Kodi Makhalidwe a M’Baibulo Ndiwo Ali Abwino Koposa?
Kodi Makhalidwe a M’Baibulo Ndiwo Ali Abwino Koposa?
“ANTHU akufuna mfundo zikuluzikulu za makhalidwe abwino zowateteza ndi kuwatsogolera.” Anatero munthu wina wa ku German wodziŵa bwino zolembalemba ndi kuulutsa mawu pa wailesi yakanema. Ndithudi mfundo imeneyi n’njomveka. Kuti anthu akhazikike ndiponso kupita patsogolo, ayenera kukhala ndi maziko olimba a miyezo yovomerezeka ndi wina aliyense yomwe imasonyeza chomwe chili cholondola kapena cholakwika, chabwino kapena choipa. Koma funso n’lakuti: Kodi ndi miyezo iti imene ili yabwino kwambiri kwa anthu onse?
Ngati makhalidwe abwino a m’Baibulo atakhala miyezo yogwiritsidwa ntchito, angathandize munthu aliyense kusangalala ndi moyo wabata ndi wachimwemwe. Mokulira, zimenezo zingachititse anthu amakhalidwe amenewo kukhala okondwa ndi okhazikika kwambiri. Kodi zinthu zili choncho? Tiyeni tipende zomwe Baibulo likunena pa nkhani ziŵiri zofunika kwambiri: kukhulupirika muukwati ndi kuona mtima m’moyo watsiku ndi tsiku.
Khulupirikani kwa Mwamuna Kapena Mkazi Wanu
Mlengi wathu analenga Adamu ndipo kenako anapanga Hava kuti akhale mnzake. Ukwati wawo unali woyamba m’mbiri ndipo unayenera kukhala ubwenzi wosatha. Mulungu anati: “Mwamuna adzasiya atate Genesis 1:27, 28; 2:24; Mateyu 5:27-30; 19:5.
wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake.” Zaka 4,000 zitadutsa, Yesu Kristu anadzabwereza kunenanso muyezo wa ukwati umenewu kwa otsatira ake onse. Kuwonjezera pamenepo, anatsutsa kugonana kunja kwa ukwati.—Malinga n’kunena kwa Baibulo, makiyi aŵiri ofunika kwambiri a ukwati wachimwemwe n’ngakuti okwatiranawo azikondana ndikuti azipatsana ulemu. Mwamuna, yemwe ndi mutu wabanja, ayenera kusonyeza chikondi chopanda dyera mwa kuyesetsa kuchita zomwe mkazi wake amakonda. Ayenera kukhala naye “monga mwa chidziŵitso” ndi ‘kusam’wawira mtima.’ Mkazi ayenera ‘kukumbukira kuti aziopa mwamuna’ wake. Okwatirana atamatsatira mfundo zimenezi zachikhalidwe, angathe kupeŵa kapena kuthetsa mavuto ambiri am’banja. Mwamuna angamafune kukhulupirika kwa mkazi wake ndi mkazi kwa mwamuna wake.—1 Petro 3:1-7; Akolose 3:18, 19; Aefeso 5:22-33.
Kodi muyezo wa Baibulo wokhala wokhulupirika kwa mnzathu wa muukwati umachititsa ukwati kukhala wachimwemwe? Talingalirani zotsatira za kufufuza kochitidwa m’dziko la Germany. Anthu anafunsidwa mfundo zomwe zili zofunika muukwati wabwino. Imodzi mwa mfundo zofunika kwambiri zomwe anthu anatchula inali yakuti nonse aŵiri muyenera kukhulupirika. Kodi simungavomereze kuti anthu okwatirana amakhala okondwa zedi akadziŵa kuti amene anakwatirana naye n’ngwokhulupirika?
Bwanji Ngati Mavuto Abuka?
Komano, bwanji ngati mwamuna ndi mkazi sakumvana? Bwanji ngati chikondi chawo chazirala? Kodi zikafika pamenepa si kwabwino kungothetsa ukwatiwo? Kapena kodi chingakhale chanzeru kutsatira muyezo wa m’Baibulo uja wokhala wokhulupirika kwa mnzako wa muukwati?
Olemba Baibulo anadziŵa kuti okwatirana onse adzakumana ndi mavuto chifukwa cha umunthu wopanda ungwirowu. (1 Akorinto 7:28) Komabe, okwatirana amene amatsatira miyezo ya m’Baibulo ya makhalidwe amayesa kukhululuka ndi kuthandizana kuthetsa mavuto awowo. Inde, pamachitika zinthu zina monga chigololo kapena ndewu, pamene moyenerera Mkristu angalingalire zopatukana kapena zachisudzulo. (Mateyu 5:32; 19:9) Koma kuthetsa ukwati mopupuluma popanda chifukwa chomveka kapena pofuna kungopeza wina wokwatirana naye kumasonyeza kusalabadira ena chifukwa chadyera. Mwachionekere sikudzetsa mtendere kapena chimwemwe m’moyo wa aliyense. Tiyeni tione chitsanzo ichi.
Peter anaona kuti banja lake silikusangalatsanso. * Choncho, anam’leka mkazi wake ndi kutenga Monika yemwe anali atathaŵa mwamuna wake. Kodi zinthu zinatha bwanji pamenepa? M’miyezi yoŵerengeka chabe, Peter anavomereza kuti kukhala ndi Monika “sichinali chinthu chapafupi monga momwe ndimalingalirira.” Chifukwa chiyani? Mofanana ndi munthu aliyense chibwenzi chake chatsopanochi chinali ndi zophophonya zambiri monga momwe analili mkazi wake wakale uja. Kuwonjezera pa mavuto amenewo, iye anapeza mavuto aakulu azachuma chifukwa chochita zinthu mopupuluma ndi kusankha kuchita zinthu mwadyera. Komanso, ana a Monika anavutika maganizo kwambiri chifukwa cha kusintha kwakukulu kwa moyo wa m’banja lawo.
Monga momwe nkhani imeneyi yasonyezera, banja likakhala pa mavuto adzaoneni, kulithaŵa sindiko njira yowathetsera. M’malo mwake, panthaŵi ya mavuto, kuchita zinthu mogwirizana ndi makhalidwe abwino a m’Mawu a Mulungu, Baibulo, kaŵirikaŵiri kungapangitse ukwatiwo kukhala wolimba ndikuti okwatiranawo akhale mogwirizana. Zimenezi n’zomwe zinachitikira Thomas ndi Doris.
Thomas ndi Doris anali atakwatirana kwa zaka zoposa 30 pamene Thomas anayamba kumwa mowa mwauchidakwa. Doris anavutika maganizo kwambiri, ndipo aŵiriwo ankauzana zoti adzasudzulana. Doris anauza wa Mboni za Yehova wina zakukhosi. Wamboniyo anam’sonyeza Doris zomwe Baibulo limanena pankhani ya ukwati, ndi kumulimbikitsa kuti asafulumire kupatukana koma kuti choyamba akakambirane ndi mwamuna wake kuti ayese kupeza njira yothetsera vutolo. Doris anachitadi zomwezo. M’miyezi yoŵerengeka chabe, analekeratu kulingalira zosudzulana. Thomas ndi Doris anali kuthandizana kuthetsa mavuto awowo. Kutsatira uphungu wa m’Baibulo kunalimbitsa ukwati wawo ndipo kunawapatsa nthaŵi yothetsera mavuto awo.
Kuona Mtima M’Zinthu Zonse
Kuti munthu akhale wokhulupirika kwa wokwatirana naye amafunika kukhala wakhalidwe labwino zedi ndi wokonda kutsatira mfundo za chikhalidwe. Khalidwe lomweli n’lofunikanso kuti tikhale oona mtima m’dziko losaona mtimali. Baibulo limatiuza zambiri zokhudza kuona mtima. Mtumwi Paulo analembera Akristu a m’zaka za zana loyamba ku Yudeya kuti: “Ife tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Ahebri 13:18, NW) Kodi zimenezo zikutanthauzanji?
Munthu woona mtima amanena zoona ndiponso sachita chinyengo. N’ngwachilungamo pochita zinthu ndi ena—wolunjika, wolemekezeka, osati wophimba anzake m’maso kapena wosocheretsa. Komanso munthu woona mtima ndi munthu wokhulupirika yemwe sachitira anthu ena ukathyali. Anthu oona mtima amalimbikitsa mzimu wodalirana ndi wokhulupirirana, womwe umadzetsa malingaliro abwino ndi kulimbikitsa unansi wamphamvu pakati pa athu.
Kodi anthu oona mtima n’ngachimwemwe? Inde, ali ndi zifukwa zokwanira zokhalira achimwemwe. Ngakhale kuti ziphuphu ndi ukathyali zafala padziko lonse—kapena tinene kuti chifukwa cha zimenezi—anthu oona mtima nthaŵi zonse amalemekezedwa. Malinga ndi kufufuza kumene kunachitidwa mwa achinyamata, 70 mwa achinyamata 100 omwe anafunsidwa anati kuona mtima ndiwo mkhalidwe wabwino kuposa makhalidwe onse abwino. Kuwonjezera apo, kaya ndife amsinkhu wotani, chofunika kwambiri kwa anthu omwe timawaona ngati anzathu ndicho kuona mtima.
Christine anaphunzitsidwa kuba ali ndi zaka 12. M’kupita kwa zaka iye anakhala katswiri wopisa anthu m’matumba. Iye akufotokoza kuti: “Masiku ena ndinkapita kunyumba ndi ndalama zochuluka zokwana madola 2,200.” Koma Christine anamangidwa kambirimbiri, ndipo nthaŵi ina iliyonse akanatha kum’tumiza kundende. Mboni za Yehova zitam’fotokozera zomwe Baibulo limanena pankhani ya kuona mtima, Christine anakopeka ndi makhalidwe abwino a m’Baibulo. Anaphunzira kumvera chenjezo lakuti: “Wakubayo asabenso.”—Aefeso 4:28.
Panthaŵi yomwe Christine amabatizidwa kuti akhale wa Mboni za Yehova, sanalinso wakuba. Anali kuyesetsa kukhala woona mtima m’zinthu zonse, chifukwa chakuti Mboni zimagogomezera kwambiri kuona mtima ndiponso makhalidwe ena achikristu. Nyuzipepala yotchedwa Lausitzer Rundschau inati: “Mawu osonyeza makhalidwe abwino monga akuti kuona mtima, kuchita zinthu mosapambanitsa, ndi kukonda anansi, amaikidwa pamwamba m’chikhulupiriro cha Mboni.” Kodi Christine akumva bwanji chifukwa cha kusintha kwa moyo wakewo? “Ndine wokondwa zedi tsopano kuti ndinaleka kuba. Ndikuona kuti ndine munthu wolemekezeka pakati pa anthu anzanga.”
Anthu Onse Amapindula
Anthu okhulupirika kwa amene anakwatirana nawo komanso amene ali oona mtima samangokhala achimwemwe iwo okha koma n’ngothandiza kwa anthu onse. Olemba anthu ntchito amafuna anthu omwe sachita ukathyali. Tonsefe timafuna kukhala ndi anansi odalirika, ndipo timakonda kugula zinthu m’masitolo a anthu achilungamo. Kodi sitimapereka ulemu kwa andale, apolisi, ndi oweruza milandu odana ndi ziphuphu? Mudzi wonse umapindula kwambiri ngati anthu am’mudzimo nthaŵi zonse amakhala oona mtima mwamwambo, osati kokha pamene aona kuti akachita moona mtima zinthu ziwakomera.
Kuwonjezera pamenepo, okwatirana okhulupirika ndiwo amapanga mabanja olimba. Ndipotu anthu ambiri angagwirizane ndi wandale wa ku Ulaya yemwe anati: “Kufikira lerolino, mabanja [osunga mwambo] akhalabe malo ofunika kwambiri poteteza anthu komanso kuti akhale aphindu.” M’banja lamtendere ndi momwe makolo ndi ana amakhala ndi ufulu wonse wokhala otetezereka mwa maganizo. Anthu amene ali okhulupirika muukwati ndiye kuti akuthandiza anthu onse kukhalira pamodzi mogwirizana.
Talingalirani mmene aliyense angapindulire kutakhala kuti okwatirana sakulekana, kulibe makhoti opereka chisudzulo, kapena milandu yolimbirana ana. Nanga bwanji kudakakhala kuti kulibiretu atsinzina n’tole, akuba katundu wam’sitolo, ochita katangale pa ndalama kapena katundu wakampani, akuluakulu aboma akatangale, kapena a zasayansi achinyengo? Kodi zimenezo zikukhala ngati zosatheka? Sizotero kwa omwe amachita chidwi ndi Baibulo komanso zomwe limanena kuti zidzachitika m’tsogolo. Salmo 37:29.
Mawu a Mulungu amalonjeza kuti posachedwapa Ufumu wa Yehova wa Umesiya uyamba kulamulira anthu onse padziko lapansi. Mu Ufumu umenewu nzika zake zonse zidzaphunzitsidwa kukhala mogwirizana ndi makhalidwe a m’Baibulo. Panthaŵiyo, “olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Makhalidwe a M’Baibulo Ndiwo Ali Abwino Koposa
Anthu mamiliyoni ambiri omwe apenda Malemba Oyera mosamalitsa azindikira kuti uphungu wa m’Baibulo n’ngozikika m’nzeru yaumulungu, yomwe n’njapamwamba zedi kuposa malingaliro a anthu. Anthu oterowo amaliona Baibulo kukhala lodalirika ndi lothandiza kwambiri m’moyo m’dziko lathu lamakonoli. Amadziŵa kuti adzapindula kwambiri ngati atamvera uphungu wa m’Mawu a Mulungu.
Choncho, anthu amenewo amamvera malangizo am’Baibulo akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Mwakuchita zimenezo, amasintha miyoyo yawo kotheratu, ndipo amapindulitsanso anthu okhala nawo limodzi. Ndipo amakulitsa chidaliro champhamvu ‘m’moyo ulinkudza,’ pamene makhalidwe a m’Baibulo adzatsatiridwa ndi mtundu wonse wa anthu.—1 Timoteo 4:8.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Mayina asinthidwa m’nkhani ino.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Panthaŵi ya mavuto, kukhala mogwirizana ndi miyezo ya m’Baibulo kaŵirikaŵiri kungapangitse ukwati kukhala wolimba ndi kuupangitsa kukhala wabata
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Ngakhale kuti ziphuphu zafala padziko lonse—kapena tinene kuti chifukwa cha ziphuphuzi—anthu oona mtima nthaŵi zonse amalemekezedwa