dyera, timadzimva kuti tachitadi moyenera ndipo timakhutira. Timazindikira kuti “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Palitu chifukwa chofunika kwambiri chochitira zimenezi.

Mlengi wathu anatipanga mwapadera kwambiri mwakuti zokhumba ndi zofunika zazikulu za anthu anzathu timakhudzidwa nazo. Kuthandiza ena kumadzetsa chisangalalo m’mitima yathu. Komanso, Baibulo limatitsimikizira kuti pamene tipereka kanthu kwa winawake wosoŵa, Mulungu amalingalira kuti chifundocho tam’chitira iyeyo.​—Miyambo 19:17.

Kusiyapo kupatsa chikhutiro cha mu mtima, kodi kulabadira zosoŵa zathu zauzimu kungatithandize m’njira ina iliyonse? Chabwino, wamalonda wina ku Middle East wotchedwa Raymond amakhulupirira kuti kungatithandize. “Cholinga changa chachikulu, chinali chopanga ndalama,” iye akutero. “Koma kuchokera panthaŵi yomwe ndinavomereza mu mtima mwanga kuti Mulungu alipodi ndi kuti Baibulo limafotokoza zofuna zake, ndinasinthiratu. Kupeza zofunika m’moyo uno kumabwera pa malo achiŵiri tsopano m’moyo wanga. Mwa kuyesa kukondweretsa Mulungu, ndathandizidwa kupeŵa malingaliro ovulaza achidani. Ngakhale kuti bambo anga anamwalira pankhondo inayake, ndilibe lingaliro lobwezera anthu achiwembuwo.”

Monga momwe Raymond anaonera, kusamalira bwino zofuna za “munthu wauzimu” kungapoletse mabala akuluakulu a m’maganizo. Komatu, pokhapokha titapirira mavuto omwe amadza tsiku lililonse, si moyo wonse womwe udzakhala wokhutiritsa.

Tingakhale Ndi “Mtendere wa Mulungu”

M’dziko lotopetsa lino, ndi masiku oŵerengeka chabe omwe amadutsa popanda zovuta. Kumachitika ngozi, zofuna zathu sizikwaniritsidwa, ndipo anthu amatikhumudwitsa. Zochitika zobwezera m’mbuyo ngati zimenezi zingachotse chimwemwe chathu. Komabe, kwa omwe akutumikira Yehova Mulungu, Baibulo likulonjeza chikhutiro cha m’kati​—“mtendere wa Mulungu.” Kodi mtendere umenewu tingaupeze bwanji?

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) M’malo moyesa kusenza tokha mavuto athu, tifunikira kupemphera mwakhama, kum’senza Mulungu nkhaŵa zathu zonse zatsiku ndi tsiku. (Salmo 55:22) Chikhulupiriro chakuti amamva mapemphero amenewo kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu, chidzawonjezeka pamene tikukula mwauzimu ndi kuzindikira momwe Mulungu amatithandizira.​—Yohane 14:6, 14; 2 Atesalonika 1:3.

Titalimbitsa chidaliro chathu mwa Yehova Mulungu, “Wakumva pemphero,” tidzakhoza bwino kupirira mayesero, monga matenda osatha, ukalamba, kapena umasiye. (Salmo 65:2) Komabe, kunena za moyo watanthauzo lenileni tiyeneranso kulingalira za m’tsogolo.

Kondwerani M’chiyembekezo cha M’tsogolo

Baibulo limalonjeza “miyamba yatsopano ndi dziko latsopano,” boma lakumwamba lolungama, ndi losamalira lomwe lidzalamulira mtundu wa anthu womvera. (2 Petro 3:13) M’dziko latsopano lolonjezedwa ndi Mulungulo, nkhondo ndi chisalungamo zidzaloŵedwa m’malo ndi mtendere ndi chilungamo. Ameneŵatu si malingaliro wamba, koma ndi chikhulupiriro chotsimikizirika chomwe chiyenera kulimba tsiku ndi tsiku. Iyitu ndi nkhani yabwino zedi ndipo chilitu chifukwa chabwino chokondwerera.​—Aroma 12:12; Tito 1:2.

John, wotchulidwa koyambirira uja, tsopano akuona kuti moyo wake uli ndi tanthauzo lalikulu. “Ngakhale kuti zachipembedzo ndinali nazo kutali, nthaŵi zonse ndinkakhulupirira Mulungu,” iye akutero. “Koma sindinali kuchita kalikonse pa chikhulupiriro chimenechi kufikira pamene Mboni za Yehova ziŵiri zinandifikira. Ndinawapanikiza nawo mafunso monga akuti, ‘N’chifukwa chiyani tili padziko pano? Ziyembekezo zathu zam’tsogolo n’zotani?’ Mayankho awo okhutiritsa a m’Malembawo anandichititsa kulingalira za chifuno cha moyo kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wanga. Chimenecho chinali chiyambi chabe. Ndinakulitsa ludzu la choonadi lomwe linandichititsa kusintha moyo wanga wonse. Ngakhale kuti sindinenso wolemera mwakuthupi, mwauzimu ndimadzimva kuti ndine m’pondamatiki.”

Mofanana ndi John, mwinamwake inuyo mwanyalanyaza uzimu wanu kwa zaka zambiri. Komatu mwa kukulitsa “mtima wanzeru,” mungautsitsimule. (Salmo 90:12) Mofunitsitsa ndiponso mutachita khama, mungapeze chimwemwe chenicheni, mtendere, ndi chiyembekezo. (Aroma 15:13) Inde, ndipo moyo wanu ungakhale ndi tanthauzo lalikulu.

[Chithunzi patsamba 6]

Pemphero lingatidzetsere “mtendere wa Mulungu”

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi mukudziŵa chimene chingapangitse moyo wabanja kukhala wokhutiritsa kwambiri?