Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Posachedwapa—Dziko Lopanda Nkhaŵa

Posachedwapa—Dziko Lopanda Nkhaŵa

Posachedwapa​—Dziko Lopanda Nkhaŵa

MOWONJEZEREKA moyo ukufuna zochuluka, ndipo zifukwa zodera nkhaŵa n’zambiri. Pamene takwiya kungakhale kovuta kuti tilamulire malingaliro athu. Inde, ngakhale anthu amene amakonda moyo angakhale osakondwa chifukwa chotaya chikhulupiriro! Taonani zitsanzo zingapo.

M’nthaŵi zakale, mneneri Mose anataya mtima kwambiri mwakuti anauza Mulungu kuti: “Mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang’ane tsoka langa.” (Numeri 11:15) Akuthaŵa adani ake, mneneri Eliya anafuula nati: “Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova.” (1 Mafumu 19:4) Ndipo mneneri Yona anati: “Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ayi.” (Yona 4:3) Komatu Mose, Eliya ndi Yona sanadziphe ayi. Onseŵa ankadziŵa lamulo la Mulungu lakuti: “Usaphe.” (Eksodo 20:13) Pokhala ndi chikhulupiriro champhamvu mwa Mulungu, anadziŵa bwino lomwe kuti palibe chomwe Mulungu chingam’lake ndipo ankadziŵanso kuti moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.

Bwanji nanga za mavuto amene tikukumana nawo lerolino? Kuwonjezera pa kupsinjika maganizo kapena matenda, nthaŵi zina tingafunikire kupirira kuzunzidwa ndi a m’banja lathu, anansi athu, kapena amene timagwira nawo ntchito limodzi. Baibulo limanena za anthu omwe n’ngodzala “ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndewu, chinyengo, udani; akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu awo, opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi chachibadwidwe, opanda chifundo.” (Aroma 1:28-31) Kukhala pakati pa anthu amtunduwu tsiku ndi tsiku kungapange moyo kuoneka ngati wotopetsa. Kodi amene akufuna chitonthozo ndi kutsitsimulidwa tingaŵathandize motani?

Kufunitsitsa Kumvetsera

Masoka ndi kuvutika zingasokoneze munthu maganizo. Munthu wanzeru anati: “Nsautso iyalutsa wanzeru.” (Mlaliki 7:7) Choncho munthu amene akutchula zodzipha tisamuone ngati akunena zocheza. Vuto lakelo, kaya ndi la mumtima, matenda, la maganizo, kapena lauzimu, lifunikira thandizo lamwamsanga. Komanso thandizo la madokotala limasiyanasiyana, choncho munthuyo ayenera kudzisankhira mtundu wa mankhwala omwe angafune.​—Agalatiya 6:5.

Kaya ndi chifukwa chotani chofunira kudzipha chimene munthu angakhale nacho, kupeza munthu wozindikira, wachifundo, ndi wodekha amene angam’khulupirire kungathetse nkhaŵa yakeyo. A m’banja ndi mabwenzi ofunitsitsa kumvetsera angathe kuthandiza. Kuwonjezera pa kukhala bwenzi lenileni ndi kusonyeza chifundo, malingaliro olimbikitsa otengedwa m’Mawu a Mulungu angathandize kwambiri anthu amene ataya chikhulupiriro.

Thandizo Lauzimu kwa Opsinjika Maganizo

Mungadabwe kumva mmene kuŵerenga Baibulo kulili kolimbikitsa. Ngakhale kuti si buku lopereka malangizo okhalira ndi maganizo athanzi, Baibulo lingatithandize kuona kufunika kwa moyo. Mfumu Solomo inati: “Ndidziŵa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.” (Mlaliki 3:12, 13) Kuwonjezera pa ntchito yokhutiritsa imene imapangitsa moyo kukhala watanthauzo, zinthu zodziŵikiratu monga kamphepo kayeziyezi, kuwala kwa dzuŵa, maluŵa, mitengo, ndi mbalame zili mphatso zopatsidwa ndi Mulungu zomwe tingasangalale nazo.

Komanso cholimbikitsa kwambiri ndicho mawu otsimikizika a m’Baibulo akuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, amatisamalira. (Yohane 3:16; 1 Petro 5:6, 7) Moyenerera wamasalmo anati: “Wolemekezeka Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.” (Salmo 68:19) Ngakhale kuti tingadzione ngati osafunika ndi opanda pake, Mulungu akutilimbikitsa kupemphera kwa iye. Khalani wotsimikizira kuti aliyense amene adzapempha thandizo kwa iye modzichepetsa ndi moona mtima sadzam’nyalanyaza.

Ndithudi palibe amene angayembekezere moyo wopanda mavuto lerolino. (Yobu 14:1) Koma choonadi cha m’Mawu a Mulungu chasonyeza anthu ambiri kuti kudzipha si ndiko njira yabwino yothetsera mavuto awo. Tangolingalirani mmene mtumwi Paulo anathandizira woyang’anira ndende wosautsika maganizo uja. ‘Atautsidwa kutulo take, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am’ndende adathaŵa.’ Nthaŵi yomweyo, woyang’anira ndende ameneyu anaganiza kuti kudzipha kunali bwino kusiyana ndi imfa yochititsa manyazi ndiponso mwinamwake kumupha mwa kum’zunza chifukwa chakuti walephera ntchito yake. Mtumwi Paulo anafuula nati: “Usadzipweteka wekha; tonse tili muno.” Paulo sanalekere pomwepo. Kwenikweni iye ndi Sila anatonthoza woyang’anira ndendeyo ndi kum’yankha funso lake lakuti: “Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?” Iwo anayankha nati: “Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.” Kenako anam’lalikira iye mawu a Yehova ndi onse apabanja lake, ndipo zotsatira zake zinali zakuti “[a]nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.” Woyang’anira ndende ameneyo ndi onse apabanja pake anasangalala kwambiri ndipo anapeza tanthauzo latsopano la moyo.​—Machitidwe 16:27-35.

Lerolino, n’kotsitsimulatu kwambiri kudziŵa kuti Mulungu si ndiye amene amachititsa zoipa! Mawu ake amatchula za mzimu woipa, “iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana” kuti ndiye “wonyenga wa dziko lonse.” Komatu kam’tsalira kanthaŵi. (Chivumbulutso 12:9, 12) Posachedwapa, mavuto onse amene Satana ndi ziŵanda zake adzetsa kwa anthu okhala m’dzikoli adzatha pamene Mulungu adzaloŵererapo. Ndiyeno dziko latsopano lachilungamo lomwe Mulungu walonjeza lidzathetseratu zonse zochititsa kutaya chikhulupiriro ndi kudzipha.​—2 Petro 3:13.

Chitonthozo kwa Onse Opempha Thandizo

Ngakhale tsopano lino, awo amene ali opsinjika maganizo angapeze chitonthozo cha m’Malemba. (Aroma 15:4) Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.” (Salmo 51:17) Zoona, mosapeŵeka timakumana ndi ziyeso ndi zotsatira za kupanda ungwiro. Koma kuphunzira chidziŵitso cholondola cha Atate wathu wakumwamba, wachifundo, wachikondi, ndi wololera kudzatitsimikizira kuti ndife amtengo wapatali kwa iye. Mulungu angakhale Bwenzi lathu lapamtima ndi Mlangizi wathu. Ngati tikulitsa unansi weniweni ndi Yehova Mulungu, sadzatikhumudwitsa. Mlengi wathuyo akuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.”​—Yesaya 48:17.

Kudalira Mulungu kwathandiza anthu ambiri. Mwachitsanzo: Mara anali atalefulidwa kale ndi kupsinjika maganizo kwanthaŵi yaitali pamene mwana wake wamwamuna mmodzi yekhayo anamwalira pangozi yagalimoto. * Anasoŵa mtendere ndipo anafuna kudzipha. Koma tsopano, amadzuka m’maŵa kwambiri tsiku lililonse ndi kuyamba kugwira ntchito zake zapakhomo. Amasangalala kumvetsera nyimbo ndi kuthandiza ena. Chiyembekezo chakuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama” chachotsa wina mwa ululu wa imfa yomvetsa chisoni ya mwana wake wokondedwa ndipo chalimbikitsa chikhulupiriro chake mwa Mulungu. (Machitidwe 24:15) Popeza kuti Mara analibe cholinga chodzakhala ngati mngelo kumwamba, mawu a pa Salmo 37:11 amukhudza mtima kwambiri, mawuwo amati: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”

Mkazi wina wa ku Brazil, Sandra, ankayesetsa kwambiri kuti akhale mayi wabwino kwambiri kwa ana ake atatu. Iye akuvomereza kuti: “Ndinali wotanganidwa kwambiri mwakuti bambo anga atamwalira mwadzidzidzi, komanso ine nthaŵi yomweyo n’nkutulukira kuti mwamuna wanga ali pa chibwenzi ndi mkazi wina, sindinalingalire n’komwe zopemphera kwa Mulungu kuti andithandize.” Mokhumudwa Sandra anayesa kudzipha. N’chiyani chomwe cham’thandiza kusintha? Kuyamikira kwake zinthu zauzimu. “Usiku uliwonse ndisanagone, ndimaŵerenga Baibulo, ndipo ndimayesa kuyerekezera zomwe zachitikira anthu m’nkhani yomwe ndikuŵerenga ngati kuti zikundichitikira ine. Ndimaŵerenganso magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ndipo kwenikweni ndimakonda kuŵerenga mbiri za moyo wa anthu ena chifukwa chakuti zimandithandiza kukhutira ndi moyo wanga.” Chifukwa chakuti akudziŵa kuti Yehova ndiye bwenzi lake lapamtima, waphunzira kutchula mwachindunji zimene akufuna m’mapemphero ake.

M’tsogolo Momwe Simudzakhala Kupsinjika Maganizo

N’kotonthozatu zedi kudziŵa kuti kuvutika kwa anthu kumeneku n’kwakanthaŵi! Mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, ana ndi akuluakulu omwe amene padakali pano akuzunzika chifukwa cha upandu, kupanda chilungamo, kapena tsankho adzakondwera. Monga momwe salmo la ulosi linaloserera, Mfumu yoikika ya Yehova, Yesu Kristu, “adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi.” Komanso, “adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.” Ndithudi, “adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”​—Salmo 72:12-14.

Nthaŵi yakuti mawu aulosi ameneŵa akwaniritsidwe yayandikira. Kodi mukalingalira zodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi m’mikhalidwe yoteroyo m’makhudzidwa mumtima? Ngati ndi choncho, ndiyetu muli ndi chifukwa chokhalira wachimwemwe ndi kuona moyo monga mphatso yochokera kwa Mulungu. Ndipo ngati m’mauza ena malonjezo a m’Malemba otonthozaŵa, mungadzetse chimwemwe chachikulu m’miyoyo ya anthu omwe akufuulira thandizo m’dziko lopanda chifundo ndi chikondi lino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Tasintha mayina ena.

[Chithunzi patsamba 6]

Pali nthaŵi zambiri zosangalala lerolino

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi mukuyembekezera dziko momwe simudzakhala kupsinjika maganizo?