Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, yesani kuyankha mafunso otsatirawa:

N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti kukwaniritsidwa kwa ulosi wonena za “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano” wopezeka pa Yesaya 65:17-19 sunali kukhudza kubwerera kwa Ayuda kuchokera kuukapolo kokha?

N’chifukwa chakuti mtumwi Petro ndi mtumwi Yohane, analemba za nkhaniyi m’zaka za zana loyamba, mosonyeza kukwaniritsidwa kwa m’tsogolo komwe kudzabweretsanso madalitso omwe adakali m’tsogolo. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1-4)​—4/15, masamba 10-12.

Kodi n’chiyani chimene mwina chinkachirikiza nthanthi zamakedzana za Agiriki zonena za anthu achiwawa amphamvu ngati milungu?

Mwina kunali kukometsa ndiponso kupotoza mfundo yakuti Chigumula chisanadze angelo ena anavala matupi aumunthu ndipo anakhala moyo wa chiwawa, ndiponso makhalidwe achiwerewere padziko lapansi. (Genesis 6: 1,  2)​—4/15, tsamba 27.

Kodi ndi ngozi zina zotani zimene Akristu okhwima angapeŵe paukwati?

N’kofunika kupewa phwando la chiphokoso. Zotere zingachitike ngati anthu akumwa moŵa mwachisawawa ndiponso ngati pali kuvina kwadzaoneni nyimbo zokweza kwambiri. Anthu amene sanaitanidwe sayenera kupita kuphwando la ukwati, pokhapokha ngati analengeza poyera kuti aliyense atha kupitako. Mkwati ayenera kuonetsetsa kuti Akristu odalirika adzakhalapo mpaka chikondwererocho chitatha nthaŵi yabwino.​—5/1, masamba 19-22.

Kodi mawu a pa Salmo 128:3 onena za ana, “onga timitengo ta azitona” pagome lodyera la munthu amasonyeza lingaliro lotani?

Nthaŵi zambiri mtengo wa azitona umaphukira mphukira zatsopano m’tsinde mwake. Pamene mtengo wokalambawo sukubalanso zipatso zambiri, mphukira zatsopanozo zingakule kukhala mitengo yamphamvu yozungulira mtengo wokalambawo. Mofananamo, makolo angasangalale kukhala ndi ana obala zipatso otumikira Yehova pamodzi nawo.​—5/15, tsamba 27.

Kodi ndi mapindu ena otani amene ana amapeza m’banja la makhalidwe abwino?

Chimakhala chiyambi chawo cha kuona ulamuliro m’njira yoyenera, kuyamikira ubwino wamakhalidwe oyenera, ndiponso unansi wabwino ndi anthu ena. Mkhalidwe ngati umenewu ungawathandizenso kukulitsa unansi wawo ndi Mulungu.​—6/1, tsamba 18.

Kodi m’dziko lina ku Far East anachita zotani kuti alimbikitse kufunika kwa mfundo yakuti Akristu onse ndi abale?

Mipingo yonse inalangizidwa kuti asamaitane abale ena mayina aulemu. M’malomwake, onse aziwaitana mofanana monga abale.​—6/15, masamba 21, 22.

Kodi Mboni za Yehova zimalandira mankhwala opangidwa kuchokera ku magazi?

Timakhulupirira kuti lamulo la Baibulo la ‘kusala mwazi’ limaletsa kuikidwa mwazi wathunthu kapena zinthu zikuluzikulu zimene zili m’mwazimo (plasma, maselo ofiira, maselo oyera, ndi tizidutswa ta m’magazi). (Machitidwe 15:28, 29) Koma pa za tizigawo totengedwa m’zinthu zimenezi, Mkristu aliyense amadzisankhira yekha chochita, pokumbukira zimene Baibulo limanena ndiponso unansi wake ndi Mulungu.​—6/15, tsamba 29-31.

Kodi n’zothekadi kupeza mtendere wa mumtima lerolino?

Inde. Kupyolera m’Baibulo, Yesu Kristu akutsogolera anthu ku njira yakulambira koyera ndiponso ku mtendere wofotokozedwa pa Yesaya 32:18. Komanso, anthu amene akupeza mtendere umenewu ali ndi chiyembekezo chodzasangalala ndi mtendere wosatha pano padziko lapansi mokwaniritsa Salmo 37:11, 29.​—7/1, tsamba 7.

Kodi ndi ntchito yotani imene George Young anali nayo m’mbiri yamakono yateokalase?

Kuyambira m’chaka cha 1917, iye anali akunyamula kuunika kwa uthenga wabwino wa Ufumu m’mayiko ambiri. Utumiki wake unam’yendetsa ku Canada konse, ku zilumba za ku Caribbean, ku Brazil ndi kumayiko ena a ku South America, ku Central America, ku Spain, ku Portugal, komwe kale ankakutcha kuti Soviet Union, ndiponso ku United States.​—7/1, tsamba 22-7.

Kodi 1 Akorinto 15:29 amatanthauzanji akamanena za anthu ena kuti “abatizidwa [kuti akhale] akufa” NW?

Mfundo n’njakuti pamene Akristu adzozedwa ndi mzimu woyera, amaloŵetsedwa m’njira yamoyo imene imawatsogolera ku imfa, ndipo nthaŵi yomweyo amaukitsidwira kumoyo wakumwamba.​—7/15, tsamba 17.

Kodi mtumwi Paulo ankachita chiyani panthaŵi imene yatchedwa kuti zaka zake zosatchulidwa?

N’kutheka kuti iye ankathandiza kukhazikitsa kapena kulimbikitsa mipingo ya ku Suriya ndi ku Kilikiya. Mavuto ambiri otchulidwa pa 2 Akorinto 11:23-27 ayenera kuti anachitika m’nthaŵi imeneyi, kusonyeza kuti anali kuchita utumiki wakhama.​—7/15, masamba 26, 27.

Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tisamayembekezere zinthu mopambanitsa?

Kumbukirani kuti Yehova amamvetsa zinthu. Kupemphera kwa iye kungatithandize kulinganiza malingaliro athu ndipo zimenezi zimasonyeza kudzichepetsa. Thandizo lina ndilo kupeza malingaliro atsopano mwa kulankhulana ndi mnzathu wokhwima maganizo.​—8/1, masamba 29, 30.