Kufuulira Thandizo
Kufuulira Thandizo
“MULUNGU wandiiŵala ine!” analira motero mkazi wina wa ku Brazil. Mwamuna wake atamwalira mwadzidzidzi, anaganiza kuti moyo wake tsopano unalibe tanthauzo lililonse. Kodi munayesapo kutonthoza munthu wopsinjika maganizo chotero kapena amene mwinamwake akudandaula n’cholinga chakuti mum’thandize?
Ena amataya mtima kwambiri mwakuti amangodzipha—ndipo ambiri amene amachita zimenezi ndi achinyamata. Malinga n’kunena kwa nyuzipepala ya Folha de S. Paulo, kufufuza kochitika m’Brazil kwasonyeza kuti “kudzipha kwa achinyamata kwawonjezeka ndi 26 peresenti.” Mwachitsanzo, tamvani nkhani ya Walter, * mnyamata wa ku São Paulo. Iye analibe makolo, analibe nyumba, sanali pantchito, analibe mabwenzi omwe akanam’thandiza. Kuti athane ndi mavuto akewo, Walter anangoganiza zodziponya kuchokera pa mlatho.
Edna, mayi wopanda mwamuna, anali kale ndi ana aŵiri pamene anakumana ndi mwamuna wina. Patangotha mwezi umodzi wokha, iwo anayamba kukhalira limodzi m’nyumba ya amayi ake a mwamunayu, omwe anali okhulupirira kwambiri zamizimu ndiponso anali chidakwa. Mwana wina wa Edna anayamba kumwa moŵa mwauchidakwa, ndipo mayiyu anavutika maganizo kwambiri kotero kuti anafuna kudzipha. Mapeto ake, sanathenso kuyang’anira bwino ana akewo.
Bwanji nanga anthu okalamba? Maria anali wokonda kuseŵera ndi wosatopa n’kulankhula. Koma pamene anali kukalamba, anayamba kudera nkhaŵa ntchito yake ya unesi chifukwa chakuti ankaopa kuti adzayamba kulakwitsa zinthu. Zimenezi zinam’detsa nkhaŵa. Atalephera kudzichiza ndi mankhwala ena, anafunafuna thandizo lamankhwala kuchipatala, ndipo mankhwala omwe analandirawo anam’thandiza kwabasi. Koma atam’chotsa ntchito ali ndi zaka 57, nkhaŵa inam’gwiranso mwamphamvu kwambiri kwakuti analibe njira iliyonse yoithetsera. Maria anayamba kuganiza zodzipha.
“Pafupifupi 10 peresenti ya anthu opsinjika maganizo amayesa kudzipha,” anatero Pulofesa José Alberto Del Porto wa pa Yunivesite ya São Paulo. “Sitingakhulupirire kuti anthu odzipha n’ngochuluka powayerekeza ndi ophedwa ndi anthu ena, komatu zimenezi n’zoona ndipo n’zomvetsa chisoni,” anatero Dr. David Satcher, dokotala wamkulu wa ku United States.
Nthaŵi zina kuyesa kudzipha kumakhala kuli kupempha thandizo. Ndipotu kwenikweni a m’banjalo ndi mabwenzi afunikira kuchitira munthu wotaya chiyembekezo ameneyo chinthu chabwino. Ndithudi, sikungakhale kothandiza kugwiritsa ntchito mawu
ngati akuti: “Usadzimvere chisoni,” “Anthu ambiri ali m’mavuto aakulu kuposa iweyo” kapena kuti, “Nafenso timakumana ndi mavuto nthaŵi ndi nthaŵi.” M’malo mwake, bwanji osakhala bwenzi lenileni ndi womvetsera wabwino? Inde, yesani kuthandiza wopsinjika maganizoyo kuona kuti moyo n’ngwamtengo wapatali.Wolemba mabuku wa ku France Voltaire analemba kuti: “Munthu amene angadziphe lerolino chifukwa chopsinjika maganizo, akanakonda kukhalabe ndi moyo ngati akanadikira kwa mlungu umodzi.” Chotero, kodi anthu amene apsinjika maganizo angadziŵe motani kuti moyo n’ngwofunika kwambiri?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Tasintha mayina ena.
[Chithunzi patsamba 3]
Chiŵerengero chowonjezeka cha achinyamata ndi achikulire amadzipha
[Chithunzi patsamba 4]
Kodi mungathandize motani munthu amene wataya mtima?