Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Lapansi—Malo Ongoyeserapo Anthu?

Dziko Lapansi—Malo Ongoyeserapo Anthu?

Dziko Lapansi​—Malo Ongoyeserapo Anthu?

HA! WAKHOZA. Wophunzira amene anali atalemba mayeso ovuta kwa milungu iŵiri tsopano walandira zotsatira zake zosangalatsa. Tsopano atha kukayamba ntchito imene wakhala akuilakalaka.

Ndi mmene anthu ochuluka amaonera moyo wapadziko lapansi. Amauona ngati mayeso owakonzekeretsa zinazake amene munthu aliyense ayenera kukumana nawo. “Okhoza” mayesowo amapita kwinakwake kumene adzakhala ndi moyo wabwinopo pambuyo pa imfa. Zikanakhaladi zomvetsa chisoni kwambiri ngati moyo umene tili nawowu​—wosasangalatsa kwa anthu ochuluka​—ndiwo moyo wokha wabwino umene anthu angayembekezere. Ngakhale kuti anali wathanzi labwino ndi wolemera kwa nthaŵi yayitali ya moyo wake, munthu wotchulidwa m’Baibulo wotchedwa Yobu anati: “Munthu wobadwa ndi mkazi n’ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto.”​—Yobu 14:1.

Polongosola zimene ambiri amalingalira, buku lotchedwa New Catholic Encyclopedia limati: “Ulemerero wa kumwamba ndiwo mapeto a munthu okonzedwa ndi Mulungu. . . . Chimwemwe cha munthu chimaonedwa kuti chingapezedwe ataloŵa m’moyo wamtendere wokhawokha wakumwamba.” Zotsatira za kufufuza kochitidwa ndi tchalitchi cha Church of Christ ku United States posachedwapa ati zinasonyeza kuti 87 peresenti ya anthu ofunsidwawo amakhulupirira kuti akamwalira adzapita kumwamba.

Anthu ochuluka osakhala Akristu alinso n’chiyembekezo chochoka padziko lapansi n’kupita kumalo abwino pambuyo pa imfa. Mwachitsanzo, Asilamu ali n’chiyembekezo chopita ku paradaiso wakumwamba. Otsatira timagulu tachibuda totchedwa Dziko Loyera ku China ndi Japan amakhulupirira kuti mwa kumatchula mosalekeza mawu akuti “Amitabha,” amene ndi dzina la Buda wa Kuwala Kopanda Malire, iwo adzabadwanso ku Dziko Loyera, kapena kuti ku Paradaiso Wakumadzulo, kumene adzakhala ndi moyo m’chimwemwe chosayerekezeka.

Komano Baibulo, lomwe ndilo buku lopatulika lotembenuzidwa m’zinenero zochuluka koposa komanso lofala kwambiri padziko lonse lapansi, silinena kuti dziko lapansi ndi malo amene anthu adzathaŵapo, kapena ngati penapake pongoyambira. Mwachitsanzo, limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) M’Baibulo mulinso mawu odziŵika bwino a Yesu akuti: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.”​—Mateyu 5:5.

Malingaliro otchuka onena kuti kukhala kwathu padziko lapansi ndi kwa kanthaŵi chabe akutanthauza kuti imfa ndi njira yopitira ku moyo wosangalatsa kwambiri wa pambuyo pa imfa. Ngati zili motero, ndiye kuti mosakayikira imfa ndi dalitso. Koma kodi ndi mmene anthu amaonera imfa, kapena kodi amayesa kutalikitsa moyo wawo? Zochitika zimasonyeza kuti anthu akakhala ndi thanzi labwino ndi chisungiko, iwo safuna kufa.

Ngakhale zili motero, chifukwa chakuti moyo padziko lapansi wadzadza ndi zoipa ndi mavuto, ambiri amaonabe kumwamba kukhala malo okha amene munthu angapezeko mtendere weniweni ndi chimwemwe. Kodi kumwamba ndi malo amtendere wokhawokha, kumene zoipa ndi zosokoneza sizingachitike? Ndipo kodi moyo wa pambuyo pa imfa udzangokhala kumwamba basi? Mwina mudzadabwa kuona mayankho a Baibulo. Chonde ŵerenganinso nkhani yotsatira.