Kodi Mumadziŵa Kudikira?
Kodi Mumadziŵa Kudikira?
TALINGALIRANI kuchuluka kwa nthaŵi imene anthu amawononga chaka chilichonse podikira pokha. Amadikira pamzera ku sitolo kapena komwetsera galimoto mafuta. Amadikira ku lesitilanti kuti alandire chakudya. Amadikira kuti aonane ndi dokotala kapena dokotala wa mano. Amadikira mabasi ndi sitima. Inde, pamoyo wa munthu nthaŵi yambiri imatha n’kudikirira zinthu kuti zichitike. Malingana ndi kuyerekezera kwina, ku Germany kokha anthu amawononga maola 4.7 biliyoni pachaka kudikira pandandanda wa galimoto pokha! Munthu wina anaŵerengera kuti maola ameneŵa n’ngofanana ndi chiwonkhetso cha nthaŵi imene anthu pafupifupi 7,000 amayembekeza kukhala ndi moyo.
Kudikira kungakhale kowawa kwambiri. Masiku ano, kumaoneka kuti palibe nthaŵi yokwanira yochitira zinthu zonse, ndipo poganiza za zinthu zina zimene tikanatha kuchita, kudikira kungakhale kopweteka kwambiri. Wolemba nkhani wotchedwa Alexander Rose nthaŵi ina anati: “Chinthu chimodzi chopweteka kwambiri pamoyo wa munthu ndi kudikira.”
Benjamin Franklin, nduna ya boma la America anaona kuti kudikira kungakhalenso kotayitsa ndalama kwambiri. Zaka zoposa 250 zapitazo, ananena kuti: “Nthaŵi ndi ndalama.” N’chifukwa chake anthu amalonda safuna kuchedwa chisawawa nthaŵi ya malonda. Katundu wambiri wopangidwa m’nthaŵi yochepa angapange ndalama zambiri. Amalonda amene amathandiza anthu mwachindunji amayesetsa kuthandiza anthu mwamsanga—kuperekera chakudya, kuika kapena kutenga ndalama ku banki mwachangu popanda kutsika m’galimoto, ndi zina zotero—chifukwa amadziŵa kuti kukondweretsa makasitomala kumaphatikizapo kuchepetsa nthaŵi yodikira.
Kuwononga Miyoyo Yathu
Nthaŵi ina Ralph Waldo Emerson, wolemba ndakatulo wa ku America wa m’zaka za m’ma 1800 anadandaula kuti: “Nthaŵi yochuluka ya anthu imawonongeka chifukwa cha kudikira!” Chaposachedwapa, wolemba nkhani wotchedwa Lance Morrow anadandaula za kutopetsa ndi
kuŵaŵa kodikira. Ndiyeno ananena za “vuto losaonekera lobwera chifukwa cha kudikira.” Kodi n’lotani? “Kudziŵa kuti chinthu chofunika kwambiri pamoyo wa munthu, nthaŵi, imene ili mbali ina ya moyo wamunthu, ikuwonongeka, kutaika mosabwezeretsekanso.” N’zachisoni koma n’zoona. Nthaŵi imene imataika podikira siipezekanso.N’zoona kuti chikhala kuti moyo si waufupi, bwenzi kudikira kusali vuto kwenikweni. Koma moyo n’ngwaufupi. Zaka zambirimbiri zapitazo, wamasalmo wa m’Baibulo analemba kuti: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi aŵiri, kapena tikakhala nayo mphamvu ndi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithaŵa ife tomwe.” (Salmo 90:10) Kaya timakhala kuti kapena ndife anthu otani, miyoyo yathu, imene ndi masiku, maola, mphindi zimene timakhala nazo tikabadwa, n’zochepa. Komabe, sitingapeŵe zochitika zina zimene zimatipangitsa kuwononga ina mwa nthaŵi yofunika imeneyi podikira zinthu kapena anthu.
Kuphunzira Kudikira
Ambirife tinakwerapo galimoto limene dalaivala wake amangofuna kupambana galimoto zimene zili patsogolo pake. Nthaŵi zambiri, si kuti dalaivalayo amakhala akuthamangira zinazake—amakhala alibe chinthu chofunika kuchita mofulumira. Komabe, sangathe kulolera dalaivala wina kulamulira liŵiro lake. Kusaleza kwake mtima kumasonyeza kuti sanaphunzire kudikira. Kuphunzira? Inde, kudziŵa kudikira ndi chinthu chofunika kuphunzira. Palibe amabadwa nako. Ana amafuna kuwasamala mwamsanga akakhala ndi njala kapena pamene sakumva bwino. Kokha akamakula m’pamene amazindikira kuti nthaŵi zina afunika kudikira zinthu zimene akufuna. Ndithudi, kudikira ndi chochitika chosapeŵeka pamoyo, kudziŵa kudikira moleza mtima pofunika kutero kumasonyeza kukhwima maganizo.
N’zoona, pali nthaŵi zimene kusaleza mtima kumakhala komveka. Mwamuna wachinyamata amene akuthamangira kuchipatala ndi mkazi wake chifukwa chakuti ali pafupi kubereka, m’pomveka kusaleza mtima ndi zinthu zom’chedwetsa. Angelo omuuza Loti kuchoka mu Sodomu sanafune kudikira pamene Loti ankachita zochedwa. Chiwonongeko chinali pafupi, ndipo miyoyo ya Loti ndi a m’banja lake inali pachiswe. (Genesis 19:15, 16) Komabe, nthaŵi zambiri pamene anthu amakakamizidwa kudikira si kuti miyoyo imakhala ili pachiswe. Nthaŵi ngati zimenezi, zinthu zingakhale bwino kwambiri ngati aliyense akanaphunzira kuleza mtima ngakhale ngati tikudikira chifukwa chakuti munthu wina sakugwira bwino ntchito yake kapena alibe chidwi chofuna kutithandiza. Komanso, ngati aliyense akanaphunzira kugwiritsa ntchito mwanzeru nthaŵi imene akudikira bwenzi kuleza mtima kuli kosavuta. Bokosi lili patsamba 5 lili ndi malingaliro ena amene angapangitse kudikira kukhala kopiririka komanso kopindulitsa.
Sitiyenera kuiŵala kuti mzimu wosaleza ungasonyeze mkhalidwe wodzitukumula, wodziona kuti iwe ndi wofunika kwambiri kosati n’kudikira. Aliyense amene ali ndi khalidwe limeneli, ayenera kulingalira mawu a m’Baibulo otsatiraŵa: “Wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima.” (Mlaliki 7:8) Kudzikuza, kapena kunyada, ndi nthenda yaikulu pakhalidwe la munthu, ndipo mwambi wa m’Baibulo umati: “Yense wonyada mtima anyansa Yehova.” (Miyambo 16:5) Choncho, kuphunzira kuleza mtima—kuphunzira kudikira—kungafune kuti tidzipende tokha bwinobwino komanso unansi wathu ndi anthu amene timakhala nawo pafupi.
Kuleza Mtima Kudzafupidwa
Kaŵirikaŵiri kudikira sikuŵaŵa ngati tatsimikiza kuti chimene tikudikiracho n’chaphindu, choyeneradi kudikirira ndipo zitanizitani chichitikadi. Pachifukwa chimenechi, ndi bwino kuona kuti olambira oona mtima a Mulungu onse akudikira kukwaniritsidwa kwa malonjezo aakulu a m’Baibulo. Mwachitsanzo, mu salmo louziridwa ndi Mulungu timauzidwa kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Mtumwi Yohane anabwereza lonjezo limeneli pamene anati: “Iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (Salmo 37:29; 1 Yohane 2:17) Ndithudi, ngati tingadzakhale kosatha, kudikira sikungakhale vuto kwenikweni. Koma pakalipano sitikhala ndi moyo kosatha. Kodi n’koyenera kukamba za moyo wosatha?
Tisanayankhe funsoli, kumbukirani kuti Mulungu analenga makolo athu oyamba ndi chiyembekezo Genesis 3:15; Aroma 5:18.
chokhala ndi moyo kosatha. Popeza anachimwa n’chifukwa chake anataya chiyembekezo chimenecho, chawo ndi cha ana awo omwe—kudzanso ife. Komabe, atangochimwa kumene, Mulungu analengeza chifuno chake chochotsa zimene kusamvera kwawo kunadzetsa. Analonjeza kubwera kwa “mbewu,” imene inadzadziŵika kuti ndi Yesu Kristu.—Zili ndi ife aliyense payekha kusankha kaya kupindula ndi kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake kapena ayi. Kuti titero kumafuna kuleza mtima. Motithandiza kuti tiphunzire mtundu umenewu wa kuleza mtima, Baibulo limatilimbikitsa kulingalira za wolima munda. Amadzala mbewu ndipo sangachitire mwina koma kudikira moleza mtima—akumachita zonse zofunika kuti ateteze mbewu zake—mpaka nthaŵi yokolola. Ndiyeno kuleza kwake mtima kumam’pindulitsa, ndipo amaona zipatso za ntchito yake. (Yakobo 5:7) Mtumwi Paulo anatchula chitsanzo china cha kuleza mtima. Anatikumbutsa za amuna ndi akazi okhulupirira akale. Ankayembekezera kukwaniritsidwa kwa zolinga za Mulungu, koma anayenera kudikira nthaŵi yoikika ya Mulungu. Paulo anatilimbikitsa kutsanzira anthu ameneŵa, “amene alikuloŵa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.”—Ahebri 6:11, 12.
Inde, kudikira ndi chinthu chosapeŵeka pamoyo. Koma sikuyenera kukhala chinthu chodetsa nkhaŵa nthaŵi zonse. Kwa anthu amene akudikira kukwaniritsidwa kwa zolinga za Mulungu, kungakhale kosangalatsa. Nthaŵi imene akudikira angaigwiritse ntchito kukulitsa unansi wabwino ndi Mulungu ndiponso kuchita ntchito zimene zimasonyeza chikhulupiriro chawo. Ndipo mwa kupemphera, kuphunzira, ndi kusinkhasinkha, angakhale ndi chikhulupiriro cholimba chakuti zonse zimene Mulungu walonjeza zidzachitika panthaŵi yake.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 5]
CHEPETSANI KUŴAŴA KODIKIRA!
Konzekereranitu! Ngati mukudziŵa kuti mukadikira, konzekerani kukaŵerenga, kulemba, kuluka, kapena kuchita ntchito ina yothandiza.
Gwiritsani ntchito nthaŵiyo kusinkhasinkha, chinthu chimene chili chovuta kwambiri m’dziko lathu losinthasinthali.
Ikani ena mwa mabuku oŵerenga pafupi ndi telefoni kuti muzigwiritsa ntchito ngati akudikiritsani; m’mphindi zisanu kapena khumi, mutha kuŵerenga masamba ambiri ndithu.
Mukamadikira pagulu, gwiritsani ntchito nthaŵiyo kulankhula ena ndipo kambiranani nawo nkhani za phindu, ngati n’kotheka.
Sungani polembapo kapena choŵerenga m’galimoto lanu kaamba ka nthaŵi zodikira mosayembekezera.
Tsinzinani, pumani, kapena pempherani.
KWENIKWENI KUDIKIRA KWABWINO NDI NKHANI YA KHALIDWE NDI KUKONZEKERERATU.