Kodi Kupambana Mumati N’kutani?
Kodi Kupambana Mumati N’kutani?
DIKISHONALE ina imamasulira kupambana monga “kupeza chuma, kuyanjidwa, kapena kutchuka.” Kodi tanthauzoli n’lokwanira? Kodi chuma, kuyanjidwa, kapena kutchuka n’zokhazo zimadziŵikitsa kupambana? Musanayankhe, lingalirani izi: Yesu Kristu sanali wolemera mwakuthupi m’nthaŵi ya moyo wake. Anthu ambiri sanam’yanje; ngakhale anthu otchuka sanamuone ngati wofunika. Komabe, Yesu anali munthu wopambana. Chifukwa chiyani?
Adakali padziko lapansi, Yesu anali “nacho chuma cha kwa Mulungu.” (Luka 12:21) Pambuyo pa chiukiriro chake, Mulungu anam’fupa mwa kumuveka korona “wa ulemerero ndi ulemu.” Yehova “anam’kwezetsa [Mwana wake] nam’patsa dzina limene liposa maina onse.” (Ahebri 2:9; Afilipi 2:9) Moyo wa Yesu unakondweretsa mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11) Moyo wake wapadziko lapansi unali wopambana chifukwa chakuti unakwaniritsa chifuno chake. Yesu anachita chifuno cha Mulungu ndi kudzetsera dzina lake ulemu. Choteronso Mulungu analemekeza Yesu mwa kum’patsa chuma, kum’yanja, ndi kum’tchukitsa mwapadera zomwe sizinachitikepo kwa katswiri aliyense wamaphunziro, wandale, kapena aliyense wotchuka m’zamaseŵera. Yesu analidi munthu wopambana kuposa aliyense amene anayenda padziko lapansi.
Makolo achikristu amazindikira kuti ngati ana awo atsatira mapazi a Kristu, kukhala nacho chuma cha kwa Mulungu monga momwe anachitira Yesu, adzatuta madalitso ochuluka tsopano lino komanso adzasangalala ndi mphoto zosaneneka m’dongosolo lazinthu likudzalo. Palibe njira ina yabwino kwa achinyamata yotsatirira mapazi a Kristu kuposa kugwira ntchito yomwe Yesuyo anagwira—mwa kuchita utumiki wa nthaŵi zonse ngati kuli kotheka.
Komabe, m’zikhalidwe zina, muli miyambo yomwe imaletsa achinyamata kuchita utumiki wa nthaŵi zonse. Pamene mnyamata wamaliza maphunziro ake, amati ayenera kupeza ntchito, kukwatira, ndi kumanga mudzi. Nthaŵi zina, achinyamata ochokera m’mafuko azikhulupiriro zotero amalakwa mwa kutaya mwayi woloŵa utumiki wa nthaŵi zonse. (Miyambo 3:27) Chifukwa chiyani? Pofuna kusangalatsa anthu ena, amagwirizana ndi miyezo ya chikhalidwe cha panthaŵiyo. Zimenezi n’zomwe zinam’chitikira Robert. *
Pamene Chikhalidwe ndi Chikumbumtima Zisemphana
Robert analeredwa monga wa Mboni za Yehova. M’zaka za unyamata wake, khalidwe lake ndiponso mabwenzi omwe anali kusankha anali osayenera. Amayi ake anayamba kum’dera nkhaŵa. Kenako, amayi akewo anapempha mpainiya, mtumiki wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova, kuti am’limbikitse. Robert akusimba zomwe zinachitika pambuyo pake.
“Ndinayamikira kwambiri chidwi chomwe mpainiya ameneyu anandionetsa. Chitsanzo chake chabwinocho chinandisonkhezera kuti ndikadzamaliza sukulu ntchito yanga idzakhale ya upainiya. Pamenepo amayi anayambanso kudera nkhaŵa—koma pachifukwa chosiyana. Mwaona nanga, m’chikhalidwe chathu m’pomveka kuti mtsikana achite upainiya atangomaliza sukulu, koma mnyamata amayenera kupeza chuma choyamba, ndiyeno pambuyo pake angaganize zochita upainiyawo.”
“Ndinaphunzira ntchito ndipo kenako ndinayamba bizinesi yangayanga. Posakhalitsa ndinaloŵerera m’bizinesi ndipo ndinkangopita kumisonkhano ndi kolalikira chifukwa chozoloŵera basi. Chikumbumtima changa chinanditsutsa kwambiri—ndinkadziŵa kuti ndikanatha kum’tumikira Yehova mokwanira. Ndithudi, panali matatalazi kuti ndimasuke ku zomwe ena ankafuna kuti ndichite, koma ndine wokondwa kuti ndinaterodi. Ndinakwatira tsopano, ndipo ine ndi mkazi wanga takhala tikuchita upainiya kuyambira zaka ziŵiri zapitazo. Posachedwapa, anandivomereza kukhala mtumiki wotumikira mu mpingo. Ndinganene moona mtima kuti tsopano ndikukhutira zedi pom’tumikira Yehova ndi mtima wanga wonse, monga momwe ndingathere.”
Magazini ino yakhala ikulimbikitsa achinyamata mobwerezabwereza kuti ngati n’kotheka aphunzire ntchito kapena maphunziro ena alionse ofunika adakali pasukulu. Ndi chifuno chotani? Kuti alemere? Iyayi. Chifukwa chachikulu n’chakuti adzathe kudzithandiza okha bwino lomwe akadzakula ndikuti adzatumikire Yehova mokwanira monga momwe angathere, makamaka mu utumiki wa nthaŵi zonse. Komatu zachitika kaŵirikaŵiri kuti anyamata ndi asungwana amaloŵerera kwambiri m’ntchito zakuthupi kotero kuti utumiki amauona ngati wosafunika kwenikweni. Ena saganiza n’komwe zoyamba utumiki wa nthaŵi zonse. Chifukwa chiyani satero?
Zimene Robert ananena pankhani imeneyi zingatithandize kumvetsa chifukwa chake. Mateyu 6:33 lili lotonthoza kwabasi kwa Akristu.
Ataphunzira ntchito yake, Robert anayamba bizinesi. Posapita nthaŵi, inasanduka chizoloŵezi chopanda tsogolo lodziŵika bwino. Cholinga chake chinali kukhala wokhutira pa nkhani yachuma. Koma kodi pali wina aliyense m’kati kapena kunja kwa mpingo wachikristu amene anakwaniritsapo cholinga chimenecho? Akristu ayenera kuyesetsa kuti akhale odzidalira pachuma, posamalira maudindo awo azachuma mwakhama; koma ayeneranso kuzindikira kuti m’nthaŵi zokayikitsa zino, n’ngochepa omwe amakhutiradi ndi chuma chomwe alinacho. N’chifukwa chaketu lonjezo la Yesu lolembedwa paRobert n’ngwokondwa kuti anasankha kutsatira zokhumba za mtima wake mmalo motsatira miyambo ya chikhalidwe chake. Lerolino, akusangalala ndi ntchito mu utumiki wa nthaŵi zonse. Inde, utumiki wa nthaŵi zonse ndi ntchito yapamwamba zedi. Robert ali pamtendere m’maganizo mwake chifukwa chakuti akutumikira Yehova, ‘monga momwe angathere.’
Gwiritsani Bwino Ntchito Maluso Anu
M’gulu la Mboni za Yehova muli anthu ambiri a mphatso zosiyanasiyana. Ena n’nganzeru zapamwamba, ena ali ndi maluso antchito zamanja. Mphatso zonsezi zimachokera kwa Yehova, amene amapatsa “[anthu] moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) Popanda moyo, mphatso zimenezi zingakhale zopanda phindu.
Choncho, n’koyenera kuti tigwiritse ntchito miyoyo yathu yodzipatulira potumikira Yehova. N’zomwe mnyamata wina wamaluso anachita. Anakhalako m’zaka za zana loyamba C.E. Anali wa m’banja lotchuka, anathera unyamata wake wonse mu mzinda wotchuka wa Tariso wa ku Kilikiya. Ngakhale kuti anali Myuda, anatengera unzika wa Roma kuchokera kwa atate wake. Zimenezo zinam’patsa ufulu ndi mwayi wochuluka. Atakula, anaphunzitsidwa Chilamulo ndi Gamaliyeli, mmodzi wa “mapulofesa” otchuka m’nthaŵiyo. Zinaoneka kuti posapita nthaŵi, ‘chuma, kuyanjidwa, ndi kutchuka’ zidzakhala zake.—Machitidwe 21:39; 22:3, 27, 28.
Kodi mnyamata ameneyu anali yani? Dzina lake anali Saulo. Koma m’kupita kwa nthaŵi Saulo anakhala Mkristu ndipo pambuyo pake anadzakhala mtumwi Paulo. Anaika pambali zimene ankafuna kuchita poyamba ndi kupatulira moyo wake wonse ku utumiki wa Yehova monga Mkristu. Paulo anatchuka, osati monga loya womveka, koma monga mlaliki wachangu wa uthenga wabwino. Atathera pafupifupi zaka 30 m’ntchito ya umishonale, Paulo analemba kalata yopita kwa mabwenzi ake ku Filipi. M’kalata imeneyi anatchula zina mwa zomwe anachita mmbuyomu asanakhale Mkristu, ndiyeno anati: “Chifukwa cha [Yesu Kristu] ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadziwonjezere Kristu.” (Afilipi 3:8) Ayi, Paulo sananong’oneze bondo chifukwa cha njira yomwe anagwiritsira ntchito moyo wake!
Nanga bwanji za maphunziro omwe Paulo analandira kuchokera kwa Gamaliyeli? Kodi anaŵagwiritsa ntchito m’njira iliyonse? Inde! Kangapo konse anathandizira “m’chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino.” Koma ntchito yaikulu ya Paulo inali kukhala mlaliki wa uthenga wabwino—chinthu chomwe maphunziro ake oyambirirawo sakanam’phunzitsa.—Afilipi 1:7; Machitidwe 26:24, 25.
Chimodzimodzinso lerolino, ena akhoza kugwiritsa ntchito mphatso ndi maluso awo ngakhalenso maphunziro awo kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu. Mwachitsanzo, Amy ali ndi digiri ya ku yunivesite m’zamalonda ndi inanso m’zamalamulo. Nthaŵi inayake anali pantchito yapamwamba pakampani ina ya maloya, koma tsopano akutumikira monga wantchito wodzifunira wosalipidwa pa ofesi ina yanthambi ya Watch Tower Society. Amy akufotokoza mmene moyo wake ulili panopa kuti: “Ndikukhulupirira kuti ndasankha chochita chabwino m’moyo. . . . Sindikhumbira ngakhale pang’ono kuti n’takhala ngati mnzanga aliyense wa ku yunivesite. Ndikunyadira ndi zomwe ndinasankha. Ndili ndi chilichonse chomwe ndingafune—moyo wokhutira ndi wokondwa komanso ntchito yoyenera ndi yokhutiritsa.”
Amy anasankha njira yomwe inam’patsa mtendere wamalingaliro, chikhutiro, ndi madalitso a Yehova. Ndithudi makolo achikristu amafunanso zomwezo mwa ana awo!
Kupambana mu Utumiki Wachikristu
Indedi, m’pofunika kumakuona bwino kupambana mu utumiki wachikristu weniweniwo. N’chapafupi kudzimva kukhala wopambana titathera
nthaŵi yosangalatsa mu utumiki wakumunda, kugaŵira mabuku ofotokoza Baibulo kapena kukambirana nkhani za m’Baibulo mosonkhezera ndi mwininyumba. Koma ngati nthaŵi zambiri sitipeza khutu lomvetsera, tingayesedwe mwa kulingalira kuti tikungotaya nthaŵi yathu. Komabe, kumbukirani kuti limodzi la matanthauzo a kupambana ndi ‘kupeza chiyanjo.’ Kodi timafuna kupeza chiyanjo chayani? Cha Yehovatu basi. Chiyanjo chimenechi tingachilandire kaya anthu amvetsere uthenga wathu kapena ayi. Yesu anaphunzitsa ophunzira ake phunziro lamphamvu kwambiri lokhudzana n’zimenezi.Mungakumbukire kuti Yesu anatumiza alaliki a Ufumu okwana 70 “kumudzi uliwonse, ndi malo alionse kumene ati afikeko mwini.” (Luka 10:1) Anafunikira kukalalikira m’matauni ndi m’midzi paokha popanda Yesu kuwatsogolera. Chimenechi chinali chinthu chachilendo kwa iwo. Chotero, Yesu anaŵapatsa malangizo atsatanetsatane asanawatumize. Ngati atakumana ndi “mwana wa mtendere,” anafunikira kum’chitira umboni womveka bwino wokhudza Ufumuwo. Komabe, ngati atakanidwa, anafunikira kungochokapo ndi kupitiriza ulendo wawo, osadera nkhaŵa za chilichonse. Yesu anafotokoza kuti awo amene anali kukana kuwamvetsera kwenikweni anali kukana Yehova mwiniyo.—Luka 10:4-7, 16.
Alaliki 70 aja atamaliza ntchito yawo yolalikira, anabwerera ndi kukauza Yesu zimene zinawachitikira “mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m’dzina lanu.” (Luka 10:17) Ziyenera kuti zinali zosangalatsa zedi kwa anthu opanda ungwirowo kutulutsa zolengedwa zauzimu zamphamvu! Ngakhale zinali choncho, Yesu anachenjeza ophunzira ake achanguwo kuti: ‘Musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m’Mwamba.’ (Luka 10:20) N’kutheka kuti alaliki 70 amenewo sanali kudzakhala ndi mphamvu yotulutsa ziwanda nthaŵi zonse, ndiponso sanali kudzakhala ndi zotsatira zabwino mu utumiki nthaŵi zonse. Koma ngati akanakhalabe okhulupirika, akanayanjidwa ndi Yehova nthaŵi zonse.
Kodi Atumiki Anthaŵi Zonse M’Mawayamikira?
Nthaŵi inayake mnyamata wina anauza mkulu wachikristu kuti: “Ndikadzamaliza maphunziro anga ku sekondale, ndidzayesa kufufuza ntchito. Ndikadzapanda kuipeza, m’pamene ndidzalingalire zochita mtundu winawake wa utumiki wa nthaŵi zonse.” Komatu anthu ochuluka omwe ayamba utumiki waupainiya analibe malingaliro otereŵa. Kuti achite upainiyawo, ena sanalabadire za mwayi woloŵa ntchito yapamwamba. Ena anyalanyaza mwayi wochita maphunziro apamwamba. Mofanana ndi mtumwi Paulo, asiya zinthu zina zofunika, koma monganso Paulo, Robert, ndi Amy, sakunong’oneza bondo chifukwa cha zosankha zawo. Akuyamikira kwambiri mwayi wawo wogwiritsa ntchito mphatso zawo potamanda Yehova, yemwe ndi woyenerera kupatsidwa zabwino zonse zomwe iwo angapereke.
Pazifukwa zosiyanasiyana, Mboni zambiri zokhulupirika za Yehova zikulephera kuchita upainiya. Mwinamwake ali ndi maudindo a m’Malemba omwe afunikira kuwasamalira. Komabe, ngati akutumikira Mulungu ndi ‘mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse, ndi nzeru zawo zonse,’ Yehova akukondwera nawo. (Mateyu 22:37) Ngakhale kuti iwo akulephera kuchita upainiya, amazindikira kuti awo amene akuchita upainiyawo asankha ntchito yabwino.
Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano.” (Aroma 12:2) Mogwirizana ndi uphungu wa Paulowu, sitiyenera kulola miyezo yachikhalidwe kapena yakudziko kuwumba malingaliro athu. Kaya mungathe kuchita upainiya kapena ayi, pangani utumiki wa Yehova kukhala chifuno cha moyo wanu. Mudzapambana mukakhalabe ndi chiyanjo cha Yehova.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Mayina asinthidwa.
[Chithunzi patsamba 19]
Musataye nthaŵi chifukwa cha chizoloŵezi chopanda tsogolo lodziŵika bwino