Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anafupidwa Atafufuza kwa Nthaŵi Yaitali

Anafupidwa Atafufuza kwa Nthaŵi Yaitali

Anafupidwa Atafufuza kwa Nthaŵi Yaitali

“YEHOVA? Yehova ndani?” Silvia wa zaka zisanu ndi zitatu anali ataona dzinalo m’Baibulo la Chialameniya, limene linali chuma cha banja lina. Anam’sonyeza ndi mtsikana wina wamng’ono. Anafunsafunsa, koma panalibe aliyense m’Yerevan, ku Armenia kumene anali kukhala amene akanatha kumuuza kuti Yehova ndani​—makolo ake, aphunzitsi ake, ngakhale abusa a tchalitchi chakwawoko sanamuuze.

Silvia anakula, kumaliza sukulu, n’kupeza ntchito, koma sanadziŵebe kuti Yehova ndani. Monga wachikulirepo, anathaŵa ku Armenia, ndipo patapita nthaŵi anafika ku Poland, kumene amakhala m’kachipinda kakang’ono ndi othaŵa ena. Mmodzi mwa amene anali kukhala nawo m’chipindamo anali kulandira alendo nthaŵi zambiri. “Kodi alendo akoŵa ndani?” Silvia anafunsa. “Ndi Mboni za Yehova, zimene zimandiphunzitsa Baibulo,” anayankha motero.

Mtima wa Silvia unagunda ndi chimwemwe pamene anamva dzina lakuti Yehova. Tsopano, anayamba kuphunzira kuti Yehova ndani ndiponso mmene alili Mulungu wa chikondi. Komabe, posakhalitsa, anakakamizika kuthaŵanso ku Poland. Anawoloka nyanja ya Baltic kuthaŵira ku Denmark, kufunafuna chitetezo. Ananyamula katundu wochepa. Koma pakati pa katunduyo panalinso mabuku ophunzirira Baibulo ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Patsamba lomaliza la buku lina, Silvia anapezapo mpambo wa maadiresi a maofesi a nthambi a Watch Tower Society. Ameneyu anali wina wa katundu wake wofunika kwambiri​—njira yokha yogwirizanirana ndi Yehova!

Ku Denmark, Silvia anatengeredwa ku kampu ya anthu othaŵa kwawo, ndipo nthaŵi yomweyo anayamba kufufuza kumene kunali Mboni za Yehova. Chifukwa cha mpambo wake uja wa maadiresi anadziŵa kuti ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society m’Denmark inali m’tauni ya Holbæk. Koma kodi kunali kuti kumeneko? Silvia anasamutsidwa kupita ku kampu ina pasitima ya pamtunda, ndipo ali paulendo wopita kumeneko, sitimayo inadzera ku Holbækiko! Kachiŵirinso, mtima wake unagunda ndi chimwemwe.

Pasanapite nthaŵi tsiku lina kuli dzuŵa, Silvia anakwera sitima kubwerera ku Holbæk ndipo anayenda kuchoka pasiteshoni kupita ku ofesi ya nthambi. Akukumbukira kuti: “Nditaloŵa m’kati ndi kuona malowo, ndinakhala pa benchi n’kulankhula ndekha kuti, ‘Malo ano ndi paradaiso!’” Anam’landira bwino kwambiri panthambipo ndipo pomaliza pake anatha kukhala ndi phunziro lakelake la Baibulo.

Koma anasamutsidwa kambirimbiri. Kumalo osiyanasiyana othaŵirakowo, Silvia ankafunafuna Mboni za Yehova n’kuyambiranso phunziro lake la Baibulo. Komabe, patapita zaka ziŵiri, anali ataphunzira zambiri kuti apatulire moyo wake kwa Yehova. Anabatizidwa ndipo posapita nthaŵi anayamba utumiki wa nthaŵi zonse. Mu 1998 boma la Denmark linam’patsa chilolezo chokhala komweko.

Silvia ali ndi zaka 26 tsopano ndipo akutumikira pamalo amene anamukumbutsa za paradaiso, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Denmark. “Ndinganenenji?” akutero tsopano. “Ndakhala ndikufunafuna Yehova kuyambira ndidakali mtsikana wamng’ono. Tsopano ndam’peza. Ndinkaganiza zom’tumikira moyo wanga wonse, ndipo n’zimene ndikuchita kumene pa Beteli. Ndikupemphera kuti pamalo pano padzakhale kwathu kwa zaka zikudzazo!”