Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulemekeza Ulamuliro N’chifukwa Chiyani Kuli Kofunika?

Kulemekeza Ulamuliro N’chifukwa Chiyani Kuli Kofunika?

Kulemekeza Ulamuliro N’chifukwa Chiyani Kuli Kofunika?

KODI ndani amene sasangalala kuti apolisi ali ndi mphamvu zomanga zigaŵenga zimene zimatibera katundu kapena kuopseza mabanja athu? Nanga kodi sitiyamikira kuti makhoti ali ndi mphamvu zolanga zigaŵenga n’cholinga choteteza anthu?

Komanso tingakumbukire za ntchito zina zaboma zomwe ndi zofunika kwambiri, monga kukonzanso misewu, zaumoyo, ndi zamaphunziro, zomwe kaŵirikaŵiri zimalipiridwa ndi ndalama za misonkho yosonkhanitsidwa mwalamulo la boma. Akristu oona ndiwo ali patsogolo kuzindikira kuti kulemekeza ulamuliro woikidwa moyenerera n’kofunika. Komano kodi ulemu umenewo umafika mpaka pati? Nanga kodi ndi m’mbali ziti za moyo zomwe kulemekeza ulamuliro kuli kofunika?

Ulamuliro M’madera Omwe Tikukhala

Baibulo limauza anthu onse, okhulupirira komanso osakhulupirira, kuti azilemekeza boma, limene limachitira anthu zinthu zabwino. Mtumwi wachikristu Paulo analemba kalata kwa okhulupirira anzake ku Roma ponena za nkhani imeneyi, ndipo n’kopindulitsa kwambiri kupenda zimene ananena, zolembedwa pa Aroma 13:1-7.

Paulo anali nzika ya Roma, ndipo panthaŵi imeneyo Roma anali ulamuliro wamphamvu wa dziko lonse. Kalata ya Paulo, yolembedwa pafupifupi m’chaka cha 56 C.E., inalangiza Akristu kukhala nzika zopereka chitsanzo chabwino. Analemba kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.”

Pamenepa Paulo akufotokoza kuti kukanakhala kulibe ulamuliro uliwonse waumunthu ngati Mulungu akanapanda kuulola. Motero maulamuliro aakulu ali ndi malo ake m’chifuno cha Mulungu. Chotero “iye amene atsutsana nawo ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu.”

Pamene kuli kwakuti nzika zomwe zimachita zinthu zabwino zingayamikiridwe ndi maulamuliro aakulu, maulamuliro ameneŵa alinso ndi mphamvu zopereka chilango kwa anthu olakwa. Anthu amene amachita zoipa ali ndi chifukwa chachikulu kwambiri choopera ufulu wa boma wa “kubwezera chilango,” chifukwa chakuti maboma amachita zimenezi monga “mtumiki wa Mulungu.”

Paulo akumaliza mfundo zake mwa kunena kuti: “Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima. Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi.”

Udindo wogaŵa ndalama za misonkho uli m’manja mwa maulamuliro aakulu, osati mwa wokhoma msonkho. Pokhala nzika yokhulupirika, Mkristu amakhala ndi chikumbumtima chabwino. Amadziŵa kuti mwa kugonjera ku maulamuliro aakulu ndi kukhoma misonkho, iye samangochirikiza nawo mkhalidwe wa dera limene akukhala komanso amakhala mogwirizana ndi zofuna za Mulungu.

Banja ndi Ulamuliro

Bwanji ponena za ulamuliro m’banja? M’masiku oyambirira a moyo wake, kaŵirikaŵiri khanda limalira kapena kufuula n’cholinga choti alisamale. Koma kholo lanzeru limazindikira zimene kwenikweni khandalo likufuna ndipo silidzachita zinthu chifukwa cha kukalipa kwamwanako. Ana ena, akamakula, amapatsidwa ufulu wochita zinthu zimene akufuna ndipo amaloledwa kukhala ndi njira yawoyawo yochitira zinthu. Chifukwa chopanda chidziŵitso, iwo angayambe kuloŵerera m’zauchigaŵenga kapena zolakwa zina, ndiyeno n’kusokoneza banja ndiponso anthu ena, zomwe olamulira ochuluka amazidziŵa bwino kwambiri.

“Makolo amalanga ana mochedwa kwambiri,” anatero Rosalind Miles, mlembi wa buku lakuti Children We Deserve. “Nthaŵi yofunika kuyamba kulanga ndi pamene mwana wabadwa kumene.” Ngati kuyambira paukhanda makolo amayankhula mokoma mtima, mosonyeza ulamuliro wachikondi ndipo sasinthasintha pazochita zawo, ana awo angaphunzire mofulumira kumvera ulamuliro woterowo ndiponso chilango chake chachikondi.

Baibulo lili ndi chidziŵitso chochuluka chokhudza ulamuliro wa m’banja. M’buku la Miyambo, mwamuna wanzeruyo Solomo akufotokoza mochititsa chidwi za kugwirizana kwa makolo osonyeza kuopa Mulungu pamaso pa ana awo, mwa kunena kuti: “Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako.” (Miyambo 1:8) Makolo akamachita zinthu mogwirizana chonchi pamaso pa ana awo, anawo amadziŵa zofuna za makolo awo. Iwo angayese kuzembera kholo lina ndi kusangalatsa kholo linalo poyesayesa kuchita zofuna zawo, koma ulamuliro wa makolo ogwirizana umakhala chitetezo cha achinyamata.

Baibulo limafotokoza kuti bambo ali ndi udindo waukulu pa zinthu zauzimu osati kokha kwa ana ake komanso kwa mkazi wake. Zimenezi zafotokozedwa kukhala umutu. Kodi umutu umenewu uyenera kugwiritsidwa ntchito motani? Paulo akunena kuti monga momwe Kristu alili Mutu wa mpingo momwemonso mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake. Ndiyeno Paulo akuwonjezera kuti: “Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia [mkwatibwi wake wauzimu], nadzipereka yekha m’malo mwake.” (Aefeso 5:25) Mwamuna akatsatira chitsanzo cha Kristu ndi kugwiritsa ntchito umutu mwachikondi, iye adzalandira “ulemu waukulu” kwa mkazi wake. (Aefeso 5:33, NW) Nawonso ana a m’banja lotero adzaona kufunika kwa ulamuliro wopatsidwa ndi Mulungu ndipo adzalimbikitsidwa kuumvera.​—Aefeso 6:1-3.

Kodi makolo amene alibe mnzawo wa muukwati, kuphatikizapo makolo amene mnzawo wokwatirana naye anamwalira, angatani ndi nkhani imeneyi? Kaya ndi bambo kapena mayi, iwo angagwiritse ntchito mwachindunji ulamuliro wa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Nthaŵi zonse Yesu ankayankhula monga munthu waulamuliro, ulamuliro wa Atate wake ndiponso wa Malemba ouziridwa.​—Mateyu 4:1-10; 7:29; Yohane 5:19, 30; 8:28.

Baibulo lili ndi mfundo zachikhalidwe zochuluka zokhudza mavuto amene ana amakumana nawo. Mwa kupeza mfundo zimenezi ndi kuzitsatira, kholo lingapereke kwa ana uphungu wachikondi komanso wothandiza. (Genesis 6:22; Miyambo 13:20; Mateyu 6:33; 1 Akorinto 15:33; Afilipi 4:8, 9) Makolo angagwiritsenso ntchito nkhani zotengedwa m’Baibulo zolembedwa kuti ziwathandize mmene angaphunzitsire ana awo kudziŵa phindu lolemekeza ulamuliro wa m’Malemba. *

Mpingo Wachikristu ndi Ulamuliro

“Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.” (Mateyu 17:5) Mawu ameneŵa, oyankhulidwa ndi Yehova Mulungu mwiniyo, anavomereza Yesu kukhala munthu woyankhula mwa ulamuliro wa Mulungu. Zimene iye anayankhula zinalembedwa m’nkhani za m’Mauthenga Abwino anayi amene tikhoza kuwagwiritsa ntchito mosavuta.

Atangotsala pang’ono kukwera kumwamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Monga Mutu wa mpingo wake, Yesu samangoyang’anira odzozedwa omwe akutsatira mapazi ake pano padziko lapansi, komanso kuyambira pamene anatsanulira mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E., iye wagwiritsa ntchito odzozedwa ameneŵa ngati ngalande ya choonadi, monga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47; Machitidwe 2:1-36) Kodi iye wachitanji kuti akwaniritse zonsezi n’cholinga cholimbitsa mpingo wachikristu? “Pamene iye anakwera kumwamba . . . [a]napereka mphatso mwa amuna.” (Aefeso 4:8, NW) “Mphatso mwa amuna” zimenezi ndi akulu achikristu, amene amasankhidwa ndi mzimu woyera ndipo amapatsidwa mphamvu zosamalira zinthu zauzimu za okhulupirira anzawo.​—Machitidwe 20:28.

Chifukwa cha zimenezi, Paulo akulangiza kuti: “Kumbukirani atsogoleri anu, amene anayankhula nanu Mawu a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.” Popeza kuti amuna okhulupirika ameneŵa amatsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri, n’chanzeru kutsanzira chikhulupiriro chawo. Ndiyeno Paulo akuwonjezera kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; [“nthaŵi zonse pozindikira ulamuliro wawo wa pa inu,” The Amplified Bible] pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: Pakuti ichi sichikupindulitsani inu.”​—Ahebri 13:7, 17.

Kodi chimachitika n’chiyani pamene malangizo ngati ameneŵa anyalanyazidwa? Anthu ena a mumpingo wachikristu woyambirira anachita zimenezo ndipo anakhala ampatuko. Humenayo ndi Fileto akutchulidwa kukhala anthu amene anasanduliza chikhulupiriro cha ena ndipo amene zokamba zawo zopanda pake ‘zinadetsa choyera.’ Chimodzi mwa zonena zawo chinali chakuti chiukiriro chinachitika kale, mwachionekere chauzimu kapena chophiphiritsira, choncho kunalibe chiukiriro china m’tsogolo mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.​—2 Timoteo 2:16-18, NW.

Ulamuliro woikidwa unathandizapo. Akulu achikristu anatha kutsutsa nkhani zoterozo chifukwa chakuti monga oimira Yesu Kristu, iwo anagwiritsa ntchito ulamuliro wa Malemba. (2 Timoteo 3:16, 17) Ndi mmenenso zilili lerolino mumpingo wachikristu, umene umafotokozedwa kukhala “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Timoteo 3:15) Ziphunzitso zonyenga sizidzaloledwa ngakhale pang’ono kuti zisokoneze “chitsanzo cha mawu a moyo,” amene asungidwa m’Baibulo monga choikiziridwa chabwino kwambiri kuti tiwagwiritse ntchito.​—2 Timoteo 1:13, 14.

Pamene kuli kwakuti kulemekeza ulamuliro kukucheperachepera m’dziko lino, ife monga Akristu timazindikira kuti ulamuliro woyenera wa m’madera omwe tikukhala, m’banja, ndi mumpingo wachikristu unakhazikitsidwa kuti utipindulitse. Kulemekeza ulamuliro n’kofunika chifukwa cha thanzi lathu lakuthupi, la m’maganizo, ndi lauzimu. Mwa kugonjera ndi kulemekeza ulamuliro woikidwa ndi Mulungu woterowo, tidzatetezedwa ndi olamulira akuluakulu kwambiri, Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, kwa ubwino wathu wamuyaya.​—Salmo 119:165; Ahebri 12:9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Onani mabuku akuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza ndi Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Baibulo lili ndi chidziŵitso chochuluka chokhudza ulamuliro wa m’banja

[Chithunzi patsamba 6]

Makolo amene alibe mnzawo wa muukwati angagwiritse ntchito mwachindunji ulamuliro wa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu

[Zithunzi patsamba 7]

Akristu amazindikira kuti maulamuliro oyenera a m’banja, mumpingo wachikristu, ndi m’madera omwe akukhala anakhazikitsidwa kuti awapindulitse

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Chithunzi chojambulidwa ndi Josh Mathes, Collection of the Supreme Court of the United States