Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuphunzira—N’kothandiza ndi Kokondweretsa

Kuphunzira—N’kothandiza ndi Kokondweretsa

Kuphunzira​—N’kothandiza ndi Kokondweretsa

‘Ukaifunafuna . . . udzam’dziŵadi Mulungu.’​—MIYAMBO 2:4, 5.

1. Kodi kuŵerenga kongosangalala kungatidzetsere motani chimwemwe chochuluka?

ANTHU ambiri amaŵerenga pofuna kungosangalala. Ngati nkhaniyo n’njosangalatsa, kuŵerenga kungakhale kotsitsimula. Kuwonjezera pa ndandanda yawo yanthaŵi zonse ya kuŵerenga Baibulo, Akristu ena amapeza chimwemwe chenicheni mwa kuŵerenga apo ndi apo m’Masalmo, Miyambo, m’nkhani za m’Mauthenga Abwino, kapena zigawo zina za Baibulo. Kukongola kwa chinenerocho ndi malingaliro ake zimawasangalatsa kwabasi. Ena pofuna kuŵerenga kongosangalala amasankha kuŵerenga Yearbook of Jehovah’s Witnesses, magazini a Galamukani!, mbiri za anthu zosindikizidwa m’magazini ano, kapena zochitika za m’mbiri, za malo ndi chilengedwe cha dziko, komanso maphunziro a zachilengedwe.

2, 3. (a) Kodi chidziŵitso chakuya chauzimu tingachiyerekezere motani ndi chakudya chotafuna? (b) Kodi kuphunzira kumaphatikiza kuchitanji?

2 Ngakhale kuti kuŵerenga koti angosangalala kungakhale kotsitsimula, kuphunzira kumafuna kulingalira mwakuya. M’ngelezi wafilosofi Francis Bacon analemba kuti: “Mabuku ena n’ngwofunika kuwalawa, ena kuwameza, koma ena oŵerengeka ayenera kutafunidwa ndi kupukusidwa.” Mwachionekere Baibulo lili m’gulu lotsirizali. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Za iye [Kristu, wochitiridwa chithunzi ndi Melikizedeke Mfumu ndi Wansembe] tili nawo mawu ambiri kuwanena, ndi otilaka powatanthauzira, popeza mwagontha m’makutu. . . . Chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:11, 14) Chakudya cholimba chiyenera kutafunidwa chisanamezedwe ndi kupukusidwa. Chidziŵitso chakuya chauzimu chimafuna kusinkhasinkha kuti chimveke bwino ndi kugwiritsidwa ntchito.

3 Dikishonale ina imamasulira “kuphunzira” kukhala “mchitidwe kapena njira yogwiritsira ntchito malingaliro pofuna kupeza chidziŵitso kapena kumvetsetsa, mwachitsanzo, poŵerenga, pofufuza, ndi zina zotero.” Chotero zikutanthauza kuti kuphunzira kumafuna zambiri zoposa kungoŵerenga mwachisawawa, mwinamwake kudula mzera kunsi kwa mawu pamene mukuŵerenga. Kuphunzira kumatanthauza ntchito, kugwiritsa ntchito nzeru, ndi kugwiritsa ntchito mphamvu za kulingalira. Komabe, ngakhale kuti kuphunzira kumafuna khama, sizikutanthauza kuti sikungakhale kosangalatsa.

Kupanga Phunziro Kukhala Losangalatsa

4. Malinga n’kunena kwa wamasalmo, kodi kuphunzira Mawu a Mulungu kungakhale motani kotsitsimula ndi kopindulitsa?

4 Kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu kungatitsitsimule ndi kutilimbikitsa. Wamasalmo ananenetsa kuti: “Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni [“zikumbutso” NW] za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru; malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.” (Salmo 19:7, 8) Malamulo ndi zikumbutso za Yehova zimatsitsimula moyo wathu, kukulitsa uzimu wathu, kutipatsa chimwemwe cha mumtima, ndi kuŵalitsa maso athu ndi masomphenya oonekera bwino a zifuno zodabwitsa za Yehova. Si kusangalatsa kwake!

5. Kodi kuphunzira kungatidzetsere chimwemwe chochuluka m’njira ziti?

5 Tikamaona zotsatira zabwino za ntchito yathu, timaigwira mokondwera. Chotero kuti phunziro likhale losangalatsa, tiyenera kuchita changu kugwiritsa ntchito chidziŵitso chatsopano chomwe tachipeza. Yakobo analemba kuti: “Iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.” (Yakobo 1:25) Kufulumira kugwiritsa ntchito mwaumwini mfundo zophunziridwa kumakhutiritsa kwambiri. Kufufuza ndi cholinga chapadera chofuna kupeza yankho la funso lomwe tinafunsidwa pamene tinali pantchito yolalikira kapena kuti yophunzitsa kudzadzetsanso chimwemwe chochuluka kwa ife.

Kukulitsa Chikondwerero M’Mawu a Mulungu

6. Kodi wolemba Salmo 119 anafotokoza motani chikondwerero chake m’mawu a Yehova?

6 Wolemba Salmo 119, mwinamwake Hezekiya adakali mfumu yachinyamata, anafotokoza chikondwerero chake m’Mawu a Yehova. Mwa kulakatula ngati ndakatulo, iye anati: “Ndidzadzikondweretsa nawo malemba anu; sindidzaiŵala mawu anu. Mboni zanu zomwe ndizo zondikondwetsa . . . Ndidzadzikondweretsa nawo malamulo anu, amene ndiwakonda. Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo; popeza chilamulo chanu chindikondweretsa. Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.”​—Salmo 119:16, 24, 47, 77, 174.

7, 8. (a) Malinga ndi buku lina la maumboni, kodi ‘kudzikondweretsa’ m’Mawu a Mulungu kumatanthauzanji? (b) Kodi tingasonyeze motani kuti timakonda Mawu a Yehova? (c) Kodi Ezara anadzikonzekeretsa motani asanayambe kuŵerenga Chilamulo cha Yehova?

7 Potanthauzira mawu otembenuzidwa kuti ‘kudzikondweretsa’ mu Salmo 119, dikishonale ina ya Malemba Achihebri imati: “Mmene aligwiritsira ntchito pa vesi 16 likufanana matanthauzo ndi [aneni] a mawu akuti kukondwera . . . ndi kusinkhasinkha . . . M’ndandanda wa aneniwo ndi uwu: kondwera, sinkhasinkha, sangalala ndi . . . Mawu ameneŵa angatanthauze kuti kusinkhasinkha kwatanthauzo ndiko njira yomwe munthu amapezera nayo chimwemwe m’mawu a Yahweh. . . . Tanthauzoli likuphatikizapo kukhudzika maganizo.” *

8 Inde, kukonda kwathu Mawu a Yehova kuyenera kuchokera mumtima, phata la malingaliro onse. Tiyenera kumaganizirabe za ndime zina zomwe tangoziŵerenga kumene. Tiyenera kulingalira mozama mfundo zakuya zauzimu, ziyenera kuloŵa mumtima mwathu, ndi kusinkhasinkha pa mfundo zimenezo. Zimenezi zimafuna kuganiza modekha ndiponso pemphero. Monga Ezara, tifunikira kukonzekeretsa mitima yathu ku kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu. Analemba za iye kuti: “Ezara adaikiratu [“anakonzekeretsa” NW] mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m’Israyeli malemba ndi maweruzo.” (Ezara 7:10) Onani zolinga zitatu zomwe Ezara anakonzekeretsera mtima wake: kuphunzira, kuzigwiritsa ntchito payekha, ndi kuphunzitsa ena. Tiyenera kutsanzira chitsanzo chake.

Kuphunzira Monga Mbali ya Kulambira

9, 10. (a) Kodi wamasalmo anasonyeza motani kulingirira Mawu a Yehova? (b) Kodi mneni wachihebri wotembenuzidwa kuti “lingirira” amatanthauzanji? (c) N’chifukwa chiyani kuli kofunika kwa ife kuti tiziona kuphunzira Baibulo monga “mbali ya kulambira”?

9 Wamasalmo anati anasonyeza kulingirira malamulo, malangizo, ndi zikumbutso za Yehova. Iye anaimba kuti: “Ndidzalingirira pamalangizo anu, ndi kupenyerera mayendedwe anu. Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda; ndipo ndidzalingalira pa malemba anu. Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse. Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira [zikumbutso] zanu.” (Salmo 119:15, 48, 97, 99) Kodi ‘kulingirira’ Mawu a Yehova kumatanthauzanji?

10 Mneni wachihebri wotembenuzidwa kuti “lingirira” amatanthauzanso “sinkhasinkha, lingalira mozama,” “lingalira za nkhani inayake m’maganizo mwako.” “Amagwiritsidwa ntchito ponena za kuganizira mwakachetechete ntchito za Mulungu . . . ndi mawu a Mulungu.” (Theological Wordbook of the Old Testament) Mawu akuti “ndilingiriramo” akunena za “kusinkhasinkha kwa wamasalmoyu,” “kuphunzira kwake [chilamulo cha Mulungu] mosonkhezeredwa ndi chikondi chake cha Mawu a Mulungu,” monga “mbali ya kulambira.” Kufunika kophunzira Mawu a Mulungu kumawonjezereka ngati kuphunzirako tikuona monga mbali ya kulambira kwathu. Choncho kuyenera kuchitidwa mwachikumbumtima komanso mwapemphero. Kuphunzira ndi mbali ya kulambira kwathu ndipo timaphunzira kuti tipititse patsogolo kulambira kwathu.

Kukumba Mozama M’Mawu a Mulungu

11. Kodi Yehova amavumbula motani malingaliro akuya auzimu kwa anthu ake?

11 Poyamikira monthunthumira, wamasalmo anafuula nati: “Ha! ntchito zanu n’zazikulu, Yehova, zolingalira zanu n’zozama ndithu.” (Salmo 92:5) Ndipo mtumwi Paulo anatchula “zakuya za Mulungu,” malingaliro ozama omwe Yehova akuvumbulira anthu ake “mwa Mzimu” wake wogwira ntchito pagulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. (1 Akorinto 2:10; Mateyu 24:45) Gulu la kapolo likupereka chakudya chauzimu mwakhama kwa aliyense​—likupereka “mkaka” kwa atsopano koma “chakudya chotafuna” kwa “anthu akulu misinkhu.”​—Ahebri 5:11-14.

12. Perekani chitsanzo cha “zakuya za Mulungu” zomwe gulu la kapolo lazifotokoza.

12 Kuti timvetse “zakuya za Mulungu” zoterezi m’pofunika kuphunzira mwapemphero ndi kumalingalira za Mawu ake. Mwachitsanzo, kwasindikizidwa nkhani zabwino kwabasi zomwe zikusonyeza mmene Yehova angachitire chilungamo ndi chifundo panthaŵi imodzi. Kusonyeza kwake chifundo sikukutanthauza kuti chilungamo chake chikuchepa; m’malo mwake, chifundo chaumulungu ndicho chisonyezero cha chilungamo cha Mulungu komanso chikondi chake. Poweruza wochimwa, choyamba Yehova amalingalira kaye ngati n’kotheka kusonyeza chifundo pa maziko a nsembe ya dipo ya Mwana wake. Ngati wochimwayo n’ngwosalapa kapena kuti n’ngwoukira, Mulungu amalola chilungamo kugwira ntchito yake popanda kudodometsedwa ndi chifundo. Mwa njira iliyonse, n’ngwokhulupirika ku mfundo zake zokwezeka zachikhalidwe. * (Aroma 3:21-26) ‘Ha! kuya kwake kwa nzeru za Mulungu!’​—Aroma 11:33.

13. Kodi tingasonyeze motani kuyamikira ‘chiŵerengero chachikulu’ cha choonadi chauzimu chomwe chavumbulidwa kale pakali pano?

13 Mofanana ndi wamasalmo, timakondwa chifukwa chakuti Yehova amatiuza malingaliro ake ambiri. Davide analemba kuti: “Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Maŵerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziŵerenga zichuluka koposa mchenga.” (Salmo 139:17, 18) Ngakhale kuti zomwe tikudziŵa lerolino n’kachigawo kochepa chabe ka zolingalira zosaŵerengeka zomwe Yehova adzavumbula ku nthaŵi zanthaŵi, tikuyamikira kwambiri ‘chiŵerengero chachikulu’ cha choonadi chauzimu chamtengo wapatali chomwe chavumbulidwa kale ndipo tidzapitirizabe kukumba mozama m’chiŵerengero chimenecho, kapena m’matanthauzo a Mawu a Mulungu.​—Salmo 119:160 NW, mawu am’munsi.

Pakufunika Khama ndi Zipangizo Zodalirika

14. Kodi Miyambo 2:1-6 ikugogomeza motani kufunika kwa khama pophunzira Mawu a Mulungu?

14 Kuphunzira Baibulo mozama kumafuna khama. Mfundo imeneyi ikuonekera bwino lomwe pamene tiŵerenga mosamalitsa Miyambo 2:1-6. Taonani aneni amphamvu omwe Mfumu yanzeruyo Solomo inagwiritsa ntchito pogogomeza kufunikira kwa khama kuti tipeze chidziŵitso, nzeru, ndi kuzindikira kwaumulungu. Iye analemba kuti: ‘Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.’ Inde, kuphunzira kopindulitsa kumafuna kufufuza, kukumba, ngati kuti tikufunafuna chuma chobisika.

15. N’chitsanzo chiti cha m’Baibulo chomwe chikusonyeza kufunika kwa njira zabwino zophunzirira?

15 Phunziro lokhutiritsa mwauzimu limafunanso njira zabwino zophunzirira. Solomo analemba kuti: “Chitsulo chikhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira [“chidzafuna mphamvu zambiri,” NW].” (Mlaliki 10:10) Ngati mmisiri akugwiritsa ntchito chipangizo chodulira zinthu chosathwa kapena ngati sakuchigwiritsa ntchito mwaluso, amangotaya mphamvu zake pachabe ndipo ntchito yake sikhala yaukatswiri. Mofananamo, mapindu amene timapeza panthaŵi imene tathera pophunzira amasiyana kwambiri, mogwirizana ndi njira zophunzirira zimene timatsata. Malingaliro abwino kwambiri othandiza kuwongolera njira zathu zophunzirira tingawapeze mu Phunziro 7 la Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase. *

16. Ndi malingaliro abwino ati omwe aperekedwa kuti atithandize kuphunzira mozama?

16 Pamene mmisiri ayamba kugwira ntchito yake, amasonkhanitsa zida zomwe adzafuna kuzigwiritsa ntchito. Mofananamo, pamene nthaŵi yathu yophunzira yakwana, tiyenera kusankha m’laibulale yathu zida zomwe zidzatithandiza pophunzirapo. Podziŵa kuti kuphunzira ndi ntchito ndi kuti kumafuna kuganiza mwakhama, ndi bwinonso kuti tizoloŵere kukhala moyenera pampando. Ngati tikufuna kukhala atcheru, kukhala pampando wa pathebulo kapena padesiki kungathandize kwambiri kusiyana ndi kugona pabedi kapena kukhala pampando wochezerapo wawofuwofu. Mutasumika maganizo pa zimene mukuŵerenga kwakanthaŵi, zidzakuthandizani kuyamba mwadziwongola kaye ndi kutuluka panja kukapitidwa kamphepo kayeziyezi.

17, 18. Perekani zitsanzo za momwe mungagwiritsire ntchito zipangizo zabwino zophunzirira zomwe mulinazo.

17 Tilinso ndi zipangizo zambiri zapamwamba zophunzirira. Chapamwamba koposa zonsezi ndicho Baibulo la New World Translation, lomwe tsopano lonse lathunthu kapena zigawo zake zikupezeka m’zinenero 37. M’Baibulo la New World Translation laukulu wapakati (osati laling’ono kwambiri) muli malifalensi ochuluka ndiponso “M’ndandanda wa Mabuku a m’Baibulo” womwe umasonyeza dzina la wolemba, malo komwe bukulo linalembedwera, ndi utali wa nthaŵi yomwe zolembedwazo zinachitikira. Lilinso ndi mbali yosonyezera mawu a m’Baibulo, zowonjezera, komanso mapu. M’zinenero zina, Baibulo limeneli lasindikizidwanso monga kope lalikulu, lodziŵika ndi dzina lakuti Baibulo la Malifalensi. Baibuloli lili ndi zonse zotchulidwa pamwambazi ndi zinanso zambiri, kuphatikizapo mawu am’munsi ambirimbiri, omwenso ali ndi mbali yosonyeza komwe chidziŵitso chowonjezereka cha mawu am’munsiŵa chikupezeka. Kodi zomwe zilipo m’chinenero chanu mukuzigwiritsa ntchito mokwanira kuti zikuthandizeni kukumba mwakuya m’Mawu a Mulungu?

18 Chida chinanso chamtengo wapatali chophunzirira ndicho insaikulopediya ya Baibulo ya mavoliyumu aŵiri yotchedwa Insight on the Scriptures. Ngati muli nayo m’chinenero chimene m’mamva, igwiritseni ntchito nthaŵi zonse pamene mukuphunzira. Idzakupatsani mfundo zofunika kuzidziŵa m’nkhani zambiri za m’Baibulo. Chida china chothandizanso ndicho buku lakuti “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial.” Pamene muyamba kuŵerenga buku latsopano la Baibulo, ndi bwino kupenda phunziro lolongosola bukulo m’buku limeneli la “All Scripture” kuti mudziŵe bwino malo ndi mbiri yake yonse, komanso mfundo zachidule zopezeka m’buku la Baibulo limenelo ndi phindu lake kwa ife. Chipangizo chatsopano chowonjezera pa zipangizo zochuluka zophunzirira zosindikizidwa ndicho Watchtower Library ya pa kompyuta, yomwe tsopano ikupezeka m’zinenero zisanu ndi zinayi.

19. (a) N’chifukwa chiyani Yehova watipatsa zipangizo zabwino zophunzirira Baibulo? (b) Kodi chofunika n’chiyani kuti tiŵerenge ndi kuphunzira bwino Baibulo?

19 Yehova wapereka zipangizo zonsezi kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti atumiki ake apadziko lapansi athe ‘kufunafuna chidziŵitso chenicheni cha Mulungu.’ (Miyambo 2:4, 5) Zizoloŵezi zabwino za kuphunzira zimatithandiza kum’dziŵa bwino Yehova ndi kupanga naye ubwenzi wolimba. (Salmo 63:1-8) Inde, kuphunzira ndi ntchito, koma ntchito yake n’njokondweretsa ndi yothandiza. Komabe, kumatenga nthaŵi, ndipo mwinamwake mukulingalira kuti, ‘Nthaŵi n’ngaipeze kuti ine yakuti ndiziŵerenga Baibulo ndi kupanga phunziro laumwini modekha?’ Mbali imeneyi ndi yomwe tidzakambirane m’nkhani yomaliza ya nkhani zotsatizanazi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 New International Dictionary of Old Testament Theology & Exegesis, Voliyumu 4, masamba 205-7.

^ ndime 12 Onani Nsanja ya Olonda, ya August 1, 1998, tsamba 13, ndime 7. Monga pulogalamu ya kuphunzira Baibulo, mungapende nkhani zonse zophunziridwa m’kope limenelo komanso nkhani zakuti “Justice,” “Mercy,” ndi “Righteousness” mu insaikulopediya ya Baibulo ya Insight on the Scriptures, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc. Uphungu wabwino wa njira zophunzirira ukupezekanso m’makope a Nsanja ya Olonda otsatiraŵa: August 15, 1993, masamba 13-17; November 1, 1986, masamba 13-14.

Kubwereza mwa Mafunso

• Kodi tingapange motani phunziro laumwini kukhala lotsitsimula ndi lopindulitsa?

• Mofanana ndi wamasalmo, kodi ‘kudzikondweretsa’ ndi Mawu a Yehova komanso ‘kuwalingirira’ tingakuchite motani?

• Kodi Miyambo 2:1-6 akusonyeza motani kufunika kwa khama pophunzira Mawu a Mulungu?

• N’zipangizo zabwino zophunzirira ziti zomwe Yehova wapereka?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 14]

Kusinkhasinkha modekha ndi pemphero zimatithandiza kukonda Mawu a Mulungu mowonjezereka

[Zithunzi patsamba 17]

Kodi zida zophunzirira zomwe muli nazo m’mazigwiritsa ntchito mokwanira pokumba mwakuya m’Mawu a Mulungu?