Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tetezani Dzina Lanu

Tetezani Dzina Lanu

Tetezani Dzina Lanu

MUNTHU amene amalemba mapulani a nyumba zokongola amadzipangira dzina monga katswiri wolemba mapulani a nyumba. Mtsikana wochita bwino kusukulu amadziŵika monga wophunzira wanzeru. Ngakhalenso munthu amene sachita china chilichonse angadzipangire dzina lakuti ndi waulesi. Potsindika ubwino wa kupanga dzina labwino, Baibulo limati: “Dzina labwino n’lofunika kuposa chuma chambiri, mbiri yabwino iposa siliva ndi golide.”​—Miyambo 22:1, An American Translation.

Munthu amakhala ndi dzina labwino mwakuchita zinthu zing’onozing’ono zambiri kwa nthaŵi yaitali. Komabe, kungochita chinthu chimodzi chokha chopusa kungaipitse dzinalo. Mwachitsanzo, kungochita chigololo kamodzi kokha kungaipitse mbiri yabwino. Mu chaputala 6 cha buku la m’Baibulo la Miyambo, Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inachenjeza za mikhalidwe ndi zochitika zomwe zingaipitse mbiri yathu komanso kuwononga unansi wathu ndi Yehova Mulungu. Zina mwa zimenezi ndizo kupanga malumbiro mosalingalira bwino, ulesi, chinyengo, ndi chisembwere​—zinthu zimene kwenikweni Yehova amadana nazo. Kumvera malangizo ameneŵa kudzatithandiza kuteteza dzina lathu labwino.

Dzipulumutseni ku Malumbiro Opusa

Chaputala 6 cha Miyambo chikuyamba ndi mawu akuti: “Mwananga, ngati waperekera mnzako chikole, ngati wapangana kulipirira mlendo, wakodwa ndi mawu am’kamwa mwako, wagwidwa ndi mawu a m’kamwa mwako. Chita ichi tsono; mwananga, nudzipulumutse; popeza waloŵa m’dzanja la mnzako, pita nudzichepetse, num’dandaulire mnzako.”​Miyambo 6:1-3.

Mwambi umenewu ukulangiza kupeŵa kuloŵerera m’zamalonda za ena, makamaka za anthu achilendo. Inde, Aisrayeli anafunikira ‘kuthandiza mbale wawo akasaukira chuma, ndi pamene sangathe kudzisamala.’ (Levitiko 25:35-38) Koma akathyali ena achiisrayeli analoŵerera kwambiri m’zamalonda achinyengo ndipo anapeza chuma chochuluka mwa kukopa ena ‘kuwalipirira chikole’ potero akumaŵagwetsera m’ngongole. Zofananazo zingachitikenso lerolino. Mwachitsanzo, mabugwe azachuma angafune wosainira wachiŵiri asanavomere zopereka ngongole yomwe akulingalira kuti n’njovuta kubweza. N’kupandatu nzeru kudzipereka mosalingalira bwino kukachitira ena umboni pankhani ngati zimenezi! Ndithudi, zingatigwetse m’mavuto azachuma, ngakhalenso kutipatsa dzina loipa ku mabanki komanso ku mabungwe ena okongoza ndalama!

Bwanji ngati tachita chinthu chomwe poyamba chimaoneka ngati n’chabwino koma kupenda mosamalitsa kwasonyeza kuti n’chachabechabe? Uphungu wake n’ngwakuti uchotse kudzikuza “num’dandaulire mnzako”​—kum’pempha mosaleka. Tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tithetse vutolo. Buku lina lamaumboni linati: “Yesayesani njira zonse kufikira mutagwirizana ndi mdani wanu ndipo thetsani nkhaniyo, kuti pangano lanu la ndalama lisakuipireni kapena kuipira banja lanu.” Ndipotu zimenezi ziyenera kuchitidwa mofulumira ndithu, pakuti mfumu ikuwonjezera kuti: “Usaone tulo m’maso mwako, ngakhale kuodzera zikope zako. Dzipulumutse wekha ngati mphoyo ku dzanja la msaki, ndi mbalame ku dzanja la msodzi.” (Miyambo 6:4, 5) Ndi kwabwino kuchoka m’mapangano opusa a zandalama ngati n’kotheka m’malo motcheredwa nawo msampha.

Chitani Khama Monga Nyerere

“Pita kunyerere, waulesi iwe, penya njira zawo nuchenjere,” akulangiza motero Solomo. Ndi nzeru zotani zomwe tingaphunzire pa njira za tinyerere ting’onoting’onoto? Mfumuyo ikuyankha kuti: “Zilibe mfumu, ngakhale kapitawo, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zawo m’malimwe; nizituta zinthu zawo m’masika.”​Miyambo 6:6-8.

Nyerere n’nzogwirizana modabwitsa ndipo zimachitira zinthu limodzi mochititsa chidwi. Mwanzeru zachibadwa, zimasonkhanitsa chakudya cham’tsogolo. Zilibe “mfumu, kapitawo kapena mkulu [‘wolamulira,’ NW].” N’zoona kuti zimakhala ndi manthu, koma ntchito yake n’njoikira mazira basi ndipo ndiye mayi wa nyerere zonsezo. Salamulira. Ngakhale kuti sizikhala ndi mtsogoleri wozilamulira kapena kapitawo woziyang’anira, nyerere zimagwira ntchito mosatopa.

Mofanana ndi nyerere, kodi nafenso sitifunikira kuchita khama? Kugwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa kuti tichite bwino pantchito yanthu n’kwabwino kwa ife kaya pali wotiyang’anira kapena ayi. Inde, kusukulu, kuntchito kwathu, komanso pogwira ntchito zauzimu ndi anzathu, tiyenera kuchita bwino koposa. Monga momwe nyerere zimapindulira ndi khama lawo, momwemonso Mulungu akufuna kuti ‘tione zabwino m’ntchito zathu zonse.’ (Mlaliki 3:13, 22; 5:18) Chikumbumtima chabwino ndi chikhutiro ndizo mphoto ya kugwira ntchito molimbika.”​—Mlaliki 5:12.

Pogwiritsa ntchito mafunso aŵiri odzutsa chidwi, Solomo akuyesa kugalamutsa waulesi kuti asachite zala lende, akumati: “Udzagona mpaka liti, waulesi iwe? Udzauka ku tulo tako liti?” Mwa kuyerekezera kulankhula kwa munthu waulesi, mfumuyo ikupitiriza kuti: “Tulo ta pang’ono, kuodzera pang’ono, kungomanga manja pang’ono, ndi kugona; ndipo umphaŵi wako udzafika ngati mbala, ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa [“msilikali,” NW].” (Miyambo 6:9-11) Pamene waulesi akadagona, umphawi umam’fikira mofulumira ngati wakuba, ndipo kusauka kumam’kantha ngati munthu wonyamula lupanga. Minda ya munthu waulesi siichedwa kumera thengo ndi khwisa. (Miyambo 24:30, 31) Bizinesi yake imaloŵa pansi pa kanthaŵi kochepa. Kodi wolemba anthu ntchito angalekerere waulesi kwautali wotani? Ndipo kodi wophunzira amene n’ngwaulesi n’kuŵerenga angayembekezere kuchita bwino kusukulu?

Khalani Oona Mtima

Potchula khalidwe linanso limene limawononga mbiri ya munthu komanso unansi wake ndi Mulungu, Solomo akupitiriza kuti: “Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu; amayenda ndi m’kamwa mokhota; amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake, amalankhula ndi zala zake; zopotoka zili m’mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu.”​Miyambo 6:12-14.

Mawu ameneŵa akunena za munthu wachinyengo. Kaŵirikaŵiri wabodza amayesa kubisa bodza lakelo. Motani? Osati ndi “m’kamwa mokhota” mokha komanso polankhula ndi manja. Katswiri wina wa zamaphunziro anati: “Kulankhula ndi manja, kamvekedwe ka mawu, ngakhalenso kaonekedwe ka nkhope ndiwo machenjera enanso amene amagwiritsidwa ntchito pochita chinyengo; kuseli kwa maonekedwe okoma mtimawo kumakhala kuli maganizo oipa ndi mzimu wa kusagwirizana.” Munthu wopanda pake woteroyo amaganiza zochita zinthu zonyansa ndipo nthaŵi zonse amayambitsa mikangano. Kodi chidzam’chitikira n’chiyani?

“Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka,” ikuyankha motero mfumu ya Israyeli. “Adzasweka msangamsanga, palibe chom’pulumutsa.” (Miyambo 6:15) Akadziŵika kuti n’ngwabodza, mbiri yake imawonongeka msangamsanga. Ndani adzam’khulupiriranso? Ndithudi mapeto ake n’ngomvetsa chisoni kwambiri, chifukwa chakuti “onse a mabodza” andandalikidwa limodzi ndi anthu omwe chilango chawo chidzakhala imfa yosatha. (Chivumbulutso 21:8) Mwa njira iliyonse, tiyenera kuyesetsa “kukhala nawo makhalidwe abwino.”​—Ahebri 13:18.

Danani Ndi Chimene Yehova Amadana Nacho

Kudana ndi choipa​—si mmene kumatetezera kupeŵa kuchita zinthu zomwe zingawononge mbiri yathu! Kodi si koyenera tsono kukulitsa chizoloŵezi chodana ndi chomwe chili choipa? Komano chenicheni chomwe tiyenera kudana nacho n’chiyani? Solomo akufotokoza kuti: “Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Mulungu azida; ngakhale zisanu ndi ziŵiri zim’nyansa: maso a kunyada, lilime lonama ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziŵembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu mmangummangu; mboni yonama yonong’ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.”​Miyambo 6:16-19.

Zinthu zisanu ndi ziŵiri zomwe miyambo akutchula ndizo zikuluzikulu ndipo zikuphatikizamo pafupifupi mitundu yonse ya machimo. “Maso akunyada” ndi “mtima woganizira ziŵembu zoipa” ndi machimo omwe amachitidwa m’maganizo. “Lilime lonama” ndi “mboni yonama yonong’ona mabodza” ndiwo machimo apakamwa. “Manja akupha anthu osachimwa” ndi “mapazi akuthamangira mphulupulu mmangummangu” ndizo machitachita onyansa. Ndipo chomwe Yehova amadana nacho kwambiri ndicho mthirakuŵiri yemwe amakondwera kwambiri kuyambanitsa anthu omwe akanatha kukhalira limodzi mwamtendere. Kuwonjezeka kwa chiŵerengerocho kuchoka pa zisanu ndi chimodzi kufika pa zisanu ndi ziŵiri kukusonyeza kuti ndandandayo sinafike kumapeto, chifukwa chakuti anthu akupitirizabe kuwonjezera zoipa zomwe amachita.

Ndithudi, tifunikira kudana kwambiri ndi zinthu zomwe Mulungu amadana nazo. Mwachitsanzo, tiyenera kupeŵa “maso akunyada” kapena kusonyeza kunyada m’njira ina iliyonse. Ndipo kunong’ona mabodza oipa ndithudi kuyenera kupeŵedwa, chifukwa chakuti ‘kungapikisanitse abale’ mosavuta. Mwa kufalitsa mphekesera yoipa, mijedo yachinyengo, kapena mabodza, sitingati “[ti]kupha anthu osachimwa,” koma kunena zoona tingawononge mbiri yabwino ya munthu wina.

‘Usasirire Kukongola Kwake’

Solomo akuyamba chigawo chotsatira cha uphungu wake mwa kunena kuti: “Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a amako; uwamange pamtima pako osaleka; uwalunze pakhosi pako.” Chifukwa chake? “Adzakutsogolera ulikuyenda, ndi kukudikira uli m’tulo. Ndi kulankhula nawe utauka.”​Miyambo 6:20-22.

Kodi kukula mwa Malemba kungatiteteze ku msampha wa chisembwere? Inde, kungatitetezedi. Akutitsimikizira kuti: “Malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo; zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi ku lilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere.” (Miyambo 6:23, 24) Kukumbukira uphungu wa m’Mawu a Mulungu ndi kuugwiritsa ntchito monga ‘nyali ya ku mapazi athu, ndi kuunika kwa panjira pathu’ kudzatithandiza kusamvera mawu okopa a mkazi wa mikhalidwe yoipa, kapena a mwamuna woipa.​—Salmo 119:105.

“Asakuchititse kaso m’mtima mwako,” ikuchenjeza motero mfumu yanzeruyo, “asakukole ndi zikope zake.” Chifukwa chiyani? “Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama [“Hule,” NW], udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatali.”​Miyambo 6:25, 26.

Kodi Solomo akutchula mkazi wokwatiwa wachigololo kukhala hule? Mwinamwake. Kapena n’zotheka kuti akusiyanitsa zotsatira za kuchita chisembwere ndi hule ndi zotsatira za kuchita chigololo ndi mkazi wamwini. Amene ali paubwenzi ndi hule angathe kunyenyeka ndi kukhala ngati ‘nyenyeswa,’ angagwe mu umphawi wadzaoneni. Angathenso kutenga matenda opatsirana mwa kugonana opweteka kwambiri ndi opundula, kuphatikizapo AIDS yakuphayo. Komabe, munthu wofuna kupanga chibwenzi ndi mkazi wamwini angakhale pangozi yaikulu mwachindunji pansi pa Chilamulo. Mkazi wokwatiwa wochita chigololo amaika pangozi “moyo wa mtengo wapatali” wa bwenzi lake lamtserilo. Buku lina la maumboni linati: “Kuposa kufupikitsa moyo mwa kusadziletsa . . . amayembekezera chinthu chinanso. Wochimwayo n’ngoyenera kulandira chilango cha imfa.” (Levitiko 20:10; Deuteronomo 22:22) Mwanjira iliyonse, mosasamala kanthu za kukongola kwake, mkazi wotero si woyenera kukopeka naye.

‘Musatenge Moto Pachifuwa Chanu’

Pogogomeza kuopsa kwa chigololo, Solomo akupitiriza kufunsa kuti: “Kodi mwamuna angatenge moto pachifuwa chake, osatentha zovala zake? Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake?” Pofotokoza tanthauzo la fanizolo, iye akuti: “Chomwecho woloŵa kwa mkazi wa mnzake; wom’khudzayo sadzapulumuka chilango.” (Miyambo 6:27-29) Wochimwa wotero adzalangidwa ndithu.

“Anthu sanyoza mbala ikaba, kuti ikhutitse mtima wake pomva njala,” akutikumbutsa motero. Komabe, “ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kaŵiri; idzapereka chuma chonse cha m’nyumba yake.” (Miyambo 6:30, 31) Mu Israyeli wakale, mbala inkafunikira kulipira ngakhale kuti zikatanthauza kupereka zonse zimene anali nazo. * Chotero n’koyeneratu kwambiri kupereka chilango kwa munthu wachigololo, yemwe alibiretu choŵiringula pa chomwe wachitacho!

“Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru,” akutero Solomo. Munthu wopanda nzeru n’ngwosalingalira bwino, chifukwa chakuti iye “[ama]wononga moyo wakewake.” (Miyambo 6:32) M’kaonekedwe kakunja, angaoneke ngati munthu wolemekezeka, koma munthu wam’kati ali ndi vuto lalikulu la kusoŵa uchikulire weniweni.

Pali zambiri zomwe wachigololo amatuta. “Adzalasidwa nanyozedwa; chitonzo chake sichidzafafanizidwa. Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna, ndipo sadzachitira chifundo tsiku lobwezera chilango. Sadzalabadira chiwombolo chilichonse, sadzapembedzeka ngakhale uchulukitsa malipo.”​Miyambo 6:33-35.

Wakuba angalipirire zomwe anaba, koma wachigololo sangalipire chilichonse kuti asalandire chilango. Angalipire chiyani kwa mwamuna waukali? Ngakhale atachonderera motani, n’zokayikitsa ngati wolakwayo angachitiridwe chifundo. Palibe njira iliyonse imene wachigololo angakonzere tchimo lake. Chitonzo ndi manyazi zounjikana padzina lake sizichoka konse. Komanso, mwanjira iliyonse sangathe kudziwombola kapena kudzigulira yekha ufulu kuti asalandire chilango pa mlandu wakewo.

Ndithudi n’kwanzeru kukhala wosadetsedwa ndi chigololo komanso zochitika zina kapena mikhalidwe imene ingaipitse dzina lathu labwino imenenso ingadzetse chitonzo pa Mulungu! Choncho, tisamaletu kwambiri mwa kusapanga malonjezo opusa. Tilole khama ndi chilungamo kukometsera mbiri yathu. Ndipo pamene tikuyesetsa kudana ndi zimene Yehova amadana nazo, tipangetu dzina labwino ndi iye komanso ndi anthu anzathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 28 Malinga ndi Chilamulo cha Mose, wakuba ankayenera kubwezera kuŵirikiza kawiri, kanayi, kapena kuŵirikiza kasanu. (Eksodo 22:1-4) Mawu akuti “kasanu ndi kaŵiri” mwachionekere akutanthauza chilango cha kalavula gaga, chomwe chingathe kukhala kuŵirikiza kambirimbiri zomwe anali atabazo.

[Chithunzi patsamba 25]

Khalani wosamala kwambiri pothandiza kusainira ngongole

[Chithunzi patsamba 26]

Gwirani ntchito mwakhama ngati nyerere

[Chithunzi patsamba 27]

Peŵani miseche yachabe