Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Amakamba za Ubwino ndi Chikondi’

‘Amakamba za Ubwino ndi Chikondi’

‘Amakamba za Ubwino ndi Chikondi’

M’ZAKA za posachedwapa, Mboni za Yehova ku France zasinjiriridwa kwambiri. Otsutsawo anena nkhani zabodza pofuna kuti anthu aziona Mbonizo molakwika. Kumayambiriro a 1999, Mboni za Yehova m’dziko lonse la France zinagaŵira mathirakiti 12 miliyoni a mutu wakuti People of France, You Are Being Deceived! (Anthu a mu France, Mukunyengedwa) M’thirakiti limeneli, analembamo zotsutsa manenanena oipitsa dzina lawo amene amaneneredwa.

Patapita masiku ochepa okha ndawalayo itatha, a Jean Bonhomme, amene ndi dokotala, komanso anali phungu wa Nyumba ya Malamulo, anatumiza kalata kwa okonza nyuzipepala yakumeneko yoti ikaŵerengedwe ndi anthu onse. Iwo analemba kuti: “Nthaŵi zambiri, Mboni za Yehova zimabwera ku nyumba kwanga. Zimabwera kudzakamba nane za ubwino ndi chikondi cha padziko lonse. . . . Sizimachita kundiumiriza kuti zibwere. Zimalankhula maganizo awo modekha n’kumvetsera mokoma mtima zimene ndimakayikira.”

Ponena za mmene Mboni za Yehova zimaonera zinthu zauzimu, a Bonhomme ananena kuti: “Kwa iwo, kusakhala ndi nzeru pa zinthu za dziko n’kosavulaza m’pang’ono pomwe. Komano, kwa andale ena, kusakhala ndi nzeru pa zinthu za dziko kungasokoneze kwambiri mtendere wa anthu ndi umodzi wa dziko.”