Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Yafika Nthaŵi”!

“Yafika Nthaŵi”!

“Yafika Nthaŵi”!

“Nthaŵi yake idadza yakuchoka kutuluka m’dziko lino lapansi, kumka kwa Atate.”​—YOHANE 13:1.

1. Pamene Paskha wa mu 33 C.E. akuyandikira, anthu m’Yerusalemu ali chire ndi nkhani yotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

ATANGOBATIZIDWA mu 29 C.E., Yesu anayamba moyo womwe unali kudzam’fikitsa pa “nthaŵi” ya imfa yake, kuukitsidwa, ndi ulemerero. Tsopano ndi nyengo ya ngululu ya mu 33 C.E. Pangopita milungu yochepa kuchokera pamene bwalo lamilandu lalikulu lachiyuda, Sanihedirini, linapangana kupha Yesu. Atadziŵa zimene akufuna kuchita, mwina atamva kwa Nikodemo, woweruza wa m’Sanihedirini amene wakhala waubwenzi kwa iye, Yesu watulukamo m’Yerusalemu ndipo wapita kumidzi ya kutsidya la Mtsinje wa Yordano. Pamene Phwando la Paskha liyandikira, anthu akusonkhana m’Yerusalemu kuchokera kumidzi, ndipo nkhani imene ili m’kamwa mwa anthu mumzindawu ndi ya Yesu. “Muyesa bwanji inu?” akufunsana motero. “Sadzadza kuphwando kodi?” Ansembe aakulu ndi Afarisi akuwonjezera kugunda kwa mitima ya anthuwo mwa kulamula kuti aliyense amene adzaona Yesu adzawauze kumene ali.​—Yohane 11:47-57.

2. Kodi Mariya wachita chiyani chimene chikuyambitsa mkangano, ndipo yankho la Yesu pom’teteza likusonyezanji ponena za kudziŵa kwake “nthaŵi yake”?

2 Pa Nisani 8, masiku asanu ndi limodzi tsiku la Paskha lisanafike, Yesu akupezekanso kufupi ndi Yerusalemu. Iye wabwera ku Betaniya, mudzi wakwawo kwa mabwenzi ake Marita, Mariya, ndi Lazaro, makilomita ngati atatu kuchokera ku Yerusalemu. Ndi Lachisanu madzulo, ndipo Yesu akukhala kumeneko kaamba ka Sabata. Tsiku lotsatira madzulo pamene Mariya akum’tumikira pogwiritsa ntchito mafuta a mtengo wapamwamba koposa, ophunzirawo sakusangalala. Yesu akuyankha kuti: “Mleke iye, pakuti anachisungira ichi tsiku la kuikidwa kwanga. Pakuti osauka muli nawo pamodzi ndi inu nthaŵi zonse; koma simuli ndi Ine nthaŵi zonse.” (Yohane 12:1-8; Mateyu 26:6-13) Yesu akudziŵa kuti ‘nthaŵi yake yadza yakuchoka kutuluka m’dziko lino lapansi, kumka kwa Atate.’ (Yohane 13:1) Kwangotsala masiku asanu kuti ‘apereke moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.’ (Marko 10:45) Kuyambira pamenepo, zonse zimene Yesu akuchita ndi kuphunzitsa akuzichita mwachangu. Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife pamene tikudikira mwachidwi mapeto a dongosolo ili la zinthu! Taonani zimene zinachitika kwa Yesu tsiku lotsatira.

Tsiku la Yesu Loloŵa Mwaulemerero

3. (a) Kodi Yesu akuloŵa motani m’Yerusalemu Lamlungu pa Nisani 9, ndipo anthu ambiri om’zungulira akutani? (b) Kodi Yesu akuwayankha motani Afarisi amene akudandaula za khamulo?

3 Lamlungu, pa Nisani 9, Yesu akudza ku Yerusalemu mwaulemero. Pamene akuyandikira mzindawo, atakwera pa mwana wamphongo wa bulu mokwaniritsa Zekariya 9:9, anthu ochuluka amene asonkhana kudzamuona akuyala malaya awo pamsewu, pamene ena akudula nthambi za mitengo ndi kuziyala pansi. “Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m’dzina la Ambuye,” iwo akufuula motero. Afarisi ena m’chikhamucho akufuna kuti Yesu adzudzule ophunzira ake. Koma Yesu akuwayankha kuti: “Ndinena ndi inu, ngati aŵa akhala chete miyala idzafuula.”​—Luka 19:38-40; Mateyu 21:6-9.

4. N’chifukwa chiyani m’Yerusalemu mukuyambika chipwirikiti pamene Yesu akuloŵa mumzindawo?

4 Milungu yochepa zimenezi zisanachitike, ochuluka m’khamulo anamuona Yesu akuukitsa Lazaro. Tsopano ameneŵa akusimbirabe ena za chozizwitsacho. Chotero pamene Yesu akuloŵa m’Yerusalemu, chipwirikiti chikuyambika mumzindawu. “Ndani uyu?” anthu akufunsa motero. Ndipo makamuwo akunenabe kuti: “Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.” Poona zimene zikuchitika, Afarisi akudandaula kuti: “Dziko litsata pambuyo pake pa Iye.”​—Mateyu 21:10, 11; Yohane 12:17-19.

5. N’chiyani chikuchitika pamene Yesu akupita ku kachisi?

5 Mwachizoloŵezi chake pochezera Yerusalemu, Yesu, Mphunzitsi Wamkulu, akupita ku kachisi kukaphunzitsa. Kumeneko anthu akhungu ndi olumala akudza kwa iye, ndipo akuwachiritsa. Pamene ansembe aakulu ndi alembi aona zimenezi ndipo akumva ana m’kachisi akufuula kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide,” iwo akupsa mtima. “Mulinkumva kodi chimene alikunena awa?” iwo akukalipa. Yesu akuwayankha kuti: “Inde: simunaŵerenga kodi, Mkamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?” Pamene Yesu akupitiriza kuphunzitsa, iye akuona zonse zimene zikuchitika m’kachisimo.​—Mateyu 21:15, 16; Marko 11:11.

6. Kodi zochita za Yesu zikusiyana motani tsopano ndi zimene anachita poyamba, ndipo n’chifukwa chiyani?

6 Zochita za Yesu n’zosiyana kwambiri tsopano ndi zimene anachita miyezi isanu ndi umodzi yapitayo! Panthaŵiyo, analoŵa m’Yerusalemu kudzachita Phwando la Misasa, “si poonekera, koma monga mobisalika.” (Yohane 7:10) Ndipo nthaŵi zonse anali wosamala kwambiri kuchoka pamalo ngati moyo wake wakhala pangozi. Koma tsopano akuloŵa moonekera mumzinda momwe anthu auzidwa kuti am’gwire! Komanso Yesu sanali kudzilengeza kuti ndi Mesiya. (Yesaya 42:2; Marko 1:40-44) Sanali kufuna kudzilengeza mosokosera ena kapenanso kuti nkhani zopindika zonena za iye zifalitsidwe ndi anthu. Makamu tsopano akum’lengeza poyera kuti ndiye Mfumu ndi Mpulumutsi​—Mesiya​—ndipo akudzudzula atsogoleri achipembedzo pomuuza kuti aletse makamu ameneŵa kunena zinthuzo! N’chifukwa chiyani wasintha? Chifukwa chakuti “yafika nthaŵi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe,” monga momwe Yesu akulengezera tsiku lotsatira.​—Yohane 12:23.

Kuchita Chamuna​—Kenako Ziphunzitso Zopulumutsa Moyo

7, 8. Kodi zochita za Yesu pa Nisani 10, mu 33 C.E., zikufanana motani ndi zimene anachita m’kachisi pa Paskha wa mu 30 C.E.?

7 Atafika pakachisi Lolemba, pa Nisani 10, Yesu akuchitapo kanthu pa zimene anaona masana a dzulo. Akuyamba “kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda m’Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda; ndipo sa[ku]lola munthu aliyense kunyamula chotengera kupyola pakati pa Kachisi.” Podzudzula olakwawo, iye akuti: “Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.”​—Marko 11:15-17.

8 Zimene Yesu wachita zafanana ndi zimene anachita zaka zitatu zapitazo pamene anapita kukachisi pa Paskha wa mu 30 C.E. Koma chidzudzulo chake panthaŵi ino n’choŵaŵa kusiyana ndi choyamba chija. Amalonda a m’kachisi tsopano akutchedwa “achifwamba.” (Luka 19:45, 46; Yohane 2:13-16) Ndi otero chifukwa chakuti akudulitsa kwambiri zinthu zawo kwa anthu amene akufuna kugula ziŵeto zokapereka nsembe. Ansembe aakulu, alembi, ndi akulu a anthu amva zimene Yesu akuchita ndipo kachiŵirinso akufunafuna njira zom’phera. Koma sakudziŵa kuti athana naye bwanji Yesuyo, popeza anthu onse, pochita chidwi ndi chiphunzitso chake, akum’mamatira kuti amvetsere.​—Marko 11:18; Luka 19:47, 48.

9. Kodi Yesu akuphunzitsa phunziro lotani, ndipo kodi omvetsera ake pakachisi akuwapempha kuti chiyani?

9 Pamene Yesu akupitiriza kuphunzitsa m’kachisi, iye akuti: “Yafika nthaŵi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe.” Inde, iye akudziŵa bwino kuti wangotsala ndi masiku ochepa a moyo wake monga munthu padziko lapansi. Atalongosola mmene mbewu ya tirigu iyenera kufa kaye kuti ibale chipatso​—kuimira imfa yake ndi kukhala kwake njira yoperekera moyo kwa ena​—Yesu akupempha omvetsera ake kuti: “Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzam’chitira ulemu iyeyu.”​—Yohane 12:23-26.

10. Kodi Yesu akumva bwanji ponena za imfa yoŵaŵa imene adzafa?

10 Poganizira za imfa yake yoŵaŵa yomwe adzafa pakangopita masiku anayi okha, Yesu akupitiriza kuti: “Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine ku nthaŵi iyi.” Koma zimene Yesu adzakumana nazo n’zosapeŵeka. “Koma,” iye akutero, “chifukwa cha ichi ndinadzera nthaŵi iyi.” Inde, Yesu akugwirizana ndi makonzedwe onse a Mulungu. Ndi wotsimikiza mtima kulola chifuniro cha Mulungu kutsogolera zochita zake mpaka pa imfa yake yansembe. (Yohane 12:27) N’chitsanzo chabwino kwambiri chimene anatipatsa​—chosonyeza kugonjera ku chifuniro cha Mulungu ndi mtima wonse!

11. Ndi ziphunzitso zotani zimene Yesu akuphunzitsa khamu lomwe langomva kumene mawu ochokera kumwamba?

11 Podera nkhaŵa kwambiri ndi mmene imfa yake idzakhudzira mbiri ya Atate wake, Yesu akupemphera kuti: “Atate, lemekezani dzina lanu.” Khamu lomwe lili m’kachisi likudabwa pamene kukumveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.” Mphunzitsi Wamkuluyo akugwiritsa ntchito mpata umenewu kuuza khamulo chifukwa chimene mawuwo amvekera, zomwe zidzakhala zotsatira za imfa yake, ndi chifukwa chimene iwo ayenera kusonyezera chikhulupiriro. (Yohane 12:28-36) Yesu wakhala ndi zochita zambiri pamasiku aŵiri omaliza. Koma tsiku lalikulu lidakali patsogolo.

Tsiku la Chidzudzulo

12. Lachiŵiri pa Nisani 11, kodi atsogoleri achipembedzo akuyesa motani kukola Yesu, ndipo n’chiyani chikuchitika?

12 Lachiŵiri, pa Nisani 11, Yesu akuloŵanso m’kachisi kukaphunzitsa. Pali omvetsera aukali. Ponena za zimene Yesu anachita dzulo lake, ansembe aakulu ndi akulu a anthu akum’funsa kuti: “Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?” Mphunzitsi Wamkulu akuwasokoneza ndi yankho lake, ndipo akusimba mafanizo atatu osaiŵalika​—aŵiri onena za munda wa mpesa ndipo limodzi lonena za phwando laukwati​—osonyeza kuipa mtima kwa om’tsutsa. Atakwiya ndi zimene amva, atsogoleri achipembedzo akufuna kum’gwira. Koma iwo akuopa khamulo, lomwe limaona Yesu monga mneneri. Chotero akuyesa kum’kola kuti anene mawu ena amene angam’pezere chifukwa chom’mangira. Mayankho amene Yesu akupereka akuwasoŵetsa chonena.​—Mateyu 21:23–22:46.

13. Kodi Yesu akuwalangiza motani omvetsera ake ponena za alembi ndi Afarisi?

13 Popeza kuti alembi ndi Afarisi amanena kuti amaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu, Yesu akulimbikitsa omvetsera ake kuti: “Zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zawo; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.” (Mateyu 23:1-3) Chidzudzulo champhamvu chapoyera chimenechi! Koma Yesu sanathane nawobe. Ili ndi tsiku lake lomalizira pa kachisi, ndipo molimba mtima akuvumbula zochita zawo zonse​—chimodzi ndi chimodzi ngati bingu losatha.

14, 15. Kodi ndi chidzudzulo chopyoza chiti chimene Yesu akupereka kwa alembi ndi Afarisi?

14 “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga!” Yesu akunena motero kasanu ndi kamodzi. Iwo ndi onyenga chifukwa chakuti, monga momwe Yesu akulongosolera, atsekera anthu Ufumu wakumwamba, kuletsa amene akuloŵamo kuti asaloŵemo. Onyenga ameneŵa adutsa nyanja ndi mtunda kuti akatembenuze munthu mmodzi, n’kum’panga mwana wa chiwonongeko chosatha. Ponyalanyaza “zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro,” iwo asamala kwambiri za kupereka chachikhumi. Kwenikweni, akutsuka “kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m’katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa” chifukwa chakuti akubisa kuvunda kwawo kwam’kati podzionetsera ngati achipembedzo. Kuwonjezera apo, iwo amamanga manda a aneneri ndi kuwakongoletsa kungofuna kuti aonetsere poyera zimene akuchitira anthu ena, ngakhale kuti iwo ndi “ana a iwo amene anapha aneneri.”​—Mateyu 23:13-15, 23-31.

15 Podzudzula om’tsutsawo chifukwa cha kusayamikira kwawo zinthu zauzimu, Yesu akuti: “Tsoka inu, atsogoleri akhungu.” Kunena za khalidwe, iwo n’ngakhungu chifukwa chakuti amagogomezera kwambiri kufunika kwa golidi wa kachisi m’malo mwa kufunika kwauzimu kwa malo olambirirawo. Popitiriza, Yesu akutulutsa mawu ake opyoza kwambiri owadzudzula. Iye akuti: “Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthaŵa kulanga kwake kwa gehena?” Inde, Yesu akuwauza kuti chifukwa chotsatira njira yawo yoipayo, iwo adzawonongedwa kotheratu. (Mateyu 23:16-22, 33) Ifenso tikhale olimba mtima polengeza uthenga wa Ufumu, ngakhale pamene zingaphatikizepo kuvumbula chipembedzo chonyenga.

16. Atakhala m’Phiri la Azitona, kodi Yesu akupatsa ophunzira ake ulosi wofunika uti?

16 Kenako Yesu akutuluka m’kachisi. Pamene dzuŵa likupendekeka, iye ndi atumwi ake akukwera Phiri la Azitona. Atakhala kumeneko, Yesu akupereka ulosi wonena za kuwonongedwa kwa kachisi ndi chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu. Mpaka m’nthaŵi yathu ino, mawu aulosi amenewo ndi ofunikabe. Madzulo amenewo, Yesu akuuza ophunzira ake kuti: “Mudziŵa kuti akapita masiku aŵiri, Paskha ufika, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kupachikidwa pamtanda [“mtengo wozunzirapo,” NW].”​—Mateyu 24:1-14; 26:1, 2.

Yesu ‘Akonda Ake a Iye Yekha Kufikira Chimaliziro’

17. (a) Pochita Paskha pa Nisani 14, kodi ndi phunziro lotani limene Yesu akuphunzitsa atumwi 12 amenewo? (b) Ndi chikumbukiro chotani chimene Yesu akuyambitsa pambuyo potulutsa Yudase Isikariote?

17 Pamasiku aŵiri otsatira​—Nisani 12 ndi 13​—Yesu sakudzionetsera pakachisi. Atsogoleri achipembedzo akufuna kumupha, ndipo iye sakufuna kuti chilichonse chim’sokoneze kuchita Paskha ndi atumwi ake. Lachinayi pamene dzuŵa likuloŵa, tsiku la Nisani 14 likuyamba​—tsiku lomaliza la moyo wa Yesu monga munthu wapadziko lapansi. Madzulo amenewo, Yesu ndi atumwi ake ali limodzi m’nyumba ina ya m’Yerusalemu kumene akonzekera kukachitirako Paskha. Pamene akuchita Paskha pamodzi, akuphunzitsa atumwi 12 amenewo phunziro labwino la kudzichepetsa mwa kusambitsa mapazi awo. Atatulutsa Yudase Isikariote, amene walola kupereka Ambuye ake pamtengo wa ndalama zasiliva makumi atatu​—mtengo wa kapolo wamba malinga ndi Chilamulo cha Mose​—Yesu akuyambitsa Chikumbutso cha imfa yake.​—Eksodo 21:32; Mateyu 26:14, 15, 26-29; Yohane 13:2-30.

18. N’chiyaninso chimene Yesu mwachikondi akuphunzitsa atumwi ake 11 okhulupirikawo, ndipo akuwakonzekeretsa motani kaamba ka kuchoka kwake komwe kwayandikirako?

18 Atachita Chikumbutso choyambirira chimenecho, atumwi akuyamba kutsutsana kwadzaoneni pankhani yonena kuti wamkulu ndani pakati pawo. M’malo mowakalipira, Yesu moleza mtima akuwaphunzitsa za kufunika kotumikira ena. Pozindikira bwino kuti iwo akhala naye m’mayesero ake, akupanga nawo pangano la ufumu. (Luka 22:24-30) Yesu akuwalamulanso kuti azikondana monga momwe iye anawakondera. (Yohane 13:34) Ali chikhalirebe m’chipindamo, Yesu mwachikondi akuwakonzekeretsa kaamba ka kuchoka kwake komwe kwayandikira. Akuwatsimikizira kuti iwo ali mabwenzi ake, kuwalimbikitsa kusonyeza chikhulupiriro, ndipo akuwalonjeza kuti mzimu woyera udzawathandiza. (Yohane 14:1-17; 15:15) Asanatuluke m’nyumbamo, Yesu akuchonderera Atate wake kuti: “Yafika nthaŵi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu.” Ndithudi, Yesu wakonzekeretsa atumwiwo za kuchoka kwake, ndipo ndithudi ‘wakonda ake a iye yekha kufikira chimaliziro.’​—Yohane 13:1; 17:1.

19. N’chifukwa chiyani Yesu ali ndi nkhaŵa yaikulu m’munda wa Getsemane?

19 Mwina nthaŵi yapitirira pakati pa usiku pamene Yesu ndi atumwi ake 11 okhulupirikawo akufika m’munda wa Getsemane. Nthaŵi zambiri ankapita kumeneko ndi atumwi ake. (Yohane 18:1, 2) Kwangotsala maola ochepa kuti Yesu afe monga kuti anali mpandu woipitsitsa. Nkhaŵa ya chochitika chimenechi komanso mmene chingadzetsere chitonzo pa Atate wake n’njaikulu kwambiri moti pamene Yesu akupemphera, thukuta lake likugwera pansi ngati madontho a magazi. (Luka 22:41-44) “Yafika nthaŵi.” Yesu akuuza atumwi ake. “Onani wakundiperekayo ali pafupi.” Mawu ali m’kamwa, Yudase Isikariote akufika, atatsagana ndi chikhamu cha anthu onyamula miuni ndi nyali ndi zida. Iwo abwera kudzagwira Yesu. Iye sakukana. Akufotokoza kuti: “Pakutero, malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?”​—Marko 14:41-43; Mateyu 26:48-54.

Mwana wa Munthu Alandira Ulemerero!

20. (a) Kodi Yesu akukumana ndi nkhanza zotani atamangidwa? (b) Kutangotsala timphindi kuti afe, n’chifukwa chiyani Yesu akufuula kuti: “Kwatha”?

20 Atamangidwa, Yesu akuimbidwa mlandu ndi mboni zonama, kupezedwa mlandu ndi oweruza okondera, kuweruzidwa ndi Pontiyo Pilato, kunyozedwa ndi ansembe ndi makamu a anthu, ndi kutonzedwa ndi kuzunzidwa ndi asilikali. (Marko 14:53-65; 15:1, 15; Yohane 19:1-3) Podzafika Lachisanu masana, Yesu akukhomeredwa pamtengo wozunzirapo ndi misomali ndipo akumva ululu waukulu pamene kulemera kwa thupi lake kupangitsa kuti mnofu ung’ambike m’manja ndi m’mapazi ake mmene akhoma misomali. (Yohane 19:17, 18) Cha m’ma 3 koloko masana, Yesu akufuula kuti: “Kwatha.” Inde, iye wamaliza zonse zimene anabwera kudzachita padziko lapansi. Popereka mzimu wake kwa Mulungu, akuwerama mutu ndi kumwalira. (Yohane 19:28, 30; Mateyu 27:45, 46; Luka 23:46) Patsiku lachitatu kuchokera pamene wamwalira, Yehova akuukitsa Mwana wake. (Marko 16:1-6) Masiku 40 pambuyo pa kuukitsidwa kwake, Yesu akukwera kumwamba ndipo akulandira ulemerero.​—Yohane 17:5; Machitidwe 1:3, 9-12; Afilipi 2:8-11.

21. Kodi Yesu tingam’tsanzire motani?

21 Kodi mapazi a ‘Yesu tingawalondole’ motani? (1 Petro 2:21) Mofanana naye, tiyeni tiyesetse mwamphamvu pogwira ntchito yolalikira za Ufumu ndi yopanga ophunzira ndipo tikhale olimba mtima poyankhula mawu a Mulungu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Machitidwe 4:29-31; Afilipi 1:14) Tisaiwale konse kuti tili m’nthaŵi yotani kapena kulephera kufulumizana kuchikondano ndi ntchito zabwino. (Marko 13:28-33; Ahebri 10:24, 25) Tiyeni tilole zochita zathu zonse kutsogoleredwa ndi chifuniro cha Yehova Mulungu pokhalanso ozindikira kuti tikukhala mu “nthaŵi ya chimaliziro.”​—Danieli 12:4.

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi kudziŵa kwa Yesu kuti imfa yake inali pafupi kunakhudza motani utumiki wake womalizira pakachisi ku Yerusalemu?

• N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ‘anakonda ake a iye yekha kufikira chimaliziro’?

• Kodi zochitika m’maola ochepa omalizira a moyo wa Yesu zinasonyeza chiyani ponena za iye?

• Kodi Kristu Yesu tingam’tsanzire motani mu utumiki wathu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Yesu “anawakonda kufikira chimaliziro”