Lingaliro Laumulungu la Khalidwe Loyera
Lingaliro Laumulungu la Khalidwe Loyera
“Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.”—YESAYA 48:17.
1, 2. (a) Kodi anthu ochuluka amaiona motani nkhani ya kugonana? (b) Kodi Akristu amaiona motani nkhani ya kugonana?
LEROLINO, m’madera ambiri a dziko lapansi, anthu tsopano amaona khalidwe kukhala chosankha cha munthu aliyense payekha. Anthu amaona kugonana kukhala njira yachibadwa yosonyezera chikondi imene anthu angachite nthaŵi ina iliyonse imene akufuna, osati monga chinthu cha muukwati mokha iyayi. Iwo amati ngati palibe amene akuvulazidwa, ndiye kuti sikulakwa munthu kudzisankhira yekha khalidwe lake. Malinga ndi kuona kwawo, palibe amene ayenera kunena mnzake pankhani ya khalidwe, makamaka pankhani ya kugonana.
2 Awo amene am’dziŵa Yehova ali ndi malingaliro ena. Iwo n’ngokondwa kutsatira chitsogozo cha m’Malemba chifukwa chakuti amakonda Yehova ndipo amafuna kum’kondweretsa. Iwo amadziŵa kuti Yehova amawakonda ndipo amawapatsa chitsogozo choti chiwathandize, chitsogozo choti chiwapinduliredi ndi kuwapatsa chimwemwe. (Yesaya 48:17) Tsono poti Mulungu ndiye Gwero la moyo, n’kwanzeru kuti azim’dalira iye powauza mmene angagwiritsire ntchito matupi awo, makamaka pankhani iyi yokhudzana kwambiri ndi kupatsira moyo.
Mphatso ya Mlengi Wachikondi
3. Kodi anthu ochuluka m’Matchalitchi Achikristu aphunzitsidwa zotani ponena za kugonana, ndipo kodi zimenezo zikugwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa?
3 Mosiyana ndi zimene dzikoli likuphunzitsa, ena m’Matchalitchi Achikristu akhala akuphunzitsa kuti kugonana n’chinthu chochititsa manyazi, Genesis 2:25) Mulungu anawauza kuti akhale ndi ana, nati: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Sichikanakhala chilugamo kuti Mulungu alamule Adamu ndi Hava kuti abale ana kenako n’kuwalanga potsatira malangizowo.—Salmo 19:8.
chauchimo, ndi kuti “tchimo loyambirira” m’munda wa Edene linachitika pamene Hava ananyenga Adamu kuti agone naye. Lingaliro limeneli likutsutsana ndi zimene Malemba ouziridwa amanena. Baibulo limanena za anthu aŵiri oyambirirawo kukhala “mwamuna ndi mkazi wake.” (4. N’chifukwa chiyani Mulungu analenga anthu kuti azitha kugonana?
4 M’lamulo lomwe linaperekedwa kwa makolo athu oyambirira limenelo, lomwe linabwerezedwa kwa Nowa ndi ana ake aamuna, tikuonamo cholinga chachikulu cha kugonana, chomwe ndi kubala ana. (Genesis 9:1) Ngakhale zili motero, Mawu a Mulungu amasonyeza kuti atumiki ake okwatirana sakulamulidwa kuti azigonana pofuna kukhala ndi ana pokha ayi. Mchitidwe umenewu pakati pa mwamuna ndi mkazi wake umatha kukwaniritsa zosoŵa za mumtima ndi zakuthupi ndipo umadzetsa chimwemwe kwa okwatirana. Kwa iwo, ndi njira ina yosonyezera chikondi chakuya kwa wina ndi mnzake.—Genesis 26:8, 9; Miyambo 5:18, 19; 1 Akorinto 7:3-5.
Malire Oikidwa ndi Mulungu
5. N’chiyani chimene Mulungu waletsa anthu pankhani ya kugonana?
5 Ngakhale kuti kugonana ndi mphatso yoperekedwa ndi Mulungu, si kuti anthu ayenera kukuchita monga momwe akufunira. Mfundo imeneyi ikukhudzanso ngakhale anthu okwatirana. (Aefeso 5:28-30; 1 Petro 3:1, 7) Kugonana ndi munthu yemwe sunakwatirane naye n’koletsedwa. Baibulo silipita m’mbali pankhani imeneyi. M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa mtundu wa Israyeli, munali lamulo lakuti: “Usachite chigololo.” (Eksodo 20:14) Pambuyo pake, Yesu anawonjezapo “zachiwerewere” ndi “zachigololo” pamodzinso ndi “maganizo oipa” zomwe zimatuluka mumtima wa munthu ndi kumuipitsa. (Marko 7:21, 22) Mtumwi Paulo anauziridwa kulangiza Akristu a ku Korinto kuti: “Thaŵani dama.” (1 Akorinto 6:18) Ndiponso m’kalata yake yopita kwa Ahebri, Paulo analemba kuti: “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse; ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.”—Ahebri 13:4.
6. M’Baibulo, kodi mawu akuti “dama” amatanthauzanji?
6 Kodi mawu akuti “dama” akutanthauzanji? Mawuwo amatembenuza mawu achigiriki akuti por·neiʹa, amene nthaŵi zina amatchulidwa pofuna kutanthauza kugonana kwa anthu omwe ndi mbeta. (1 Akorinto 6:9) Penapakenso, monga pa Machitidwe 21:25 ndi pa Agalatiya 5:19, mawuwo ali ndi matanthauzo ambiri ndipo amatanthauzanso chigololo, kugonana kwa pachibale, ndi kugonana kwa munthu ndi nyama. Zochitika za mtundu winanso zokhudzana ndi kugonana zochitika pakati pa anthu aŵiri osakwatirana, monga kugonana m’kamwa ndi kugonana kumatako komanso kugwiragwira mpheto ya wina pofuna kum’dzutsira chilakolako, kungatchedwenso kuti por·neiʹa. M’Mawu a Mulungu, zochitika zonsezi n’zoletsedwa—mwachindunji kapena m’mawu ena.—Levitiko 20:10, 13, 15, 16; Aroma 1:24, 26, 27, 32. *
Kupindula ndi Malamulo a Mulungu a Khalidwe
7. Kodi timapindula motani ngati tisunga khalidwe loyera?
7 Kumvera chitsogozo cha Yehova pankhani ya kugonana kungakhale kovuta kwambiri kwa anthu opanda ungwiro. Wafilosofi wachiyuda wotchukayo wa m’zaka za m’ma 1100 wotchedwa Maimonides analemba kuti: “M’Torah yense [Chilamulo chonse cha Mose] mulibe lamulo linanso loletsa chinthu lovuta kulitsatira kuposa lamulo loletsa makhalidwe oipa achiwerewere.” Koma ngati titsatira chitsogozo cha Mulungu, timapindula kwambiri. (Yesaya 48:18) Mwachitsanzo, kumvera malangizo pankhaniyi kumatithandiza kukhala otetezeka ku matenda opatsirana mwa kugonana, ena amene ndi osachiritsika ndipo n’ngakupha. * Timatetezedwa ku mimba zapathengo. Kutsatira nzeru zaumulungu kumatithandizanso kukhala ndi chikumbumtima choyera. Kuchita zimenezi kumalimbikitsa kudzilemekeza kwathu ndi kuti enanso atilemekeze, kuphatikizapo anansi athu, mkazi kapena mwamuna wathu, ana athu, ndi abale ndi alongo athu achikristu. Kumatipangitsanso kukhala ndi maganizo abwino ndiponso oyenera ponena za kugonana amene adzatithandiza kukhala achimwemwe muukwati. Mkazi wina wachikristu analemba kuti: “Choonadi cha Mawu a Mulungu ndicho chitetezo chabwino koposa chimene munthu angakhale nacho. Posachedwapa ndiloŵa m’banja, ndipo pambuyo pokwatiwa ndidzakhala wofunitsitsa kuuza mwamuna wachikristu amene adzandikwatireyo kuti ndakhala wodzisunga mpaka pano.”
8. Kodi khalidwe lathu loyera lingalimbikitse motani kulambira koyera?
8 Mwa kudzisungira khalidwe loyera, tingathandizirenso kutsutsa malingaliro olakwika ponena za kulambira koona ndipo tingapangitse anthu kukopeka ndi Mulungu amene timam’lambira. Mtumwi Petro analemba kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.” (1 Petro 2:12) Ngati anthu osatumikira Yehova sangaone khalidwe lathu loyera kapena ngati anyansidwa nalo, tingakhale otsimikizira kuti Atate wathu wakumwamba akuona, akuyamikira, ngakhalenso kusangalala pamene tiyesayesa kutsatira chitsogozo chake.—Miyambo 27:11; Ahebri 4:13.
9. N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira chitsogozo cha Mulungu, ngakhale ngati sitingamvetse zifukwa zake? Perekani chitsanzo.
9 Kukhulupirira Mulungu kumaphatikizapo kum’dalira kuti akudziŵa zimene zingatipindulitse, ngakhale ngati sitikumvetsa chifukwa chimene akutitsogolera m’njira imeneyo. Nachi chitsanzo china cha m’Chilamulo cha Mose. Lamulo lina lokhudza misasa ya asilikali linalamula kuti chimbudzi cha anthu chizifotseredwa pansi kunja kwa msasa. (Deuteronomo 23:13, 14) Mwinamwake Aisrayeli sanali kumvetsa chifukwa chimene anapatsidwira langizo limenelo; mwinanso ena anaganiza kuti n’losafunika. Koma kuchokera pamenepo, sayansi ya za thupi la munthu tsopano yazindikira kuti lamulo limeneli linathandizira kuti madzi awo asamakhale oipa ndi oyambitsa matenda ndipo lamulo lomwelo linalinso chitetezo ku matenda odza ndi tizilombo. Mofananamo, pali zifukwa zauzimu, zifukwa zokhudza makhalidwe a anthu, zifukwa za malingaliro a mumtima, zifukwa zakuthupi, ndi za m’maganizo zimene zinapangitsa Mulungu kulamulira kuti kugonana kuzichitika muukwati mokha basi. Tiyeni tsopano tikambirane zitsanzo zingapo za m’Baibulo za anthu amene anasunga khalidwe loyera.
Yosefe—Anadalitsidwa ndi Khalidwe Lake Labwino
10. Ndani anayesa kunyenga Yosefe, ndipo Yosefe anati chiyani poyankha?
10 Muyenera kuti mukudziŵa za chitsanzo cha m’Baibulo cha Yosefe, mwana wa Yakobo. Pamene anali ndi zaka 17 zakubadwa, iye anali kapolo wa Potifara, kazembe wa alonda a Farao wa Igupto. Yehova anadalitsa Yosefe, ndipo m’kupita kwa nthaŵi Genesis 39:1-9.
anaikidwa kukhala woyang’anira nyumba yonse ya Potifara. Pamene anali ndi zaka zakubadwa za m’ma 20, Yosefe anali atakhala “wokoma thupi ndi wokongola.” Pokopeka naye, mkazi wa Potifara anayesa kum’nyenga. Yosefe analongosola malingaliro ake mosapita m’mbali, ndipo analongosola kuti kulola kuchita zimenezo sikudzakhala kungopita mbuye wake pansi komanso “kuchimwira Mulungu.” N’chifukwa chiyani Yosefe anali ndi malingaliro amenewo?—11, 12. Ngakhale kuti panalibe lamulo la Mulungu lolembedwa loletsa dama ndi chigololo, chingakhale chifukwa chiyani chimene Yosefe analili ndi malingaliro amenewo?
11 Umboni ukusonyeza kuti Yosefe sanasankhe kukana poopa kuti anthu am’tulukira ayi. Banja la Yosefe linkakhala kutali kwambiri, ndipo atate wake ankaganiza kuti iye anafa. Yosefe akanati achite chiwerewere, banja lake silikanadziŵa kalikonse. Mwina Potifarayo ndi antchito ake aamuna sakanadziŵanso za tchimo limenelo, popeza nthaŵi zina sanali kukhalamo m’nyumbamo. (Genesis 39:11) Koma Yosefe anadziŵa kuti khalidwe limenelo silingabisike kwa Mulungu.
12 Yosefe ayenera kuti anakana malinga ndi zimene ankadziŵa ponena za Yehova. M’posakayikitsa kuti anali kudziŵa zimene Yehova ananena m’munda wa Edene kuti: “Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Kuwonjezera apo, Yosefe ayenera kuti anali kudziŵa zimene Yehova anauza mfumu yachifilisiti yomwe inafuna kunyenga agogo aakazi a makolo a Yosefe, Sara. Yehova anauza mfumuyo kuti: ‘Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wam’tenga: Pakuti iye ndiye mkazi wa mwini. . . . Ndipo inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: Chifukwa chake sindinakuloleza iwe kuti um’khudze mkaziyo.’ (Genesis 20:3, 6) Chotero pamene Yehova anali asanapereke lamulo lolembedwa, malingaliro ake ponena za ukwati anali odziŵika bwino lomwe. Kuzindikira khalidwe labwino kwa Yosefe, pamodzinso ndi kufunitsitsa kwake kuti akondweretse Yehova, zinam’pangitsa kukana chisembwere.
13. Kodi mwina n’chifukwa chiyani Yosefe sakanatha kupeŵa mkazi wa Potifara?
13 Komabe, mkazi wa Potifara sanaimire pomwepo, ndipo anam’chonderera “tsiku ndi tsiku” kuti agone naye. Bwanji Yosefe sanangom’peŵa? N’zoonadi, koma monga kapolo anayenera kugwira ntchito yake ndipo sakanachitiranso mwina. Umboni womwe akatswiri odziŵa za midzi yamakedzana apeza ukusonyeza kuti malinga ndi kamangidwe ka nyumba zachiigupto, munthu anayenera kudutsa m’kati mwenimweni mwa nyumba kuti afike kuzipinda zosungirako zinthu. Chotero, mwina sizinali zotheka kuti Yosefe apeŵe kuonana ndi mkazi wa Potifara.—Genesis 39:10.
14. (a) N’chiyani chinachitika pamene Yosefe anathaŵa mkazi wa Potifara? (b) Kodi Yehova anam’dalitsa motani Yosefe chifukwa cha kukhulupirika kwake?
14 Tsiku linafika pamene analimo aŵiriŵiri m’nyumbamo. Mkazi wa Potifara anagwira Yosefe amvekere: “Gona ndi ine”! Yosefe anathaŵa. Powawidwa mtima ndi kukana kwakeko, mkaziyo anam’semera mlandu wakuti anafuna kum’gwirira. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Kodi Yehova anafupa kukhulupirika kwake nthaŵi yomweyo? Iyayi. Yosefe anaponyedwa m’ndende ndipo anamangidwa m’matangadza. (Genesis 39:12-20; Salmo 105:18) Yehova anaona chisalungamo chimenecho ndipo m’kupita kwa nthaŵi anakweza Yosefe kuchoka m’ndende kukakhala m’nyumba yachifumu. Anakhala wolamulira wachiŵiri wamkulu koposa m’Igupto ndipo anadalitsidwa ndi mkazi ndi ana. (Genesis 41:14, 15, 39-45, 50-52) Kuwonjezera apo, nkhani ya kukhulupirika kwa Yosefe inalembedwa zaka zoposa 3,500 zapitazo kuti atumiki a Mulungu kuyambira nthaŵiyo aziiphunzira. Ndi madalitsotu aakulu chifukwa cha kumamatirabe ku malamulo olungama a Mulungu! Mofananamo, ifenso lerolino mwina sitingawaone mofulumira mapindu okhalira ndi khalidwe lokhulupirika, koma tingakhale otsimikizira kuti Yehova amaona ndipo adzatidalitsa panthaŵi yake.—2 Mbiri 16:9.
‘Pangano la Yobu ndi Maso Ake’
15. Kodi ‘pangano la Yobu ndi maso ake’ linali lotani?
15 Winanso amene anasunga kukhulupirika ndiye Yobu. Pamayesero oyambitsidwa ndi Mdyerekezi, Yobu analongosola mmene moyo wake unalili ndipo ananena kuti ndi wokonzeka kulandira chilango chachikulu ngati, kuphatikizapo zinthu zina, anaswanso mfundo yamakhalidwe ya Yehova yokhudza kugonana. Yobu anati: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?” (Yobu 31:1) Ndi mawuwa, Yobu ankatanthauza kuti pofunitsitsa kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu, anatsimikizira mtima wake kuti adzapeŵa kuyang’anitsitsa mkazi mom’sirira. Inde, anali kuwaona akazi m’zochitika za tsiku ndi tsiku ndipo ayenera kuti anali kuwathandiza akafuna thandizo. Koma ponena za kuchita chidwi ndi mkazi chifukwa chom’funa, zimenezo sanachite n’komwe. Mayesero ake asanayambe, anali mwamuna wolemera kwambiri, “anaposa anthu onse a kum’maŵa.” (Yobu 1:3) Komabe, sanagwiritse ntchito chuma chakecho kuti akope nacho akazi ambiri. N’zoonekeratu kuti sanayese n’komwe kulingalira za kuchita chiwerewere ndi akazi ena ocheperapo msinkhu.
16. (a) N’chifukwa chiyani Yobu ali chitsanzo chabwino kwa Akristu okwatirana? (b) Kodi khalidwe la anthu m’tsiku la Malaki linasiyana motani ndi khalidwe la Yobu, nanga lero?
16 Chotero m’nthaŵi yabwino ndi yovuta yomwe, Yobu anasungabe khalidwe lake labwino. Yehova anaona zimenezi ndipo anam’dalitsa kwambiri. (Yobu 1:10; 42:12) N’chitsanzo chabwino kwambiri chimenetu Yobu anasonyeza kwa Akristu okwatirana, amuna ndi akazi omwe! N’chifukwa chake Yehova anam’kondadi kwabasi! Koma m’malo mwake, khalidwe la anthu ambiri lerolino likufanana kwambiri ndi zimene zinali kuchitika m’tsiku la Malaki. Mneneri ameneyo anatsutsiratu zimene amuna ambiri anachita pothaŵa akazi awo, nthaŵi zambiri kuti akakwatire akazi ena achitsikana. Guwa la nsembe la Yehova linakutidwa ndi misozi ya akazi okanidwa, ndipo Mulungu anatsutsa awo amene ‘anachita chosakhulupirika’ kwa akazi awo.—Malaki 2:13-16.
Mtsikana Wodzisunga
17. Kodi ndi motani mmene Msulami analili ngati “munda wotsekedwa”?
17 Munthu wachitatu yemwe anasunga kukhulupirika ndiye namwali wa ku Sulami. Pokhala wachitsikana ndi wokongola, si mnyamata wobusa ziweto yekha amene anakopeka naye komanso mfumu ya Israyeli yolemerayo, Solomo. Nkhani yonse yosangalatsayo ya m’Nyimbo ya Solomo, ikusimba kuti Msulamiyo anakhalabe wodzisunga, zimene zinapangitsa kuti ena am’lemekeze. Ngakhale kuti Solomo anakanidwa ndi mtsikanayu, iye anauziridwa kulemba nkhani yake. Mbusa yemwe mtsikanayu anakonda anali kulemekezanso khalidwe la Nyimbo ya Solomo 4:12) M’Israyeli wakale, minda yokongola inkakhala ndi ndiwo zosiyanasiyana zamasamba, maluŵa onunkhira bwino, ndi mitengo yochititsa chidwi. Minda yoteroyo nthaŵi zambiri inkakhala yotchingidwa ndi mpanda wa mitengo yomera kapena ndi khoma ndipo panali khomo limodzi lokha lolowera lomwenso ankalikhoma. (Yesaya 5:5) Kwa mbusayo, kuyera kwa khalidwe la Msulami ndi kusangalatsa kwake zinali ngati munda wokongola kwambiri woterewu. Anali wodzisunga kotheratu. Chikondi chake anali kudzachisonyeza kwa mwamuna wake wam’tsogoloyo basi.
mtsikanayu lodzisunga. Panthaŵi ina mnyamatayo atasinkhasinkha anati Msulamiyo anali ngati “munda wotsekedwa.” (18. Kodi nkhani za Yosefe, Yobu, ndi Msulami zikutikumbutsa chiyani?
18 Pankhani ya kusunga khalidwe labwino, Msulami anasonyeza chitsanzo chabwino koposa kwa akazi achikristu lerolino. Yehova anaona ndipo anayamikira khalidwe labwino la mtsikana wa ku Sulami ameneyu ndipo anam’dalitsa monga momwe anadalitsira Yosefe ndi Yobu. Zochita zawo zosonyeza kukhulupirika zinalembedwa m’Mawu a Mulungu kuti zikhale chitsogozo chathu. Ngakhale kuti nkhani za kuyesayesa kwathu posunga kukhulupirika sizilembedwa m’Baibulo lerolino, Yehova ali ndi “buku la chikumbutso” lolembamo awo ofuna kuchita chifuniro chake. Tisaiwale konse kuti Yehova ‘amatchera khutu’ ndipo amasangalala pamene tiyesetsa kukhalabe ndi khalidwe loyera.—Malaki 3:16.
19. (a) Kodi khalidwe loyera tiyenera kuliona motani? (b) Kodi nkhani yotsatira idzalongosola chiyani?
19 Ngakhale ngati anthu opanda chikhulupiriro angatiseke ndi kutinyoza, ifeyo tikusangalala kuti tikumvera Mlengi wathu wachikondi. Tili ndi khalidwe lapamwamba, khalidwe laumulungu. N’chinthu chonyaditsa, cha mtengo wapatali. Mwa kusungabe khalidwe lathu loyera, tidzasangalala ndi dalitso la Mulungu ndipo tingakhalebe ndi chiyembekezo chowala chodzakhala ndi madalitso osatha m’tsogolo. Koma m’zochitika zenizeni tsopano, kodi tingachitenji kuti tidzisungire khalidwe loyera? Nkhani yotsatira idzayankha funso lofunika kwambiri limeneli.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya March 15, 1983, masamba 29-31.
^ ndime 7 N’zomvetsa chisoni kuti nthaŵi zina Mkristu wopanda mlandu amatha kutenga matenda opatsirana mwa kugonana kwa mwamuna kapena mkazi wake wosakhulupirira amene sanatsatire chitsogozo cha Mulungu.
Kodi Mungalongosole?
• Kodi Baibulo limaphunzitsanji ponena za kugonana?
• Kodi mawu akuti “dama” m’Baibulo amatanthauza chiyani?
• Kodi kukhala ndi khalidwe loyera kumatipindulira motani?
• N’chifukwa chiyani Yosefe, Yobu, ndi namwali wa ku Sulami ali zitsanzo zabwino kwa Akristu lerolino?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 9]
Yosefe anathaŵa kuti asachite chisembwere
[Chithunzi patsamba 10]
Mtsikana wachisulami anali monga “munda wotsekedwa”
[Chithunzi patsamba 11]
Yobu anali ‘atapangana ndi maso ake’