Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungayandikirire kwa Mulungu

Mmene Mungayandikirire kwa Mulungu

Mmene Mungayandikirire kwa Mulungu

“Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu,” amatero Yakobo 4:8. Posonyeza mmene Yehova Mulungu alili wofunitsitsa kuti anthu akhale naye paubwenzi wolimba, anapereka Mwana wake m’malo mwathu.

POSIMBA za mphatso yachikondiyo, mtumwi Yohane analemba kuti: “Tikonda [Mulungu] ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Koma kuti ife tiyandikire kwa Mulungu, tiyenera kutsatira njira zinazake. N’zofanana ndi njira zinayi zomwe timayandikirira kwa anthu anzathu, monga momwe tafotokozera m’nkhani yoyambayo. Tiyeni tsopano tizipende njirazo.

Pendani Mikhalidwe Yosangalatsa ya Mulungu

Mulungu ali ndi mikhalidwe yambiri yosangalatsa, ina yaikulu kwambiri ndiyo chikondi, nzeru, chilungamo, ndi mphamvu zake. Nzeru ndi mphamvu zake zikusonyezedwa mokulira ponse paŵiri mumlengalenga ndi m’dziko lotizingali, m’magulu akuluakulu a nyenyezi ndi m’tinthu tating’onoting’ono totchedwa maatomu. Wamasalmo analemba kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.”​—Salmo 19:1; Aroma 1:20.

Chilengedwe nachonso chimasonyeza chikondi cha Mulungu. Mwachitsanzo, chipangidwe chathu chimasonyeza kuti Mulungu amafunadi kuti tisangalale ndi moyo. Anatipanga kuti tizitha kuona mitundu yosiyanasiyana, kumva kukoma kwa zakudya ndi kununkhiza, kusangalala ndi nyimbo, kuseka, kusangalala n’zinthu zokongola, ndi kutipatsanso maluso ena ambiri komanso mikhalidwe yapadera yomwe n’njosafunika kwenikweni kuti tikhale ndi moyo. Inde, Mulungu alidi wooloŵa manja, wachifundo, ndi wachikondi​—mikhalidwe imene mosakayikira imawonjezera kukhala kwake “Mulungu wachimwemwe.”​—1 Timoteo 1:11, NW; Machitidwe 20:35.

Yehova amanyadira zedi mfundo yakuti ufumu wake ndi kuchirikizidwa kwa ufumuwo ndi zolengedwa zake zanzeru n’zozikika kotheratu pa chikondi. (1 Yohane 4:8) N’zoona kuti Yehova ndiye Mfumu ya Chilengedwe Chonse, koma iye amakhala ndi anthu, makamaka atumiki ake omvera, monga momwe atate wachikondi amakhalira ndi ana ake. (Mateyu 5:45) Sazengereza kuwachitira chilichonse chabwino. (Aroma 8:38, 39) Monga momwe tatchulira kale, anapereka moyo weniweniwo wa Mwana wake wobadwa yekha m’malo mwathu. Inde, ndife amoyo ndipo tili n’chiyembekezo cha moyo wosatha chifukwa cha chikondi cha Mulungu.​—Yohane 3:16.

Yesu anatipatsa chidziŵitso chakuya cha umunthu wa Mulungu chifukwa chakuti anatsanzira Atate wake kotheratu. (Yohane 14:9-11) Sanali wodzikonda m’pang’ono pomwe, anali wolingalira za ena, ndi wanzeru. Nthaŵi inayake, anthu anadza kwa Yesu ndi mwamuna wina wogontha yemwenso anali wachibwibwi. Mungalingalire mmene munthu ameneyu analili womangika m’chikhamu cha anthu. Chosangalatsa n’chakuti Yesu anam’tengera pambali munthu ameneyu ndi kum’chiritsa komweko. (Marko 7:32-35) Kodi anthu amene amasamala za malingaliro anu ndiponso amene amakulemekezani m’mawayamikira? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mudzayandikiradi kwa Yehova ndi Yesu pamene mukuphunzira zochuluka za iwo.

Lingalirani za Mikhalidwe ya Mulungu

Wina angakhale ndi mikhalidwe yosangalatsa, koma tifunikira kulingalira za munthu ameneyo kuti tikhale naye paubwenzi. Zilinso chimodzimodzi ndi Yehova. Kusinkhasinkha za mikhalidwe yake ndiyo njira yachiŵiri yofunika kwambiri poyandikira kwa iye. Mfumu Davide, mwamuna yemwe anakondadi Yehova yemwenso anali “wa pamtima [pa Yehova],” anati: “Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pa ndekha za ntchito ya manja anu.”​—Machitidwe 13:22; Salmo 143:5.

Pamene mukuona zodabwitsa za chilengedwe kapena kuŵerenga Mawu a Mulungu, Baibulo, kodi m’masinkhasinkha pa zomwe mukuona ndi kuŵerengazo monga Davide? Tayerekezerani kuti mnyamata wangolandira kumene kalata kuchokera kwa atate ake omwe amaŵakonda kwabasi. Kodi kalata imeneyo adzaiona motani? N’chachidziŵikire kuti sadzaiŵerenga mopupuluma ndi kuiponya m’dilowa mofulumira. M’malo mwake, adzaŵerenga mosamalitsa, kutengamo mfundo iliyonse ndi kuimvetsa bwino lomwe. Mofananamo, Mawu a Mulungu n’ngamtengo wapatali kwa ife, monga momwe analili kwa wamasalmo yemwe anaimba kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse.”​—Salmo 119:97.

Lankhulanani Bwino Nthaŵi Zonse

Kulankhulana kwabwino n’komwe kumalimbikitsa ubwenzi uliwonse. Kumaloŵetsamo kulankhula ndi kumvetsera​—ndipotu osati ndi malingaliro okha komanso ndi mtima womwe. Timalankhula ndi Mlengi wathu kudzera mu pemphero, lomwenso n’kulankhula mwachindunji ndi Mulungu mom’lambira. Yehova amakondwera ndi mapemphero a anthu omwe amam’konda ndi kum’tumikira omwenso amavomereza Yesu Kristu monga nthumwi Yake yaikulu.​—Salmo 65:2; Yohane 14:6, 14.

Kalelo, Mulungu ankalankhula ndi anthu m’njira zosiyanasiyana, kuphatikizapo m’masomphenya, m’maloto, komanso kudzera mwa angelo. Koma masiku ano, amalankhula ndi anthu kudzera m’Mawu ake olembedwa, Baibulo Lopatulika. (2 Timoteo 3:16) Mawu olembedwawo ali ndi mapindu ochuluka. Angaŵerengedwe nthaŵi ina iliyonse. Monga kalata, angaŵerengedwe mobwerezabwereza. Ndipotu sangapotozedwe monga muja zimakhalira kaŵirikaŵiri posimba nkhani mobwerezabwereza. Chotero litengeni Baibulo monga mpukutu waukulu wa makalata ochokera kwa Atate wanu wokondedwa wakumwamba, ndipo kupyolera m’makalata ameneŵa m’loleni kukuyankhulani tsiku ndi tsiku.​—Mateyu 4:4.

Mwachitsanzo, Baibulo limasonyeza mmene Yehova amaonera chabwino ndi choipa. Limafotokoza cholinga chake cha mtundu wa anthu ndi cha dziko lapansi. Ndiponso limavumbula mmene anali kuchitira ndi anthu komanso mitundu yosiyanasiyana, kuyambira alambiri okhulupirika kufikira adani amphamvu. Mwa kulola mbiri yonse ya momwe Yehova anali kuchitira ndi anthu kulembedwa mwanjira imeneyi, Yehova watifotokozera mwapadera kwambiri tsatanetsatane wa umunthu wake. Wavumbula chikondi, chimwemwe, chisoni, kukhumudwa, mkwiyo, chifundo, nkhaŵa zake​—inde, mndandanda wa malingaliro ake ndi mmene anali kumvera, ndi zifukwa zochitira chilichonse cha zimenezi​—zonsezi m’njira yakuti athu amvetse mosavuta.​—Salmo 78:3-7.

Mutaŵerenga chigawo china cha Mawu a Mulungu, kodi kuŵerenga kwanuko mungapindule nako motani? Kwenikweni, kodi mungayandikire motani kwa Mulungu? Choyamba, lingalirani pa zomwe mwaŵerenga ndi kuphunzira zokhudza Mulungu monga munthu, mukumalola mfundozo kufika mumtima mwanu. Ndiyeno muuzeni Yehova m’pemphero malingaliro anu ndi mmene mukumvera mumtima mwanu pa nkhani yomwe mwangophunzira kumeneyo komanso momwe mudzachitira kuti mupindule nayo. Kumeneku ndiko kulankhulana. Inde, ngati mukulingalira zinthu zinanso, ndithudi zimenezi mungathenso kuziphatikiza m’pemphero lanulo.

Chitani Zinthu Limodzi ndi Mulungu

Baibulo limanena za amuna ena okhulupirika akale kuti anayenda ndi Mulungu kapena kuti anayenda pamaso pa Mulungu woona. (Genesis 6:9; 1 Mafumu 8:25) Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Kwenikweni zikutanthauza kuti anali kukhala tsiku lililonse ngati kuti Mulungu anali nawo pomwepo. N’zoona kuti anali anthu ochimwa. Komabe, ankakonda malamulo a Mulungu ndi mfundo zake zachikhalidwe, ndipo anakhala mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu. Yehova amayandikira kwa oterowo, ndipo amawasamalira, monga momwe Salmo 32:8 likusonyezera. Ilo limati: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.”

Nanunso Yehova angakhale bwenzi lanu lapamtima​—bwenzi lomwe lidzayenda nanu, lidzakusamalirani, ndi kukupatsani malangizo autate. Mneneri Yesaya anam’fotokoza Yehova kuti ndiye ‘amene akuphunzitsa iwe kupindula, amene akutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.’ (Yesaya 48:17) Tikamalandira mapindu ameneŵa, timakhutira kuti Yehova ali “pa dzanja [lathu] lamanja,” titero kunena kwake, monga momwe Davide anachitira.​—Salmo 16:8.

Dzina la Mulungu Limafotokoza Mikhalidwe Yake

Zipembedzo zambiri komanso chiŵerengero chowonjezereka cha matembenuzidwe a Baibulo alephera kugwiritsa ntchito ndi kudziŵikitsa dzina lenileni la Mulungu. (Salmo 83:18) Komatu m’zolembedwa zoyambirira zachihebri, dzinalo​—Yehova​—likupezekamo pafupifupi nthaŵi 7000! (Modumphadumpha, pamene anali kuchotsa dzina la Mulunguli, otembenuza Baibulo ambiri anaika mayina a milungu yambiri yonyenga yotchulidwa m’zolembedwa zoyambirirazo, monga Baala, Beli, Merodaki, ngakhalenso Satana!)

Anthu ena akulingalira kuti kuchotsa dzina la Mulungu si nkhani yodetsa nkhaŵa kwenikweni. Koma talingalirani: Kodi n’kovuta kapena n’chapafupi kupanga ubwenzi wamphamvu ndi wodziŵika bwino ndi munthu wopanda dzina? Mayina aulemu akuti Mulungu ndi Ambuye (omwenso amagwiritsidwa ntchito potchula milungu yonyenga) angangosonyeza mphamvu za Yehova, ulamuliro wake, kapena malo ake, koma dzina lake lokhalo n’lomwe limam’dziŵikitsa iye yekha basi. (Eksodo 3:15; 1 Akorinto 8:5, 6) Dzina lenileni la Mulungu woona limasonyeza mikhalidwe yake ndi zochita zake. Katswiri wa zaumulungu Walter Lowrie molondola anati: “Munthu yemwe sadziŵa dzina la Mulungu ndiye kuti sam’dziŵa kwenikweni monga munthu.”

Lingalirani chitsanzo cha Maria, Mkatolika wodzipereka wa ku Australia. Mboni za Yehova zitakumana naye kwanthaŵi yoyamba, Maria analola kuti Mbonizo zimuonetse dzina la Mulungu m’Baibulo. Kodi anachitanji? “Nditaona dzina la Mulungu m’Baibulo kwanthaŵi yoyamba, ndinalira. Ndinasonkhezereka kwambiri pozindikira kuti ndadziŵadi dzina lenileni la Mulungu ndipo nditha kuligwiritsa ntchito.” Maria anapitiriza kuphunzira Baibulo, ndipo kwanthaŵi yoyamba m’moyo wake, anam’dziŵa Yehova monga munthu ndipo anali wokhoza kupanga naye ubwenzi wosatha.

Inde, ‘tingayandikire kwa Mulungu,’ ngakhale kuti sitingathe kumuona ndi maso athuŵa. Tingathe “kuona” umunthu wake wokongola mochititsa kasowo m’malingaliro ndi m’mitima yathu ndipo potero kukulitsa chikondi chathu mwa iye. Chikondi choterocho “ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”​—Akolose 3:14.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]

Yehova Amachitapo Kanthu Ngati Mukum’konda

UBWENZI umaphatikizapo zomwe mabwenziwo amachitirana. Pamene tiyandikira kwa Mulungu, amachitapo kanthu mwa kutiyandikira nafenso. Talingalirani mmene anakhudzidwira ndi Simeoni ndi Anna okalambawo, aŵiri onseŵa anatchulidwa mwapadera m’Baibulo. Wolemba Mauthenga Abwino Luka amatiuza kuti Simeoni anali “wolungama mtima ndi wopemphera,” podikira Mesiya. Yehova anaona makhalidwe abwino ameneŵa mwa Simeoni ndipo anasonyeza chikondi mwa mwamuna wokalamba ameneyu mwa kum’vumbulira kuti “sadzaona imfa, kufikira adzaona Kristu.” Yehova anasunga lonjezo lake ndi kutsogolera Simeoni kwa khandalo Yesu, yemwe anadza ku kachisi ku Yerusalemu ndi makolo Ake. Mwa chisangalalo ndi kuyamikira kwakukulu, Simeoni anayangata khandalo ndi kupemphera kuti: “Tsopano, Ambuye, monga mwa mawu anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu.”​—Luka 2:25-35.

“Pa nthaŵi yomweyo,” Yehova anasonyezanso chikondi chake kwa Anna wa zaka 84 mwa kum’tsogoleranso kwa Yesu. Baibulo limatiuza kuti mkazi wamasiye wosiririkayu sanachoka ku kachisi nthaŵi zonse ‘kupereka utumiki wopatulika’ kwa Yehova. Ndi chisangalalo chodzala tsaya, iye, mofanana ndi Simeoni, anathokoza Yehova kaamba ka chifundo chake chapaderacho, ndipo pambuyo pake analankhula za mwanayo “kwa anthu onse akuyembekeza chiwombolo cha Yerusalemu.”​—Luka 2:36-38.

Inde, Yehova anaona mmene Simeoni ndi Anna ankam’kondera ndi kumuopera komanso mmene anali kukhudzidwira mtima ndi kukwaniritsidwa kwa chifuno chake. Kodi nkhani za m’Baibulo ngati zimenezi sizikusonkhezerani kuyandikira kwa Yehova?

Monga Atate ake, Yesu ankazindikiranso munthu weniweni wam’kati. Akuphunzitsa m’kachisi, iye anaona “mkazi wina wamasiye waumphaŵi” akuika mosungiramo ndalama “timakobiri tiŵiri” tokha. Kwa anthu ena omuona mphatso yakeyo ikanakhala yosathandiza n’komwe, koma sizinali choncho kwa Yesu. Iye anayamikira mkazi ameneyu chifukwa chakuti anapereka zonse zimene anali nazo. (Luka 21:1-4) Choncho, tingakhale otsimikizira kuti Yehova ndi Yesu amatiyamikira ngati tiwapatsa zabwino zathu, mosasamala kanthu kuti mphatso yathuyo ndi yaikulu kapena yaing’ono.

Ngakhale kuti Mulungu amakondwera ndi omwe amam’konda, amamva chisoni kwambiri ngati anthu aleka kumutsata ndi kulondola njira zoipa. Genesis 6:6 amatiuza kuti Yehova “anavutika m’mtima mwake” chifukwa cha kuipa kwa mtundu wa anthu Chigumula cha m’tsiku la Nowa chisanafike. Patapita nthaŵi, Aisrayeli osamverawo mobwerezabwereza “[a]nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israyeli,” limatero Salmo 78:41. Inde, Mulungu sali “Mlengi wa Zonse” wopanda malingaliro. Ndithudi nayenso ndi munthu, yemwe malingaliro ake sali ofooka kapena ochepa mphamvu chifukwa chopanda ungwiro monga momwe alili athuŵa.

[Zithunzi patsamba 7]

Kuganizira za chilengedwe cha Yehova ndi njira imodzi yoyandikirira kwa iye