Kudzikuza Kumadzetsa Manyazi
Kudzikuza Kumadzetsa Manyazi
“Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; Koma nzeru ili ndi odzichepetsa.”—MIYAMBO 11:2.
1, 2. Kodi kudzikuza n’chiyani, ndipo kwadzetsa mavuto m’njira ziti?
MLEVI wansanje watsogolera gulu lachiwawa kuukira maulamuliro oikidwa ndi Yehova. Mwana wamwamuna wa mfumu wofunitsitsa malo aulamuliro wakonza chiŵembu choukira ndi kulanda ufumu wa atate wake. Mfumu yosaleza mtima yanyalanyaza malangizo achindunji a mneneri wa Mulungu. Aisrayeli atatuŵa ali ndi khalidwe limodzi: kudzikuza.
2 Kudzikuza ndi khalidwe la mtima lomwe n’loopsa kwambiri kwa aliyense. (Salmo 19:13) Munthu wodzikuza amachita zinthu mopyola muyeso popanda chilolezo chochitira zimenezo. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimadzetsa mavuto aakulu. Ndithudi, kudzikuza kwasakazitsa mafumu ndi kugwetsa maufumu aakulu. (Yeremiya 50:29, 31, 32; Danieli 5:20) Kwatcheranso misampha atumiki ena a Yehova ndi kuwagwetsera ku chiwongongeko.
3. Kodi tingaphunzire motani za kuopsa kwa kudzikuza?
3 Pachifukwa chabwino Baibulo limati: “Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; koma nzeru ili ndi odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Baibulo limatipatsa zitsanzo zotsimikizira kuti mwambi umenewu n’ngwoona. Kupenda zina mwa zitsanzo zimenezi kudzatithandiza kuona kuwopsa kwa kuchita zinthu mopitirira muyeso wake. Choncho, tiyeni tione momwe nsanje, kufunitsitsa malo aulamuliro, ndi kusaleza mtima zinachititsira amuna atatu otchulidwa m’ndime yoyamba aja kuchita modzikuza, ndi kuwadzetsera manyazi.
Kora—Wopanduka Wansanje
4. (a) Kodi Kora anali yani, ndipo ndi pa zochitika zosaiŵalika zotani zomwe iye mosakayikira anatenga nawo mbali? (b) M’zaka zake zakumapeto, kodi Kora anatsogolera pa chochitika chochititsa manyazi chotani?
4 Kora anali Mlevi wachikohati, mbale weniweni wa Mose ndi Aroni. Mwachionekere, iye anakhala wokhulupirika kwa Yehova kwa zaka zambiri. Kora anali ndi mwayi wokhala m’khamu la anthu omwe anapulumutsidwa mozizwitsa pa Nyanja Yofiira, ndipo mwachidziŵikire anathandiza kupereka chiweruzo cha Yehova kwa Aisrayeli olambira mwana wa ng’ombe pa Phiri la Sinai. (Eksodo 32:26) Koma pambuyo pake, Kora anatsogolera anthu kutsutsana ndi Mose ndi Aroni. Ena mwa anthu ameneŵa anali Arubeni omwe ndi Datani, Abiramu, ndi Oni, komanso akalonga 250 a Israyeli. * “Mukula mphamvu inu,” iwo anatero kwa Mose ndi Aroni, “pakuti khamu lonse n’nlopatulika, onseŵa, ndipo Yehova ali pakati pawo; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?”—Numeri 16:1-3.
5, 6. (a) N’chifukwa chiyani Kora anapandukira Mose ndi Aroni? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Kora kwenikweni anachepetsa malo ake m’makonzedwe a Mulungu?
5 Atakhulupirika kwa zaka zambiri, n’chifukwa chiyani Kora pambuyo pake anapanduka? Ndithudi utsogoleri wa Mose pa Israyeli sunali wopondereza, pakuti iye anali “wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.” (Numeri 12:3) Koma zikuoneka kuti Kora ankachitira nsanje Mose ndi Aroni ndi kuipidwa ndi utsogoleri wawo, ndipo zimenezi zinam’chititsa kulankhula molakwa kuti, mwakufuna kwawo komanso chifukwa cha dyera, Mose ndi Aroni anali kudzikuza pa msonkhano wonsewo.—Salmo 106:16.
6 Mbali ina ya vuto la Kora mwachionekere inali yakuti sanali kuyamikira maudindo ake m’makonzedwe a Mulungu. Ndithudi, Alevi achikohati sanali ansembe, koma anali aphunzitsi a Chilamulo cha Mulungu. Analinso kunyamula zipangizo ndi zotengera za m’chihema zikafunikira kunyamulidwa. Imeneyotu sinali ntchito yamaseŵera, chifukwa chakuti zotengera zopatulika zinali kugwiridwa ndi anthu okhawo omwe anali oyera m’zachipembedzo ndi mwamakhalidwe. (Yesaya 52:11) Choncho, pamene Mose anali kudzudzula Kora, kwenikweni, anali kum’funsa kuti, Kodi ntchito yomwe wapatsidwa ukuyesa chinthu chaching’ono kotero kuti ufunanso ntchito ya ansembe? (Numeri 16:9, 10) Kora analephera kuzindikira kuti ulemerero waukulu ndiwo kutumikira Yehova mokhulupirika mogwirizana ndi makonzedwe ake—osati kukhala pamalo kapena paudindo wapamwamba.—Salmo 84:10.
7. (a) Kodi Mose anachita nawo motani Kora ndi anthu ake? (b) Kodi kupanduka kwa Kora kunathetsedwa motani?
7 Mose anaitana Kora ndi anthu ake kuti m’maŵa wotsatira adzasonkhane pa chihema chokomanako aliyense atatenga mbale yofukizamo ndi chofukiza chake. Kora ndi anthu ake analibe ulamuliro wopereka nsembe zofukiza, popeza kuti iwo sanali ansembe. Ngati akanabwera ndi mbale zofukizamo ndi zofukiza, ndithudi zimenezi zikanasonyezeratu kuti anthu ameneŵa anali kulingalirabe kuti anali ndi ufulu wochita monga ansembe—ngakhale kuti anali ndi nthaŵi yonse ya usiku yakuti akanalingalira mosamalitsa za nkhaniyo. Khamu lonse litasonkhana m’maŵa wotsatira, moyenereradi Yehova anasonyeza mkwiyo wake. Koma Arubeni, “dziko linayasama pakamwa pake ndi kuŵameza.” Ena onse, kuphatikizapo Kora, moto wochokera kwa Mulungu unaŵanyeketsa. (Deuteronomo 11:6; Numeri 16:16-35; 26:10) Kudzikuza kwa Kora kunadzetsatu manyazi osaneneka—kukanidwa ndi Mulungu!
Kanani ‘Chizoloŵezi cha Kuchita Nsanje’
8. Kodi ‘chizoloŵezi cha kuchita nsanje’ chingaonekere motani pakati pa Akristu?
8 Nkhani ya Kora ndi chenjezo kwa ife. Popeza kuti ‘chizoloŵezi cha kuchita nsanje’ chili mwa anthu opanda ungwiro, chingathe kuonekera ngakhale mu mpingo wachikristu. (Yakobo 4:5) Mwachitsanzo, tingakhale ongokhumba maudindo. Mofanana ndi Kora, tingachitire nsanje omwe ali m’maudindo omwe ife tikufunawo. Kapena tingakhale ngati Mkristu wina wa m’zaka za zana loyamba wotchedwa Diotrefe. Iye ankatsutsa kwambiri ulamuliro wa atumwi, mwachionekere chifukwa chakuti iye ankafuna ulamulirowo. Ndiye chifukwa chake, Yohane analemba kuti Diotrefe anali “wofuna kukhala wamkulu.”—3 Yohane 9.
9. (a) Kodi tiyenera kupeŵa malingaliro otani okhudza maudindo mumpingo? (b) Kodi kaonedwe koyenera ka malo athu m’makonzedwe a Mulungu n’kotani?
9 Inde, sikulakwa kwa mwamuna wachikristu kukalamira maudindo mumpingo. Paulonso analimbikitsa kuchita zimenezo. (1 Timoteo 3:1) Koma, sitiyenera kuona maudindo autumiki monga chosonyezera kuyenerera kwa kutamandidwa, kuchita ngati pamene tapatsidwa maudindo ameneŵa, ndiye kuti takwera sitepe limodzi la makwerero ena ake omwe tingati ndi makwerero a kupita patsogolo. Kumbukirani, Yesu anati: “Amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu.” (Mateyu 20:26, 27) Ndithudi, kungakhale kulakwa kuchitira nsanje awo amene ali ndi maudindo aakulu, kuchita ngati kuti kukhala kwathu ofunika kwa Mulungu kumadalira pa “malo a ulamuliro” m’gulu lake. Yesu anati: “Inu nonse muli abale.” (Mateyu 23:8) Inde, kaya ndi wofalitsa kapena mpainiya, wobatizidwa chatsopano kapena yemwe wachita mokhulupirika kwa nthaŵi yaitali—onse amene amatumikira Yehova ndi mtima wonse ali ndi malo apamwamba m’makonzedwe ake. (Luka 10:27; 12:6, 7; Agalatiya 3:28; Ahebri 6:10) Ndithudi ndi dalitso kugwira ntchito mothandizana ndi mamiliyoni a anthu omwe akuyesetsa kutsatira uphungu wa m’Baibulo wakuti: “Muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane.”—1 Petro 5:5.
Abisalomu—Wofunitsitsa Kuloŵa Ufumu
10. Kodi Abisalomu anali yani, ndipo anayesa motani kukopa anthu odzatula milandu kwa mfumu kuti am’konde?
10 Mbiri ya moyo wa mwana wamwamuna wachitatu wa Mfumu Davide, Abisalomu, imatipatsa chitsanzo chofunika kwambiri cha kufunitsitsa ulamuliro. Wofunitsitsa ufumu ameneyu anayesa kukopa mwachinyengo munthu aliyense wokhala ndi mlandu woyenera kufika kwa mfumu. Choyamba anapatsa anthuwo malingaliro olakwika akuti Davide analibe chidwi ndi zosoŵa zawo. Kenako iye analeka kuchita zinthu mwakabisira ndipo anavumbula cholinga chake chenicheni. “Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m’dzikomo,” anatchula mfundo yake motero Abisalomu, “kuti munthu yense amene ali ndi mlandu wake kapena chifukwa chake, akadafika kwa ine; ndipo ndikadam’chitira zachilungamo!” Zochita zandale zachinyengo za Abisalomuzo zinalibe malire. Baibulo limati: “Pakusendera munthu aliyense kudzam’lambira, iye anatambasula dzanja lake, nam’gwira, nam’psompsona. Abisalomu anachitira zotero Aisrayeli onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wawo.” Ndi zotsatira zotani? “Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israyeli.”—2 Samueli 15:1-6.
11. Kodi Abisalomu anayesa motani kulanda ufumu wa Davide?
2 Samueli 13:28, 29) Komabe, panthaŵiyo Abisalomu ayenera kuti anali akulingalira za mpando wachifumuwo, akumaona ngati kupha Amnoni ndiyo njira yachidule yochepetsera anthu olimbirana nawo mpandowo. * Mulimonse mmene zinalili, nthaŵi itakwana, Abisalomu anachita zofuna mtima wake. Chilengezo cha ufumu wake chinaperekedwa m’dziko lonselo.—2 Samueli 15:10.
11 Abisalomu anatsimikiza mtima kulanda ufumu wa atate ake. Zaka zisanu m’mbuyomu, anali atapha Amnoni mwana wamkulu wa Davide mwaumbanda, mwachionekere kubwezera kugwiriridwa kwa Tamara, mchemwali wake wa Abisalomu. (12. Fotokozani mmene kudzikuza kwa Abisalomu kunadzetsera manyazi.
12 Kwa kanthaŵi, Abisalomu anapeza chipambano, popeza “chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.” M’kupita kwa nthaŵi, Mfumu Davide anakakamizika kuthaŵa. (2 Samueli 15:12-17) Komabe mosakhalitsa, ufumu wa Abisalomu unafafanizika Yoabu atapha Abisalomuyo, nam’ponya m’chidzenje chachikulu, ndi kum’kwirira ndi miyala. Tangolingalirani—munthu wofunitsitsa udindo wa ufumu ameneyu atamwalira, sanaikidwe m’manda kutsatira mwambo waulemu wa maliro! * Ndithudi, kudzikuza kunadzetsera Abisalomu manyazi.—2 Samueli 18:9-17.
Pewani Kufuna Udindo Mwadyera
13. Kodi mzimu wofuna malo aulamuliro ungakule motani mumtima wa Mkristu?
13 Kukhala mfumu kwa Abisalomu ndi kugwa kwake zikutipatsa ife phunziro. Lerolino, m’dziko lopanda khalidweli, si chachilendo kumva anthu akusyasyalika oyang’anira awo, kuyesa kukondweretsa oyang’anirawo mwinamwake pofuna kungoŵakhutiritsa kapena kuti apatsidwe udindo winawake mwina kukwezedwa pantchito. Panthaŵi imodzimodziyo, anthu osyasyalikaŵa angalankhule modzitamandira kwa atumiki awo, kuti atumikiwo apitirize kuŵakonda ndi kuŵachirikiza. Ngati sitisamala, mzimu umenewo wofuna udindo ungazame m’mtima mwathu. Kwenikweni, zimenezi zinachitikira ena m’zaka za zana loyamba, zomwe zinapangitsa atumwi kuchenjeza oterowo mwamphamvu.—Agalatiya 4:17; 3 Yohane 9, 10.
14. N’chifukwa chiyani tiyenera kupeŵa mzimu wofuna malo apamwamba modzitukumula?
14 Yehova alibe malo m’gulu lake okhalamo anthu achiwembu odzikuza omwe amayesa ‘kufunafuna ulemu wawowawo.’ (Miyambo 25:27) Ndithudi, Baibulo likuchenjeza kuti: “Yehova adzadula milomo yonse yotyasika, lilime lakudzitamandira.” (Salmo 12:3) Abisalomu anali ndi milomo yotyasika. Analankhula mosyasyalika kwa anthu omwe amafuna kuti aziti iyeyu n’ngwabwino—ankachita zonsezi kuti apeze malo apamwamba aulamuliro. Mosiyana naye, ndifetu odala kuti tili mu ubale umene umatsatira uphungu wa Paulo wakuti: “Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.”—Afilipi 2:3.
Sauli—Mfumu Yosaleza Mtima
15. Kodi Sauli anasonyeza motani kudzichepetsa panthaŵi inayake?
15 Panthaŵi inayake Sauli, yemwe pambuyo pake anadzakhala mfumu ya Israyeli, anali wodzichepetsa. Mwachitsanzo, lingalirani zomwe zinachitika m’zaka za unyamata wake. Pamene mneneri wa Mulungu Samueli analankhula mom’tamandira, Sauli modzichepetsa anati: “Sindili Mbenjamini kodi, wa fuko laling’ono mwa Israyeli? Ndiponso banja lathu n’lochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mawu otere ndi ine?”—1 Samueli 9:21.
16. Kodi Sauli anasonyeza motani kusaleza mtima?
16 Koma pambuyo pake kudzichepetsa kwa Sauli kunazimiririka. Ali m’nkhondo yolimbana ndi Afilisti, anatsikira ku Giligala, komwe anafunikira kuyembekezera kufikira Samueli atabwera kudzachonderera Mulungu ndi nsembe. Samueli atalephera kufika pa nthaŵi yomwe anagwirizana, Sauli modzikuza anapereka yekha nsembe yopsereza. Atangotsiriza kumene, pomwepo Samueli anafika. “Mwachitanji?” Anafunsa Samueli. Sauli anayankha 1 Samueli 13:8-13.
nati: “Chifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana . . . potero ndinadzifulumiza, ndi kupereka nsembe yopsereza.”—17. (a) N’chifukwa chiyani pa kuona koyamba, zomwe Sauli anachita zingaoneke ngati zolondola? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anatsutsa Sauli mwamphamvu atachita mosaleza mtima?
17 Pa kuona koyamba, zomwe Sauli anachitazo zingaoneke ngati zolondola. Ndiiko komwe, anthu a Mulungu anali “m’kupsinjika” “anasauka mtima,” ndipo anali kunjenjemera chifukwa chakuti anali m’mkhalidwe wochititsa nthumanzi. (1 Samueli 13:6, 7) Kwenikweni, si kulakwa kuchita zinthu mofulumira ngati mikhalidwe ikutikakamiza kutero. * Koma kumbukirani kuti Yehova amapenda mitima ndipo amadziŵa malingaliro athu. (1 Samueli 16:7) Choncho, n’kutheka kuti iye anaona mikhalidwe ina mwa Sauli yomwe sanaitchule mwachindunji m’nkhani ya m’Baibulo. Mwachitsanzo, mwinamwake Yehova anaona kuti kudzikuza n’komwe kunasonkhezera kusaleza mtima kwa Saulo. Mwinamwake Sauli sanamve bwino mumtima kuti iye—mfumu ya Israyeli yense—anafunikira kudikira winawake amene ankamuona ngati mneneri wokalamba ndi wozengereza! Mulimonse mmene zinalili, Sauli analingalira kuti kuchedwa kwa Samueli kunam’patsa ufulu wochita zonse yekha ndi kusalabadira malangizo achimvekere omwe anali atapatsidwa. Zotsatira zake? Samueli sanavomereze kufulumiza kwa Sauliko. M’malo mwake, iye anam’weruza Sauli nati: “Ufumu wanu sudzakhala chikhalire . . . chifukwa inu simunasunga chimene Yehova anakulamulirani.” (1 Samueli 13:13, 14) Kachiŵirinso, kudzikuza kunadzetsa manyazi.
Peŵani Kusaleza Mtima
18, 19. (a) Fotokozani mmene kusaleza mtima kungachititsire mtumiki wamakono wa Mulungu kuchita modzikuza. (b) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ponena za kayendedwe ka mpingo wachikristu?
18 Nkhani ya kuchita modzikuza kwa Sauli inalembedwa m’Mawu a Mulungu kuti ife tipindule nayo. (1 Akorinto 10:11) N’chapafupi kwa ife kukwiya chifukwa cha zophophonya za abale athu. Monga Sauli, sitingathe kuugwira mtima, tikumalingalira kuti ngati tikufuna kuti zinthu ziyende bwino lomwe, ziyenera zikhale m’manja mwathu. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mbale n’ngwaluso poyendetsa zinthu zina m’gulu. Amasunga nthaŵi, n’ngwozindikira bwino njira zatsopano zoyendetsera mpingo, ndipo ali ndi mphatso ya kulankhula ndi kuphunzitsa. Panthaŵi imodzimodziyo, wazindikira kuti ena akulephera kulingana naye pa miyezo yake yapamwambayo, ndipo ntchito saigwira monga momwe iye angafunire. Kodi zimenezi zingam’patse ufulu wosonyeza kusaleza mtima? Kodi ayenera kuneneza abale akewo, mwinamwake akumawonjezera kuti chipanda khama lake palibe chomwe chikanachitika ndipo mpingowo sibwenzi ukuyenda bwino? Kumeneku kungakhaletu kudzikuza kwadzaoneni!
19 Kodi n’chiyani kwenikweni chomwe chimagwirizanitsa mpingo wachikristu? Kodi kungakhale kuyendetsa zinthu mwaluso? kugwira bwino ntchito? kapena kuzama kwa chidziŵitso? Kunena zoona, zinthu zimenezi n’zothandiza kuti mpingo uyende bwino. (1 Akorinto 14:40; Afilipi 3:16; 2 Petro 3:18) Komabe, Yesu ananena kuti mokulira om’tsatira ake adzadziŵika ndi chikondi. (Yohane 13:35) N’chifukwa chaketu akulu osamalira, pamene akulinganiza zinthu mwaluso, amazindikira kuti mpingo si bizinesi yomwe imafuna uyang’aniro woumitsa zinthu; m’malo mwake, n’ngwopangidwa ndi nkhosa zimene zimafuna kusamalidwa mwachikondi. (Yesaya 32:1, 2; 40:11) Kunyalanyaza mfundo zachikhalidwe zimenezi modzikuza kaŵirikaŵiri kumadzetsa mikangano. Koma mgwirizano waumulungu umadzetsa mtendere.—1 Akorinto 14:33; Agalatiya 6:16.
20. Kodi tidzaphunziranji m’nkhani yotsatira?
20 Nkhani za m’Baibulo za Kora, Abisalomu, ndi Sauli zikusonyeza bwino lomwe kuti kudzikuza kumadzetsa manyazi, monga momwe Miyambo 11:2 ikunenera. Komabe, vesi la m’Baibulo lomwelo likuwonjezera kuti: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.” Kodi kudzichepetsa n’chiyani? N’zitsanzo ziti za m’Baibulo zomwe zingathandize kumveketsa bwino mkhalidwe umenewu, ndipo ifeyo tingasonyeze motani kudzichepetsa lerolino? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Popeza kuti Rubeni anali mwana woyamba wa Yakobo, mbadwa zake zomwe zinagwirizana ndi Kora m’chipanduko chakecho ziyenera kuti zinali kuipidwa chifukwa chakuti Mose—mbadwa ya Levi—ndiye amene anali ndi ulamuliro wa utsogoleri pa iwo.
^ ndime 11 Kileabu, mwana wamwamuna wachiŵiri wa Davide, sakutchulidwa pena paliponse pambuyo pa kubadwa kwake. Ayenera kuti anamwalira Abisalomu asanapanduke.
^ ndime 12 Mu nthaŵi za m’Baibulo mwambo woika mtembo m’manda chinali chochitika chapadera kwambiri. Choncho, kuikidwa m’manda mosatsata mwambo umenewu linali tsoka lalikulu ndipo kaŵirikaŵiri zinali kusonyeza kukanidwa ndi Mulungu.—Yeremiya 25:32, 33.
^ ndime 17 Mwachitsanzo, Pinehasi anachita mofulumira kuletsa mliri womwe unapha Aisrayeli zikwizikwi, ndipo Davide analimbikitsa anyamata ake anjala kudya naye limodzi mkate woonekera “m’nyumba ya Mulungu”. Mulungu sanatsutse iliyonse ya njira zimenezi kuti kunali kudzikuza.—Mateyu 12:2-4; Numeri 25:7-9; 1 Samueli 21:1-6.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi kudzikuza n’chiyani?
• Kodi nsanje inam’chititsa motani Kora kuchita modzikuza?
• Kodi tikuphunziranji pa nkhani ya Abisalomu wofunitsitsa udindoyo?
• Kodi tingapeŵe motani mzimu wa kusaleza mtima womwe Sauli anasonyeza?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 10]
Sauli sanaleze mtima ndipo anachita modzikuza