Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusiya Ntchito Yopanga Zida Kuyamba Ntchito Yopulumutsa Miyoyo

Kusiya Ntchito Yopanga Zida Kuyamba Ntchito Yopulumutsa Miyoyo

Mbiri ya Moyo Wanga

Kusiya Ntchito Yopanga Zida Kuyamba Ntchito Yopulumutsa Miyoyo

YOSIMBIDWA NDI ISIDOROS ISMAILIDIS

Ndinali n’tagwada misozi ikutsikira m’masaya mwanga. “Chonde, Mulungu, chikumbumtima changa chikundiuza kuti sindingapitirize kugwira ntchito yopanga zida,” ndinatero m’pemphero. “Ndayesetsa kuti ndipeze ntchito ina, koma ndalephera. Maŵa ndikukapereka kalata yanga yosiyira ntchito. Chonde, Yehova, musalole ana athu anayi kuti afe ndi njala.” Kodi ndinafika bwanji pamfundo imeneyi?

MOYO unali wamtendere ndi wosavuta ku Drama, kumpoto kwa Greece, komwe ndinabadwira m’chaka cha 1932. Atate wanga ankakonda kundiuza zomwe iwo ankafuna kuti ndichite. Ankandilimbikitsa kupita ku United States kukaphunzira. Greece atasakazidwa m’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, mawu ofala kwambiri kwa Agiriki anali akuti: “Mukhoza kutibera katundu, koma simungabe zinthu zomwe zili m’maganizo mwathu.” Ndinali wotsimikiza kuchita maphunziro apamwamba ndi kupeza kanthu kenakake kamene munthu aliyense sangadzathe kuba.

Kuyambira ndili mwana, ndinaloŵa m’magulu osiyanasiyana a achinyamata amene ankachirikizidwa ndi Tchalitchi cha Greek Orthodox. M’magulu amenewo ankatiuza kuti tizipeŵa magulu oopsa ampatuko. Ndikukumbukira bwino kwambiri gulu limodzi, la Mboni za Yehova, likutchulidwa chifukwa chakuti iwo ankalingaliridwa kuti anali okana Kristu.

M’chaka cha 1953 nditamaliza maphunziro anga pa sukulu yophunzitsa maluso a manja mu Athens, ndinapita ku Germany kukaona ngati ndikanatha kupeza ntchito komanso kupita ku sukulu panthaŵi imodzimodziyo. Koma zimenezo sizinaphule kanthu, choncho ndinapita kumayiko ena. Pambuyo pa milungu yoŵerengeka, ndinafika padoko lina m’dziko la Belgium ndilibiretu ndalama. Ndikukumbukira kuti ndinaloŵa m’tchalitchi, n’kukhala pansi, n’kulira mwamphamvu moti pomwe ndinayang’anapo panagwera misozi. Ndinapemphera kuti ngati Mulungu atandithandiza kuti ndipite ku United States, sindingapite kukafuna chuma chakuthupi koma kukaphunzira ndiponso kuyesetsa kukhala Mkristu wabwino komanso nzika yabwino. Ndiyeno m’chaka cha 1957, ndinafika ku United States.

Moyo Watsopano M’dziko la United States

Moyo m’dziko la United States unali wovuta kwa mlendo wosadziŵa chinenero ndiponso woti alibe ndalama. Ndinkagwira ntchito ziŵiri usiku ndipo ndimayesetsa kupita kusukulu masana. Ndinaphunzira pa makoleji angapo ndi kupeza digiri ya m’makoleji aang’onoang’ono. Kenako ndinapita ku Yunivesite ya California ku Los Angeles ndi kupeza digiri yoyambirira ya sayansi ya physics. Mawu a atate wanga onena zakuti ndiphunzire anandipangitsa kuti ndizingopitirizabe kuphunzira m’zaka zovutazi.

Panthaŵiyi, ndinapalana ubwenzi ndi Ekaterini, mtsikana wokongola wachigiriki, ndipo tinakwatirana mu 1964. Mwana wathu woyamba wamwamuna anabadwa zaka zitatu pambuyo pake, ndipo m’zaka zosachepera zinayi, tinakhala ndi ana ena aamuna aŵiri ndiponso mwana wamkazi. Kunali kovuta kwambiri kusamalira banja ndiponso panthaŵi yomweyo kumakaphunzira pa yunivesite.

Ndinkagwira ntchito ku U.S. Air Force pa kampani yopanga mamisaelo ndi zinthu zakuthambo mu mzinda wa Sunnyvale, ku California. Ndinali wotanganidwa ndi ntchito zosiyanasiyana za m’mlengalenga ndi zakuthambo, ndiponso kupanga loketi ya Agena ndi zombo zopita kuthambo za Apollo. Ndinalandiranso mendulo chifukwa chochirikiza nawo maulendo a Apollo 8 ndi Apollo 11. Pambuyo pochita zimenezo, ndinapitiriza maphunziro anga ndipo ndinakhala wotanganidwa kwambiri ndi ntchito zosiyanasiyana za zida za nkhondo za m’mlengalenga. Pamenepo, ndinaganiza kuti ndafikapo​—mkazi wokongola, ana abwino anayi, ntchito yapamwamba, ndi nyumba yabwino.

Mnzanga Wakhama

Kumayambiriro kwa chaka cha 1967, kumalo komwe ndinkagwira ntchito, ndinadziŵana ndi Jim, munthu wodzichepetsa kwambiri ndiponso wokoma mtima. Nthaŵi zonse nkhope ya Jim inali yosangalala, ndipo sankakana ndikamuitana kuti tikacheze panthaŵi yopuma. Ankagwiritsa ntchito mipata imeneyi kukambirana nane za chidziŵitso cha m’Baibulo. Jim anandiuza kuti iye ankaphunzira ndi Mboni za Yehova.

Ndinamva chisoni kumva kuti Jim analoŵa m’gulu lachipembedzo limeneli. Zinatheka bwanji kuti munthu wabwino chotereyu asocheretsedwe ndi gulu lachipembedzo lokana Kristu? Komabe, chidwi chake kwa ine komanso mmene ankachitira nane zinthu mokoma mtima zinali kundikopa. Zinkaoneka kuti tsiku lililonse iye anali ndi kanthu kena kachilendo kuti ndiŵerenge. Mwachitsanzo, tsiku lina anabwera kuofesi yanga n’kunena kuti: “Isidoros, nkhani ya mu Nsanja ya Olonda iyi ikunena za kulimbitsa moyo wabanja. Pita nayo kunyumba, ndipo ukaiŵerenge pamodzi ndi mkazi wako.” Ndinamuuza kuti ndiŵerenga kopelo, koma pambuyo pake ndinapita kuchimbudzi n’kung’amba magaziniyo m’timapepala ting’onoting’ono ndi kutiponyera m’bini.

Kwa zaka zitatu, ndinakhala ndikung’amba buku lililonse ndiponso magazini alionse amene Jim ankandipatsa. Chifukwa chokhala ndi malingaliro oipa ponena za Mboni za Yehova, komanso kwinaku ndikuyesetsa kuti Jim akhalebe bwenzi langa, ndinaganiza kuti n’kwabwino kumumvera zomwe amafuna kunena ndipo kenako n’kuzifafaniza mwamsangamsanga.

Komabe ngakhale zinali choncho, chifukwa cha kukambirana kumeneko, ndinadziŵa kuti zambiri mwa zinthu zimene ndinkakhulupirira ndiponso kuchita zinali zopanda maziko a m’Baibulo. Ndinazindikira kuti ziphunzitso za Utatu, moto wa helo, ndi chiphunzitso chakuti moyo sumafa sizinali za m’Malemba. (Mlaliki 9:10; Ezekieli 18:4; Yohane 20:17) Monga munthu wonyadira Greek Orthodox, sindinafune kuvomereza poyera kuti Jim anali wolondola. Koma chifukwa chakuti ankagwiritsa ntchito Baibulo nthaŵi zonse ndipo sanali kungofotokoza malingaliro ake, potsirizira pake ndinazindikira kuti iye anali ndi uthenga wochokera m’Baibulo wofunika kwambiri kwa ine.

Mkazi wanga anazindikira kuti panali kuchitika kanthu kenakake, ndipo anandifunsa ngati ndinali nditayankhulana ndi mnzanga amene anali wa Mboni. Nditamuyankha kuti inde, iye anati: “Tiyeni tipite ku tchalitchi china chilichonse, koma osati kwa Mboni za Yehova.” Komabe, posakhalitsa ine ndi mkazi wanga, pamodzi ndi ana athu, tinkafika mokhazikika pa misokhano ya Mboni.

Chosankha Chovuta

Pamene ndimaphunzira Baibulo, ndinaŵerenga mawu aŵa a mneneri Yesaya akuti: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi mtumiki wa Mulungu wokonda mtendereyo angagwire bwanji ntchito yolemba mapulani komanso kupanga zida zowononga?’ (Salmo 46:9) Sizinanditengere nthaŵi yaitali kuti nditsimikizire zosintha ntchito.

Kunena zoona, zinali zothetsa nzeru kwambiri. Ndinali pantchito yolemekezeka kwambiri. Ndinavutika kwa zaka zambiri ndi ntchito zolimba, maphunziro, ndiponso kudzipereka kuti ndifike pamalo ameneŵa. Ndinali nditafika pa mpando wapamwamba pantchito, koma tsopano ndinafunikira kusiya ntchitoyo. Komabe, chikondi changa chachikulu pa Yehova ndi kufunitsitsa kuchita chifuniro chake zinapambana.​—Mateyu 7:21.

Ndinaganiza zogwira ntchito pa kampani ina mu mzinda wa Seattle, ku Washington. Komabe, posapita nthaŵi yaitali ndinakhumudwa nditaona kuti ndinali wokhudzidwanso kwambiri ndi ntchito imene sigwirizana ndi Yesaya 2:4. Zoyesayesa zanga zoti ndizigwira ntchito za mtundu wina zinalephereka, ndipo chikumbumtima changa chinandivutitsanso. Ndinadziŵa bwino lomwe kuti sindingapitirize kugwira ntchitoyo ndipo panthaŵi imodzimodziyo n’kukhala ndi chikumbumtima chokoma.​—1 Petro 3:21.

Zinali zoonekeratu kuti patsogolo pake tinali kudzapanga kusintha kwakukulu kwambiri. M’miyezi isanu ndi umodzi, tinasintha moyo wathu ndi kuchepetsa ndi theka ndalama zomwe tinkawononga. Kenako tinagulitsa nyumba yathu yabwino kwambiri komanso yapamwamba ndi kugula ina yaing’ono mu mzinda wa Denver ku Colorado. Tsopano ndinali wokonzeka kusankha chochita chotsiriza, chomwe chinali kusiya ntchito. Ndinalemba pa taipi kalata yanga yosiyira ntchito, ndi kufotokoza za chikumbumtima changa. Usiku umenewo, ana atagona, ndinagwada pansi pamodzi ndi mkazi wanga ndipo tinapemphera kwa Yehova, monga momwe ndafotokozera kumayambiriro kwa nkhani ino.

Mwezi umodzi usanathe, tinasamukira ku Denver, ndipo milungu iŵiri pambuyo pake, mu July 1975, ine ndi mkazi wanga tinabatizidwa. Sindinathe kupeza ntchito kwa miyezi isanu ndi umodzi, ndipo tinkawononga pang’onopang’ono ndalama zomwe tinasunga. M’mwezi wachisanu ndi chiŵiri, ndalama zathu zomwe zinatsala ku banki zinali zosakwanira malipiro a pamwezi a chikole chogulira nyumbayo. Ndinayamba kufunafuna ntchito ya mtundu uliwonse yomwe ndikanatha kupeza, koma mwamsanga pambuyo pake ndinapeza ntchito yauinjiniya. Malipiro ake anali pafupifupi theka basi la ndalama zomwe ndinkalandira m’mbuyomo; komabe, zinali zambiri kwabasi kusiyana ndi zomwe ndinapempha kwa Yehova. Ndinali wosangalalatu kwambiri chifukwa choika zinthu zauzimu pamalo oyamba!​—Mateyu 6:33.

Kulera Ana Athu Kuti Azikonda Yehova

Panthaŵi imodzimodziyo ine ndi Ekaterini tinali otanganidwa kwambiri ndi ntchito yovuta kwabasi yolera ana athu anayi mogwirizana ndi mfundo zachikhalidwe za Mulungu. N’chosangalatsa kuti, taŵaona ana onse, mothandizidwa ndi Yehova, akukhala Akristu okhwima m’nzeru, ndi kupereka miyoyo yawo kotheratu ku ntchito yofunika yolalikira Ufumu. Ana athu aamuna onse atatu, Christos, Lakes, ndi Gregory anamaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndipo tsopano akutumikira m’ntchito zosiyanasiyana, kuchezera ndi kulimbitsa mipingo. Toula, mwana wathu wamkazi, akutumikira monga wantchito wodzifunira pa likulu la Mboni za Yehova ku New York. Tinakhudzidwa mitima kwambiri pamene timawaona onsewo akusiya ntchito zawo zabwino kwambiri komanso za malipiro ochuluka n’cholinga chofuna kutumikira Yehova.

Ambiri akhala akutifunsa za chinsinsi cha kulera ana mwachipambano koteroko. Ndi zoona kuti palibe njira imodzi yeniyeni yolerera ana, koma tinayesetsa kukhomereza m’mitima yawo kukonda Yehova ndi anansi. (Deuteronomo 6:6, 7; Mateyu 22:37-39) Anawo anaphunzira kuti sitingauze Yehova kuti timam’konda pokhapokha ngati zochita zathu zikusonyeza kuti timam’konda.

Tsiku limodzi pamlungu, makamaka Loŵeruka, tinkaloŵa mu utumiki monga banja. Nthaŵi zonse tinkachita phunziro la Baibulo labanja Lolemba madzulo pambuyo pa chakudya komanso tinkachita phunziro la Baibulo ndi mwana aliyense payekha. Nthaŵi yomwe anawo anali ang’onoang’ono, tinkaphunzira ndi mwana aliyense kwanthaŵi yochepa maulendo angapo pa mlungu, ndipo pamene ankakula, timakhala ndi maphunziro otalikirapo kamodzi pa mlungu. Panthaŵi ya maphunziroŵa, ana athu anatseguka nzeru ndipo ankakambirana nafe momasuka za mavuto awo.

Komanso monga banja tinkakhala ndi nthaŵi zosangalala zomwe zinali zolimbikitsa. Tonsefe tinkakonda kuimba zida zoimbira nyimbo tikakhala pamodzi, ndipo mwana aliyense ankakonda kuimba nyimbo yomwe amaikonda kwambiri. Nthaŵi zina kumapeto a sabata tinkaitana mabanja ena kuti tidzalimbikitsane nawo pocheza. Komanso tinkakhala ndi maulendo a tchuthi pamodzi monga banja. Paulendo wina woterowo, tinatha milungu iŵiri tikuona mapiri a ku Colorado ndiponso tikugwira ntchito ya mu utumiki wakumunda ndi mipingo ya m’deralo. Ana athu amakumbukira bwino pamene anagwira ntchito nawo m’madipatimenti osiyanasiyana pa misonkhano yachigawo ndi kuthandiza pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’malo osiyanasiyana. Pamene tinapita ndi anawo ku Greece kuti akaone achibale awo, iwo anathanso kukumana ndi Mboni zambiri zokhulupirika zimene zinaponyedwapo m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Zimenezi zinawalimbikitsa kwambiri, ndi kuwathandiza kusankha kukhalabe okhazikika ndi olimba mtima pachoonadi.

Inde, nthaŵi zina ena mwa anawo ankapulupudza kapena kusankha mabwenzi olakwika. Nthaŵi zina, inkawasoŵetsa mtendere mwinamwake mwa kukhwimitsa kwambiri zinthu zina. Koma kutsatira “kuwongolera maganizo kwa Yehova,” monga momwe timaŵerengera m’Baibulo, kunathandiza kutikonzera zinthu tonsefe.​—Aefeso 6:4, NW; 2 Timoteo 3:16, 17.

Nthaŵi Yosangalatsa Kwambiri M’moyo Wanga

Ana athu atayamba utumiki wa nthaŵi zonse, ine ndi Ekaterini tinayamba kuganizaganiza mozama za chimene tingachite kuti tikulitse gawo lathu m’ntchito yopulumutsa miyoyo imeneyi. Choncho, mu 1994, nditapuma mofulumira pantchito, tonse aŵirife tinayamba kutumikira monga apainiya okhazikika. Utumiki wathu umaphatikiza kuchezera makoleji ndi mayunivesite a m’dera lomwe tikukhala, komwe timalalikira kwa ophunzira ndi kuchita maphunziro a Baibulo ndi ena mwa iwo. Chifukwa chakuti ndimamvetsa mavuto awo popeza kuti nanenso ndinali ndi mavuto ofananawo zaka zochepa zapitazo, ndakhala wopambana kwambiri pamene ndikuwathandiza kuphunzira za Yehova. Zakhala zosangalatsa kwambiri kuphunzira ndi ana a sukulu ochokera ku Bolivia, Brazil, Chile, China, Egypt, Ethiopia, Mexico, Thailand, ndi Turkey! Ndimachitanso ulaliki wapatelefoni, makamaka kwa anthu amene amayankhula chinenero chakwathu ku Greece.

Ngakhale kuti ndili ndi zopinga zambiri chifukwa cha lilime langa lachigiriki komanso ukalamba, ndakhala ndikuyesetsa kudzipereka ndi kukhala ndi mzimu ngati wa Yesaya, yemwe ananena kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Tasangalala kuthandiza anthu oposera asanu ndi mmodzi kupatulira miyoyo yawo kwa Yehova. Imeneyi ndi nthaŵi yomwe yakhala yosangalatsa kwambiri kwa ife.

Nthaŵi inayake, moyo wanga unakhudzidwa kwambiri ndi kupanga zida zoopsa kwambiri zophera anthu anzanga. Koma Yehova mwa ukoma mtima wake wochuluka, ananditsekulira njira komanso banja langa kuti tikhale atumiki odzipatulira ndi kupereka miyoyo yathu kufikitsa kwa anthu uthenga wabwino wa moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso. Ndikamalingalira zosankha zovuta kwambiri zomwe ndinayenera kuchita, mawu a pa Malaki 3:10 amandibwerera m’maganizo: “Mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoŵeka malo akuulandira.” Iye watichitiradi zomwezo, mogwirizana ndi kufuna kwathu!

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 27]

Lakes: Atate wanga ankadana ndi chinyengo. Iwo ankayesetsa kuti asachite zachinyengo, makamaka pokhazikitsa chitsanzo chabwino kwa banja lawo. Ankatiuza kaŵirikaŵiri kuti: “Chidzakhala chinthu chapadera ngati mutapatulira miyoyo yanu kwa Yehova. Muyenera kukhala ofunitsitsa kupereka nsembe kwa Yehova. Ndilo tanthauzo la kukhala Mkristu.” Mawu ameneŵa anakhazikika mu mtima mwanga ndipo anandipangitsa kutsatira chitsanzo chawo popereka nsembe kwa Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 27]

Christos: Ndimayamikira kwambiri kukhulupirika ndi mtima wonse kwa makolo anga kwa Yehova komanso kudzipereka kwawo ndi mtima wonse ku udindo wawo monga makolo. Monga banja, tinkachita chilichonse pamodzi, kuyambira mu utumiki wathu mpaka masiku athu a tchuthi. Ngakhale kuti akanatha kukhala ndi zinthu zina zochuluka, makolo anga anali ndi moyo wosafuna zinthu zochuluka ndipo anaika mtima pa utumiki. Lerolino, ndimadziŵa kuti ndimakhala wosangalala kwambiri chifukwa chokhala wotanganidwa mu utumiki wa Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 28]

Gregory: Ndinalimbikitsidwa kwambiri ndi chitsanzo cha makolo anga komanso umboni wa chisangalalo chawo mu utumiki wa Yehova kusiyana ndi mmene ndinalimbikitsidwira ndi mawu awo a kukulitsa utumiki wanga. Zimenezi zinandisonkhezera kwambiri kupendanso mikhalidwe yanga, kutaya nkhaŵa zilizonse zokhudza kuyamba utumiki wa nthaŵi zonse, ndiponso kudzipereka kwambiri pa ntchito ya Yehova. Ndimathokoza makolo anga chifukwa chondithandiza kupeza chimwemwe chomwe chimadza chifukwa cha kudzipereka kwanga.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 28]

Toula: Nthaŵi zonse makolo anga ankagogomeza kuti unansi wathu ndi Yehova ndiwo mphatso yamtengo wapatali kwambiri yomwe tingakhale nayo ndiponso kuti njira yomwe tingakhalire ndi chisangalalo chenicheni ndiyo kupatsa Yehova zonse zomwe tingathe basi. Anapanga Yehova kukhala weniweni kwa ife. Atate wanga kaŵirikaŵiri ankatiuza kuti pali chimwemwe choposa chomwe chimadza chifukwa cha kugona ndi chikumbumtima choyera, podziŵa kuti wayesetsa kuchita zomwe ungathe kuti ukondweretse mtima wa Yehova.

[Chithunzi patsamba 25]

Nthaŵi yomwe ndinali msilikali ku Greece, 1951

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili pamodzi ndi Ekaterini mu 1966

[Chithunzi patsamba 26]

Banja langa mu 1996: (kuchokera kulamanzere kupita kulamanja, kumbuyo) Gregory, Christos, Toula; (kutsogolo) Lakes, Ekaterini, ndi ine