Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chifukwa Chiyani Alibe Ana?

Kodi N’chifukwa Chiyani Alibe Ana?

Kodi N’chifukwa Chiyani Alibe Ana?

DELE ndi mkazi wake Fola, * amakhala ndi kugwira ntchito paofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ku Nigeria. Atangoyamba kumene kutumikira kumeneko, amayi ake a Fola anapita kukamuona. Anayenda ulendo wautali kukakambirana naye nkhani imene inali kuwadetsa nkhaŵa kwambiri, imene inkawasoŵetsa tulo.

“M’mandichitira zinthu zabwino kwambiri,” anatero mayiwo pouza Dele ndi fola. “M’manditumizira mphatso, ndipo m’mabwera kudzandiona. Kusonyeza chikondi kumeneku n’nkwamtengo wapatali zedi kwa ine. Koma kumandikhudzanso kwambiri chifukwa nthaŵi zonse ndimadzifunsa kuti kodi ndani adzakuchitirani zinthu ngati zimenezi mukadzafika msinkhu wangawu? Tsopano mwatha zaka ziŵiri muli m’banja, koma mulibe ndi mwana yemwe. Kodi simukulingalira kuti ndi nthaŵi yoti musiye kutumikira pa Beteli ndi kukayamba banja?”

Malingaliro amayiwo anali akuti: Dele ndi Fola atumikira mokwanira pa Beteli. Tsopano ndi nthaŵi yoti ayambe kuganiza zatsogolo lawo. Ndithudi angasiire anthu ena ntchito yawoyo. Sikuti Dele ndi Fola adzasiya utumiki wanthaŵi zonse, koma angachite mbali ina ya utumiki, umene ungawalole kukhala ndi ana ndi kupeza chimwemwe chokhala kholo.

Nkhaŵa ya Amayi

Mpake mayiwo kudera nkhaŵa. N’kwachibadwa kufuna kukhala ndi ana ndipo chikhumbo chimenechi n’chofala pa chikhalidwe ngakhalenso kwa munthu payekha. Kubereka kumadzetsa chimwemwe ndiponso chiyembekezo. “Chipatso cha m’mimba ndicho mphoto yake,” limatero Baibulo. Inde, kubereka ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mlengi wathu wachikondi.​—Salmo 127:3.

M’madera ambiri, okwatirana amaumirizidwa kwambiri ndi anthu kuti abereke ana. Mwachitsanzo, ku Nigeria, kumene akazi ambiri amakhala ndi ana asanu ndi m’modzi, patsiku laukwati n’kofala kumva anthu akufuna kwabwino akuuza banja latsopanolo kuti: “Pakatha miyezi isanu ndi inayi, tikufuna kumva kulira kwa mwana m’nyumba mwanu.” Mkwatibwi ndi mkwati angalandire bedi la mwana monga mphatso. Apongozi awo amayang’ana kalendala pafupipafupi. Ngati mkwatibwi sakhala ndi mimba m’kati mwa chakacho kapena kuposerapo, amafufuza kuti aone ngati pali vuto lililonse limene angathandize kulithetsa.

Amayi ambiri amalingalira kuti anthu amakwatirana chifukwa chofuna kubereka ana kuti akulitse mtundu wawo. Amayi a Fola anamuuza kuti: “N’chifukwa chiyani unakwatiŵa ngati sufuna kukhala ndi ana? Munthu wina anabereka iwe; iwenso ubereke ana ako.”

Kuphatikiza apo, pali nkhani zina zofunika kuzilingalira. M’mayiko ambiri mu Afirika, boma silichita zambiri kuti lithandize kusamalira anthu okalamba. Kaŵirikaŵiri, makolo okalamba amasamalidwa ndi ana awo, monga mmene makolowo anasamalira anawo ali aang’ono. Choncho amayi a Fola ankaganiza kuti kokha ngati ana awowo abereka ana awoawo, ndiye kuti m’zaka zaukalamba sadzakhala osungulumwa, osafunika, osauka, kapena osoŵa wina owaika m’manda atamwalira.

M’madera ambiri mu Afirika, kusakhala ndi ana amakuona ngati kutembereredwa. M’malo ena, akazi amafunika kuonetsa kuti ndi obereka asanakwatiwe n’komwe. Akazi ambiri amene ali osabereka amakafuna mankhwala osula kuti mwina akhaleko ndi mwana.

Chifukwa cha malingaliro ameneŵa, okwatirana amene amasankha kusabereka amawaona ngati akudzimana chinthu china chabwino. Amaonedwa monga odabwitsa, osalingalira zam’tsogolo, ndi omvetsa chisoni.

Chimwemwe Ndiponso Udindo

Anthu a Yehova amadziŵa kuti ngakhale kuli kwakuti n’kosangalatsa kukhala ndi ana, palinso udindo. Baibulo pa 1 Timoteo 5:8, limati: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.”

Makolo ayenera kusamalira mabanja awo mwakuthupi ndi mwauzimu, ndipo zimenezi zimafuna nthaŵi yambiri ndi khama. Sakhala ndi malingaliro akuti popeza Mulungu ndiye amatipatsa ana, ndi udindo wakenso kuwasamalira. Amadziŵa kuti kusamalira ana mogwirizana ndi mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo ndi udindo wanthaŵi zonse umene Mulungu anapatsa Makolo; si ntchito yoti angasiire anthu ena.​—Deuteronomo 6:6, 7.

Ntchito yolera ana ndi yovuta kwambiri makamaka mu “masiku otsiriza” ano a “nthaŵi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Kuphatikiza pa kuipiraipira kwa mikhalidwe ya zachuma, kusakhulupirira Mulungu kwa anthu kowonjezerekako kumapangitsa kulera ana lerolino kukhala kovuta. Ngakhale zili choncho, padziko lonse mabanja ambiri achikristu asenza udindo umenewu ndipo akulera mwachipambano ana oopa Mulungu “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Yehova amakonda ndiponso kudalitsa makolo ameneŵa kaamba ka ntchito yawo yaikulu.

Chifukwa Chake Ena Sakhala ndi Ana

Komabe, okwatirana ambiri achikristu, alibe ana. Ena n’ngosabereka komabe salera ana a anthu ena. Okwatirana ena amene ali obereka amachita kufuna kuti asabereke. Okwatirana ameneŵa si kuti alibe ana chifukwa chozemba udindo kapena kuopa mavuto okhala kholo. Koma, atsimikiza mtima kupereka chisamaliro chawo chonse ku mbali zosiyanasiyana za utumiki wanthaŵi zonse umene si ungatheke kuuchita kwinaku ukulera ana. Ena amatumikira monga amishonale. Ena amatumikira Yehova m’ntchito yoyendayenda kapena pa Beteli.

Monga Akristu ena onse, amazindikira kuti pali ntchito yofunika kuigwira mwamsanga. Yesu anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” Ntchito imeneyi ikuchitika lerolino. Ndi ntchito yofunika, popeza “chimaliziro” chidzawononga awo amene samvera uthenga wabwino.​—Mateyu 24:14; 2 Atesalonika 1:7, 8.

Nthaŵi yathu ino ikufanana ndi nthaŵi imene Nowa ndi banja lake anamanga chingalawa chachikulu chimene chinawapulumutsa pa Chigumula chachikulu. (Genesis 6:13, 16; Mateyu 24:37) Ngakhale kuti ana onse atatu a Nowa anali okwatira, palibe amene anali ndi ana mpaka Chigumula chitatha. Chifukwa chimodzi chimene sanaberekere ana chingakhale chakuti mabanja ameneŵa ankafuna kusamalira ndi mphamvu zawo zonse ntchito imene anali nayo. China chingakhale chakuti sankafuna kulera ana m’dziko lamakhalidwe oipa ndi lachiwawa m’mene “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu . . . ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.”​—Genesis 6:5.

Ngakhale kuti zimenezi sizikutanthauza kuti n’kulakwa kukhala ndi ana lerolino, mabanja ambiri achikristu safuna kukhala ndi ana n’cholinga choti akhale ndi nthaŵi yokwanira yogwirira ntchito yofunika mwamsanga imene Yehova wapatsa anthu ake kuti aigwire. Mabanja ena akhala kaye kwa kanthaŵi asanayambe kukhala ndi ana; ena asankha kukhala opanda ana ndipo alingalira zodzakhala ndi ana mu dziko latsopano lolungama la Yehova. Kodi kumeneko n’kusalingalira za m’tsogolo? Kodi akumanidwa kanthu kena kake m’moyo? Kodi ndi oyenera kuwamvera chisoni?

Miyoyo Yosungika ndi Yachimwemwe

Dele ndi Fola, amene atchulidwa poyamba paja, tsopano atha zaka zoposa 10 ali m’banja, ndipo atsimikiza mtima kupitiriza kukhalabe opanda ana. “Achibale athu akupitirizabe kutikakamiza kuti tikhale ndi ana,” akutero Dele. “Nkhaŵa yawo yaikulu ndi ya chisungiko chathu cham’tsogolo. Nthaŵi zonse timawathokoza chifukwa chotiganizira, koma timawafotokozera bwinobwino kuti timasangalala kwambiri ndi zimene tikuchita. Kunena za chisungiko, timawauza kuti timadalira Yehova, amene amasamalira umoyo wa onse amene amakhalabe okhulupirika kwa iye. Timafotokozanso kuti kukhala ndi ana sikutanthauza kuti anawo adzasamalira makolo awo atakalamba. Anthu ena sasamala kwenikweni za makolo awo, ena sangathe kuthandiza, ndiponso ena amamwalira msanga makolo awo ali moyo. Koma, mwa Yehova tsogolo lathu n’lotsimikizirika.”

Dele ndi anthu ena onga iye amakhulupirira ndi mtima wonse lonjezo la Yehova kwa atumiki ake okhulupirika lakuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Amakhulupiriranso kuti “mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake silili logontha, kuti silingamve.”​—Yesaya 59:1.

Chifukwa chinanso chokhalira ndi chidaliro chimenechi n’chakuti timaona mmene Yehova akuthandizira atumiki ake okhulupirika. Mfumu Davide analemba kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa.” Tangolingalirani zimenezo! Kodi munaonapo mtumiki wokhulupirika wa Yehova aliyense ‘atasiyidwa’?​—Salmo 37:25.

M’malo molingalira zam’mbuyo n’kumadzimvera chisoni, awo amene agwiritsa ntchito moyo wawo kutumikira Yehova komanso Akristu anzawo amalingalira zam’mbuyo ndi chikhutiro. Mbale Iro Umah watha zaka 45 ali mu utumiki wanthaŵi zonse ndipo tsopano akutumikira monga woyang’anira woyendayenda ku Nigeria. Iye akuti: “Ngakhale kuti ine ndi mkazi wanga tilibe mwana, nthaŵi zonse timadziŵa kuti Yehova amatisamalira mwauzimu ndi mwakuthupi. Sitisoŵa kanthu. Sadzatitaya tikakalamba. Zaka zimenezi za mu utumiki wanthaŵi zonse zakhala zosangalatsa kwambiri m’moyo wathu. Tili osangalala kuti tikutumikira abale athu, ndipo abale athu amayamikira utumiki wathu, ndipo amatichirikiza.”

Mosasamala kanthu kuti mabanja ambiri sanabereke ana akuthupi, koma ali ndi ana osiyanasiyana: Ophunzira achikristu amene amalambira Yehova. Mtumwi Yohane anali ndi zaka ngati 100 pamene analemba kuti: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.” (3 Yohane 4) Kukhulupirika kwa “ana” a Yohane​—awo amene anawaphunzitsa “choonadi”​— kunam’dzetsera chimwemwe kwabasi.

Lerolino timapeza chimwemwe chofananacho. Bernice wa ku Nigeria, wakhala m’banja zaka 19 ndipo alibe mwana mwakufuna kwawo. Kwa zaka 14, wakhala akutumikira monga mpainiya. Pamene akuyandikira zaka zimene sikudzathekanso kuti abereke ana akeake, sakudandaula n’komwe kuti wathera moyo wake kupanga ophunzira. Iye akuti: “Ndimasangalala kuona ana anga auzimu akukula. Ngakhale ndikanakhala ndi ana angaanga, ndikukayikira ngati akanandikonda mmene amachitira amene ndawathandiza kuphunzira choonadi. Amanditenga ngati ndine mayi wawo owabereka, amandiuza chimwemwe chawo ndiponso mavuto awo ndipo amandipempha kuti ndiwalangize. Amandilembera makalata, ndiponso timayenderana.

“Ena amaona ngati n’kutembereredwa kukhala wopanda mwana. Amati udzavutika utakalamba. Koma ine sindikuganiza choncho. Ndikudziŵa kuti ngati ndikutumikira Yehova ndi mtima wonse, adzandifupa ndi kundiyang’anira. Sadzanditaya n’takalamba.”

Mulungu Amawakonda Ndiponso Amawayamikira

Awo amene abereka ndi kulera ana ‘oyenda m’choonadi’ ali ndi zifukwa zochuluka zokhalira othokoza. Ndiye chifukwa chake Baibulo limati: “Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amako akondwere, amako wakukubala asekere!”​—Miyambo 23:24, 25.

Akristu amene sanakhoze kubereka ndi kulera ana m’dzikoli adalitsidwa m’njira zina. Ambiri a mabanja ameneŵa achita mbali yaikulu pofutukula zinthu za Ufumu mokulira. M’kupita kwa zaka, azoloŵerana nawo utumiki, apeza nzeru, ndi maluso zomwe zawatheketsa kuthandiza kwambiri pantchito ya Ufumu. Ambiri apita patsogolo ndi ntchitoyi.

Ngakhale alibe ana chifukwa chofuna kuchita zinthu za Ufumu, iwo adalitsidwa ndi Yehova powapatsa banja lachikondi lauzimu limene limayamikira kwambiri kudzimana kumene apanga. Zili monga mmene Yesu ananenera kuti: “Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana, ndi minda . . . ndipo nthaŵi ilinkudza, moyo wosatha.”​—Marko 10:29, 30.

Onse amene ali okhulupirika ndi amtengotu wapatali zedi kwa Yehova! Mtumwi Paulo akutsimikizira okhulupirika onse ameneŵa, amene ali ndi ana ndi amene alibe kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.”​—Ahebri 6:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha mayina.

[Zithunzi patsamba 23]

Mabanja amene alibe ana adalitsidwa ndi banja lachikondi lauzimu