Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenera Kufufuza za Zipembedzo Zina?

Kodi Muyenera Kufufuza za Zipembedzo Zina?

Kodi Muyenera Kufufuza za Zipembedzo Zina?

“NDINAKHALA ndikufika pa misonkhano yachikristu kwa pafupifupi chaka chimodzi, ndipo ndinkasangalala kuuzako ena za Ufumu wa Mulungu,” anatero Miguel, amene tsopano ndi wa Mboni za Yehova ku South America. “Kenako ndinayamba kumvetsera mapulogalamu a zipembedzo a pawailesi ndiponso kuonerera alaliki a zipembedzo a pawailesi yakanema. Ndinkaganiza kuti mapulogalamu oterowo andithandiza kudziŵa bwino za anthu a zipembedzo zina. Ndinazindikira kuti zophunzitsa zawo sizimagwirizana ndi Baibulo, komabe ndinkachita nazo chidwi.”

Ku dziko lomwelo, Jorge anali wachangu pophunzitsa ena za kulambira koona. Komabe, panthaŵi ina, nayenso anayamba kumvetsera mapulogalamu a zipembedzo a pawailesi ndiponso a pawailesi yakanema. “Mufunikira kudziŵa zimene anthu ena akuganiza,” ankakonda kunena choncho. Akafunsidwa za ngozi yomwe ingakhalepo chifukwa chomvetsera ndi kuonerera zophunzitsa zonyenga zoterozo, iye ankayankha kuti: “Palibe chimene chingafooketse chikhulupiriro cha munthu amene amadziŵa choonadi cha Baibulo.” Zochitika zimenezi zikubutsa funso lofunika lakuti, Kodi n’kwanzeru kumvetsera zimene anthu ena amakhulupirira?

Kuzindikira Chikristu Choona

Atumwi atafa, kulambira koona kunadetsedwa ndi kupita patsogolo kwa Chikristu cha dzina lokha. Pooneratu zimenezi, Yesu ananena njira imodzi yosiyanitsira mitundu imeneyi ya Chikristu chonyenga ndi Chikristu choona. Poyamba, iye anachenjeza kuti: “Yang’anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m’kati mwawo ali afisi olusa.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” (Mateyu 7:15-23) Otsatira oona a Yesu amachita zimene iye anaphunzitsa, ndipo amazindikiridwa mosavuta chifukwa cha zipatso zawo zabwino. Monga momwe Yesu mwiniyo anachitira, iwo amachezera anthu kuti awafotokozere za Ufumu wa Mulungu kuchokera m’Malemba. Motsatira chitsanzo cha Yesu, iwo saloŵerera nawo m’ndale za dziko ndi m’mikangano ya anthu. Amavomereza Baibulo kukhala Mawu a Mulungu ndipo amalilemekeza monga choonadi. Iwo amadziŵikitsa dzina la Mulungu. Komanso iwo sachita nawo nkhondo chifukwa chakuti amayesetsa kukhala ndi chikondi chimene Mulungu amaphunzitsa. M’malo mwake, iwo amachitirana monga abale.​—Luka 4:43; 10:1-9; Yohane 13:34, 35; 17:16, 17, 26.

Malinga ndi Malemba, n’kotheka “kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.” (Malaki 3:18) Olambira oona lerolino ndi ogwirizana m’maganizo ndi m’zochita, monga momwe Akristu a zaka za zana loyamba analili. (Aefeso 4:4-6) Mutazindikira gulu la Akristu enieni loterolo, kodi n’chifukwa chiyani muyenera kuchita chidwi ndi zikhulupiriro za anthu ena?

Chenjerani ndi Aphunzitsi Onyenga

Baibulo limavomereza kuti ngakhale pambuyo pophunzira choonadi cha Baibulo, pamakhala chiwopsezo cha kudetsedwa mwauzimu chifukwa cha ziphunzitso zonyenga. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.” (Akolose 2:8) Lemba limenelitu likutipatsa chithunzithunzi chabwino kwambiri! Monga mimbulu yofuna kukulandani ndi kukulikwirani, aphunzitsi onyenga ndi owopsa kwabasi.

Ndi zoona kuti Paulo ankadziŵa zimene anthu ena amakhulupirira. Nthaŵi ina iye anayambapo kukamba nkhani mwa kunena kuti: “Amuna inu a Atene, m’zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa. Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIŴIKA.” (Machitidwe 17:22, 23) Komabe, Paulo sankadzaza maganizo ake nthaŵi zonse ndi nzeru za Agiriki odziŵa kulankhula pagulu.

Kudziŵa magwero ndi zikhulupiriro za zipembedzo zonyenga n’kosiyana kwambiri ndi kudzaza maganizo anu ndi zinthu zimenezo. * Yehova waika “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti atiphunzitse mogwiritsa ntchito Mawu ake. (Mateyu 4:4; 24:45) Paulo yemweyo analemba kuti: “Simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda. Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye?”​—1 Akorinto 10:20-22.

Aphunzitsi ena onyenga mwina anali Akristu oona m’mbuyomo, koma panthaŵi ina anachoka m’choonadi ndi kusokera. (Yuda 4, 11) Zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Atatha kulankhula za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene amaimira gulu la Akristu odzozedwa, Yesu analankhula za “kapolo woipa,” gulu limene limadandaula kuti, “Mbuye wanga wachedwa,” n’kuyamba kumenya akapolo anzake. (Mateyu 24:48, 49) Kaŵirikaŵiri, anthu ameneŵa ndiponso owatsatira awo alibe ziphunzitso zawozawo zomveka bwino; iwo ndi ongosangalatsidwa ndi kuphwasula zikhulupiriro za anthu ena. Ponena za iwo, mtumwi Yohane analemba kuti: “Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musam’landire iye kunyumba, ndipo musam’lankhule.”​—2 Yohane 10; 2 Akorinto 11:3, 4, 13-15.

Anthu oona mtima amene akufunafuna choonadi amachita bwino kulingalira mozama za zimene amamva kuchokera m’zipembedzo zosiyanasiyana. M’kupita kwa nthaŵi, Mulungu adzadalitsa anthu oona mtima amene akufunafuna choonadi. Ponena za nzeru ya Mulungu, Baibulo limati: ‘Ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo . . . udzam’dziŵadi Mulungu.’ (Miyambo 2:4, 5) Popeza kuti adziŵa Mulungu kudzera m’Baibulo ndiponso mu mpingo wachikristu ndi kuti aona mmene Yehova amadalitsira anthu amene akutsogozedwa ndi chidziŵitso chimenecho, Akristu oona sapitirizabe kumvetsera zophunzitsa za zipembedzo zonyenga.​—2 Timoteo 3:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Buku lakuti Mankind’s Search for God, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., limapereka chidziŵitso chokwanira bwino cha chiyambi ndiponso ziphunzitso za zipembedzo zambiri za dzikoli.