Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulemekeza Ulamuliro N’chifukwa Chiyani Kukuchepa?

Kulemekeza Ulamuliro N’chifukwa Chiyani Kukuchepa?

Kulemekeza Ulamuliro N’chifukwa Chiyani Kukuchepa?

“Kuchitira mwano ulamuliro wokhazikitsidwa, wachipembedzo ndi wakudziko, woyang’anira chikhalidwe cha anthu ndi wandale, komwe kwafala padziko lonse lapansi tsiku lina kungadzaonedwe kukhala chochitika chapadera cha m’zaka khumi zapitazo.”

PAPITA zaka zambiri kuchokera m’ma 1960, zaka khumi zimene wolemba mbiri komanso wafilosofi Hannah Arendt ankafotokoza. Lerolino, kunyoza ulamuliro n’kofala kwambiri kusiyana ndi kale lonse.

Mwachitsanzo, lipoti la posachedwapa m’nyuzipepala yotchedwa The Times ya ku London linati: “Makolo ena amakana kugonjera ku ulamuliro wa aphunzitsi pa mwana wawo ndipo aphunzitsi akapereka chilango kwa mwana wawo, makolowo amadandaula.” Kaŵirikaŵiri, ana awo akamapatsidwa chilango ku sukulu, makolowo amapita ku sukulu komweko osati kukangoopseza aphunzitsiwo koma kukalimbana nawo.

Woyankhulira National Association of Head Teachers in Britain (Bungwe la Aphunzitsi Aakulu M’dziko la Britain) anagwidwa mawu akumati: “Anthu amanena kuti ‘ndili ndi ufulu,’ m’malo monena kuti ‘ndili ndi maudindo.’” Kuwonjezera pa kulephera kukhomereza malingaliro olemekeza ulamuliro m’mitima ya ana awo, makolo ena sadzudzula ana awo, ndipo amakana kuti ena awadzudzule. Ana ofuna “ufulu” wawo amanyoza ulamuliro wa makolo ndiponso wa aphunzitsi, ndipo chotsatira chake n’chodziŵikiratu, “mbadwo watsopano wosalemekeza n’komwe ulamuliro ndipo wosazindikira kwenikweni pakati pa chabwino ndi choipa,” analemba motero wolemba nkhani m’nyuzipepala ina Margarette Driscoll.

Magazini ya Time m’nkhani yake yakuti “Mbadwo Wosokonezeka” inatchula za kusokeretsedwa kwa achinyamata ambiri a ku Russia mwa kugwira mawu mkulu wina wotchuka woimba nyimbo za chamba cha rap yemwe anati: “Kodi munthu aliyense wobadwira m’dziko lino, mmene mulibe chinthu chokhalitsa ndipo mulibe chilungamo, angadalire bwanji anthu?” Katswiri wa chikhalidwe Mikhail Topalov anavomereza mawu akuti: “Achinyamata ameneŵa si kuti n’ngopanda nzeru. Aona makolo awo akunyengezedwa ndi boma, aŵaona akuluza ndalama zawo ndiponso ntchito zawo. Kodi tingawayembekezere kulemekeza olamulira?”

Komabe, kungakhale kulakwa kunena kuti achinyamata okha ndiwo amene sakhulupirira ulamuliro. Lerolino, anthu a misinkhu yonse sakhulupirira mtundu uliwonse wa ulamuliro, ndipo amaunyozanso. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe ulamuliro womwe ungakhulupiriridwe? Ulamuliro wofotokozedwa kukhala “mphamvu kapena ufulu woteteza, kuweruza, kapena kuletsa zochita za anthu ena,” ungakhale wothandiza kwambiri ngati utagwiritsidwa ntchito moyenera. Ungapindulitse munthu aliyense payekha komanso anthu onse a m’deralo. Nkhani yotsatirayi idzafotokoza mmene zimenezi zilili.