Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupatula Nthaŵi Yoŵerenga ndi Kuphunzira

Kupatula Nthaŵi Yoŵerenga ndi Kuphunzira

Kupatula Nthaŵi Yoŵerenga ndi Kuphunzira

“[Chitani] machawi [“patulani nthaŵi yofunika,” NW], popeza masiku ali oipa.”​—AEFESO 5:16.

1. N’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kulinganiziratu nthaŵi yathu, ndipo kagwiritsidwe ntchito kathu ka nthaŵi kangavumbule chiyani mwa ife?

ENA amati “kusankha nthaŵi ndiko kusunga nthaŵi.” Munthu amene amalinganiziratu kuchuluka kwa nthaŵi yomwe adzagwiritsa ntchito pa zinthu zomwe adzachita kaŵirikaŵiri amapindula kwambiri ndi nthaŵi yake. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Kanthu kali konse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake.” (Mlaliki 3:1) Tonsefe tili ndi nthaŵi yofanana; zimangodalira pa momwe timaigwiritsira ntchito. Momwe timasanjira zinthu zomwe tidzayambirira kuchita ndi mmene timagaŵira nthaŵi yathu kwenikweni zimavumbula zinthu zomwe mtima wathu umakonda kwambiri.​—Mateyu 6:21.

2. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, kodi Yesu ananenanji chokhudza chosoŵa chathu chauzimu? (b) Kodi n’kudzipenda kotani komwe tiyenera kuchita?

2 Timakakamizika kuthera nthaŵi ina pakudya ndi kugona chifukwa chakuti n’zofunika zathupi. Koma bwanji nanga zofunika zathu zauzimu? Tikudziŵa kuti nazonso ziyenera kukhutiritsidwa. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) N’chifukwa chake “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” nthaŵi ndi nthaŵi amatikumbutsa kufunika kwa kupatula nthaŵi yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo. (Mateyu 24:45) Mungadziŵe kuti kuchita zimenezi n’kofunika kwabasi, koma mungati mulibiretu nthaŵi yophunzirira kapena kuŵerenga Baibulo. Ngati ndi choncho, tiyeni tipende njira zopezera mipata yochuluka m’moyo wathu yoŵerengera Mawu a Mulungu, yopangira phunziro laumwini, ndi yosinkhasinkha.

Kupeza Nthaŵi Yoŵerenga ndi Kuphunzira Baibulo

3, 4. (a) Kodi mtumwi Paulo anapereka malangizo otani a mmene tingagwiritsire ntchito nthaŵi yathu, ndipo kodi zimenezi zimaphatikizapo chiyani? (b) Kodi Paulo anatanthauzanji potipatsa malangizo akuti ‘tipatule nthaŵi yofunika’?

3 Polingalira za nthaŵi yomwe tikukhala ino, m’pofunika kuti tonsefe timvere mawu a mtumwi Paulo akuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵitsani chifuniro cha Ambuye n’chiyani.” (Aefeso 5:15-17) Inde, uphungu umenewu ukukhudza mbali zonse za miyoyo yathu monga Akristu odzipatulira, kuphatikizapo kupeza nthaŵi yopemphera, kuphunzira, kupezeka m’misonkhano, komanso kuyesetsa nthaŵi zonse kutenga nawo mbali m’kulalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.”​—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

4 Zikuoneka kuti atumiki ambiri a Yehova lerolino akulephera kupanga chizoloŵezi choŵerenga Baibulo ndi kuliphunzira mozama. N’chachidziŵikire kuti sitingawonjeze ola lina lapadera ku tsiku lathu, choncho uphungu wa Paulowu uyenera kuti ukutanthauza zinazake. M’Chigiriki, mawu akuti “kupatula nthaŵi yofunika” amatanthauza kuipatula ku chochitika china mwa kusachita chinthu chimenecho. M’buku lake lotchedwa Expository Dictionary, W. E. Vine anawapatsa tanthauzo la “kugwiritsa ntchito bwino mpata uliwonse, kupanga mphindi ina iliyonse kukhala yopindulitsa chifukwa chakuti n’kosatheka kubwezeretsa nthaŵi yotayika.” Kodi nthaŵi yofunika yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo tingaipatule kuchiyani kapena kuti?

Tiike Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba

5. N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri,’ ndipo tingazitsimikizire motani?

5 Kuwonjezera pa ntchito zathu zakuthupi, tilinso ndi zinthu zambiri zauzimu zoti tizisamalire. Monga atumiki a Yehova odzipatulira, ndife “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Pa chifukwa chimenechi, Paulo analangiza Akristu ku Filipi kuti ‘atsimikizire zinthu zofunika kwambiri.’ (Afilipi 1:10, NW) Zimenezi zikutanthauza kuti zinthu zofunika ziyenera kuikidwa patsogolo. Nthaŵi zonse, tiyenera kulingalira zinthu zauzimu choyamba tisanalingalire za zinthu zakuthupi. (Mateyu 6:31-33) Komabe, m’pofunikanso kusamala kuti tikwaniritse maudindo athu auzimu. Kodi mbali zosiyanasiyana za moyo wathu wachikristu tikuzigaŵira nthaŵi motani? Oyang’anira oyendayenda anapereka lipoti lakuti pa “zinthu zofunika kwambiri” zomwe Mkristu ayenera kuzisamalira, phunziro laumwini ndi kuŵerenga Baibulo n’zomwe zimanyalanyazidwa.

6. Kodi kupatula nthaŵi yofunika kungaphatikizepo chiyani kumbali ya ntchito yakuthupi ndi ntchito yapanyumba?

6 Monga momwe taonera, kupatula nthaŵi yofunika kumafuna “kugwiritsa ntchito bwino mpata uliwonse” komanso “kupanga mphindi iliyonse kukhala yopindulitsa.” Choncho ngati kaŵerengedwe ndi kaphunziridwe kathu ka Baibulo n’kosakhutiritsa, ndibwino kuti tipende ndi kuona mmene nthaŵi yathu tikuigwiritsira ntchito. Ngati ntchito yathu yakuthupi n’njotangwanitsa kwambiri, mwakuti imatidyera nthaŵi yambiri ndi mphamvu zochuluka, tiyenera kupemphera kwa Yehova kuti atithandize pa nkhani imeneyi. (Salmo 55:22) N’zotheka kusintha ndi kukhala ndi nthaŵi yokwanira yochitira zinthu zofunika kwambiri zokhudza kulambira Yehova, kuphatikizapo kuphunzira ndi kuŵerenga Baibulo. Ena anena molondola kuti ntchito za akazi sizitha. Chotero alongo achikristu ayeneranso kugwira ntchito zofunika kwambiri moyambirira ndi kusunga nthaŵi yodziŵikiratu yoŵerengera Baibulo ndi kuliphunzira mosamalitsa.

7, 8. (a) Kodi nthaŵi yoŵerenga ndi kuphunzira tingaipatule kuzochitika zotani kaŵirikaŵiri? (b) Kodi cholinga cha kusangalala n’chiyani, ndipo kukumbukira zimenezi kudzatithandiza motani kuika zinthu zofunika patsogolo?

7 Mokulira, ambiri a ife tingawombole nthaŵi yophunzira mwa kusachita zinthu zopanda phindu. Mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndi nthaŵi yochuluka motani imene ndimathera poŵerenga magazini akudziko kapena nyuzipepala, poonerera mapulogalamu a pa wailesi yakanema, pomvetsera nyimbo, kapena popanga maseŵera a pa vidiyo? Kodi ndimathera nthaŵi yochuluka pa kompyuta kuposa yomwe ndimathera poŵerenga Baibulo? Paulo anati: “Musakhale opusa, koma dziŵitsani chifuniro cha Ambuye n’chiyani.” (Aefeso 5:17) Kugwiritsa ntchito wailesi yakanema mopyola muyeso kukuoneka kuti n’chifukwa chachikulu chomwe Mboni zambiri sizipatulira nthaŵi yokwanira yopanga phunziro laumwini ndi kuŵerenga Baibulo.​—Salmo 101:3; 119:37, 47, 48.

8 Ena anganene kuti sangangokhalira kuphunzira nthaŵi zonse, chifukwa chakuti nthaŵi zina amafuna kusangalala. Ngakhale kuti izi n’zoona, tingachite bwino kulingalira za kuchuluka kwa nthaŵi yomwe timathera pazinthu zosangalatsa ndi kuiyerekezera ndi nthaŵi yomwe timathera pophunzira kapena kuŵerenga Baibulo. Tingadabwe n’zotsatira zake. Ngakhale kuti kusangalala ndi kuseŵera n’zofunika, ziyenera kuikidwa m’malo ake oyenera. Cholinga cha kusangalala ndi kuseŵera n’chakuti tipeze mphamvu zatsopano zochitira zinthu zauzimu. Mapulogalamu ambiri a pa wailesi yakanema ndi maseŵera a pa vidiyo n’ngotopetsa, pamene kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu kumatsitsimula ndi kulimbikitsa.​—Salmo 19:7, 8.

Mmene Ena Amapezera Nthaŵi Yophunzira

9. Kodi kutsatira malangizo operekedwa m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku​—1999 kuli ndi mapindu otani?

9 Mawu oyambirira m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku ka 1999 anati: “Kupenda lemba latsiku ndi tsiku ndi ndemanga zake m’kabukuka m’maŵa kudzakuthandizani kwabasi. Mudzamva monga kuti Yehova, Mlangizi Wamkuluyo, akukudzutsani ndi malangizo ake. Ulosi umanena za Yesu Kristu kuti anali kupindula ndi malangizo a Yehova m’maŵa uliwonse motere: ‘Iye [Yehova] andigalamutsa m’maŵa ndi m’maŵa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.’ Malangizo amenewo anapatsa Yesu ‘lilime la ophunzira’ kuti ‘adziŵe kunena mawu akuchirikiza iye amene ali wolema.’ (Yes. 30:20; 50:4; Mat. 11:28-30) Kudzutsidwa kuti mulandire uphungu wapanthaŵi yake wochokera m’Mawu a Mulungu m’maŵa uliwonse sikudzangokuthandizani kupirira zothetsa nzeru zanu komanso kukukonzekeretsani kuthandiza ena ndi ‘lilime la ophunzira’.” *

10. Kodi ena amapeza motani nthaŵi yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo, ndipo amapindula motani?

10 Akristu ambiri amatsatira malangizo ameneŵa mwa kuŵerenga lemba latsiku ndi ndemanga zake komanso mwa kulaŵirira m’mamaŵa kuŵerenga Baibulo kapena kuphunzira. Ku France mpainiya wokhulupirika amadzuka mofulumira m’maŵa uliwonse ndi kupatula mphindi 30 kuti aŵerenge Baibulo. N’chiyani cham’khozetsa kuchita zimenezi kwa zaka zambiri? Mlongoyu anati: “Ndine wosonkhezereka kwambiri, ndipo ndimatsatira ndandanda yanga ya kuŵerenga nthaŵi zonse zivute zitani!” Mosasamala kanthu za nthaŵi yochitira phunziro tsiku ndi tsiku yomwe tasankha, chinthu chofunika ndicho kusaphonya ndandandayo nthaŵi zonse. René Mica, yemwe wakhala akutumikira monga mpainiya kwa zaka zopitirira 40 ku Ulaya, ndi Kumpoto kwa Africa, anati: “Chiyambire 1950 cholinga changa nthaŵi zonse chinali kuŵerenga Baibulo lonse chaka chilichonse, ndipo ndachita zimenezi nthaŵi 49 tsopano. Ndikuona kuti kuŵerenga Baibulo lonse kwandithandiza kukhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Mlengi wanga. Kusinkhasinkha m’Mawu a Mulungu kwandithandiza kuzindikira bwino chilungamo cha Yehova ndi mikhalidwe yake ina ndipo kwakhala gwero la mphamvu zosaneneka.” *

‘Chakudya cha Panthaŵi Yake’

11, 12. (a) Kodi ‘n’chakudya’ chauzimu chotani chomwe “mdindo wokhulupirika” wapereka? (b) Kodi ‘chakudyacho’ chaperekedwa motani panthaŵi yake?

11 Monga momwe kudya nthaŵi zonse kumathandizira kukhala ndi thupi lathanzi labwino, ndandanda yabwino ya kuphunzira ndi kuŵerenga Baibulo imachirikizanso thanzi labwino lauzimu. Mu Uthenga wabwino wa Luka, timaŵerenga mawu a Yesu akuti: “Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitawo wa pabanja lake, kuwapatsa iwo phoso lawo panthawi yake?” (Luka 12:42) Kwa zaka zoposa 120 tsopano, ‘chakudya [chauzimu] cha panthaŵi yake’ chaperekedwa mu Nsanja ya Olonda, komanso m’mabuku ndi m’zofalitsa zinanso zofotokoza Baibulo.

12 Onani mawuwo akuti “panthaŵi yake.” Panthaŵi yoyenerera, “Mlangizi [wathu] Wamkulu,” Yehova, kudzera mwa Mwana wake komanso gulu la kapolo, watsogolera anthu ake pankhani ya chiphunzitso ndi khalidwe. Zangokhala ngati tonsefe tamvera limodzi mawu akutiuza kuti: “Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.” (Yesaya 30:20, 21) Komanso, pamene anthu aŵerenga Baibulo mwatcheru ndi zofalitsa zonse zofotokoza Baibulo, kaŵirikaŵiri amaona kuti mfundo zofotokozedwa mmenemo zikuwakhudza mwachindunji. Inde, malangizo ndi chitsogozo zaumulungu zidzafika kwa ife panthaŵi yake, kutithandiza kupeŵa ziyeso kapena kusankha mwanzeru zoyenera kuchita.

Zoloŵerani Kudya Kwabwino

13. Kodi zina mwa zizoloŵezi za kudya mopereŵera mwauzimu n’zotani?

13 Kuti tipindule mokwanira ndi ‘chakudya’ chapanthaŵi yake chimenechi, tiyenera tikhale n’zizoloŵezi zabwino za kudya mokwanira. M’pofunika kukhala ndi ndandanda yanthaŵi zonse ya kuŵerenga Baibulo ndi phunziro laumwini ndiyeno kumaitsatira nthaŵi zonse. Kodi muli ndi zizoloŵezi zabwino za kudya mwauzimu nthaŵi zonse, komanso nthaŵi yokhazikika ya phunziro lozama laumwini? Kapena kodi m’mangoŵerenga mwachisawawa zofalitsa zomwe zapangidwa mosamalitsa kaamba ka ife, kudya mothamanga, titero kunena kwake, kapenanso kusadya kumene chakudya china? Kuzoloŵera kudya mopereŵera mwauzimu kwapanga ena kukhala ofooka m’chikhulupiriro, ngakhale kugwa kumene.​—1 Timoteo 1:19; 4:15, 16.

14. N’chifukwa chiyani kuŵerenga mosamalitsa nkhani imene ingaoneke ngati yodziŵika kale kuli kopindulitsa?

14 Ena angalingalire kuti akudziŵa kale ziphunzitso zikuluzikulu ndi kuti si nkhani zonse zimene zimakhala zatsopano. Choncho, kuphunzira mwadongosolo ndi kupezeka pa misokhano n’zosafunika kwenikweni. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti tifunikira kukumbutsidwa zinthu zomwe tinaziphunzira kale. (Salmo 119:95, 99; 2 Petro 3:1; Yuda 5) Monga momwe wophika wabwino amakonzera mtundu umodzimodziwo wa chakudya chokoma m’njira zosiyanasiyana, gulu la kapolo limapereka chakudya chauzimu chopatsa thanzi m’njira zosiyanasiyana. Ngakhale m’nkhani zomwe mitu yake yaphunziridwapo kale mobwerezabwereza, m’makhala mfundo zabwino kwambiri zomwe sitingafune n’komwe kuziphonya. Mfundo n’njakuti zomwe timapeza pamene tikuŵerenga kwenikweni zimadalira pa kuchuluka kwa nthaŵi ndi khama lomwe tathera paphunziro lathulo.

Mapindu Auzimu a Kuŵerenga ndi Kuphunzira

15. Kodi kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo kumatithandiza motani kukhala atumiki abwino a Mawu a Mulungu?

15 Mapindu omwe timapeza poŵerenga ndi kuphunzira Baibulo n’ngosaneneka. Timathandizidwa kukwaniritsa umodzi wa maudindo athu achikristu, kuti ifeyo aliyense payekha akhale “wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (2 Timoteo 2:15) Titaŵirikiza kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo, m’pamenenso tingadzaze maganizo athu ndi malingaliro a Mulungu moŵirikiza. Chotero, monga Paulo, tidzakhala okhoza ‘kukambirana ndi anthu za m’Malemba, kuwatanthauzira, ndi kuwatsimikizira’ choonadi chosangalatsa cha zifuno za Yehova. (Machitidwe 17:2, 3) Maluso athu akuphunzitsa adzapita patsogolo, ndipo zokambirana za athu, nkhani zathu, ndi uphungu wathu zidzakhala zomangirira mwauzimu.​—Miyambo 1:5.

16. Kodi kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu kumatipindulitsa m’njira zaumwini ziti?

16 Kuwonjezera pamenepo, nthaŵi yomwe timathera popenda Mawu a Mulungu idzatithandiza kuumba moyo wathu mogwirizana kotheratu ndi njira za Yehova. (Salmo 25:4; 119:9, 10; Miyambo 6:20-23) Kudzalimbitsa mikhalidwe yathu yauzimu, monga kudzichepetsa, kumvera, komanso chimwemwe. (Deuteronomo 17:19, 20; Chivumbulutso 1:3) Tikamagwiritsa ntchito chidziŵitso chomwe timapeza poŵerenga ndi kuphunzira Baibulo, timasangalala polandira mzimu wa Mulungu nthaŵi zonse m’moyo wathu, ndipo zotsatira zake zimakhala unyinji wosaneneka wa chipatso cha mzimu m’chilichonse chimene timachita.​—Agalatiya 5:22, 23.

17. Kodi kuŵirikiza kwathu kuŵerenga Baibulo mwaumwini ndi mmene timaliphunzirira zimakhudza motani ubwenzi wathu ndi Yehova?

17 Chofunika koposa n’chakuti nthaŵi yomwe tidzapatula ku zochita zina kuti tiŵerenge ndi kuphunzira Mawu a Mulungu idzatidzetsera mapindu osaneneka pa ubwenzi wathu ndi Mulungu. Paulo anapempherera Akristu anzake kuti ‘akadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro cha [Mulungu] mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti akayende koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo.’ (Akolose 1:9, 10) Mofananamo, kuti ‘tikayende koyenera Yehova,’ tiyenera ‘kudzazidwa ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu.’ Ndithudi, kupeza kwathu madalitso ndi chivomerezo za Yehova mokulira zimadalira pa momwe timaŵirikizira kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo mwaumwini komanso mmene timachitira zimenezo.

18. Ndi madalitso otani omwe tingalandire ngati titatsatira mawu a Yesu a pa Yohane 17:3?

18 “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Limeneli ndi limodzi la Malemba omwe Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri pothandiza ena kuzindikira kufunika kwa kuphunzira Mawu a Mulungu. Ndithudi n’kofunika kwabasi kuti aliyense wa ife achite zimenezo payekha. Chiyembekezo chathu chodzakhala ndi moyo kosatha chikudalira kotheratu pa kukula kwathu m’chidziŵitso cha Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu. Ndipo tangolingalirani zomwe zimenezo zikutanthauza. Kuphunzira kwathu zochuluka zokhudza Yehova sikudzatha konse, ndipotu tidzaphunzira za iye kunthaŵi zosatha!​—Mlaliki 3:11; Aroma 11:33.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Kofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

^ ndime 10 Onani nkhani yakuti “Pamene Amaliŵerenga ndi Mmene Amapindulira,” m’kope la Nsanja ya Olonda ya May 1, 1995, masamba 20-1.

Kubwereza mwa Mafunso

• Kodi kagwiritsidwe kathu ntchito ka nthaŵi kamavumbulanji?

• Kodi nthaŵi yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo ingapatulidwe ku zochitika zotani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala zizoloŵezi zathu za mmene timadyera mwauzimu?

• Kodi kuŵerenga ndi kuphunzira Malemba kumadzetsa mapindu otani?

[Mafunso]

[Zithunzi pamasamba 20, 21]

Kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo nthaŵi zonse kudzatitheketsa ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi’

[Zithunzi patsamba 23]

Kulinganiza moyenerera nthaŵi yochitira zinthu zina ndi yochitira zinthu zauzimu m’moyo wathu wotanganidwawu kumatipindulitsa kwambiri