Sonyezani Mtima wa Kristu
Sonyezani Mtima wa Kristu
“Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Kristu Yesu.”—AROMA 15:5.
1. Kodi mtima wa munthu ungakhudze motani moyo wake?
MTIMA wa munthu umasintha moyo kotheratu. Mtima wamphwayi kapena wakhama, mtima wabwino kapena woipa, mtima wa mkangano kapena wa mgwirizano, mtima wodandaula kapena woyamikira ungasonkhezere kwambiri momwe munthu amachitira zinthu m’mikhalidwe inayake komanso mmene anthu ena amamuonera. Munthu wa mtima wabwino angakhale wosangalala ngakhale ali m’mikhalidwe yovuta kwambiri. Koma munthu wa mtima woipa, palibe chimene chimaoneka ngati chabwino kwa iye, ngakhale pamene kuli koonekeratu kuti moyo uli bwino.
2. Kodi munthu amaphunzira motani kukhala ndi mtima wakutiwakuti?
2 Mtima, wabwino kapena woipa, ungaphunziridwe. Kwenikweni, umaphunziridwa kumene. Ponena za mwana wakhanda, insaikulopediya yotchedwa Collier’s Encyclopedia imati: “Mtima umene pambuyo pake amadzakhala nawo amachita kuutengera kapena kuuphunzira, mosasiyana konse ndi mmene angatengere kapena kuphunzira chinenero kapena luso lina lililonse.” Kodi timaphunzira motani kukhala ndi mtima wakutiwakuti? Ngakhale kuti pali zinthu zambiri zimene zimaphatikizidwa, malo okhala ndi mabwenzi n’zomwe zimasonkhezera kwambiri. Insaikulopediya yotchulidwa poyambayo inati: “Timaphunzira kapena kutengera mtima wa anthu amene timayanjana nawo kwambiri.” Zaka zikwi zambiri zapitazo, Baibulo linanena mawu ofananawo. Ilo linati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.”—Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33.
Chitsanzo cha Maganizo Abwino
3. Ndani yemwe anali chitsanzo chabwino pokhala ndi mtima wabwino, ndipo kodi tingam’tsanzire motani?
3 Monga momwe analili chitsanzo chabwino pa china chilichonse, Yesu Kristu anasonyezanso chitsanzo chabwino pankhani ya kukhala ndi mtima wabwino. Iye anati: “Ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.” (Yohane 13:15) Kuti tifanane ndi Yesu, choyamba tiyenera kuphunzira za iye. * Timaphunzira za moyo wa Yesu ndi cholinga chochita zomwe mtumwi Petro analimbikitsa kuti: “Kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zoŵaŵa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) Cholinga chathu n’chakuti tifanane naye Yesu monga momwe kungathekere. Zimenezo zikuphatikiza kuphunzira kukhala ndi mtima umene anali nawo.
4, 5. Ndi mbali iti ya mtima wa Yesu yomwe ikutchulidwa pa Aroma 15:1-3, ndipo kodi Akristu angam’tsanzire motani?
4 Kodi chofunika n’chiyani kuti tikhale ndi mtima ngati wa Kristu Yesu? Chaputala 15 cha kalata ya Paulo yomwe analembera Aroma chimatithandiza kuyankha funso limenelo. M’mavesi oyambirira angapo a chaputala chimenechi, Paulo ananena za mkhalidwe wapadera wa Yesu pamene anati: “Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Yense wa ife akondweretse mnzake, kum’chitira zabwino, zakum’limbikitsa. Pakuti Kristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa: Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa ine.”—Aroma 15:1-3.
5 Kuti atsanzire mtima wa Yesu, Akristu akulimbikitsidwa kukhala okonzeka kutumikira zosoŵa za ena modzichepetsa m’malo mongofuna kudzikondweretsa okha. Ndithudi, kufunitsitsa kutumikira ena modzichepetsa kumeneku ndiwo mkhalidwe wa ‘amene ali olimba.’ Yesu, amene anali wolimba mwauzimu kuposa munthu wina aliyense amene anakhalako, anati ponena za iye mwini: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Mofananamo, ife monga Akristu, tiyenera kuyesetsa kutumikira ena, kuphatikizapo awo amene ali “opanda mphamvu.”
6. Kodi tingatsanzire zochita za Yesu m’njira iti pamene titsutsidwa ndi kunyozedwa?
6 Mkhalidwe winanso wabwino umene Yesu anasonyeza unakhudza kulingalira kwake ndi zochita zake zomwe nthaŵi zonse zinali zolimbikitsa. Iye sanalole konse mtima woipa wa anthu ena kusonkhezera mtima wake wabwinowo pa kutumikira Mulungu; nafenso tisalole. Pamene anali kunyozedwa ndi kuzunzidwa chifukwa cha kulambira Mulungu mokhulupirika, Yesu moleza mtima anapirira popanda kudandaula. Iye anadziŵa kuti awo amene akuyesa kusangalatsa mnzawo mwa “kum’chitira zabwino, zakum’limbikitsa,” ayenera kuyembekezera chitsutso chochokera m’dziko losakhulupirira ndi losazindikirali.
7. Kodi Yesu anasonyeza motani kuleza mtima, ndipo n’chifukwa chiyani ifeyo tiyenera kuchita chimodzimodzi?
7 Yesu anasonyeza mtima wabwino m’njira zinanso. Sanasonyeze konse kusaleza mtima ndi Yehova koma moleza mtima anayembekezera kukwaniritsidwa kwa zifuno Zake. (Salmo 110:1; Mateyu 24:36; Machitidwe 2:32-36; Ahebri 10:12, 13) Komanso, Yesu sanachitepo mosaleza mtima ndi om’tsatira ake. Iye anawauza kuti: “Phunzirani kwa Ine”; popeza kuti anali “wofatsa,” malangizo akewo anali olimbikitsa ndi otsitsimula. Ndipo chifukwa chakuti anali “wodzichepetsa mtima,” sanali wodzitukumula kapena wodzikuza. (Mateyu 11:29) Paulo akutilimbikitsa kutsanzira mikhalidwe imeneyi ya mtima wa Yesu pamene akunena kuti: “Mukhale nawo mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu.”—Afilipi 2:5-7.
8, 9. (a) N’chifukwa chiyani tifunikira kuchita khama kuti tikulitse mtima wopanda dyera? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhumudwa ngati tilephera kutsatira bwino lomwe chitsanzo chomwe Yesu anatisiyira, ndipo Paulo anali chitsanzo chabwino motani pambali imeneyi?
8 N’chapafupi kunena kuti tikufuna kutumikira ena ndi kuti tikufuna kuika zosoŵa zawo patsogolo pa zathu. Koma kupenda moona mtima mkhalidwe wathu wa maganizo kungavumbule kuti mitima yathu siilidi yofunitsitsa kuchita zimenezo. Chifukwa chiyani? Choyamba, chifukwa chakuti tinatengera mikhalidwe yadyera kuchokera kwa Adamu ndi Hava; chachiŵiri, chifukwa chakuti tikukhala m’dziko lomwe limachirikiza dyera. (Aefeso 4:17, 18) Kuti tikhale ndi mtima wopanda dyera kaŵirikaŵiri zimatanthauza kukulitsa kalingaliridwe kosiyana kotheratu ndi chibadwa chathu chopanda ungwirochi. Kuchita zimenezo kumafunatu kutsimikiza mtima ndi khama.
9 Kupanda kwathu ungwiro kodziŵikiratuko, komwe ndi kosiyana kotheratu ndi chitsanzo changwiro chomwe Yesu anatisiyira, nthaŵi zina kungatifooketse. Tingalingalire kuti kukhala ndi mtima wonga umene Yesu anali nawo kuli kosatheka. Koma tamvani mawu a Paulo olimbikitsawo akuti: “Ndidziŵa kuti m’kati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza. Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichita. Pakuti monga mwa munthu wa m’kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.” (Aroma 7:18, 19, 22, 23) Zoonadi, kupanda ungwiro kwa Paulo kunam’lepheretsa mobwerezabwereza kuchita chifuno cha Mulungu monga momwe iye ankafunira, koma mtima wake—momwe anali kuganizira ndi kumvera ponena za Yehova ndi malamulo Ake—unali chitsanzo chabwino. Wathunso ungakhale chitsanzo chabwino.
Kuwongolera Mtima Wolakwika
10. Kodi Paulo analimbikitsa Afilipi kukulitsa mtima wotani?
10 Kodi n’zotheka kuti ena afunika kuwongolera mtima wolakwika? Inde. Zimenezi zinachitikirapo Akristu ena a m’zaka za zana loyamba. M’kalata yake yopita kwa Afilipi, Paulo ananena za kukhala ndi mtima woyenera. Iye analemba kuti: ‘Si kunena kuti ndinalandira kale [moyo wakumwamba mwa chiukiriro choyamba], kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Yesu Kristu. Abale, ine sindiŵerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira; koma chinthu chimodzi ndichichita; poiŵaladi za m’mbuyo, ndi kutambalitsira za m’tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu. Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima.’—Afilipi 3:12-15.
11, 12. Kodi Yehova amativumbulira mtima woyenera m’njira ziti?
11 Mawu a Pauloŵa akusonyeza kuti aliyense amene, pambuyo pa kukhala Mkristu, salingalira n’komwe za kufunika kwa kupita patsogolo ali ndi mtima wolakwika. Munthu wotere walephera kutengera mtima wa Kristu. (Ahebri 4:11; 2 Petro 1:10; 3:14) Kodi mkhalidwe wa munthu wotereyu n’ngwopanda chiyembekezo? Ndithudi ayi. Mulungu angatithandize kusintha mtima wathu ngati tikufunadi kutero. Paulo akupitiriza kunena kuti: “Ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu.”—Afilipi 3:15.
12 Komabe, ngati tikufuna kuti Yehova ativumbulire mtima woyenera, tiyenera kuchita mbali yathu. Kuphunzira Mawu a Mulungu mwapemphero mothandizidwa ndi zofalitsa zachikristu zoperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kudzatheketsa awo amene ‘ali nako kulingalira kwina mumtima’ Mateyu 24:45) Akulu achikristu, oikidwa ndi mzimu woyera ‘kuti aŵete Eklesia wa Mulungu,’ adzasangalala kupereka chichirikizo. (Machitidwe 20:28) Ndifetu oyamikira zedi kuti Yehova amalingalira mwakuya za kupanda ungwiro kwathu ndi kuti mwachikondi amatipatsa thandizo! Tiyeni tizililandira.
kukulitsa mtima woyenera. (Kuphunzira Kuchokera kwa Ena
13. Kodi timaphunziranji m’nkhani ya m’Baibulo ya Yobu ponena za mtima woyenera?
13 Mu Aroma chaputala 15, Paulo akusonyeza kuti kusinkhasinkha pa zitsanzo za m’mbiri kungatithandize kusintha mtima wathu. Iye analemba kuti: “Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Atumiki ena okhulupirika a Yehova m’nthaŵi zakalezo anafunikira kusintha mbali zina za malingaliro awo. Mwachitsanzo, nthaŵi zonse Yobu anali ndi mtima wabwino. Sanalingalirepo kuti Yehova ndiye amene anali kuchititsa zinthu zoipa, ndipo sanalole konse kuti mavuto agwedeze chidaliro chake mwa Mulungu. (Yobu 1:8, 21, 22) Komabe, iye anali ndi mtima wofuna kudziyesa wolungama. Yehova anatsogolera Elihu kuti athandize Yobu kuthetsa mtima wodzilungamitsawu. M’malo mokhumudwa, Yobu anavomereza modzichepetsa kufunika kwa kusintha mtima woterowo chotero nthaŵi yomweyo anayamba kuchitapo kanthu.—Yobu 42:1-6.
14. Kodi tingafanane motani ndi Yobu pamene tapatsidwa uphungu wokhudza mtima umene tili nawo?
14 Kodi ifeyo tidzachita monga Yobu ngati Mkristu mnzathu atatiuza mwachikondi kuti tinali kusonyeza kuti tili ndi mtima wolakwika? Monga Yobu, tisayesetu “kunenera Mulungu cholakwa.” (Yobu 1:22) Ngati tivutika popanda chifukwa chilichonse, tisadandaule kapena kulingalira kuti Yehova ndiye amene akuchititsa zovuta zathuzo. Tipeŵetu kudzilungamitsa, tikumakumbukira kuti kaya tili ndi maudindo otani muutumiki wa Yehova, ndife chabe “akapolo opanda pake.”—Luka 17:10.
15. (a) Ndi mtima wolakwika wotani womwe ena mwa otsatira a Yesu anasonyeza? (b) Kodi Petro anasonyeza motani kuti anali ndi mtima wabwino?
15 M’kati mwa zaka za zana loyamba, ena omwe anamvetsera Yesu anasonyeza mtima wosayenera. Nthaŵi inayake, Yesu ananena mawu enaake omwe anali ovuta kuwamvetsa. Poyankha, “ambiri a akuphunzira ake, pakumva izi, anati, Mawu aŵa ndi osautsa; akhoza kumva aŵa ndani?” Awo amene analankhula mwanjira imeneyi mwachionekere anali ndi mtima wolakwika. Ndipo mtima wawo wolakwikawo unaŵachititsa kuleka kumvetsera Yesu. Nkhaniyo imati: “Pa ichi ambiri a akuphunzira ake anabwerera m’mbuyo, ndipo sanayendayendanso ndi Iye.” Kodi onse anali ndi mtima Yohane 6:60, 66-68) Mtimatu wabwino kwabasi! Pamene tapeza mafotokozedwe kapena kumveketsa bwino Malemba zomwe poyamba zingativute kuvomereza, kodi sikudzakhala bwino kusonyeza mtima womwe Petro anasonyeza? Kungakhaletu kupusa zedi kuleka kutumikira Yehova kapena kulankhula mosemphana kotheratu ndi “chitsanzo cha mawu a moyo” kokha chifukwa chakuti zinthu zinazake n’zovuta kuzimvetsa kuyamba n’kuyamba!—2 Timoteo 1:13.
wolakwika? Ayi. Nkhaniyo ikupitiriza kuti: “Chifukwa chake Yesu anati kwa khumi ndi aŵiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka? Simoni Petro anam’yankha iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani?” Ndiyeno, tingatero kuti Petro anayankha funso lake lomwe kuti: “Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.” (16. Ndi mtima wochititsa nthumanzi wotani womwe atsogoleri achipembedzo achiyuda a m’tsiku la Yesu anasonyeza?
16 Atsogoleri achipembedzo achiyuda a m’zaka za zana loyamba analephera kusonyeza mtima womwe Yesu anali nawo. Kutsimikiza mitima kwawo kusafuna kumvera Yesu kunasonyezedwa pamene Yesuyo anaukitsa Lazaro kwa akufa. Kwa aliyense wa mtima woyenera, chozizwitsa chimenecho chikanakhala umboni wamphamvu wakuti Yesu anatumidwadi ndi Mulungu. M’malo mwake, timaŵerenga kuti: “Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri. Ngati tim’leka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.” Anagwirizana kuchitanji? “Kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe Iye.” Kuwonjezera pa kupanga chiwembu cha kupha Yesu, anafunanso kuwononga umboni wachionekere wakuti iye analidi wochita zozizwitsa. “Ansembe aakulu anapangana kuti akaphe Lazaronso.” (Yohane 11:47, 48, 53; 12:9-11) Zingakhaletu zonyansa kwambiri titati tikulitse mzimu ngati umenewu ndi kukwiya kapena kukhumudwa ndi zinthu zomwe kwenikweni tinayenera kukondwera nazo! Inde, zingakhale zoopsatu zedi!
Kutengera Mtima Wabwino wa Kristu
17. (a) Kodi Danieli anasonyeza mtima wopanda mantha pa zochitika zotani? (b) Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali wolimba mtima?
17 Atumiki a Yehova n’ngamtima wabwino nthaŵi zonse. Pamene adani a Danieli anapanga chiŵembu chakuti akhazikitse lamulo loletsa kupempha kanthu kwa mulungu aliyense kapena kwa munthu wina aliyense kupatula kwa mfumu yokha kwa masiku 30, Danieli anadziŵa kuti zimenezi zidzasokoneza unansi wake ndi Yehova Mulungu. Kodi anasiya kupemphera kwa Mulungu kwa masiku 30? Ayi, mosaopa iye anapitirizabe kupemphera kwa Yehova katatu patsiku, monga momwe anali kuchitira nthaŵi zonse. (Danieli 6:6-17) Mofananamo Yesu sanalole kuopsezedwa ndi adani ake. Tsiku linalake pa Sabata, anaona mwamuna wopuwala dzanja. Yesu anadziŵa kuti Ayuda ambiri amene anali pamalowo sadzasangalala ngati atachiritsa munthu aliyense pa Sabata. Iye anaŵafunsa mosapita m’mbali kuti afotokoze malingaliro awo pa nkhaniyo. Iwo atakana kuyankha, Yesu anangoŵaleka ndi kuchiritsa munthuyo. (Marko 3:1-6) Yesu sanali kuzengereza konse kukwaniritsa ntchito yake akaona kuti n’koyenera kuti aigwire.
18. N’chifukwa chiyani ena amatitsutsa, koma kodi tiyenera kuchita motani ndi mtima wawo woipawo?
18 Mboni za Yehova lerolino zimadziŵa kuti nazonso siziyenera kuopsezedwa ndi zinthu zoipa zomwe otsutsa angaŵachitire. Zikapanda kutero, ndiye kuti sizidzakhoza kusonyeza mtima womwe unali ndi Yesu. Ambiri amatsutsa Mboni za Yehova, ena chifukwa chakuti alibe chidziŵitso cholondola ndipo ena chifukwa chakuti amadana ndi Mbonizo kapena uthenga wawo. Komatu tisalole mtima wawo waudaniwo kukhudza mtima wathu wabwino. Sitiyenera kulola anthu ena kulamulira mmene timalambirira.
19. Kodi tingasonyeze motani mtima wonga womwe unali ndi Yesu Kristu?
Mateyu 23:2, 3) Tiyenera kutsanzira chitsanzo chake. Kunena zoona, abale athu n’ngopanda ungwiro, komatu nafenso ndife opanda ungwiro. Ndipo kodi n’kutinso komwe tingakapeze anansi abwino ndi mabwenzi okhulupirikadi kuposa mu ubale wathu wapadziko lonse? Yehova sanatimveketserebe zonse m’Mawu ake olembedwa, koma kodi ndi gulu liti la chipembedzo lomwe limaŵamvetsa bwino koposa? Tikhaletu ndi mtima wabwino nthaŵi zonse, mtima umene Yesu Kristu anali nawo. Mwazina, zimenezi zimaphatikizapo kudziŵa mmene tingayembekezere Yehova, monga momwe tidzaphunzirira m’nkhani yotsatira.
19 Nthaŵi zonse Yesu anali kusonyeza mtima wabwino kwa om’tsatira komanso ku makonzedwe a Mulungu, ngakhale pamene kuchita zimenezo kunali kovuta zedi. ([Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., limafotokoza bwino lomwe moyo ndi utumiki wa Yesu.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi miyoyo yathu imakhudzidwa motani ndi mtima umene tili nawo?
• Fotokozani mtima wa Yesu Kristu.
• Kodi tingaphunzirenji pa mtima umene Yobu anali nawo?
• Kodi mtima woyenera kukhala nawo pamene tiyang’anizana ndi chitsutso n’ngotani?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 7]
Mkristu wa mtima wabwino amayesetsa kuthandiza ena
[Chithunzi patsamba 9]
Kuphunzira Mawu a Mulungu mwa pemphero kumatithandiza kutengera mtima wa Kristu