Kulengeza Ufumu wa Mulungu ku Zilumba za Fiji
Ndife a Iwo Omwe Ali Ndi Chikhulupiriro
Kulengeza Ufumu wa Mulungu ku Zilumba za Fiji
NTHAŴI ina Yesu Kristu ananenapo za njira ziŵiri. Ina ndi yotakata ndipo ipita ku imfa. Ina ndi yopapatiza koma ipita ku moyo. (Mateyu 7:13, 14) Kuti anthu athe kusankha njira yoyenera, Yehova Mulungu analinganiza kuti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14) Chifukwa chake, anthu kulikonse akumvera uthenga wa Ufumu, ndipo ena akusankha moyo mwa kukhala “iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Tikukulimbikitsani kuŵerenga za zosankha za moyo zimene ena achita ku Fiji ndi zilumba zina zapafupi ndi kumeneko za ku South Pacific.
Anakhulupirira Yehova
Mere anali mtsikana wopita kusukulu pamene anayamba kumva uthenga wa Ufumu mu 1964. Chifukwa chokhala kutali pachilumba china, anali kukumana ndi Mboni za Yehova kamodzikamodzi. Komabe pomalizira pake, anatha kupeza chidziŵitso cholondola cha Baibulo. Panthaŵi imeneyo, anali wokwatiwa ndi mwamuna amene anali mfumu m’mudzimo. Chifukwa chakuti Mere anasankha kutsata mfundo za m’Baibulo, mwamuna wake pamodzi ndi abale ake anali kumam’chitira nkhanza. Ndipo anthu anzake a m’mudzimo amam’nyodola. Komano, anabatizidwa mu 1991.
Pasanapite nthaŵi yaitali, Josua mwamuna wa Mere, anasintha mtima wake. Ndipo anayamba kukhala nawo ndi pa zokambirana zomwe za Baibulo zimene Mere anali kukambirana ndi ana awo. Josua analeka kupita ku tchalitchi cha Methodist. Komabe, monga mfumu, anali kutsogolerabe misonkhano ya m’mudzimo mlungu uliwonse. Kwa anthu a m’mudzimo, Josua anaoneka kukhala munthu wosakhulupirika chifukwa chakuti tchalitchi cha Methodist chinali chapadera pamoyo wakumudzi wa ku Fiji. Ndiye chifukwa chake mbusa wakumeneko analimbikitsa Josua kuti abwerere ku chipembedzo chake chakale.
Molimba mtima, Josua ananenetsa kuti iye ndi banja lake anasankha kulambira Yehova Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi” ndipo sadzasiya. (Yohane 4:24) Pamsonkhano wina wotsatira wa m’mudzimo, mfumu yaikulu inalamula kuti Josua ndi banja lake athamangitsidwe m’mudzimo. Anapatsidwa masiku asanu ndi aŵiri kuti achoke pa chilumbacho ndi kusiya nyumba yawo, munda wawo, ndi mbewu zawo—inde, zonse zimene anali kukhalira moyo.
Abale auzimu pa chilumba china anathandiza Josua ndi banja lake. Anawathandiza ndi malo okhala komanso malo olima. Josua ndi mwana wake wamkulu wamwamuna ndi obatizidwa tsopano. Ndipo mwana wina wamwamuna ndi wofalitsa wosabatizidwa wa uthenga wabwino. Posachedwapa Mere analembetsa upainiya wokhazikika (wolengeza Ufumu nthaŵi zonse). Kusankha kwawo kutumikira Yehova kunawatayitsa udindo wawo ndi zinthu zawo zakuthupi. Koma monga mtumwi Paulo, amayesa zonsezo zopanda pake poyerekeza ndi zimene apeza.—Afilipi 3:8.
Kusankha Kokhudza Chikumbumtima
Kusankha kutsatira chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo kumafuna chikhulupiriro ndi kulimba mtima. Zinali choncho ndi mkazi wina wachitsikana wotchedwa Suraang, amene amakhala ku Tarawa, chilumba china cha ku Kiribati. Suraang anapempha chilolezo kuti asamagwire mbali ina ya ntchito yake monga nesi pachipatala. Pempho lake silinavomerezedwe, choncho anam’tumiza kukagwira ntchito ku chipatala chaching’ono kuchilumba chakutali kumene anakhala yekha motalikirana ndi okhulupirira anzake.
Pachilumbacho, ndi mwambo kuti onse amene
angofika kumene apereke nsembe kwa “mzimu” wakumeneko. Anthuwo amakhulupirira kuti wina akalephera kutero amafa. Popeza kuti Suraang sanawalole kum’chitira iye ndi gulu lake mwambo umenewu wopembedza mafano, anthu a m’mudzimo anadikirira kumuona ataphedwa ndi mzimu wokhumudwawo. Popeza kuti Suraang ndi gulu lake sanavulazidwe, anakhala ndi mpata waukulu wochitira umboni wabwino.Koma mayeso a Suraang sanathere pomwepo. Anyamata ena a pachilumbacho amayesa zosangalatsa kukopa mtsikana wodzacheza. Komabe, Suraang anapeŵa kunyengerera kwawo nakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu. Ndipotu, anakhoza kutumikira monga mpainiya wokhazikika ngakhale kuti amakhala ali pantchito maola 24 tsiku lililonse kuyembekezera kuitanidwa monga nesi.
Lisanachitike phwando limene linachitidwa polemekeza Suraang pamene anali kukonzekera kuchoka pa chilumbacho, akulu a mudziwo ananena kuti anali mmishonale weniweni woyamba amene anawachezera. Chifukwa cha kulimbikira kwake kutsatira mfundo za m’Baibulo, ena pachilumbacho alandira uthenga wa Ufumu.
Zovuta za Kumaloko
Kutalikirana kwa midzi ina kumachititsa kuti anthu a Yehova azidzipanikiza kwambiri kuti alalikire nawo ndi kukhala nawo pa misonkhano yachikristu. Taganizani chitsanzo cha Mboni zinayi zobatizidwa—mwamuna mmodzi ndi akazi atatu—amene amatha maola angapo popita ndi pobwera ku misonkhano. Ulendo wawo wapansi umaphatikizapo kuwoloka mitsinje itatu popita ndi pobwera. Ngati madzi ali odzaza, mbaleyo amayamba iye kuwoloka akusambira komanso akukoka chimphika chachikulu chimene chimakhala ndi zikwama zawo, mabuku, ndi zovala za kumsonkhano. Kenako amasambira kubwerera kukathandiza alongo atatuwo.
Kagulu kena kamene kamasonkhana kuchilumba chakutali cha Nonouti ku Kiribati, kamakumana ndi zovuta zosiyana. Nyumba imene amasonkhanamo mumaloŵa anthu asanu ndi aŵiri kapena asanu ndi atatu basi. Ena odzasonkhana amakhala panja n’kumasuzumira m’kati kudzera m’mipata ya mpanda wa waya. Malo osonkhanawo amaonekera kwa anthu ena a m’mudzimo amene amakhala akuchokera ndi kupita ku matchalitchi awo ochititsa kaso. Inde, atumiki a Yehova amadziŵa kuti mmene Mulungu amaonera, anthu, osati nyumba, ndiwo amene ali ofunikadi. (Hagai 2:7) Mlongo mmodzi yekha wobatizidwa pachilumbacho ndi wokalamba ndipo sangathe kuyenda mtunda wautali. Komabe, amathandizidwa mu ntchito yolalikira ndi mtsikana wina wofalitsa wosabatizidwa amene amam’kankha m’ngolo yokankha ndi manja. Anthu ameneŵa amayamikiradi choonadi!
Ofalitsa oposa 2,100 amene akutumikira kuzilumba za Fiji ali otsimikiza kupitiriza kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ali ndi chidaliro kuti ena ambiri adzakhala “a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.”
[Mapu patsamba 8]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Australia
Fiji