Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimwemwe Chosatha—Kumwamba Kapena Padziko Lapansi?

Chimwemwe Chosatha—Kumwamba Kapena Padziko Lapansi?

Chimwemwe Chosatha​—Kumwamba Kapena Padziko Lapansi?

KODI chimwemwe chanu chimadalira kwenikweni kumene mukukhala? Anthu ambiri angavomereze mosakaika kuti chimwemwe chimadalira kwambiri pa zinthu monga thanzi labwino, kukhala ndi cholinga m’moyo, ndi unansi wabwino ndi anthu ena. Mwambi wina m’Baibulo umati: “Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng’ombe yonenepa pali udani.”​—Miyambo 15:17.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti mudzi wathuwu, dziko lapansi, waona udani, chiwawa, ndi mitundu ina ya zoipa, kuyambira kalekale. Koma bwanji za kumwamba, kapena kuti malo a mizimu, kumene anthu ambiri amati adzapita akamwalira? Kodi kwangokhala kwabata ndi mtendere basi, popanda zosokoneza za mtundu uliwonse, monga momwe ambiri amaganizira?

Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu amakhala kumwamba pamodzi ndi mamiliyoni ambiri a zolengedwa zauzimu zotchedwa angelo. (Mateyu 18:10; Chivumbulutso 5:11) Angeloŵa amanenedwa kukhala ‘ana a Mulungu.’ (Yobu 38:4, 7) Mofanana ndi anthu, angelonso ali ndi ufulu wa kudzisankhira; sali ngati makina osaganiza. Chotero, iwonso angasankhe kuchita chabwino kapena kuchita choipa. Kodi angelo angasankhe kuchita choipa? Ena angadabwe kumva kuti zaka zikwi zambiri kalelo, angelo ambiri ndithu, kunena molunjika, anachimwira Mulungu​—anam’pandukira!​—Yuda 6.

Apandu Kumwamba

Uchimo unaonekera m’malo a mizimu chifukwa cha kupanduka kwa mngelo wina, yemwe anadzatchedwa kuti Satana (Wotsutsa) ndi Mdyerekezi (Woneneza). Mngelo ameneyu yemwe poyamba anali womvera anadzisankhira yekha kuchita choipa. Kenako anayamba kuipitsa malingaliro a zolengedwa zinanso zauzimu, kotero kuti podzafika nthaŵi ya Nowa, Chigumula chisanachitike, zolengedwa zambiri zimenezi zinagwirizana ndi Satana popandukira Mulungu.​—Genesis 6:2, NW, mawu am’munsi; 2 Petro 2:4.

Angelo ochimwa ameneŵa sanathamangitsidwe kumwamba nthaŵi yomweyo. M’malo mwake, iwo ankakhalabe komweko​—mwachionekere atawaletsa zinthu zina​—kwa zaka zikwi zambiri. * Komabe, Mulungu ataleka kulolera ochimwa ameneŵa, iwo ‘anaponyedwa’ pansi kuchokera kumwamba, kuti pamapeto pake adzawonongedwe. Ndiyeno kunamveka mawu kumwamba akuti: “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo.” (Chivumbulutso 12:7-12) M’posakayikitsa kuti angelo okhulupirika anasangalala kwambiri kuti, pomalizira pake, kumwamba kunalibenso angelo onyansa amenewo oyambitsa mavuto!

Polingalira mfundo zosadziŵika ndi anthu ambiri zimenezi, n’zoonekeratu kuti paliponse pamene zolengedwa zolingalira zinyalanyaza malamulo a Mulungu ndi mfundo zake zachikhalidwe sipakhala mtendere weniweni. (Yesaya 57:20, 21; Yeremiya 14:19, 20) Koma pamene onse amvera lamulo la Mulungu, pamakhala bata ndi mtendere. (Salmo 119:165; Yesaya 48:17, 18) Chotero, zikanakhala kuti anthu onse amakonda Mulungu ndi kum’mvera ndipo amakondana iwo eni, kodi dziko lapansi silikanakhala malo osangalatsa, achimwemwe chokhachokha? Baibulo limayankha kuti inde!

Nanga bwanji za anthu amene mwadyera safuna kusintha njira zawo zoipa? Kodi adzakhala akusokoneza mtendere wa anthu amene akufunadi kuchita chifuniro cha Mulungu mpaka kalekale? Iyayi, Mulungu sanalekerere angelo oipawo kumwamba, ndipo sadzalekerera anthu oipa pano padziko lapansi.

Dziko Lapansi Loyeretsedwa Bwino

“Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga,” anatero Mulungu. (Yesaya 66:1) Popeza iye ndiye chimake cha kuyera kopatulika, Mulungu sadzalola kuti “choikapo mapazi” ake chikhale chodetsedwa ndi zoipa kunthaŵi zosatha. (Yesaya 6:1-3; Chivumbulutso 4:8) Monga momwe anachotserako mizimu yoipa kumwamba, adzachotsaponso anthu onse oipa padziko lapansi, monga momwe malemba a m’Baibulo otsatiraŵa amasonyezera:

“Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwoŵa adzalandira dziko lapansi.”​—Salmo 37:9.

“Owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”​—Miyambo 2:21, 22.

“N’kolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso, ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha chowasiyanitsa ku nkhope ya Ambuye, ndi ku ulemerero wa mphamvu yake.”​—2 Atesalonika 1:6-9.

“Dziko lapansi [la anthu oipa] lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”​—1 Yohane 2:17.

Kodi Dziko Lapansi Lidzakhalabe la Mtendere?

Ngakhale kuti Malemba amasonyeza bwino lomwe kuti kulolera anthu oipa kwa Mulungu kuli ndi malire ake, kodi tingatsimikizire motani kuti zoipa, zikadzachotsedwapo, sizidzayambiranso? Ngakhaletu pambuyo pa Chigumula cha m’tsiku la Nowa, zoipa zinayambiranso n’kuchuluka mpaka Mulungu anaimitsa zolinga zoipa za anthu mwa kusokoneza chiyankhulo chawo.​—Genesis 11:1-8.

Chifukwa chathu chachikulu chokhalira ndi chidaliro chakuti zoipa sizidzayambiranso n’chakuti dziko lapansi silidzalamulidwanso ndi anthu monga momwe zinachitikira pambuyo pa Chigumula. M’malo mwake, lidzalamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu. Polamulira kuchokera kumwamba, Ufumu umenewu ndiwo udzakhala boma lenileni la dziko lapansi. (Danieli 2:44; 7:13, 14) Sudzazengereza kuchitapo kanthu pa munthu aliyense amene akufuna kuyambitsanso zoipa. (Yesaya 65:20) Kwenikweni, m’kupita kwa nthaŵi udzawononga woyambitsa zoipa weniweniyo​—Satana Mdyerekezi​—pamodzi ndi ziwanda, angelo oipa amene anam’tsatira.​—Aroma 16:20.

Komanso, anthu sadzadanso nkhaŵa ndi chakudya, zovala, nyumba, ndi ntchito​—zinthu zimene kusoŵa kwake lerolino n’kumene kumapangitsa ena kuchita zaupandu. Inde, dziko lonse lapansi lidzasandulika kukhala paradaiso wachonde wokhala ndi zinthu zochuluka zokwanira onse.​—Yesaya 65:21-23; Luka 23:43.

Chofunika kwambiri n’chakuti Ufumu udzaphunzitsa nzika zake kukhala mwamtendere koma panthaŵi imodzimodziyo kuwatukula kufika paungwiro weniweni waumunthu. (Yohane 17:3; Aroma 8:21) Kenako, mtundu wa anthu sudzalimbananso ndi zofooka ndi malingaliro auchimo, kupangitsa kuti kumvera Mulungu mwangwiro kukhale kotheka ndi kosangalatsa, monga momwe zinalili kwa Yesu, munthu wangwiroyo. (Yesaya 11:3) Ndipotu Yesu anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale atayang’anizana ndi ziyeso zazikulu ndi chizunzo chodetsa nkhaŵa​—zinthu zimene zidzakhala zosaganizirika n’komwe m’Paradaiso.​—Ahebri 7:26.

Chifukwa Chimene Ena Amapitiradi Kumwamba

Ngakhale zili motero, anthu ochuluka oŵerenga Baibulo amadziŵa mawu a Yesu akuti: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. . . . Ndipita kukukonzerani inu malo.” (Yohane 14:2, 3) Kodi zimenezi sizikutsutsa lingaliro la moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso?

Si kuti ziphunzitso zimenezi zikutsutsana iyayi. Kunena zoona, zikuchirikizana. Choyamba, Baibulo limanena kuti pali chiŵerengero chodziŵikiratu cha Akristu okhulupirika​—okwanira 144,000​—oukitsidwa monga zolengedwa zauzimu zokakhala kumwamba. N’chifukwa chiyani akupatsidwa mfupo yodabwitsa imeneyi? Chifukwa chakuti ndiwo a m’gulu limene Yohane anaona m’masomphenya amene “anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka chikwi.” (Chivumbulutso 14:1, 3; 20:4-6) Poyerekeza ndi mabiliyoni a padziko lapansi, a 144,000 amenewo alidi “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Komanso, pokhala atakumana ndi mavuto amene anthu onse amakumana nawo, iwo, mofanana ndi Yesu, adzatha “kumva chifundo ndi zofooka zathu” poyang’anira kukonzedwanso kwa mtundu wa anthu ndi dziko lapansi.​—Ahebri 4:15.

Dziko Lapansi​—Mudzi Wosatha wa Mtundu wa Anthu

Mwa kupereka nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, Mulungu anayamba kusonkhanitsa a 144,000 zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, ndipo zikusonyeza kuti gulu limeneli linakwanira tsopano. (Machitidwe 2:1-4; Agalatiya 4:4-7) Komabe, nsembe ya Yesu siinaperekedwere machimo a anthu 144,000 okhawo iyayi, “komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yohane 2:2) Chotero, onse osonyeza chikhulupiriro mwa Yesu ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yohane 3:16) Amene ali chigonere m’manda koma amene ali m’chikumbukiro cha Mulungu adzaukitsidwa, osati kumwamba, koma kukhalanso amoyo padziko lapansi loyeretsedwa. (Mlaliki 9:5; Yohane 11:11-13, 25; Machitidwe 24:15) Kodi kumeneko adzaonanji?

Chivumbulutso 21:1-4 chikuyankha kuti: ‘Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu . . . Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.’ Tangolingalirani​—anthu kumasulidwa ku imfa, ndipo kupweteka ndi kulira kumene imachititsa zitachokeratu! Pomalizira pake, chifuniro choyambirira cha Yehova kaamba ka dziko lapansi ndi mtundu wa anthu chidzakwaniritsidwa mwaulemerero.​—Genesis 1:27, 28.

Chosankha Chathu​—Moyo Kapena Imfa

Adamu ndi Hava sanapatsidwepo mwayi wosankha kupita kumwamba. Anapatsidwa mwayi wosankha kumvera Mulungu ndi kukhala ndi moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso kapena kusam’mvera ndi kufa. N’chomvetsa chisoni kuti iwo anasankha kusamvera ndipo anabwerera ku “fumbi” la m’nthaka. (Genesis 2:16, 17; 3:2-5, 19) Mulungu sanakhalepo ndi chifuno chakuti banja la anthu lizifa ndi kupita kukakhala kumwamba kudzera m’manda. Mulungu analenga miyandamiyanda ya angelo oti azikhala kumwamba; zolengedwa zauzimu zimenezi si anthu amene anafa amene aukitsidwira kumwamba ayi.​—Salmo 104:1, 4; Danieli 7:10.

Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tilandire dalitso la moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi? Choyamba ndicho kuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo Lopatulika. “Moyo wosatha ndi uwu,” anatero Yesu m’pemphero, “kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”​—Yohane 17:3.

Kugwiritsa ntchito chidziŵitso chimenecho ndicho chinthu chachiŵiri chotsogolera ku chimwemwe chosatha m’Paradaiso. (Yakobo 1:22-24) Awo amene amatsatira Mawu a Mulungu ali ndi chiyembekezo chodzadzionera ndi maso awo kukwaniritsidwa kwa maulosi osangalatsa kwambiri monga uwu wolembedwa pa Yesaya 11:9, umene umati: ‘[Anthu] sadzaipitsa, sadzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Ngati mukufuna nkhani yolongosola chifukwa chimene Mulungu walolera zoipa kumwamba ndi padziko lapansi, onani buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., m’masamba 70-9.

[Zithunzi patsamba 7]

“Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:29