Kodi Mumatani Pakakhala Kusamvana?
Kodi Mumatani Pakakhala Kusamvana?
TSIKU lililonse timakhala ndi anthu osiyanasiyana. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimatipatsa chimwemwe ndi kutiphunzitsa zinthu zatsopano. Nthaŵi zina, zimayambitsanso kusamvana kwambiri kapena pang’ono pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Kaya kusamvanako kukhale kotani, zimene timachita zimatikhudza maganizo, mtima, komanso mwauzimu.
Tikamachita zomwe tingathe pofuna kuthetsa kusamvana bwinobwino, timakhala ndi moyo wabwinopo komanso timakhala pamtendere wochuluka ndi anthu ena. Mwambi wakale umati: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi.”—Miyambo 14:30.
Mosiyana kwambiri ndi zimenezo pali mawu oona aŵa: “Wosalamulira mtima wake akunga mudzi wopasuka wopanda linga.” (Miyambo 25:28) Ndani wa ife amene angakonde kudzilekerera ndi kulola malingaliro olakwika amene angatipangitse kuchita zosayenera—zimene zingavulaze ena ndi ife tomwe? Popanda kudziletsa, kuyankha mwaukali kungachite zomwezo. Pa Ulaliki wa pa Phiri, Yesu analimbikitsa kuti tizisanthula maganizo athu, amene angasonkhezere mmene timachitira tikakhala kuti sitinamvane ndi anzathu. (Mateyu 7:3-5) M’malo mwa kusuliza ena, tiyenera kuganiza za mmene tingakulitsire ndi kusunga unansi ndi aja amene timasiyana nawo malingaliro ndi mmene tinakulira.
Maganizo Athu
Njira yoyamba pothetsa kusamvana kumene tingokuganizira kapena kumene kulipodi n’kuzindikira kuti timakhala ndi maganizo olakwika. Malemba amatikumbutsa kuti tonse timachimwa ‘n’kupereŵera pa ulemerero wa Mulungu.’ (Aroma 3:23) Ndiponso, kuzindikira kungavumbule kuti amene wayambitsa vuto lathu si munthu winayo. Mogwirizana ndi zimenezo, tiyeni tikambirane zimene zinam’chitikira Yona.
Atalangizidwa ndi Yehova, Yona anapita ku mudzi wa Nineve kukalalikira kwa anthu za kuyandikira kwa chiweruzo cha Mulungu. Chosangalatsa chinali chakuti mudzi wonse wa Nineve unalapa n’kukhulupirira Mulungu woona. (Yona 3:5-10) Yehova anaona kuti pokhala ndi mtima wolapa anthuwo anayenera kukhululukidwa, choncho sanawawononge. “Koma sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima.” (Yona 4:1) Zinali zodabwitsa mmene Yona anachitira pa chifundo cha Yehova. N’chifukwa chiyani Yona anapsera Yehova mtima? Mwachionekere, Yona anavutika mtima kwambiri, poganiza kuti anthu amuona bwanji. Sanamvetse chifundo cha Yehova. Mokoma mtima, Yehova anapereka phunziro kwa Yona mwa chochitika chimene chinam’thandiza kusintha maganizo ake ndi kuona kukula kwa chifundo cha Mulungu. (Yona 4:7-11) N’zoonekeratu kuti Yona, osati Yehova, ndiye anafunika kusintha maganizo ake.
Aroma 12:10) Kodi ankatanthauzanji? Mfundo yake n’njakuti akutilimbikitsa kukhala ololera komanso kuwalemekeza kwambiri Akristu anzathu. Zimenezi zikuphatikizapo kuzindikira kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha zimene akufuna. Paulo akutikumbutsanso kuti: “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5) Ndiye chifukwa chake, kusamvana kusanafike potidanitsa, kungakhale kwanzeru bwanji kuona ngati tifunikira kusintha maganizo athu! Tiyenera kuyesetsa kukhala ndi maganizo a Yehova ndi kusunga mtendere ndi ena amene amakondadi Mulungu.—Yesaya 55:8, 9.
Kodi ifenso nthaŵi zina tingafunike kusintha maganizo athu pa nkhani inayake? Mtumwi Paulo akutilangiza kuti: ‘Mutsogolere pa kuchitira wina mnzake ulemu.’ (Kachitidwe Kathu
Tiyerekeze kuti ana aang’ono aŵiri akulimbirana kachidole, aliyense akukoka mwamphamvu kwambiri kuti atenge iye. Angamalankhulane mwaukali polimbanapo kufikira mmodzi ataleka kapena munthu wina wake ataloŵerera.
Nkhani ya m’buku la Genesis imatiuza kuti Abrahamu anamva kuti panali patabuka mkangano pakati pa abusa ake ndi abusa a Loti, mwana wa mbale wake. Abrahamu ndiye amene anayamba kufikira Loti n’kunena kuti: “Tisachite ndewu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale.” Abrahamu anatsimikiza mtima kuti salola mkangano uliwonse uwononge ubale wawo. Anachita zimenezo ali wokonzeka kutani? Anali wokonzeka kudzimana mwayi wake woyamba kusankha monga munthu wamkulu; anakonzekera kupereka chinachake. Abrahamu analola Loti kusankha malo amene anakonda kupitako ndi mbumba yake ndi ziweto zake. Kenaka Loti anadzisankhira malo obiriŵira ndi msipu a Sodomu ndi Gomora. Abrahamu ndi Loti anasiyana mwamtendere.—Genesis 13:5-12.
Kuti tikhale pa mtendere ndi ena, kodi tili okonzeka kuchita zinthu ndi mzimu umene Abrahamu anali nawo? Nkhani ya m’Baibulo imeneyi imatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri choti titsanzire pofuna kuthetsa kusamvana. Abrahamu anachonderera kuti: “Tisachite ndewu.” Abrahamu anafunitsitsa kuthetsa nkhaniyo mwabata. Zoonadi pempho ngati limeneli lofuna kusungitsa mtendere lingathandize kukankhira pambali kusamvana kulikonse. Ndiyeno Abrahamu anamaliza ndi mawu oti “chifukwa kuti ife ndife abale.” N’kuwonongeranji ubale wamtengo wapatali ngati umenewo chifukwa cha zokonda zake kapena kunyada? Abrahamu anayang’ana kwambiri pa zinthu zimene zinali zofunika. Anachita zimenezo podzilemekeza, panthaŵi imodzimodziyo kulemekeza mwana wa mbale wake.
Pamene kuli kwakuti zimabuka nkhani zoti mwina ena aloŵererepo kuti athetse kusamvana, kumakhala bwino kwambiri ngati nkhaniyo itathetsedwa mwachinsinsi! Yesu akutilimbikitsa kuyamba ifeyo kukhazikitsa mtendere ndi mbale wathu, kupepesa ngati kuli kofunika kutero. * (Mateyu 5:23, 24) Padzafunika kudzichepetsa, kapena kufatsa. N’chifukwa chake Petro analemba kuti: “Muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Petro 5:5) Mmene timachitira ndi olambira anzathu zimakhudza mwachindunji unansi wathu ndi Mulungu.—1 Yohane 4:20.
Mumpingo wachikristu, tingafunikire kudzimana zinthu zotiyenera pofuna kusungitsa mtendere. M’kati mwa zaka zisanu zapitazi anthu ochuluka ndithu amene tsopano akusonkhana
ndi Mboni za Yehova abwera m’banja la Mulungu la olambira oona. Zimenezi zimabweretsa chimwemwe m’mitima yathu kwambiri! Kunena zoona, zochita zathu zimawakhudza iwowa ndiponso zimakhudza ena mumpingo. Ndiye chifukwa chake tiyenera kusamala kwambiri posankha zosangalatsa, zochita za pamtima, maseŵera, kapena ntchito, tikumaganizira mmene ena angationere. Kodi zochita zathu zilizonse kapena mawu athu angamvedwe molakwika kenako kukhumudwitsa ena?Mtumwi Paulo akutikumbutsa kuti: “Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse. Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.” (1 Akorinto 10:23, 24) Monga Akristu, chimene timafuna kwambiri ndicho kulimbitsa chikondi ndi umodzi wa ubale wathu wachikristu.—Salmo 133:1; Yohane 13:34, 35.
Mawu Olamitsa
Mawu angakhale ndi mphamvu yopindulitsa. “Mawu okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.” (Miyambo 16:24) Nkhani ya Gideoni yonena za mmene anapeŵera nkhondo ndi Aefraimu imachitira chitsanzo zoona za mwambiwu.
Ali m’kati mwa nkhondo yolimbana ndi a Midyani, Gideoni anaitana fuko la Efraimu kuti lithandize. Komabe, nkhondoyo itatha, Efraimu anatembenukira Gideoni n’kumudandaulira mwaukali kuti sanawaitane pachiyambi pa nkhondoyo. Nkhaniyo imati ‘anatsutsana naye kolimba.’ Poyankha, Gideoni anati: “Ndachitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efraimu sikuposa kutchera mphesa kwa Abiezeri? Mulungu anapereka m’dzanja lanu akalonga a Midyani, Orebi ndi Zeebi, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu?” (Oweruza 8:1-3) Ndi mawu ake osankhidwa bwino komanso odekha, Gideoni anapeŵa nkhondo yachiweniweni imene ikanakhala yowononga kwambiri. Mwina vuto la fuko la Efraimu lingakhale lakuti ankadziona kukhala ofunika kwambiri komanso kunyada. Komabe, zimenezo sizinam’letse Gideoni kuyesetsa kuti abwezeretse mtendere. Kodi tingachite chimodzimodzi?
Ena mtima wawo ungadzaze mkwiyo ndipo angatide. Zindikirani mmene mtima wawo umakhudzidwira, ndipo yesetsani kumvetsa malingaliro awo. Kodi mwa njira ina tingakhale titawachititsa ifeyo kumva mmene akumveramo? Ngati zili choncho, bwanji osavomereza zimene tachita kuti vutolo likhalepo ndi kusonyeza chisoni chathu powonjezera vutolo. Mawu ochepa olingaliridwa bwino angabwezeretse unansi umene wasokonekerawo. (Yakobo 3:4) Ena amene ali okwiya angangofuna kuti mokoma mtima tikhazikitse mtima wawo pansi. Baibulo limanena kuti “posoŵa nkhuni moto ungozima.” (Miyambo 26:20) Inde, mawu osankhidwa bwinobwino n’kunenedwa ndi mzimu woyenera ‘angabweze mkwiyo’ n’kukhaladi ochiritsa.—Miyambo 15:1.
Mtumwi Paulo akulimbikitsa kuti: “Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” (Aroma 12:18) N’zoona kuti sitingathe kuwongolera mmene ena akumvera mumtima, koma tingachite mbali yathu kukhazikitsa mtendere. M’malo moumirira maganizo athu opanda ungwiro kapena a ena, tingathe tsopano kutsatira mfundo zabwino za m’Baibulo zachikhalidwe. Kuthetsa kusamvana mwa njira imene Yehova amatilangizira kudzatipatsa mtendere wosatha ndi chimwemwe.—Yesaya 48:17.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Onani nkhani zakuti “Khululukani Kuchokera Mumtima” ndiponso “Mungabweze Mbale Wanu,” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1999.
[Chithunzi patsamba 24]
Kodi timaumirira zinthu mmene tikufunira ifeyo?
[Chithunzi patsamba 25]
Abrahamu anakhazikitsa chitsanzo chabwino cha kukhala wololera pofuna kuthetsa kusamvana