Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Choloŵa Chathu Chamtengo Wapatali—Kodi Chimatanthauzanji kwa Inu?

Choloŵa Chathu Chamtengo Wapatali—Kodi Chimatanthauzanji kwa Inu?

Choloŵa Chathu Chamtengo Wapatali​—Kodi Chimatanthauzanji kwa Inu?

“Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.”​—MATEYU 25:34.

1. Kodi ndi zinthu zotani zimene anthu alandira monga choloŵa?

ANTHU onse ali ndi zinthu zimene anazipeza monga choloŵa. Kwa ena choloŵacho chimaphatikizapo moyo wa mwanaalirenji. Kwa ena uli moyo waumphaŵi. Nthaŵi zina, chifukwa cha zimene zinaichitikira kapena zimene inamva, mibadwo yakale inapatsira ana awo kudana kwambiri ndi fuko linalake. Komabe, tonsefe tili ndi chinthu chimodzi chofanana. Tonse tinalandira kuchokera kwa munthu woyambayo, Adamu, choloŵa cha uchimo. Choloŵa chimenecho chimatichititsa kufa pamapeto pake.​—Mlaliki 9:2,10; Aroma 5:12.

2, 3. Kodi ndi choloŵa chotani chimene Yehova poyambirirapo anafuna kuti ana a Adamu ndi Hava adzapatsidwe, ndipo n’chifukwa chiyani iwo sanachilandire?

2 Yehova, monga Atate wachikondi wakumwamba, pachiyambipo anapatsa anthu choloŵa chosiyana kwambiri ndi zimenezi, moyo wosatha wangwiro m’Paradaiso. Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, anapatsidwa chiyambi changwiro, chopanda tchimo. Yehova Mulungu anapereka pulaneti la Dziko Lapansi kwa anthu monga mphatso. (Salmo 115:16) Anaikamo munda wa Edene monga chitsanzo cha mmene dziko lonse lidzakhalira ndipo makolo athu oyambawo anaŵapatsa ntchito yabwino ndi yochititsa kaso. Iwo anafunika kubala ana, kusamalira dziko lapansi limodzi ndi zomera zake komanso nyama zake zosiyanasiyana, ndi kufutukula malire a Paradaiso kuzungulira dziko lonse. (Genesis 1:28; 2:8, 9, 15) Ana awo akanachita nawo zimenezi. Chinalitu choloŵa chabwino kwambiri chowapatsa!

3 Komabe, ngati iwo akanati asangalale ndi zonsezi, Adamu ndi Hava ndi ana awo anafunika kukhala ndi unansi wabwino ndi Mulungu. Anafunika kubwezera chikondi kwa Yehova ndi kumumvera, koma Adamu ndi Hava analephera kuyamikira zimene Mulungu anawapatsa ndipo sanamvere lamulo lake. Sanathe kukhalabe m’mudzi wawo wa Paradaiso ndiponso anataya ziyembekezo zaulemerero zimene Mulungu anawapatsa. Choncho, iwo sanathe kupatsira ana awo zimenezi.​—Genesis 2:16, 17; 3:1-24.

4. Kodi choloŵa chimene Adamu anachitaya tingachipeze motani?

4 Mwachifundo, Yehova anapanga makonzedwe akuti ana a Adamu ndi Hava adzakhale ndi mwayi wolandira choloŵa chimene Adamu anataya. Motani? Panthaŵi yoikika ya Mulungu, Mwana wake, Yesu Kristu, anapereka moyo wake wangwiro waumunthu m’malo mwa ana a Adamu. Mwanjirayi Kristu anaŵagula onse. Komabe, choloŵacho sichingofikira pokhala chawo. Afunika kukhala ovomerezeka ndi Mulungu, zimene zingatheke mwa kukhulupirira nsembe ya Yesu yotetezera machimo ndi kumaonetsa chikhulupiriro chimenecho mwa kukhala omvera. (Yohane 3:16, 36; 1 Timoteo 2:5, 6; Ahebri 2:9; 5:9) Kodi moyo wanu ukusonyeza kuti mumayamikira makonzedwe amenewo?

Choloŵa Chopatsiridwa Kupyolera mwa Abrahamu

5. Kodi Abrahamu anasonyeza motani kuyamikira unansi wake ndi Yehova?

5 Pamene anali kuchita chifuno chake kaamba ka dziko lapansi, Yehova anachita zinthu mwapadera ndi Abrahamu. Analangiza munthu wokhulupirika ameneyo kuti achoke ku dziko lakwawo ndi kupita ku dziko limene Mulunguyo akamusonyeza. Mofunitsitsa Abrahamu anamvera. Abrahamu atafika ku dzikolo, Yehova anati ana a Abrahamu, osati Abrahamuyo, ndiwo akalandira dzikolo monga choloŵa. (Genesis 12:1, 2, 7) Kodi Abrahamu anachitanji? Anali wofunitsitsa kutumikira Yehova kulikonse ndiponso m’njira iliyonse imene Mulungu anamulangiza kotero kuti ana ake akalandire choloŵa chawocho. Abrahamu anatumikira Yehova m’dziko lachilendo kwa zaka 100, kufikira imfa yake. (Genesis 12:4; 25:8-10) Kodi inu mukanachita zimenezo? Yehova ananena kuti Abrahamu anali “bwenzi” lake.​—Yesaya 41:8.

6. (a) Kodi Abrahamu anachitira chitsanzo chiyani mwa kufunitsitsa kwake kupereka nsembe mwana wake? (b) Kodi ndi choloŵa chamtengo wapatali chotani chimene Abrahamu akanasiyira ana ake?

6 Abrahamu anadikira kwanthaŵi yaitali kuti akhale ndi mwana, Isake, amene anali kumukonda kwambiri. Pamene mnyamatayo mwachionekere anakula kufika pokhala mnyamata wamkulu zedi, Yehova analangiza Abrahamu kuti atenge mnyamatayo ndi kukamupereka nsembe. Abrahamu sanadziŵe kuti anali pafupi kuchitira chitsanzo zimene Mulungu mwiniyo adzachita popereka Mwana wake kukhala dipo; komatu, iye anamvera ndipo anali pafupi kupereka Isake nsembe pamene mngelo wa Yehova anamuletsa. (Genesis 22:9-14) Yehova anali atanena kale kuti malonjezo ake kwa Abrahamu adzakwaniritsidwa mwa Isake. Motero, n’zachionekere kuti Abrahamu anali ndi chikhulupiriro kuti Mulungu akaukitsa Isake kuchoka kwa akufa, ngati kutakhala kofunika, ngakhale kuti chinthu chotero chinali chisanachitikepo n’kale lonse. (Genesis 17:15-18; Ahebri 11:17-19) Chifukwa chakuti Abrahamu sanakanize ngakhale mwana wake, Yehova anati: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:15-18) Izi zinasonyeza kuti Mbewu yotchulidwa pa Genesis 3:15, wolanditsa waumesiya, akabwera kudzera mu mzera wa Abrahamu. Choloŵatu chamtengo wapatali zedi chosiyira ana!

7. Kodi Abrahamu, Isake, ndi Yakobo anasonyeza motani kuyamikira choloŵa chawo?

7 Abrahamu sanazindikire tanthauzo la zimene Yehova anali kuchita panthaŵiyo; ngakhalenso mwana wake Isake kapena mdzukulu wake Yakobo, amene anakhala “oloŵa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwe,” nawo sanazindikire. Koma onse anali ndi chidaliro mwa Yehova. Sanadziphatike ku mudzi wa ufumu uliwonsewo m’dzikolo chifukwa anali kuyembekeza wabwino kwambiri, “mudzi wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.” (Ahebri 11:8-10, 13-16) Komatu, si ana onse a Abrahamu amene anayamikira kuti choloŵa chimene chinapezeka kupyolera mwa Abrahamu chinali chamtengo wapatali kwambiri.

Ena Amene Ananyoza Choloŵacho

8. Kodi Esau anasonyeza motani kuti sanayamikire kuti choloŵa chake chinali chamtengo wapatali kwambiri?

8 Esau, mwana wamkulu wa Isake, sanalemekeze ukulu wake monga woyamba kubadwa. Sanayamikire zinthu zopatulika. Motero tsiku lina pamene Esau anali ndi njala, iye anagulitsa kuyenera kwake monga woyamba kubadwa kwa mbale wake, Yakobo. Anagulitsa ndi chiyani? Anasinthitsa ndi mtanda umodzi wa mkate ndi mphodza zophika! (Genesis 25:29-34; Ahebri 12:14-17) Mtundu mwa umene malonjezo a Mulungu kwa Abrahamu akakwaniritsidwira unachokera mwa Yakobo, amene Mulungu anasintha dzina lake kukhala Israyeli. Kodi ndi mwayi wotani umene choloŵa chimenecho chinawatsegulira?

9. Chifukwa cha choloŵa chawo chauzimu, kodi n’chilanditso chotani chimene ana a Yakobo, kapena kuti Israyeli, anakhala nacho?

9 Panthaŵi ya njala, Yakobo ndi banja lake anasamukira ku Aigupto. Kumeneko anachulukana nakhala ambirimbiri, koma anasandukanso akapolo. Komabe, Yehova sanaiŵale pangano lake ndi Abrahamu. Panthaŵi yoikika ya Mulungu, analanditsa ana a Israyeli ku ukapolo nawadziŵitsa kuti akawapititsa “m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi,” dziko limene analonjeza kwa Abrahamu.​—Eksodo 3:7, 8; Genesis 15:18-21.

10. Pa phiri la Sinai, kodi ndi zochitika zina zapadera ziti zimene zinachitika mogwirizana ndi choloŵa cha ana a Israyeli?

10 Pamene ana a Israyeli anali paulendo wopita ku Dziko Lolonjezedwa, Yehova anawasonkhanitsa pa phiri la Sinai. Pamenepo anati kwa iwo: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.” (Eksodo 19:5, 6) Anthuwo atavomereza zimenezi modzifunira ndi mogwirizana onse pamodzi, Yehova anawapatsa Chilamulo chake, chinthu chimene sanachichitepo kwa anthu ena alionse.​—Salmo 147:19, 20.

11. Kodi ndi zinthu zina ziti zamtengo wapatali zimene zinaphatikizidwa mu choloŵa chauzimu cha ana a Israyeli?

11 Chinalitu choloŵa chauzimu chabwino kwambiri chimene mtundu watsopanowo unali nacho! Anali kulambira Mulungu yekhayo woona. Iye anali atawalanditsa ku Aigupto ndipo anadzionera okha zinthu zochititsa mantha zimene zinachitika pamene Chilamulo chinali kuperekedwa pa phiri la Sinai. Choloŵa chawo chinawonjezeka pamene analandira “mawu a Mulungu” owonjezereka kupyolera mwa aneneri. (Aroma 3:1, 2) Anasankhidwa ndi Yehova kuti akhale mboni zake. (Yesaya 43:10-12) Mbewu yaumesiya inali kudzaonekera mu mtundu wawo. Chilamulo chinanena za iye, chikanamuzindikiritsa, ndipo chinafunika kuwathandiza kuzindikira kuti anali kufunikira Mesiyayo. (Agalatiya 3:19, 24) Ndiponso, iwo akapatsidwa mwayi wotumikira monga ufumu wa ansembe ndi mtundu wopatulika limodzi ndi Mbewu yaumesiya.​—Aroma 9:4, 5.

12. Ngakhale kuti analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa, kodi n’chiyani chimene Aisrayeli analephera kukhala nacho? Chifukwa chiyani?

12 Mogwirizanadi ndi lonjezo lake, Yehova anatsogolera Aisrayeli kupita ku Dziko Lolonjezedwa. Koma monga momwe mtumwi Paulo kenako anadzalongosolera, chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro, dziko limenelo silinakhaledi “malo a mpumulo.” Monga gulu, sanaloŵe mu “mpumulo wa Mulungu” chifukwa analephera kuzindikira ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuno cha tsiku lopuma la Mulungu mwiniyo, limene linayamba Adamu ndi Hava atalengedwa.​—Ahebri 4:3-10, NW.

13. Chifukwa cholephera kuyamikira choloŵa chawo chauzimu, kodi Israyeli monga mtundu anataya chiyani?

13 Israyeli wakuthupi akanatha kupereka chiŵerengero chonse cha anthu amene adzagwirizana ndi Mesiya mu Ufumu wake wakumwamba monga ufumu wa ansembe ndi mtundu wopatulika. Koma iwo sanayamikire choloŵa chawo chamtengo wapatalicho. Anali Aisrayeli akuthupi ochepa chabe amene anavomereza Mesiya pamene anabwera. Motero Aisrayeli ochepa okha ndiwo anaphatikizidwa mu ufumu wa ansembe woloseredwawo. Ufumuwo unachotsedwa kwa Israyeli wakuthupi ‘nupatsidwa kwa anthu [“mtundu,” NW] akupatsa zipatso zake.’ (Mateyu 21:43) Kodi mtundu umenewo ndi uti?

Choloŵa cha Kumwamba

14, 15. (a) Yesu atafa, kodi mitundu inayamba kudzidalitsa motani mwa “mbewu” ya Abrahamu? (b) Kodi n’chiyani chimene a “Israyeli wa Mulungu” amalandira monga choloŵa?

14 Mtundu umene unapatsidwa Ufumuwo ndi “Israyeli wa Mulungu,” Israyeli wauzimu, wopangidwa ndi otsatira Yesu Kristu obadwa ndi mzimu okwana 144,000. (Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-3) Ena mwa 144,000 amenewo anali Ayuda akuthupi, koma ambiri anali ochokera m’mitundu ya Akunja. Mwa njira imeneyo lonjezo la Yehova kwa Abrahamu, lakuti kupyolera mwa “mbewu” yake mitundu yonse idzadalitsidwa, linayamba kukwaniritsidwa. (Machitidwe 3:25, 26; Agalatiya 3:8, 9) M’kukwaniritsidwa koyamba kumeneko, anthu a mwa amitundu anali kudzozedwa ndi mzimu woyera ndi kutengedwa ndi Yehova Mulungu kukhala ana auzimu, abale ake a Yesu Kristu. Choncho iwonso anakhala mbali yachiŵiri ya “mbewu” imeneyo.​—Agalatiya 3:28, 29.

15 Asanafe, Yesu anayambitsa pangano latsopano kwa Ayuda oyembekezera kudzakhala mu mtundu watsopano umenewo, pangano limene likatsimikizidwa ndi mwazi wake. Pamaziko a chikhulupiriro chawo mu nsembe yotsimikizira imeneyo, awo amene akutengedwa kukhala mu pangano limenelo akapangidwa kukhala “angwiro chikhalire.” (Ahebri 10:14-18) ‘Akayesedwa olungama’ ndi kukhululukidwa machimo awo. (1 Akorinto 6:11) Motero, m’lingaliro limenelo ali monga mmene Adamu analili asanachimwe. Komabe, ameneŵa sakakhala m’paradaiso wapadziko lapansi. Yesu ananena kuti anali kukawakonzera malo kumwamba. (Yohane 14:2, 3) Amasiya ziyembekezo zawo za padziko lapansi kuti akhale ndi ‘choloŵa chosungikira iwo m’Mwamba.’ (1 Petro 1:4) Kodi amachitanji kumeneko? Yesu analongosola kuti: “Ine ndikuikirani ufumu.”​—Luka 22:29.

16. Ndi gawo losangalatsa lotani la utumiki limene likudikira Akristu odzozedwa?

16 Kuchokera kumwamba, awo amene adzalamulira pamodzi ndi Kristu, mwa zina, adzathandiza kuchotsa padziko lapansi zizindikiro zonse za kupandukira ulamuliro wa Yehova. (Chivumbulutso 2:26, 27) Monga mbali yachiŵiri ya mbewu yauzimu ya Abrahamu, adzatenga nawo mbali pobweretsa madalitso a moyo wangwiro kwa anthu a mitundu yonse. (Aroma 8:17-21) Alitu ndi choloŵa chamtengo wapatali zedi!​—Aefeso 1:16-18.

17. Kodi ndi mbali ziti za choloŵa chawo zimene Akristu odzozedwa amasangalala nazo pamene ali padziko lapansi?

17 Komatu si kuti choloŵa chonse cha otsatira Yesu odzozedwa chili m’tsogolo. M’njira imene palibe wina akanatha kutero, Yesu anawathandiza kudziŵa Yehova, Mulungu woona yekha. (Mateyu 11:27; Yohane 17:3, 26) Mwa mawu ndi zochita zake, anawaphunzitsa chimene ‘kutama Yehova’ kumatanthauza ndiponso chimene kumvera Yehova kumaphatikizapo. (Ahebri 2:13; 5:7-9) Yesu anawaikizira chidziŵitso cha choonadi cha chifuno cha Mulungu ndipo anawatsimikizira kuti mzimu woyera ukawatsogolera kuti achimvetsetse kwambiri. (Yohane 14:24-26) Anakhomereza m’maganizo mwawo ndi m’mitima mwawo kufunika kwa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 6:10, 33) Yesu anaikizanso mwa iwo ntchito ya kuchitira umboni ndi kupanga ophunzira mwa anthu a ku Yerusalemu, Yudeya, Samariya, ndi kumalekezero ake a dziko lapansi.​—Mateyu 24:14; 28:19, 20; Machitidwe 1:8.

Choloŵa Chamtengo Wapatali cha Khamu Lalikulu

18. Kodi lonjezo la Yehova lakuti mitundu yonse idzadalitsidwa kupyolera mwa “mbewu” ya Abrahamu likukwaniritsidwa motani lerolino?

18 Mwachionekere, onse a Israyeli wauzimu, “kagulu ka nkhosa” kameneko ka oloŵa Ufumu, asankhidwa kale. (Luka 12:32) Kwa zaka zambirimbiri tsopano, Yehova waika chisamaliro pa kusonkhanitsidwa kwa khamu lalikulu la anthu enanso ochokera m’mitundu yonse. Motero, lonjezo la Yehova kwa Abrahamu lakuti kupyolera mwa “mbewu” yake mitundu yonse ikadalitsidwa likukwaniritsidwa mokulira. N’zosangalatsa kuti anthu odalitsika ameneŵa nawonso amachita utumiki wopatulika kwa Yehova ndipo amazindikira kuti chipulumutso chawo chimadalira pa kukhulupirira Mwanawankhosa wa Mulungu, Yesu Kristu. (Chivumbulutso 7:9, 10) Kodi mwavomera chiitano chokoma mtima cha Yehova chakuti mukhale m’gulu lachimwemwe limenelo?

19. Kodi anthu amitundu amene akudalitsidwa tsopano akuyembekeza choloŵa chotani?

19 Kodi ndi choloŵa chamtengo wapatali chiti chimene Yehova akupatsa awo amene si a kagulu kankhosa? Eya, si choloŵa cha kumwamba. Ndi choloŵa chimene Adamu akanapatsira ana ake, chiyembekezo cha moyo wosatha wangwiro m’paradaiso amene pang’ono ndi pang’ono adzakuta dziko lonse. Lidzakhala dziko mmene ‘simudzakhalanso imfa; ndipo simudzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.’ (Chivumbulutso 21:4) Motero, Mawu ouziridwa a Mulungu aŵa amauza inuyo kuti: “Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m’dziko, ndipo tsata choonadi. Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako. Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:3, 4, 10, 11, 29.

20. Kodi ndi motani mmene “nkhosa zina” zimakhalira ndi mbali yochuluka ya choloŵa chauzimu cha Akristu odzozedwa?

20 “Nkhosa zina” za Yesu zili ndi choloŵa m’mabwalo apadziko lapansi a Ufumu wakumwamba. (Yohane 10:16a) Ngakhale kuti sadzakhala kumwamba, mbali yochuluka ya choloŵa chauzimu chimene odzozedwa ali nacho chikupatsidwa kwa iwo. Ndi kupyolera mwa gulu lonse la odzozedwa, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kuti nkhosa zina zathandizidwa kumvetsetsa malonjezo amtengo wapatali amene ali m’Mawu a Mulungu. (Mateyu 24:45-47; 25:34) Onse pamodzi, odzozedwa ndi nkhosa zina amadziŵa Mulungu woona yekhayo, Yehova ndi kumamulambira. (Yohane 17:20, 21) Onse pamodzi, amathokoza Mulungu chifukwa cha phindu lotetezera machimo la nsembe ya Yesu. Amatumikira pamodzi monga gulu limodzi la nkhosa pansi pa Mbusa m’modzi, Yesu Kristu. (Yohane 10:16b) Onse ali mbali ya ubale umodzi wachikondi wa padziko lonse. Amagaŵana limodzi mwayi wokhala Mboni za Yehova ndi za Ufumu wake. Inde, ngati ndinu mtumiki wa Yehova wodzipatulira ndi wobatizidwa, zonsezi zikuphatikizidwa mu choloŵa chanu chauzimu.

21, 22. Kodi tonsefe tingasonyeze motani kuti timakondwera nacho choloŵa chathu chauzimu?

21 Kodi choloŵa chauzimu chimenechi ndi chamtengo wapatali motani kwa inu? Kodi mumachilemekeza mokwanira kuti kuchita chifuno cha Mulungu kukhale chinthu chofunika kwambiri m’moyo wanu? Monga umboni wa zimenezo, kodi mukulabadira uphungu wa Mawu ake ndi gulu lake wofika nthaŵi zonse pa misonkhano ya mpingo wachikristu? (Ahebri 10:24, 25) Kodi choloŵa chimenecho chilidi chofunika kwambiri kwa inu kotero kuti mukupitiriza kutumikira Mulungu mosasamala kanthu za mavuto? Kodi mumachiyamikira kwambiri zedi kwakuti mumalimbikitsidwa kutsutsa chiyeso chilichonse cha kutsata njira imene ingakuchititseni kuchitaya?

22 Tiyeni tonsefe tizikondwera nacho choloŵa chauzimu chimene Mulungu watipatsa. Pamene maso athu akuyang’anitsitsa Paradaiso amene ali m’tsogolo, tiyeni titenge mbali mokwanira mu zochita zauzimu zimene Yehova akutipatsa tsopanoli. Mwa kumangadi miyoyo yathu pa unansi wathu ndi Yehova, timapereka umboni wosatsutsika wakuti choloŵa chathu chopatsidwa ndi Mulungu chilidi chamtengo wapatali kwa ife. Tikhaletu pakati pa awo amene amalengeza kuti: “Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu ku nthaŵi za nthaŵi.”​—Salmo 145:1.

Kodi Mungalongosole Motani?

• Ngati Adamu akanakhala wokhulupirika kwa Mulungu, kodi ndi choloŵa chotani chimene akanatipatsira?

• Kodi ana a Abrahamu anachitanji ndi choloŵa chimene anali nacho?

• Kodi n’chiyani chikuphatikizidwa pa choloŵa cha otsatira odzozedwa a Kristu?

• Kodi choloŵa cha khamu lalikulu n’chiyani, ndipo angasonyeze motani kuti amachiyamikiradi?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 20]

Ana a Abrahamu analandira lonjezo la choloŵa chamtengo wapatali

[Zithunzi patsamba 23]

Kodi mumayamikira choloŵa chanu chauzimu?