Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mliri wa Chidani

Mliri wa Chidani

Mliri wa Chidani

“Anthu samvetsa za anthu amene amawada.”​—JAMES RUSSELL LOWELL, WOLEMBA NKHANI NDI WOYANJANITSA.

CHIDANI chikuoneka kuti chatizinga tonse lerolino. Mayina ngati East Timor, Kosovo, Liberia, Littleton, ndi Sarajevo, komanso Anazi amakono, wometa mpala, ndi wokweza fuko la azungu, asindikizidwa m’maganizo mwathu pamodzi ndi zithunzithunzi za mabwinja otenthedwa ndi moto, manda oponyamo anthu ambiri okumbidwa posachedwapa, ndiponso mitembo.

Zolingalira zonse za m’tsogolo mwabwino mopanda chidani, mkangano ndi chiwawa zathetsedweratu. Danielle Mitterand mkazi wa malemu pulezidenti wa ku France anakumbukira nthaŵi ya utsikana wake kuti: “Anthu ankaganiza zokhala mwaufulu ndi mwaubale pakati pa anthu amene angawakhulupirire; akumakhala ndi maganizo osatekeseka pakati pa anthu ena; ankalingalira zokhala ndi moyo wathanzi, wamtendere ndi wolemekezeka pakati pa anthu amphamvu ndi owoloŵa manja amene amawasamalira.” Kodi chinachitika n’chiyani ku malingaliro amenewo? Anadandaula kuti: “Patangopita zaka makumi asanu zokha, zolingalira zathu zikulephera kuchitika.”

Kubukanso kwatsopano kwa chidani sikungangonyalanyazidwa. Ndi chofala kwambiri, ndipo mowonjezereka chikuchita kuonekeratu poyera. Malingaliro okhala otetezeka amene anthu miyandamiyanda amangotenga kuti ndi mmene zimakhalira kwa munthu aliyense athetsedwa ndi zochita zopanda nzeru za chidani, chilichonse chooneka choopsa kuposa choyambirira. Ngakhale kuti sitikudedwa kunyumba kwathu kapena m’dziko lathu, zikutiyembekezera penapake. Mosakayikira timaona umboni wake tsiku lililonse m’nkhani ndi zochitika zaposachedwapa zoulutsidwa pa wailesi yakanema. Zina mwa izo zafalikira ngakhale pa Intaneti. Talingalirani zitsanzo zoŵerengeka chabe.

Zaka khumi zapitazi pakhala kukwera kosayerekezeka kwa kusankhana mitundu. “Utundu,” anafotokoza motero Joseph S. Nye, Jr. mkulu wa bungwe la Harvard Center for International Affairs, “ukukula mwamphamvu m’mbali zambiri za dziko lapansili, osati kufooka. Mmalo mokhala mudzi umodzi wa dziko lonse pali midzi yambiri kuzungulira dziko lonse lapansi yomwe ndi yodziŵana kwambiri. Zimenezo pambuyo pake zimapereka mpata womakangana.”

Mitundu ina ya chidani ndi yosazindikirika, yobisika m’mayiko ena kapena ngakhale m’midzi yoyandikana nayo. Pamene ometa mpala asanu anapha Sikh, nkhalamba ya ku Canada, chochitika chimenecho “chinafotokoza zimene ena amaona ngati kubukanso kwa upandu wochitika chifukwa cha chidani m’dziko lomwe nthaŵi zambiri limalemekezedwa chifukwa cha kulolerana kwa mafuko.” Ku Germany, patakhala kutsika m’zaka zapitazo, kuukira anthu a mafuko ena ndi anthu atsankho opambanitsa kunakwera ndi 27 peresenti mu 1997. “Ndi zinthu zochititsa ulesi,” inatero Nduna Yoona za M’dziko a Manfred Kanther.

Kumpoto kwa dziko la Albania lipoti lina linasonyeza kuti ana opitirira 6,000 ali pafupifupi akaidi m’nyumba zawo zomwe chifukwa choopa kuomberedwa ndi adani a mabanja awo. Ana ameneŵa akuvutika chifukwa cha kudana kwa mafuko awo, “kumene kwasokoneza miyoyo ya mabanja zikwi zambiri.” Ku United States, malinga ndi kunena kwa bungwe lazofufuzafufuza la Federal Bureau of Investigation (FBI), “kusankhana mafuko kunasonkhezera kupitirira theka la maupandu okwana 7,755 ochitidwa chifukwa cha chidani mu 1998 amene anachitidwa lipoti ku FBI.” Zina zosonkhezera maupandu otsalawo zinali tsankhu la chipembedzo, mtundu kapena fuko lake la munthu, ndi kulemala.

Kuwonjezera apo, mitu yankhani m’manyuzipepala tsiku lililonse imanena za mliri wa kuopa alendo, umene kwenikweni umanena za othaŵa kwawo, anthu amene tsopano akupitirira 21 miliyoni. N’zomvetsa chisoni kuti ambiri amene amasonyeza chidani kwa alendo ndi achinyamata, amene amasonkhezeredwa ndi atsogoleri andale osatha ntchito yawo ndi enanso ofuna pobisalirapo. Zizindikiro zina zosadziŵika msanga za mliriwu zimaphatikizapo kusakhulupirirana, kusalolera, ndi kuona molakwa anthu osiyana nawo.

Kodi ndi zifukwa zina ziti zomwe zapangitsa mliri wachidani umenewu? Nanga pakufunika kuchitanji kuti tithetse chidani? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Pachikuto, pamwamba: UN PHOTO 186705/​J. Isaac

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Daud/​Sipa Press