Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwira Ntchito “M’munda” Nyengo Yotuta Isanafike

Kugwira Ntchito “M’munda” Nyengo Yotuta Isanafike

Kugwira Ntchito “M’munda” Nyengo Yotuta Isanafike

OPHUNZIRA a Mphunzitsi Wamkulu anasokonezeka maganizo. Yesu anali atangonena kumene mwachidule nkhani ya tirigu ndi namsongole. Inali imodzi mwa mafanizo angapo amene ananena tsiku limenelo. Atatha kulankhula, anthu ambiri amene analipo anachokapo. Koma otsatira ake anadziŵa kuti mafanizo akewo ayenera kukhala ndi tanthauzo lake​—makamaka fanizo la tirigu ndi namsongole. Amadziŵa kuti Yesu sanali munthu wongonena nkhani zosangalatsa basi.

Mateyu akutiuza kuti ophunzirawo anapempha kuti: “Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m’munda.” Poyankha, Yesu anamasulira fanizolo, kuneneratu za mpatuko waukulu umene udzakhalapo pakati pa odzinenera kukhala ophunzira ake. (Mateyu 13:24-30, 36-38, 43) Zimenezo zinachitikadi, ndipo mpatuko unafala msanga mtumwi Yohane atamwalira. (Machitidwe 20:29, 30; 2 Atesalonika 2:6-12) Zotsatira zake zinafalikira moti funso limene Yesu anafunsa monga mmene analilembera pa Luka 18:8, linaoneka kukhala loyenera kwambiri kuti: “Mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?”

Kudza kwa Yesu kukakhala chiyambi cha “kututa” Akristu onga tirigu. Kukakhala chizindikiro cha “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano,” imene inayamba mu 1914. Ndiye zisatidabwitse kuti anthu anayamba kukonda choonadi cha m’Baibulo pamene nyengo yotuta inali pafupi kuyamba.​—Mateyu 13:39.

Kupenda mbiri yakale kumapereka umboni wakuti makamaka kuyambira m’ma 1400 mpaka m’tsogolo, anthu anayamba kuchita chidwi, ngakhalenso ambiri m’Matchalitchi Achikristu amene anali ngati “namsongole,” kapena Akristu onyenga. Pamene Baibulo linayamba kupezeka mosavuta komanso pamene anayamba kupanga mabuku a ndandanda ya mawu a m’Baibulo, anthu oona mtima anayamba kufufuza Malemba mosamala.

Kuunika Kuŵala

Podzafika ku ma 1800 pa amuna amenewo panali Henry Grew (1781-1862), wa ku Birmingham, ku England. Adakali ndi zaka 13, anapita ndi banja lawo ku United States kuoloka nyanja ya Atlantic, ndipo anafika pa July 8, 1795. Anakakhala ku Providence, ku Rhode Island. Makolo ake anam’phunzitsa kukonda Baibulo. Pamene Grew anali ndi zaka 25 mu 1807, anapemphedwa kukhala mbusa wa tchalitchi cha Baptist ku Hartford, ku Connecticut.

Anachita ntchito yake yophunzitsa mwakhama ndipo anayesa kuthandiza anthu amene anali kuwayang’anira kuchita zinthu mogwirizana ndi Malemba. Komabe, anakhulupirira zosunga mpingo uli woyera mwa kuchotsa munthu aliyense amene anali kuchita tchimo mwadala. Nthaŵi zina, iye pamodzi ndi amuna ena amene anali ndi udindo m’tchalitchicho, ankachotsa amene anachita dama kapena amene anachita zilizonse zodetsa.

Panali mavuto ena amene anam’detsa nkhaŵa m’tchalitchicho. Anali ndi amuna ena amene sanali a tchalitchi chimenecho koma ankachita ntchito zatchalitchicho ndipo ankatsogolera nyimbo nthaŵi ya mapemphero. Amuna amenewo anali kuvota nawonso pankhani zokhudza mpingowo ndipo pachifukwa chimenecho anali ndi ulamuliro pa nkhani zina za mpingowo. Pogwira mfundo ya kupatukana ndi dziko, Grew anakhulupirira mwamphamvu kuti amuna okhulupirika okha ndiwo ayenera kuchita zimenezo. (2 Akorinto 6:14-18; Yakobo 1:27) Mmene anaonera iyeyo, unali mwano kuti osakhulupirira aziimba nyimbo zotamanda Mulungu. Chifukwa cha zimenezo, mu 1811, a tchalitchi chimenecho anam’kana Henry Grew. Ena amene ankaona chimodzimodzi anachoka m’tchalitchicho nthaŵi yomweyo.

Kupatuka ku Matchalitchi Achikristu

Gulu limenelo, ndi Henry Grew yemwe, anayamba kuphunzira Baibulo ndi cholinga choti agwirizanitse miyoyo yawo ndi zochita zawo ndi uphungu wake. Maphunziro awowo mofulumira anawachititsa kuti amvetse kwambiri choonadi cha Baibulo ndi kuvumbula zolakwa za Matchalitchi Achikristu. Mwachitsanzo, mu 1824, Grew analemba nkhani yomveka bwino yotsutsa Utatu. Taonani mfundo yomveka bwino m’ndime iyi yotengedwa pa zimene analemba: “‘Za tsiku ilo, kapena nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo m’Mwamba, angakhale Mwana, koma ATATE ndiye.’ [Marko 13:32] Taonani panopa mmene anawasiyanitsira. Munthu, Angelo, Mwana, Atate. . . . Ambuye wathu akutiphunzitsa kuti Atate okha ndiwo anadziŵa za tsikulo. Koma malinga ndi mmene ena amanenera, zimenezi sizingakhale zoona ngati Atate, Mawu, ndi Mzimu Woyera ali anthu atatu mwa Mulungu mmodzi; popeza kuti malinga ndi [chiphunzitso chimenechi cha Utatu,] . .  . Mwana anazidziŵa zimenezo mofanana ndi Atate.”

Grew anaonetsa poyera chinyengo cha atsogoleri achipembedzo ndi akulu a nkhondo amene ankanamizira kuti akutumikira Kristu. Mu 1828 iye anati: “Kodi tingaganize za kusagwirizana kwina koposa kuja kwa Mkristu amene watuluka m’chipinda chake, mmene anali kupempherera adani ake, napita kukalamula magulu ake a nkhondo kuwapha adani omwewo moipa kwabasi mwa kuwabaya pamtima ndi zida? Nthaŵi ina, amakonda kukhala wofanana ndi Mbuye wake amene akufayo, koma nanga nthaŵi inayo amafanana ndi ndani? Yesu anapempherera amene anamupha. Akristu amapha aja amene amawapempherera.”

Pofuna kugogomeza mfundoyo mwamphamvu, Grew analemba kuti: “Kodi tidzam’khulupirira liti Wamphamvuyonseyo amene amatitsimikizira kuti ‘sapusitsika?’ Kodi tidzamvetsa liti khalidwe, inde mzimu, wa chipembedzo choyera chimene chimafuna kuti ife tipeŵe ngakhale ‘maonekedwe oipa?’ . . . Kodi si mwano kwa Mwana wa wodala, kuganiza kuti chipembedzo chake chimafuna kuti munthu akhale ngati mngelo nthaŵi ina, koma nthaŵi inanso n’kum’lola kukhala ngati chiwanda?”

Moyo Wosatha Si Wobadwa Nawo

M’zaka zimenezo kunalibe wailesi komanso wailesi yakanema, njira yodziŵika imene ankagwiritsa ntchito kunena malingaliro a munthu inali yolemba ndi kugaŵa timabuku. Cha m’ma 1835, Grew analemba kabuku kofunika kwambiri kamene kanaonetsa kuti ziphunzitso za kusafa kwa mzimu ndi moto wa helo sizinali za m’malemba. Anakhulupirira kuti ziphunzitso zimenezo zinam’chitira mwano Mulungu.

Zotsatira za kabuku kameneko zinadzafika kutali. Mu 1837, George Storrs amene anali ndi zaka 40 anapatsidwa kabukuko ali m’sitima yapamtunda. Storrs anali wa ku Lebanon, ku New Hampshire, koma panthaŵi imeneyo, amakhala ku Utica, ku New York.

Anali mbusa wolemekezeka kwambiri m’tchalitchi cha Methodist Episcopal. Ataŵerenga kabukuko, anasangalala kwambiri ndi mfundo zogomeka zoterozo zotsutsa ziphunzitso zazikulu za Matchalitchi Achikristu, zimene iye sanazikayikirepo n’komwe. Panatenga zaka asanadziŵe amene analemba kabuku kameneko, mpaka cha m’ma 1844 pamene anakumana ndi Henry Grew pamene onse ankakhala ku Philadelphia, ku Pennsylvania. Komabe, Storrs anaiphunzira nkhaniyo ali yekha kwa zaka zitatu, akumakambirana ndi abusa ena za nkhaniyo.

Pomaliza pake, George Storrs anaganiza kuti sakanakhala wokhulupirika kwa Mulungu ngati akanakhalabe m’tchalitchi cha Methodist, popeza kuti panalibe aliyense amene anatsutsa zinthu zimene anali kuphunzira. Anatula pansi udindo wake mu 1840 n’kupita ku Albany, ku New York.

Nyengo ya dzinja itangotha mu 1842, Storrs anakamba nkhani zotsatizana zisanu ndi imodzi kwa milungu isanu ndi umodzi pa mutu wakuti: “Kufufuza​—Kodi Anthu Oipa Amakhala Osafa?” Anthu anaikonda kwambiri nkhaniyi kwakuti anaikonzanso kuti aisindikize m’buku, ndipo pa zaka 40 zotsatira, inafalitsidwa makope 200,000 ku United States ndi ku Great Britain. Storrs ndi Grew anagwirizana potsutsa chiphunzitso chakuti mzimu sufa. Grew anapitiriza kulalikira mwachangu mpaka imfa yake pa August 8, 1862, ku Philadelphia.

Pasanapite nthaŵi yaitali pamene Storrs anakamba nkhani zisanu ndi imodzi zija zimene tanena posachedwapa, anasangalala ndi kulalikira kwa William Miller, amene ankayembekeza kubwera kwa Kristu m’thupi mu 1843. Kwa zaka pafupifupi ziŵiri, Storrs anatanganidwa kwambiri ndi kulalikira uthenga umenewo kumpoto chakum’maŵa konse kwa United States. Chaka cha 1844 chitatha, sanagwirizanenso ndi zoneneratu tsiku limene Kristu adzabwera, komanso sanatsutse ngati ena anafuna kufufuza zinthu mwa kuŵerengera zaka. Storrs anakhulupirira kuti kubwera kwa Kristu kunali pafupi ndi kuti Akristu anafunika kukhala ogalamuka ndi atcheru mwauzimu, okonzekera tsiku loyang’anira. Koma anachoka m’gulu la Miller chifukwa linkavomereza ziphunzitso zosachokera m’malemba, monga kusafa kwa mzimu, kuwotchedwa kwa dziko lapansi, ndi kuti anthu amene akufa osadziŵa chilichonse alibe chiyembekezo cha moyo wosatha.

Kodi Chikondi cha Mulungu Chikatsogolera Kuti?

Storrs anaipidwa ndi zimene a Adventist amanena kuti Mulungu adzaukitsa oipa ndi cholinga chokha chakuti adzawaphenso. Sanaone umboni wa m’Malemba wakuti Mulungu angachite zopanda pake ngati zimenezo komanso kulipsira mwanjiru. Storrs ndi anzake ananyanyiranso nafika ponena kuti oipa sadzaukitsidwa n’komwe. Ngakhale kuti zimawavuta kufotokoza malemba ena onena za kuuka kwa osalungama, mfundo yawoyo anaiona kukhala yogwirizana kwambiri ndi chikondi cha Mulungu. Kumvetsetsa kwinanso cholinga cha Mulungu kunali pafupi.

Mu 1870, Storrs anadwala kwambiri ndipo sanagwire ntchito kwa miyezi ingapo. Panthaŵi imeneyo, anapendanso zonse zimene anali ataphunzira kwa zaka zake zonse 74. Ananena kuti anali ataphonya mbali imodzi yofunika kwambiri ya cholinga cha Mulungu kwa anthu imene pangano la Abrahamu limasonyeza​—kuti ‘mafuko onse a dziko adzadzidalitsa okha chifukwa Abrahamu anamvera mawu a Mulungu.’​—Genesis 22:18; Machitidwe 3:25.

Mfundo imeneyo inabweretsa malingaliro atsopano m’maganizo ake. Ngati “mafuko onse” akanati adalitsidwe, kodi onse sakanayenera kumva uthenga wabwino? Kodi akanaumva bwanji uthengawo? Kodi si mamiliyoni ankhaninkhani anali atafa kale? Popitiriza kupenda Malemba, anaona kuti panali magulu aŵiri a anthu “oipa” akufa: amene anakaniratu chikondi cha Mulungu, ndi amene anafa osadziŵa chilichonse.

Omalizirawa, Storrs anaganiza motero, ayenera kudzaukitsidwa kwa akufa kuti awapatse mpata wopindula ndi nsembe ya dipo ya Kristu Yesu. Amene adzailandira adzakhala ndi moyo kwamuyaya padziko lapansi. Amene adzaikana adzawonongedwa. Inde, Storrs anakhulupirira kuti palibe aliyense amene adzaukitsidwa ndi Mulungu ali wopanda chiyembekezo. Pomaliza penipeni, palibenso wina amene adzafa chifukwa cha tchimo la Adamu kupatula Adamuyo! Koma bwanji nanga za anthu amene akukhala ndi moyo panthaŵi ya kubweranso kwa Ambuye Yesu Kristu? Storrs anafika pozindikira kuti ntchito yolalikira padziko lonse inafunikira kuchitidwa kuti iwafike anthuwo. Sankadziŵa m’pang’ono pomwe kuti kodi zimenezo zidzachitika bwanji, koma ndi chikhulupiriro analemba kuti: “Koma anthu ambiri amakana malingaliro ena ake ngati sakumvetsa mmene malingalirowo angagwirire ntchito, ngati kuti kusamvetsa kwawoko kungam’lepheretse Mulungu kuchita zimenezo.”

George Storrs anamwalira mu December 1879, ali panyumba pake ku Brooklyn, ku New York, midadada yochepa yokha kuchokera pamene panadzakhala likulu la ntchito yolalikira padziko lonse imene anaiyembekezera mwachidwi.

Kuŵala Kwinanso Kunafunika

Kodi amuna amenewo monga Henry Grew ndi George Storrs anamvetsa bwino choonadi monga mmene timamvetsera ifeyo lerolino? Ayi. Ankadziŵa vuto lawo, monga mmene Storrs ananenera mu 1847 kuti: “Tichita bwino kukumbukira kuti tangochoka kumene mu mdima wauzimu wa tchalitchi; ndipo sizingakhale zachilendo ngati titapeza kuti tidakavalabe ‘zovala zachibabulo’ ngati choonadi.” Mwachitsanzo, Grew anazindikira dipo limene Yesu anapereka, koma sanamvetse kuti linali “dipo lolingana,” ndiko kuti, moyo waumunthu wangwiro wa Yesu umene anapereka posinthanitsa ndi moyo waumunthu wangwiro wa Adamu umene anataya. (1 Timoteo 2:6, NW) Henry Grew anakhulupiriranso molakwa kuti Yesu adzabwera ndi kulamulira padziko lapansi mooneka. Komanso, Grew anasamala za kuyeretsa dzina la Yehova, nkhani imene ankachita nayo chidwi anthu ochepa kwabasi kuyambira m’zaka za zana lachiŵiri C.E.

Nayenso George Storrs sanamvetsetse bwino mfundo zina zofunika. Ankatha kuona zinthu zabodza zimene atsogoleri amatchalitchi achikristu ankanena, koma nthaŵi zina ankanyanyira. Mwachitsanzo, potsutsa mwamphamvu malingaliro ovomerezedwa ndi atsogoleri achipembedzo onena za Satana, akuti Storrs anakana mfundo yakuti Mdyerekezi ndi munthu weniweni. Anakana Utatu, komatu samadziŵa bwinobwino kuti kaya mzimu woyera unali munthu mpaka atatsala pang’ono kumwalira. Pamene George Storrs anayembekeza kubweranso kwa Kristu kuti kudzakhala kosaoneka, anaganiza kuti m’kupita kwa nthaŵi adzaoneka. Komabe, zikuoneka kuti amuna onse aŵiriŵa anali oona mtima, ndipo choonadi sanali nacho patali poyerekeza ndi ena ambiri.

“Munda” umene Yesu ananena m’fanizo la tirigu ndi namsongole mbewu zake zinali zisanache kuti nyengo yotuta iyambe. (Mateyu 13:38) Grew, Storrs, ndi ena anali kugwira ntchito “m’munda” pokonzekera kututa.

Charles Taze Russell, amene anayamba kusindikiza magazini ano mu 1879, analemba za zaka zake zoyambirira kuti: “Ambuye anatithandiza ndi anthu ambiri pophunzira Mawu Ake, amene mwa iwo panali wodziŵika bwino kwambiri, mbale wathu wokondedwa komanso wokalamba, George Storrs, amene anatithandiza kwambiri ponse paŵiri mwa kulankhula, komanso mwa kulemba. Koma sitinafune n’komwe kukhala otsatira anthu, kaya akhale abwino kapena anzeru motani, koma ‘Otsatira Mulungu monga ana okondedwa.’” Inde, ophunzira Baibulo oona mtima akanapindula ndi kuyesetsa kwa amuna ngati Grew ndi Storrs, koma kunali kofunikabe kuti apende Mawu a Mulungu, Baibulo, monga gwero lenileni la choonadi.​—Yohane 17:17.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]

Zimene Henry Grew Anakhulupirira

Anthu atonza dzina la Yehova, ndipo lifunika kuliyeretsa.

Utatu, kusafa kwa mzimu, ndi moto wa helo ndi ziphunzitso zonyenga.

Mpingo wachikristu uyenera kukhala wolekana ndi dziko.

Akristu sayenera kumenya nawo nkhondo za mayiko.

Akristu sayendera lamulo la Sabata la Loŵeruka kapena Lamlungu.

Akristu sayenera kukhala m’mabungwe achinsinsi, monga la Freemasons.

Sipayenera kukhala magulu osiyana pakati pa atsogoleri amatchalitchi achikristu ndi Akristu wamba.

Mayina aulemu achipembedzo ndi ochokera kwa wokana Kristu.

Mipingo yonse iyenera kukhala ndi bungwe la akulu.

Akulu ayenera kukhala ndi khalidwe loyera, opanda chitonzo.

Akristu onse ayenera kulalikira uthenga wabwino.

Padzakhala anthu amene adzakhala ndi moyo kwamuyaya m’Paradaiso padziko lapansi.

Nyimbo zachikristu ziyenera kukhala zotamanda Yehova ndi Kristu.

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi: Chotengedwa m’Kaundula wa bungwe la The New-York Historical Society/​69288

[Bokosi/Chithunzi patsamba 28]

Zimene George Storrs Anakhulupirira

Yesu analipira moyo wake monga mtengo wa dipo la anthu onse.

Kulalikira uthenga wabwino sikunachitikebe (1871).

Pachifukwa chimenecho, mapeto sakanakhala pafupi panthaŵi imeneyo (1871). Panayenera kudzakhala zaka za m’tsogolo zimene kulalikira kudzachitike.

Padzakhala anthu amene adzalandira moyo wosatha padziko lapansi.

Kudzakhala chiukiriro cha anthu onse amene anafa osadziŵa chilichonse. Amene adzavomereza nsembe ya dipo ya Kristu adzalandira moyo wosatha padziko lapansi. Amene adzaikana adzawonongedwa.

Ziphunzitso za kusafa kwa mzimu ndi moto wa helo n’zabodza ndipo zimanyoza Mulungu.

Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndi mwambo wa pachaka wa pa Nisani 14.

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi: NKHANI ZISANU NDI IMODZI, zimene George Storrs anakamba (1855)

[Zithunzi patsamba 29]

Mu 1909, C. T. Russell, mkonzi wa “Zion’s Watch Tower,” anasamukira ku Brooklyn, ku New York, U.S.A.